Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 11

Kodi Ubatizo Mungaukonzekele Motani?

Kodi Ubatizo Mungaukonzekele Motani?

“Cikundiletsa kubatizidwa n’ciyani?”—MAC. 8:36.

NYIMBO 50 Pemphelo Langa Lodzipelekela kwa Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

Zungulile dziko lonse, acicepele na acikulile omwe akupita patsogolo na kubatizika (Onani ndime 1-2)

1-2. Ngati palipano simunayelele ubatizo, n’cifukwa ciyani simuyenela kutaya mtima? (Onani cithunzi pacikuto.)

 NGATI mufuna kukabatizika, muli na colinga cabwino kwambili. Kodi ndinu wokonzeka palipano kutenga sitepe imeneyi? Ngati muona kuti ndinu wokonzeka ndipo akulu avomeleza, musazengeleze kubatizika. Umoyo waphindu mu utumiki wa Yehova ukukuyembekezelani.

2 Koma kodi munauzidwapo kuti muyenela kusintha mbali zina pa umoyo wanu musanabatizike? Kapena munazindikila zimenezo panokha? Ngati n’telo, musataye mtima. N’zotheka ndithu kupitabe patsogolo kuti mukayenelele ubatizo, kaya ndinu wacicepele kapena wacikulile.

‘CIKUNDILETSA N’CIYANI?’

3. Kodi nduna ya ku Itiyopiya inam’funsa ciyani Filipo? Nanga pakubuka funso lanji? (Machitidwe 8:36, 38)

3 Ŵelengani Machitidwe 8:36, 38. Nduna ya ku Itiyopiya inafunsa mlaliki Filipo kuti: “Cikundiletsa kubatizidwa n’ciyani?” Nduna ya ku Itiyopiya ija inali kufunitsitsa kubatizika. Koma kodi inali yokonzekadi kutenga sitepe yofunika imeneyo?

Nduna ya ku Itiyopiya inali yofunitsitsa kupitiliza kuphunzila za Yehova (Onani ndime 4)

4. Kodi nduna ya ku Itiyopiya inaonetsa bwanji kuti inali kufunitsitsa kudziŵa zambili?

4 Mwamuna wa ku Itiyopiya uja “anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu.” (Mac. 8:27) Iye ayenela kuti anali wotembenukila ku Ciyuda. Mosakayikila, anaphunzila za Yehova m’Malemba Opatulika Aciheberi. Ngakhale n’conco, anali wofunitsitsa kuphunzila zambili. Mwacitsanzo, kodi mwamunayo anali kucita ciyani pamene Filipo anakumana naye pamsewu? Anali kuŵelenga mpukutu wa mneneli Yesaya. (Mac. 8:28) Cimeneco cinali cakudya cauzimu cotafuna. Nduna ya ku Itiyopiya imeneyo sinakhutile kudziŵa ziphunzitso zoyambilila zokha. Inafunitsitsa kudziŵa zambili.

5. Kodi nduna ya ku Itiyopiya inacitapo ciyani pa zimene inaphunzila?

5 Mwamunayo anali waudindo pansi pa Kandake Mfumukazi ya Itiyopiya. Iye “anali woyang’anila cuma conse ca mfumukaziyo.” (Mac. 8:27) Conco, n’kutheka kuti anali wotangwanika posamalila maudindo ake. Ngakhale n’telo, anapatula nthawi yolambila Yehova. Iye sanangociphunzila coonadi, koma anacitapo kanthu pa zimene anaphunzilazo. Anayenda ulendo wautali kucokela ku Itiyopiya kupita ku Yerusalemu kuti akalambile Yehova pakacisi. Ulendo umenewu unafuna nthawi yoculuka komanso ndalama. Koma zimenezi sizinam’lepheletse kupanga ulendo wokalambila Yehova.

6-7. Kodi nduna ya ku Itiyopiya inapitiliza bwanji kukulitsa cikondi cake pa Yehova?

