Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 10

N’cifukwa Ciyani Muyenela Kubatizika?

N’cifukwa Ciyani Muyenela Kubatizika?

“Aliyense wa inu abatizidwe.”—MAC. 2:38.

NYIMBO 34 N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. N’ciyani cimacitika nthawi zambili anthu akamabatizika? Nanga inunso mungacite bwino kuganizila za ciyani?

 YELEKEZANI kuti mukuona kagulu ka anthu opita ku ubatizo. Mukuwamva akuyankha mofuula mafunso aŵili asanabatizidwe. Acibale awo komanso anzawo ali na cimwemwe codzaza tsaya. Pamene obatizikawo akutuluka m’madzi, mukumva anthu akuwomba m’manja, ndipo nkhope zawo ni zowala na cimwemwe. Mlungu uliwonse, anthu masauzande amatenga sitepe imeneyi, n’kukhala Mboni zobatizika zodzipatulila kwa Yehova Mulungu.

2 Nanga inu mudzaitenga liti sitepe imeneyi? Ngati muganizila zobatizika, ndinu munthu wosiyana na anthu ambili m’dziko loipali cifukwa ‘mukufuna-funa Yehova.’ (Sal. 14:1, 2) Nkhaniyi inalembedwela inu, kaya ndinu wacicepele kapena wacikulile. Koma ena a ife amene tinabatizika kale timafunanso kukulitsa cikhumbo cathu cotumikila Yehova kwamuyaya. Tsopano, tiyeni tikambilane zifukwa zitatu pa zifukwa zambili zomwe tili nazo zotumikila Yehova.

MUMAKONDA COONADI NA CILUNGAMO

Satana wakhala akuipitsa dzina la Yehova kwa zaka masauzande, ndipo akupitilizabe kutelo (Onani ndime 3-4)

3. N’cifukwa ninji anthu a Yehova amacikonda coonadi na cilungamo? (Salimo 119:128, 163)

3 Yehova analangiza anthu ake kuti ‘azikonda coonadi.’ (Zek. 8:19) Yesu analimbikitsa otsatila ake kufuna-funa cilungamo. (Mat. 5:6) Izi zitanthauza kuti munthu ayenela kukhala na cikhumbo cacikulu cofuna kucita coyenela, cabwino, kamanso coyela pamaso pa Mulungu. Kodi inu mumacikonda coonadi na cilungamo? Sitikaika konse kuti mumatelo. Mumadana na mabodza, komanso zoipa za mtundu uliwonse. (Ŵelengani Salimo 119:128, 163.) Munthu wonena mabodza amatengela Satana, wolamulila wadzikoli. (Yoh. 8:44; 12:31) Cimodzi mwa zolinga za Satana ni kuipitsa dzina loyela la Yehova Mulungu. Satana wakhala akufalitsa mabodza ponena za Mulungu kucokela pa cipanduko ca mu Edeni. Iye anapangitsa anthu kuganiza kuti Yehova ni Wolamulila wodzikonda komanso wosaona mtima, amene amamana anthu zinthu zabwino. (Gen. 3:1, 4, 5) Mabodza a Satana amenewo akupitiliza kupangitsa anthu kuganiza kuti Yehova ni wolamulila woipa. Anthu akasankha ‘kusakonda coonadi,’ Satana angawapangitse kucita zosalungama komanso zoipa za mtundu uliwonse.—Aroma 1:25-31.

4. Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti ni “Mulungu wacoonadi”? (Onaninso cithunzi.)

4 Yehova ni “Mulungu wacoonadi,” ndipo anthu amene amamukonda amawaphunzitsa coonadico. (Sal. 31:5) Mwakutelo, amawathandiza kumasuka ku mabodza a Satana. Yehova amaphunzitsanso atumiki ake kukhala oona mtima komanso acilungamo. Izi zimawathandiza kuti akhale na mtendele wa mumtima, komanso kuti mudzisungile ulemu. (Miy. 13:5, 6) Kodi zimenezi zacitikanso kwa inu pamene mukuphunzila Baibo? Mwaona kuti njila za Yehova ni zothandiza kwambili kwa anthu onse komanso kwa inuyo panokha. (Sal. 77:13) Conco, mumafuna kucita zimene Mulungu amati n’zabwino. (Mat. 6:33) Ndipo mumafuna kukhalila kumbuyo coonadi, komanso kuonetsa kuti zimene Satana ananena ponena za Mulungu wathu Yehova n’zabodza. Kodi mungacite bwanji zimenezo?

5. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumakonda coonadi na cilungamo?

5 Mungasankhe kukhala umoyo m’njila imene idzaonetsa kuti mukukana mabodza a Satana Mdyerekezi, komanso kuti mumakonda coonadi. Cina, mungaonetse kuti mwasankha Yehova kukhala Wolamulila wanu, ndiponso kuti mukufuna kucita zoyenela pamaso pake. Kodi mungacite motani zimenezi? Mwa kudzipatulila kwa Yehova m’pemphelo, na kuonetsa poyela kudzipatulila kwanu mwa kubatizika. Kukonda coonadi na cilungamo n’kumene kumalimbikitsa kwambili munthu kuti asankhe kubatizika.

