Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu

Kugwilitsa Nchito Bwino Mbali Yakuti “N’ciani Catsopano?”

Mbali yakuti “N’ciani Catsopano” ya pa JW Laibulale® komanso pa jw.org, imaonetsa zofalitsa zatsopano zimene zangotuluka kumene. Kodi mbaliyi mungaigwilitse nchito motani kuti mudziŵe zatsopano?

Pa JW Laibulale

  • Nkhani iliyonse ya mu mpambo wa nkhani zofanana, imatulutsidwa mwa kukonzanso mbali yakuti article series. Conco pamene mpambo wa nkhani waonekela pa mbali yakuti “N’ciyani Catsopano,” citani daunilodi mpambo watsopanowo. Kenako mungaŵelenge nkhani yatsopanoyo imene imakhala yoyamba, motsatila deti pamene nkhani zinatuluka pa mndandandawo.

  • Zofalitsa zina monga magazini, mwina simungazitsilize kuŵelenga pa nthawi imodzi. Kuti muipeze mosavuta magazini imene simunatsilize kuiŵelenga, iikeni pa mbali yakuti Favorites kufikila mutaitsiliza kuŵelenga.

PA JW.ORG

Zinthu zina monga nkhani za nyuzi na zilengezo, zimaonekela pa webusaiti ya jw.org pokha, osati pa JW Laibulale. Muzionapo kaŵili-kaŵili pa tsamba lakuti “Onani Zatsopano” pa webusaiti kuti muone nkhani zatsopano.