6 Ndunayo inaphunzila mfundo zingapo zatsopano za coonadi kwa Filipo, kuphatikizapo yakuti Yesu anali Mesiya. (Mac. 8:34, 35) Mwamunayo anakhudzika mtima kwambili ataphunzila zimene Yesu anam’citila. Kodi anacitapo ciyani? Akanafuna, akanasankha kungokhalabe munthu wolemekezeka wotembenukila ku Ciyuda. Koma anakulitsa cikondi cake pa Yehova na Mwana wake. Izi zinam’limbikitsa kupanga cisankho cacikulu cakuti abatizike, n’kukhala wotsatila wa Yesu Khristu. Conco, Filipo ataona kuti munthuyo anali wokonzeka, anam’batiza.

7 Mukatsatila citsanzo ca mdindo wa ku Itiyopiyayu, mungakhale wokonzeka kukabatizika. Inunso mungakambe motsimikiza mtima kuti, “Cikundiletsa kubatizidwa n’ciyani?” Tiyeni tione mmene mungatengele citsanzo ca nduna imeneyo. Iye anapitiliza kuphunzila, anagwilitsa nchito zimene anaphunzilazo, komanso anapitiliza kukulitsa cikondi cake pa Mulungu.

PITILIZANI KUPHUNZILA

8. Kodi Yohane 17:3 imakulimbikitsani kucita ciyani?

8 Ŵelengani Yohane 17:3. Kodi mawu a Yesu amenewa anakulimbikitsani kuyamba kuphunzila Baibo? Ni mmene zinalili kwa ambili a ife. Koma kodi mawu amenewa amatilimbikitsabe kupitiliza kuphunzila? Inde. ‘Kuphunzila za Mulungu yekha woona’ sikudzatha. (Mlal. 3:11) Tiziphunzilabe mpaka kwamuyaya. Tikamaphunzila zambili za Yehova, tidzamuyandikila kwambili.—Sal. 73:28.

9. Kodi tiyenela kucita ciyani tikaphunzila mfundo zoyambilila za coonadi?

9 Kudziŵa Yehova kumayamba mwa kuphunzila mfundo zoyambilila za coonadi. M’kalata yake yopita kwa Aheberi, mtumwi Paulo anachula ziphunzitso zoyambilila zimenezo kuti “mfundo zoyambilila.” Iye sanali kupeputsa “ciphunzitso coyambilila” ayi, koma anali kuyelekezela ciphunzitsoco na mkaka umene mwana amayamwa. (Aheb. 5:12; 6:1) Iye analimbikitsa Akhristu onse kuti apitilize kuphunzila ngakhale mfundo zozama za coonadi za m’mawu a Mulungu. Kodi njala muli nayo yofuna kuphunzila ziphunzitso zozama za m’Baibo? Kodi ndinu wofunitsitsa kukula mwauzimu, popitiliza kuphunzila za Yehova na colinga cake?

10. N’cifukwa ciyani anthu ena zimawavuta kuŵelenga?

10 Koma ambili a ife kuŵelenga kumativuta. Nanga inu bwanji? Kodi kusukulu, munali kucita khama kuŵelenga komanso kuphunzila? Kodi kuphunzilako munali kusangalala nako? Kapena munaona kuti zimakuvutani kuphunzila m’mabuku? Ngati n’conco, sindinu nokha. Yehova adzakuthandizani. Iye ni wangwilo, komanso ni Mphunzitsi wabwino koposa.

11. Kodi Yehova amaonetsa bwanji kuti ni “Mlangizi Wamkulu”?

11 Yehova amadzicha “Mlangizi [wanu] Wamkulu.” (Yes. 30:20, 21) Iye ni Mphunzitsi woleza mtima, wokoma mtima, komanso womvetsa. Amayang’ana zabwino mwa ophunzila ake. (Sal. 130:3) Ndipo satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. Muzikumbukila kuti ndiye anapanga ubongo wanu, umene ni mphatso yabwino ngako. (Sal. 139:14) Conco, mwacibadwa timakhala na cikhumbo cofuna kuphunzila. Mlengi wathu amafuna kuti tipitilize kuphunzila mpaka muyaya, komanso kuti kuphunzilako tizikondwela nako. Conco, tiyenela ‘kulakalaka’ coonadi ca m’Baibo. (1 Pet. 2:2) Dziikileni zolinga zimene mungakwanitse, komanso tsatilani ndandanda yanu yoŵelenga na kuphunzila Baibo. (Yos. 1:8) Mwa thandizo la Yehova, mudzafika posangalala nako kuŵelenga na kuphunzila za iye nthawi zonse.

