Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 14

“Mwakutelo, Onse Adzadziŵa Kuti Ndinu Ophunzila Anga”

“Mwakutelo, Onse Adzadziŵa Kuti Ndinu Ophunzila Anga”

“Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—YOH. 13:35.

NYIMBO 106 Kukulitsa Mkhalidwe wa Cikondi

ZIMENE TIKAMBILANE a

Kodi anthu ambili amene si Mboni amakhudzika motani akaona cikondi pakati pa anthu a Yehova? (Onani ndime 1)

1. Kodi anthu ambili amene amapezeka ku misonkhano yathu amacita cidwi na ciyani? (Onaninso cithunzi.)

 YELEKEZANI kuti mwamuna na mkazi wake apezeka ku msonkhano kwa nthawi yoyamba pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Iwo acita cidwi kwambili poona kuti abale na alongo awalandila na manja aŵili, komanso poona cikondi pakati pawo. Pomwe akubwelela kunyumba, mkaziyo akuuza mwamuna wake kuti, ‘Mboni za Yehova n’zosiyana kwambili na anthu ena.’

2. N’ciyani cimapangitsa anthu ena kupunthwa?

2 Kukamba zoona, cikondi cimene Akhristu mu mpingo amaonetsana n’capadela kwambili. Ngakhale n’telo, Mboni za Yehova n’zopanda ungwilo. (1 Yoh. 1:8) Conco, tikafika powadziŵa bwino abale na alongo mumpingo, tidzadziŵanso zophophonya zawo. (Aroma 3:23) N’zacisoni kuti ena alola zophophonya za ena kuwapunthwitsa.

3. Kodi cizindikilo ca otsatila oona a Yesu n’ciyani? (Yohane 13:34, 35)

3 Kumbukilani lemba la mutu wa nkhani ino. (Ŵelengani Yohane 13:34, 35.) Kodi cizindikilo codziŵila otsatila oona a Khristu n’ciyani? Ni cikondi, osati ungwilo ayi. Onani kuti Yesu sanakambe kuti: ‘Mwakutelo, mudzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga.’ Koma anati: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga.” Apa Yesu anaonetsa kuti otsatila ake komanso anthu akunja, adzazindikila otsatila ake oona, cifukwa ca cikondi cimene amaonetsana pakati pawo.

4. Kodi anthu ena angafunse ciyani za Akhristu oona?

4 Anthu amene si Mboni za Yehova angafunse kuti: ‘Kodi cikondi cimadziŵitsa bwanji otsatila oona a Yesu? Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti amawakonda atumwi ake? Nanga zingatheke bwanji masiku ano kutengela citsanzo cake?’ Ngakhale Mboni zingacite bwino kuganizila mayankho a mafunso amenewa. Kucita zimenezi kungatithandize kuonetsa cikondi mokulillapo, maka-maka tikamaona zophophonya za ena.—Aef. 5:2.

N’CIFUKWA CIYANI CIKONDI NDICO KHALIDWE LALIKULU LODZIŴILA OTSATILA OONA AKHRISTU?

5. Fotokozani mawu a Yesu a pa Yohane 15:12, 13.

5 Yesu ananena momveka bwino kuti otsatila ake adzaonetsana cikondi m’njila yapadela. (Ŵelengani Yohane. 15:12, 13.) Onani kuti Yesu anawalamula kuti: “Mukondane monga mmene inenso ndakukondelani.” Kodi izi zitanthauza ciyani? Monga anakambila Yesu, ici n’cikondi codzimana cimene cimasonkhezela Mkhristu kufika pofela wokhulupilila mnzake kukakhala kofunika. b

6. Kodi mawu a Mulungu amaonetsa bwanji kufunika kwa cikondi?

6 Mawu a Mulungu amakamba kuti cikondi n’cofunika kwambili. Kwa anthu ambili, pa Malemba awo apa mtima palinso awa: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yoh 4:8) “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mat 22:39) “Cikondi cimakwilila macimo oculuka.” (1 Pet. 4:8) “Cikondi sicitha.” (1 Ako 13:8) Malemba amenewa na ena amaonetsa poyela kufunika kokulitsa khalidwe la Mulungu limeneli na kulionetsa.