MUMAM’KONDA YESU KHRISTU

6. Kodi pa Salimo 45:4 pali zifukwa ziti zokulimbikitsani kum’konda Yesu Khristu?

6 N’cifukwa ciyani mumam’konda Yesu Khristu? Onani zifukwa zabwino izi zopezeka pa Salimo 45:4. (Ŵelengani.) Yesu amakonda coonadi, kudzicepetsa, na cilungamo. Ngati mumakonda coonadi na cilungamo, n’zosakayikitsa kuti mumam’kondanso Yesu Khristu. Tangoganizilani mmene Yesu anatetezela molimba mtima coonadi na cilungamo. (Yohane 18:37) Koma kodi Yesu amalimbikitsa bwanji khalidwe la kudzicepetsa?

7. N’ciyani cimakucititsani cidwi na kudzicepetsa kwa Yesu?

7 Yesu amalimbikitsa kudzicepetsa mwa citsanzo cake. Mwacitsanzo, iye amapeleka ulemelelo wonse kwa Atate wake, osati kwa iye mwini. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 5:19) Kodi kudzicepetsa ngati kumeneku kumakukhudzani bwanji? Kodi sikumakulimbikitsani kukonda Mwana wa Mulungu na kutengela citsanzo cake? N’zosacita kufunsa. N’cifukwa ciyani Yesu ni wodzicepetsa? Cifukwa amakonda Atate wake amene ni wodzicepetsa, na kutengela citsanzo cawo. (Sal. 18:35; Aheb. 1:3) Kodi simukopeka kutengela Yesu amene amaonetsa bwino kwambili makhalidwe a Yehova?

8. N’cifukwa ciyani timam’konda Yesu monga Mfumu yathu?

8 Yesu timam’konda monga Mfumu yathu cifukwa ni Wolamulila wabwino. Yehova anam’phunzitsa bwino Mwana wake, ndipo anamuika kukhala wolamulila. (Yes. 50:4, 5) Ganizilaninso cikondi codzimana cimene Yesu anaonetsa. (Yoh. 13:1) Monga Mfumu yanu, muyenela kum’konda kwathunthu Yesu. Iye anafotokoza kuti aja amene amam’kondadi—amene iye amawachanso mabwezi ake—amaonetsa cikondi cawo mwa kumvela malamulo ake. (Yoh. 14:15; 15:14, 15) Ha, ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala bwenzi la Mwana wa Yehova!

9. Kodi ubatizo wa Akhristu umafanana motani na wa Khristu?

9 Limodzi mwa malamulo a Yesu ni lakuti otsatila ake ayenela kubatizika. (Mat. 28:19, 20) Iye mwini anapeleka citsanzo pa nkhani imeneyi. Ngakhale n’telo, m’njila zina ubatizo wake ni wosiyana na uja wa ophunzila ake. (Onani bokosi lakuti “ Kusiyana kwa Ubatizo wa Yesu na Uja wa Otsatila Ake.”) Koma umafanana m’njila zina. Mwa kubatizika, Yesu anadzipeleka kucita cifunilo ca Atate wake. (Aheb. 10:7) Mofananamo, ubatizo wa otsatila a Khristu umakhala cisonyezelo capoyela cakuti anadzipatulila kwa Yehova Mulungu. Iwo amaika maganizo awo pakucita cifunilo ca Yehova, osati cawo. Conco, iwo amatengela citsanzo ca Mbuye wawo.

10. N’cifukwa ninji kukonda Yesu kuyenela kukulimbikitsani kubatizika?

10 Mumakhulupilila kuti Yesu ni Mwana wobadwa yekha wa Yehova, ndipo ni Mfumu yosankhidwa na Mulungu kuti itilamulile. Mumavomeleza kuti Yesu ni wodzicepetsa, ndipo amatengela ndendende citsanzo ca Atate wake. Munaphunzila kuti iye anadyetsa anjala, anatonthoza olefuka, ndipo anacilitsa odwala. (Mat. 14:14-21) Mwaona mmene iye akutsogolela mpingo wake masiku ano. (Mat. 23:10) Ndipo mukudziŵa kuti m’tsogolomu adzacita zambili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Nanga mungaonetse bwanji kuti mumam’konda Yesu? Mwa kutengela citsanzo cake. (Yoh. 14:21) Poyambila pabwino ni kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika.

MUMAM’KONDA YEHOVA MULUNGU

11. Kodi mungati cifukwa cacikulu cobatizikila n’ciyani? Zili conco cifukwa ciyani?

11 Kodi cifukwa cacikulu cobatizikila n’ciyani? Yesu anafotokoza lamulo lalikulu kwambili pa malamulo a Mulungu pamene anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Kodi umu ni mmene mumam’kondela Mulungu?