12. N’cifukwa ninji kuphunzila za umoyo wa Yesu na utumiki wake n’kofunika kwambili?

12 Nthawi zonse muzipatula nthawi yosinkhasinkha za umoyo wa Yesu na utumiki wake. Kutsatila mapazi a Yesu mosamala n’kofunika kwambili kuti titumikile Yehova, maka-maka m’nthawi zino zovuta. (1 Pet. 2:21) Yesu anakamba mosapita m’mbali mavuto amene otsatila ake adzakumana nawo. (Luka 14:27, 28) Komabe, iye anali na cidalilo cakuti otsatila ake oona angakhalebe okhulupilika kwa Mulungu, monga mmene iye anacitila. (Yoh. 16:33) Phunzilani za umoyo wa Yesu, ndipo dziikileni colinga cotengela citsanzo cake pa umoyo wanu wa tsiku na tsiku.

13. Kodi simuyenela kuleka kum’pempha ciyani Yehova? Cifukwa ciyani?

13 Kungokhala naco cidziŵitso sikokwanila. Ciyenela kutithandiza kudziŵa zambili za Yehova, na kukulitsa makhalidwe monga cikondi komanso cikhulupililo mwa iye. (1 Akor. 8:1-3) Pamene mukupitiliza kuphunzila, muzim’pempha Yehova kuti akuwonjezeleni cikhulupililo. (Luka 17:5) Iye ni wokonzeka kuyankha mapemphelo otelo. Cikhulupililo ceniceni cotsamila pa kudziŵa Mulungu molondola cidzakuthandizani kupitabe patsogolo.—Yak. 2:26.

OSALEKA KUGWILITSA NCHITO ZIMENE MUMAPHUNZILA

Cigumula cisanayambe, Nowa na banja lake anagwilitsa nchito mokhulupilika zimene anaphunzila (Onani ndime 14)

14. Kodi mtumwi Petulo anaonetsa bwanji kufunika kogwilitsila nchito zimene timaphunzila? (Onaninso cithunzi.)

14 Mtumwi Petulo anagogomeza kuti otsatila a Khristu sayenela kuleka kugwilitsa nchito zimene amaphunzila. Iye anachula nkhani ya m’Baibo yokamba za Nowa. Yehova anauza Nowa kuti adzawononga anthu onse oipa a m’nthawi yake na cigumula. Kungodziŵa cabe kuti kudzabwela cigumula sikunali kokwanila kuti Nowa na banja lake adzapulumuke. Onani kuti Petulo anakamba zimene zinacitika Cigumula cisanacitike, “pamene cingalawa cinali kupangidwa.” (1 Pet. 3:20) Inde, Nowa na banja lake anagwilitsa nchito zimene Mulungu anawaphunzitsa mwa kukhoma cingalawa. (Aheb. 11:7) Kenako, Petulo anayelekezela ubatizo na zimene Nowa anacita polemba kuti: “Cofanana ndi cingalawaco cikupulumutsanso inuyo tsopano. Cimeneci ndico ubatizo.” (1 Pet. 3:21) Conco, zimene mukucita palipano pokonzekela ubatizo tingaziyelekezele na nchito imene Nowa na banja lake anagwila yomanga cingalawa kwa zaka zambili. Nanga inuyo muyenela kucita ciyani kuti mukonzekele ubatizo?