7. N’cifukwa ciyani n’zosatheka Satana kugwilizanitsa anthu m’cikondi ceniceni?

7 Anthu ambili amafunsa kuti: ‘Kodi ningacidziŵe bwanji cipembedzo coona? Zipembedzo zonse zimati zimaphunzitsa coonadi, koma ciliconse cimaphunzitsa zosiyana ponena za Mulungu.’ Satana wakwanitsa kusoceletsa anthu pokhazikitsa zipembedzo zambili zonyenga. Ngakhale n’telo, sangakwanitse kugwilizanitsa anthu padziko lonse kuti akhale okondana. Ni Yehova yekhayo amene angacite zimenezo. Izi zili conco cifukwa cikondi ceniceni cimacokela kwa Yehova. Anthu okhawo amene ali na mzimu wa Yehova komanso dalitso lake, ndiwo amaonetsana cikondi. (1 Yoh. 4:7) N’cifukwa cake Yesu anati otsatila ake oona adzakhala na cikondi ceniceni pakati pawo.

8-9. Kodi anthu ambili amakhudzika motani akaona cikondi cimene Mboni za Yehova zimaonetsana?

8 Monga Yesu anakambilatu, anthu ambili afika powadziŵa otsatila enieni a Yesu poona cikondi ceniceni cimene amaonetsana. Citsanzo ni zimene m’bale Ian anaona pa msonkhano woyamba umene anapezekapo. Msonkhanowo unacitikila m’bwalo la maseŵelo kufupi na kwawo. M’miyezi yapambuyo, Ian analikonso ku bwalo limeneli koma kukaonelela maseŵela. Iye anati: “Panali kusiyana kwakukulu pakati pa anthu amene anaonelela maseŵela na Mboni zimene zinadzacita msonkhano. A Mboni za Yehova anali aulemu komanso ovala bwino. Naonso ana awo anaonetsa khalidwe labwino.” Iye anapitiliza kuti: “N’nakopeka kwambili kuona kuti anthu amenewo anaoneka okhutila komanso amtendele, zimene inenso n’nali kuzifunitsitsa kwambili. Sinikumbukila iliyonse ya nkhani zinakambidwa pa tsikulo, koma siniiŵala makhalidwe abwino amene Mboni zinaonetsa.” c Cikondi ceniceni pa wina na mnzake n’cimene cimabala makhalidwe abwino amenewa. Timacita nawo mwaulemu komanso mokoma mtima abale na alongo athu cifukwa cakuti timawakonda.

9 N’zimenenso zinacitikila m’bale wina dzina lake John, pamene anayamba kufika ku misonkhano ya mpingo. Iye anati: “N’nacita cidwi poona kuti aliyense kumeneko amaonetsa mzimu waubwenzi. Anaoneka ngati angwilo kwa ine. Poona cikondi cawo ceniceni, n’nakhulupilila kuti napeza cipembedzo coona.” d Zocitika ngati zimenezi komanso zina zambili, zimatsimikizila kuti anthu a Yehova ni Akhristu oona.

10. Ni panthawi iti maka-maka pomwe timakhala na mwayi woonetsa cikondi cacikhristu? (Onaninso mawu a m’munsi.)

10 Monga takambila kuciyambi, okhulupilila anzathu nawonso ni opanda ungwilo. Nthawi zina, iwo angakambe kapena kucita zinthu zimene zingatikhumudwitse. e (Yak. 3:2) Zaconco zikacitika, timakhala na mwayi woonetsa cikondi cacikhristu mwa zokamba zathu komanso zocita zathu. Kuti ticite zimenezi, tingatengele bwanji citsanzo cimene Yesu anapeleka?—Yoh. 13:15.

KODI YESU ANAONETSA BWANJI KUTI ANALI KUWAKONDA ATUMWI AKE?

Yesu anacita nawo mwacikondi atumwi ake mosasamala kanthu na zophophonya zawo (Onani ndime 11-13)

11. Kodi Yakobo na Yohane anaonetsa mzimu wotani? (Onaninso cithunzi.)

11 Yesu sanayembekezele otsatila ake kucita zinthu mwangwilo. M’malo mwake, anali kuwathandiza mwacikondi kuthetsa makhalidwe oipa, kuti Yehova awayanje. Pa nthawi ina, atumwi ake aŵili—Yakobo na Yohane—anapempha amayi awo kuti apite kwa Yesu kukawapemphela udindo wapamwamba mu Ufumu wa Mulungu. (Mat. 20:20, 21) Mwakutelo, Yakobo na Yohane anaonetsa mzimu wodzikuza komanso wodzikonda.—Miy. 16:18.

