Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
N’cifukwa ciyani munthu wochedwa “Uje” ananena kuti ‘akanawononga’ colowa cake akanakwatila Rute? (Rute 4:1, 6)
M’nthawi zochulidwa m’Baibo, ngati mwamuna wokwatila wamwalila koma osabelekako mwana kwa mkazi wake, panali kubuka mafunso monga awa: N’ciyani cidzacitikila malo ake alionse amene anali nawo? Kodi dzina la banja lake life? Cilamulo ca Mose cinali kuyankha mafunso amenewa.
N’ciyani cinali kucitikila malo a mwamuna amene wamwalila kapena amene wasauka moti n’kugulitsa malo ake? M’bale kapena wacibale wapafupi wa malemuyo ndiye anali kuwombola malowo kapena kuwagulanso. Izi zinali kuthandiza kuti malowo asacoke m’banjalo.—Lev. 25:23-28; Num. 27:8-11.
Kodi cinali kucitika n’ciyani kuti dzina la banja la malemuyo lisafe? Mwa kucita ukwati wa cokolo, umenenso unagwilitsidwa nchito pa Rute. Mwamuna anali kukwatila mkazi wa m’bale wake amene anamwalila, kapena kuti kuloŵa cokolo. Anali kucita izi kuti abeleke mwana kwa mkaziyo, amene adzachedwa na dzina la malemuyo n’kutenganso malo a malemuyo monga colowa. Makonzedwe acikondi amenewa anali kuthandizanso kuti akazi amasiye azisamalidwa.—Deut. 25:5-7; Mat. 22:23-28.
Citsanzo ni nkhani ya Naomi. Iye anakwatiwa kwa Elimeleki. Mwamuna wake komanso ana ake aamuna aŵili atamwalila, analibenso aliyense womusamalila. (Rute 1:1-5) Naomi atabwelela ku Yuda, anauza mpongozi wake Rute kuti apemphe Boazi kugulanso malo awo. Boazi anali wacibale wapafupi wa Elimeleki. (Rute 2:1, 19, 20; 3:1-4) Koma Boazi anakumbukila kuti panali wacibale wina wapafupi kwambili kuposa iye, amene Baibo imamuchula kuti “Uje.” Conco, munthuyo ndiye anayenela kukhala woyamba kupatsidwa mwayi wogulanso malowo.—Rute 3:9, 12, 13.
Poyamba, “Uje” anafuna kuthandiza mwa kugulanso malowo. (Rute 4:1-4) Ngakhale kuti munthuyo anadziŵa kuti adzatayilapo ndalama pocita zimenezo, anazindikila kuti cifukwa ca ukalamba, Naomi sangabelekenso mwana amene angatenge malo a Elimeleki kukhala colowa cake. Conco, malowo akanakhalanso a “Uje,” kuphatikiza pa colowa cimene anali naco kale. Izi zinaoneka kuti zidzam’pindulila kutsogolo.
Koma Uje atadziŵa kuti ngati angacite zimenezo angafunike kukwatila Rute, anasintha maganizo. Iye anati: “Sinditha kuuwombola, kuopela kuti ndingawononge colowa canga.” (Rute 4:5, 6) N’cifukwa ciyani anasintha maganizo?
Ngati Uje kapena munthu wina akanakwatila Rute, n’kubeleka mwana wamwamuna, mwanayo akanatenga malo a Elimeleki kukhala colowa. Kodi izi ‘zikanawononga’ bwanji “colowa” ca Uje? Ngakhale kuti Baibo siifotokoza, n’kutheka kuti cikanawonongeka mwanjila izi:
Yoyamba, popeza kuti pamapeto pake malowo sanali kudzakhala ake, koma a mwana wamwamuna wa Rute, iye anaona kuti n’kutaya cabe ndalama kuwagula.
Yaciŵili, anaopa udindo wopezela cakudya Naomi na Rute komanso kuwasamalila.
Yacitatu, Rute akanabeleka ana ena kwa Uje, anawo akanagaŵana colowa ca Uje ndi ana ake ena amene anali nawo kale.
Yacinayi, ngati Uje analibe ana ake-ake ena, mwana wamwamuna amene Rute akanabeleka akanakhala na ufulu wotenga malo a Elimeleki komanso a Uje. Conco, malo ake akanakhala a mwana wochedwa na dzina la Elimeleki, osati lake. Uje sanafune kutaya colowa cake pothandiza Naomi. Anaona kuti n’kwabwino kusiyila udindowo Boazi, amene anali woombola wotsatila. Boazi anatenga udindowo cifukwa anafuna “kuti dzina la mwamuna amene . . . anamwalila libwelele pacolowa cake.”—Rute 4:10.
Cioneka kuti Uje anali kufuna kwambili kuteteza dzina lake kuti lisafe komanso colowa cake. Anali wodzikonda. Ngakhale kuti Uje anayesetsa kuteteza dzina lake, masiku ano dzinalo sitilidziŵa. Cina, munthuyu anataya mwayi wapadela umene Boazi anakhala nawo, wokhala mu mzele wobadwila Mesiya, Yesu Khristu. Cifukwa codzikonda, Uje anapewa kuthandiza munthu wovutika, ndipo cotulukapo coipa n’cakuti anauphonya mwayi wapadelawo.—Mat. 1:5; Luka 3:23, 32.