15. Kodi kulapa mocokela pansi pa mtima kumaloŵetsamo ciyani?

15 Coyamba cimene tiyenela kucita, ni kulapa macimo athu mocokela pansi pa mtima. (Mac. 2:37, 38) Tikalapa motelomo, tidzasintha zenizeni osati mwaciphamaso. Kodi munaleka makhalidwe osakondweletsa Yehova, monga ciwelewele, kukoka fodya, kapena kukamba mawu oipa? (1 Akor. 6:9, 10; 2 Akor. 7:1; Aef. 4:29) Ngati simunatelo, pitilizani kupanga masinthidwe. Uzankoni mphunzitsi wanu wa Baibo, kapena pemphani thandizo kwa akulu mumpingo. Ngati ndinu wacicepele ndipo mumakhala na makolo anu, pitilizani kuwapempha kuti akuthandizeni kuthetsa makhalidwe oipa amene angakulepheletseni kubatizika.

16. Kodi kukhala na pulogilamu yocita zauzimu kumaphatikizapo ciyani?

16 Cina, khalani na pulogilamu yocita zauzimu. Izi ziphatikizapo kupezeka kumisonkhano yacikhristu na kutengako mbali. (Aheb. 10:24, 25) Ndipo mukayenelezedwa kuti muzilalikila pamodzi na mpingo, muzionetsetsa kuti mumalalikila nthawi zonse. Mukamatengako mbali mokwana pa nchito yopulumutsa moyo imeneyi, mudzayamba kuikonda kwambili. (2 Tim. 4:5) Ngati ndinu wacicepele ndipo mukhala na makolo anu, dzifunseni kuti: ‘Kodi makolo anga amacita kunikumbutsa nthawi zonse kuti nizipezeka kumisonkhano na kupita mu ulaliki? Kapena nimacita zimenezi modzifunila?’ Mukamacita zimenezi modzifunila, mumaonetsa cikhulupililo canu, cikondi canu, komanso ciyamikilo canu kwa Yehova Mulungu. Zimenezi ni “nchito zosonyeza kuti ndinu wodzipeleka kwa Mulungu,” inde mphatso zimene mumapatsa Yehova. (2 Pet. 3:11; Aheb. 13:15) Mphatso zonse zimene timapeleka mwa kufuna kwathu osati mokakamizika, zimakondweletsa Mulungu wathu. (Yelekezelani na 2 Akorinto 9:7.) Timacita zimenezi cifukwa timamva bwino kupatsa Yehova zabwino koposa.

PITILIZANI KUKULITSA CIKONDI CANU PA YEHOVA

17-18. Ni khalidwe lofunika liti limene lingakuthandizeni kupita patsogolo kuti mukabatizike? Nanga n’cifukwa ciyani? (Miyambo 3:3-6)

17 Pamene mukuyesetsa kupita patsogolo kuti mukabatizike, mudzakumana na mayeso. Anthu ena angakunyodoleni, kukutsutsani, ngakhale kukuzunzani cifukwa ca cikhulupililo canu catsopano. (2 Tim. 3:12) Pamene mukuyesetsa kuti mugonjetse khalidwe loipa, nthawi zina mungabwelezenso khalidwe loipalo. Kapena mungataye mtima na kukhumudwa poona kuti simukukwanilitsa msanga colinga canu. N’ciyani cingakuthandizeni kusabwelela m’mbuyo? Ni cikondi pa Yehova, khalidwe lofunika kwambili.

18 Cikondi canu pa Yehova ndilo khalidwe lofunika kwambili limene muli nalo. (Ŵelengani Miyambo 3:3-6.) Kum’konda kwambili Mulungu kudzakuthandizani kuti mupambane polimbana na mavuto. Nthawi zambili, Baibo imakamba za cikondi cosasintha ca Yehova pa atumiki ake. Izi zitanthauza kuti iye sadzasiya atumiki ake ngakhale pang’ono, kapena kuleka kuwakonda. (Sal. 100:5) Kumbukilani kuti munalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu. (Gen. 1:26) Kodi mungaonetse bwanji cikondi cimeneci?