12. Kodi Yakobo na Yohane ndiwo okha anaonetsa mzimu woipa? Fotokozani.

12 Yakobo na Yohane sindiwo okha anaonetsa mzimu wosayenela pa cocitikaco. Ponena za atumwi ena, Baibo imati: “Ophunzila 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya ndi amuna aŵili apachibalewo.” (Mat. 20:24) Tangoganizilani mkangano umene unabuka pakati pa Yakobo, Yohane, komanso atumwi enawo. Mwina ena a iwo anakamba kuti: ‘Kodi mumadziona kuti ndinu ndani kuti mupemphe malo apamwamba mu Ufumu? Sindinu nokha amene mwagwila nchito molimbika na Yesu. Nafenso ndife oyenelela kulandila mautumiki apadela amenewo!’ Mulimonsemo, atumwiwo analola cocitikaco kusokoneza cikondi cawo capaubale kwakanthawi.

13. Kodi Yesu anacitapo ciyani pa zophophonya za atumwi ake? (Mateyu 20:25-28)

13 Kodi Yesu anacitanji na cocitikaci? Iye sanakhumudwe nawo atumwiwo. Ndipo sanakambe kuti adzawasiya n’kufuna-funa atumwi ena amene ni odzicepetsa kwambili, komanso amene azikondana nthawi zonse. Komabe, Yesu anakambilana nawo moleza amuna oona mtima amenewo. (Ŵelengani Mateyu 20:25-28.) Iye anapitiliza kucita nawo mwacikondi atumwiwo, ngakhale kuti aka sikanali koyamba kapena kothela kukangana za amene anali wamkulu pakati pawo.—Maliko 9:34; Luka 22:24.

14. Kodi atumwi a Yesu anakula na mzimu wotani?

14 Mosakayikila, Yesu anaganizila mmene atumwi akewo anakulila. (Yoh. 2:24, 25) Iwo anakulila pakati pa atsogoleli acipembedzo amene anali kulimbikitsa kwambili kuchuka komanso kufuna maudindo. (Mat. 23:6) Atsogoleli acipembedzo aciyuda amenewo analinso kudziona kuti ni olungama kuposa ena. f (Luka 18:9-12) Yesu anadziŵa kuti mzimu umenewo ukanakhudza mmene atumwi ake anali kudzionela komanso kuonela anthu ena. (Miy. 19:11) Iye sanayembekezele ophunzila ake kucita zinthu mwangwilo. Ndipo akalakwitsa, anali kuleza nawo mtima. Anadziŵa kuti iwo anali anthu abwino. Conco, moleza mtima anali kuwathandiza kuti azikondana, komanso kuti agonjetse mzimu wodzikuza ndiponso wodzikonda.

TINGATENGELE BWANJI CITSANZO CA YESU?

15. Kodi tiphunzilapo ciyani pa cocitika ca Yakobo na Yohane?

15 Tingaphunzile zambili pa cocitika ca Yakobo na Yohane. Iwo analakwa kupempha malo apamwamba mu Ufumu. Koma naonso atumwi enawo analakwa polola cocitikaco kusokoneza mgwilizano wawo. Ngakhale n’telo, Yesu anacita nawo mokoma mtima komanso mwacikondi atumwi onse 12 amenewo. Kodi tiphunzilapo ciyani? N’zoona kuti cimatiŵaŵa ena akatilakwila. Ngakhale n’conco, tiyenela kucita nawo mwacikondi komanso mokoma mtima. N’ciyani cingatithandize? Tikakhumudwa na zimene Mkhristu mnzathu wacita, tizidzifunsa kuti: ‘N’cifukwa ciyani zimene wacita zikuvutitsa kwambili maganizo anga? Kapena zavumbula khalidwe loipa limene niyenela kuthetsa? Kodi n’kutheka kuti munthu amene ananikhumudwitsa akulimbana na mavuto ena ake? Ngakhale kuti nakhumudwa pa cifukwa comveka, kodi siningamuonetse cikondi codzimana mwa kunyalanyaza colakwaco?’ Tikamacita nawo mwacikondi anthu ena, timaonetsa kuti ndife otsatila oona a Yesu.

16. N’ciyani cina cimene tingaphunzile kwa Yesu?

16 Cina cimene tiphunzila kwa Yesu n’cakuti tiyenela kuwamvetsa okhulupilila anzathu. (Miy. 20:5) Yesu amatha kuona za mumtima mwa munthu, koma ife sitingathe. Koma tingathe kulolela zophophonya za abale na alongo athu. (Aef. 4:1, 2; 1 Pet. 3:8) N’cosavuta kucita zimenezi tikafika powadziŵa bwino. Ganizilani citsanzo ici.

17. Kodi wadela wina anapindula bwanji cifukwa coyesetsa kum’dziŵa bwino wokhulupilila mnzake?

17 Woyang’anila dela wina ku East Africa amakumbukila m’bale wina amene anali kumuona kuti ni wovuta kucita naye. Kodi wadelayo anacitanji? Iye anati: “M’malo momupewa m’baleyo, n’naganiza zoti nim’dziŵe bwino.” Kucita zimenezo kunathandiza wadelayo kudziŵa zimene m’baleyo anapitamo kuti akhale na umunthu wotelo. Iye anapitiliza kuti: “N’tazindikila mmene m’baleyo anavutikila kuti aiŵale zimene anapitamo, ndiponso mmene wasinthila kwambili, n’nayamba kucita naye cidwi. Ndipo tinayamba kugwilizana kwambili.” Ndithudi, tikamayesetsa kuwadziŵa bwino abale na alongo athu, cidzakhala cosavuta kuwaonetsa cikondi.

18. Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati Mkhristu mnzathu akatikhumudwitsa? (Miyambo 26:20)

18 Nthawi zina, tingaone kuti tiyenela kukambilana naye Mkhristu mnzathu amene anatilakwila. Koma coyamba, tingacite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi nikudziŵa bwino zonse zimene zinacitika?’ (Miy. 18:13) ‘Kodi n’kutheka kuti sicinali colinga cake kuti anikhumudwitse?’ (Mlal. 7:20) ‘Kodi inenso n’nalakwilapo wina mwanjila imeneyi?’ (Mlal. 7:21, 22) ‘Ngati ningakambilane naye nkhaniyo, kodi zidzangowonjezela mavuto?’ (Ŵelengani Miyambo 26:20.) Tikamaganizila mafunso ngati amenewa, cikondi cathu pa m’bale wathuyo cidzatilimbikitsa kungonyalanyaza colakwaco.

19. Kodi mudzayesetsa kucita ciyani?

19 Monga gulu, Mboni za Yehova zaonetsa kuti ndizo otsatila oona a Yesu. Ndipo aliyense payekha amaonetsa kuti ni wotsatila weniweni wa Yesu, akamaonetsa cikondi codzimana kwa abale na alongo, mosayang’ana zophophonya zawo. Mwakutelo, timathandiza ena kuzindikila cipembedzo coona, komanso kugwilizana nafe pa kulambila Yehova, Mulungu wacikondi. Conco, tiyeni tiziyesetsa kumaonetsana cikondi, cimene cimadziŵitsa Akhristu oona.

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

a Anthu ambili amakopeka na coonadi akaona cikondi ceniceni cimene timaonetsana. Komabe, cifukwa ca kupanda ungwilo, nthawi zina cingakhale covuta kucita mwacikondi na Akhristu anzathu. Tiyeni tione cifukwa cake kuonetsana cikondi n’kofunika kwambili, komanso mmene tingatengele citsanzo ca Yesu tikamaona zophophonya za ena.

c Onani nkhani yakuti Tsopano Ndinapeza Cholinga cha Moyo Wanga,” mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya November 1, 2012, masa. 13-14.

d Onani nkhani yakuti “Zinthu Zinkaoneka Ngati Zikundiyendera Bwino,” mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya May 1, 2012, masa. 18-19.

e Nkhani ino siikamba za macimo aakulu oyenela kusamalidwa na akulu, monga aja ochulidwa pa 1 Akorinto 6:9, 10.

f Patapita zaka zambili, rabi wina anati: “M’dzikoli anthu olungama monga Abulahamu alimo osacepela 30. Ngati alipo 30, ine na mwana wanga ndife ena mwa iwo. Ngati alipo 10, ine na mwana wanga tili pakati pawo. Ngati alipo asanu, ine na mwana wanga tili pakati pawo. Ngati alipo aŵili, ndine na mwana wanga. Ngati alipo mmodzi, ameneyo ndine.”