Mungaonetse ciyamikilo canu kwa Yehova tsiku lililonse (Onani ndime 19) b

19. Kodi mungakulitse bwanji ciyamikilo canu pa zonse zimene Yehova wakucitilani? (Agalatiya 2:20)

19 Coyamba, khalani woyamikila. (1 Ates. 5:18) Tsiku lililonse muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti amanikonda?’ Kenako, muyamikileni Yehova m’mapemphelo anu, na kuchula mwacindunji zimene wakucitilani. Muzitha kuona zabwino zimene Yehova amakucitilani inuyo panokha, na kuti amatelo cifukwa amakukondani. Izi n’zimene mtumwi Paulo anazindikila. (Ŵelengani Agalatiya 2:20.) Dzifunseni kuti, ‘Kodi inenso nimafuna kumuonetsa cikondi cimene iye amanionetsa?’ Cikondi canu pa Yehova cidzakuthandizani kupitiliza kukaniza mayeselo, komanso kupilila mavuto. Cidzakulimbikitsani kulambila Yehova nthawi zonse, poonetsa kuti mumam’konda Atate wanu wakumwamba.

20. Kodi muyenela kucita ciyani kuti mudzipatulile kwa Yehova? Nanga n’cifukwa ciyani ici n’cisankho cofunika kwambili?

20 M’kupita kwa nthawi, cikondi canu pa Yehova cidzakulimbikitsani kupeleka pemphelo lapadela lodzipatulila kwa Mulungu. Kumbukilani kuti mukadzipatulila kwa Yehova, mudzakhala na ciyembekezo cabwino ici: Mungakhale wake wa Yehova ku umuyaya wonse. Lonjezo limene munapanga podzipatulila lidzakuthandizani kutumikilabe Yehova pa nthawi zabwino ngakhale zovuta. Ndipo simufunikilanso kumulonjeza kaciŵili Yehova. N’zoona kuti tikadzipatulila timapanga cisankho cacikulu kwambili. Koma ganizilani izi: Mudzapanga zisankho zambili pa umoyo wanu, ndipo zina mwa izo zidzakhala zabwino kwambili. Koma simudzapangapo cisankho cabwino kuposa copatulila moyo wanu kwa Yehova. (Sal. 50:14) Satana adzayesa kucepetsa cikondi canu pa Atate wanu kuti akupangitseni kusakhulupilika kwa Mulungu. Conde, musamulole Satana kuti apambane! (Yobu 27:5) Kulimba kwa cikondi canu pa Yehova kudzakuthandizani kusungabe lonjezo lanu limene munapanga podzipatulila, komanso mudzamuyandikila kwambili Atate wanu wakumwamba.

21. N’cifukwa ninji ubatizo sindipo pothela ulendo, koma m’poyambila cabe?

21 Mukadzipatulila kwa Yehova m’pemphelo, uzani akulu mumpingo wanu kuti mukufuna kukabatizika. Nthawi zonse kumbukilani kuti ubatizo sindipo pothela ulendo. Wangokhala poyambila ulendo wotumikila Yehova mpaka muyaya. Conco, yambani palipano kukulitsa cikondi canu pa Atate wanu. Dziikileni zolinga kuti cikondi canu cizikulilako tsiku na tsiku. Kucita zimenezo kudzakufikitsani ku ubatizo. Limenelo lidzakhala tsiku losangalatsa. Koma ici n’ciyambi cabe. Lekani kuti cikondi canu pa Yehova na Mwana wake cipitilize kukulilakulila mpaka muyaya!

NYIMBO 135 Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”

a Kuti tipite patsogolo na kukayenelela ubatizo, coyamba, tikhale na colinga cabwino. Cotsatila, titenge masitepe ofunikila. Pogwilitsa nchito citsanzo ca nduna ya ku Itiyopiya, tikambilane masitepe amene wophunzila Baibo angatenge kuti akayenelele ubatizo.

b MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mlongo wacitsikana akulankhula na Yehova m’pemphelo, kumuyamikila pa zimene wam’citila.