Yehova ndiye Gwelo la zabwino zonse zimene mumasangalala nazo (Onani ndime 12-13)

12. N’cifukwa ninji Yehova mumam’konda? (Onaninso cithunzi.)

12 Tili na zifukwa zambili zom’kondela Yehova. Mwacitsanzo, mwafika podziŵa kuti iye ni “kasupe wa moyo,” komanso kuti ni Mpatsi wa “mphatso ili yonse yabwino ndi yangwilo.” (Sal. 36:9; Yak. 1:17) Ciliconse cabwino cimene mumasangalala naco, cimacokela kwa Mulungu wathu wacikondi komanso woolowa manja.

13. N’ciyani cimapangitsa dipo kukhala mphatso yabwino ngako?

13 Dipo ni mphatso yabwino ngako imene Yehova anatipatsa. Tikutelo cifukwa ciyani? Ganizilani mgwilizano umene ulipo pakati pa Yehova na Mwana wake. Yesu anati: ‘Atate amandikonda’ ndipo “ndimakonda Atate.” (Yoh. 10:17; 14:31) Mgwilizano wawo unalimba kwambili cifukwa cokhala pamodzi zaka mabiliyoni. (Miy. 8:22, 23, 30) Tsopano tangoganizilani mmene cinamuŵaŵila Mulungu kulola Mwana wake kuvutika mpaka kufa. Yehova amawakonda kwambili anthu—kupatikizapo inu—moti anapeleka Mwana wake wokondeka monga nsembe kuti inuyo na ena mukakhale na moyo kwamuyaya. (Yoh. 3:16; Agal. 2:20) Ici ndico cifukwa cacikulu kwambili cimene timam’kondela Mulungu.

14. Ni colinga citi cabwino kwambili cimene mungadziikile?

14 Cikondi canu pa Yehova cakulilako cifukwa mwadziŵa zambili zokhudza iye. Mosakayika konse, mumafuna kumuyandikila palipano mpaka muyaya. Ndipo izi n’zotheka. Amakulimbikitsani mokoma mtima kuti mukondweletse mtima wake. (Miy. 23:15, 16) Mungatelo m’mawu komanso m’zocita zanu. Muyenela kukhala umoyo woonetsa kuti mumam’kondadi Yehova. (1 Yoh. 5:3) Ici ni colinga cabwino kwambili cimene mungadziikile.

15. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumam’konda kwambili Yehova?

15 Kodi mungaonetse bwanji kuti mumam’konda Yehova? Mumayamba na kupeleka pemphelo lapadela limene mumadzipatulila kwa Mulungu yekha woona. (Sal. 40:8) Kenako, mumaonetsa poyela kudzipatulila kwanu kwamseli mwa kubatizika. Ndipo monga takambila kuciyambi kwa nkhani ino, imeneyi imakhala nthawi yokondweletsa komanso yofunika pa umoyo wanu. Mumayamba umoyo watsopano wokondweletsa Yehova, osati kudzikondweletsa nokha. (Aroma 14:8; 1 Pet. 4:1, 2) N’zoona kuti kutenga sitepe imeneyi ni nkhani yaikulu. Koma kumatsegula khomo la umoyo wabwino koposa. Motani?

16. Malinga na Salimo 41:12, kodi Yehova adzawadalitsa motani amene amadzipeleka kuti am’tumikile?

16 Yehova ni woolowa manja kwambili. Kaya mum’patse zoculuka motani, nthawi zonse iye adzakubwezelani mowilikiza. (Maliko 10:29, 30) Ngakhale m’dziko loipali iye adzakupatsani umoyo wabwino, wokondweletsa, komanso wokhutilitsa. Ndipo ico n’ciyambi cabe. Ulendo wanu umene umayambila pa ubatizo suyenela kutha. Mungapitilize kutumikila Atate wanu wokondeka kwamuyaya. Cikondi pakati pa inu na Atate wanu cidzapitilizabe kukula. Ndipo popeza Yehova adzakhalako kosatha, inunso mudzakhala kosatha.—Ŵelengani Salimo 41:12.

17. N’ciyani cimene mungapatse Yehova comwe alibe?

17 Mukadzipatulila na kubatizika, mumakhala na mwayi wopatsa Atate wanu cinthu camtengo wapatali kwambili. Ciliconse cabwino cimene munakhalapo naco, kuphatikizapo cimwemwe, ni Yehova anakupatsani. Poonetsa kuyamikila, pali cinacake cimene mungam’patse Mwini kumwamba na dziko lapansi comwe alibe—ndico utumiki wanu wokhulupilika. (Yobu 1:8; 41:11; Miy. 27:11) Iyi ni njila yabwino zedi yoseŵenzetsela moyo wanu. Inde, cikondi canu pa Yehova ndico cifukwa cacikulu cokulimbikitsani kuti mubatizike.

KODI MUYEMBEKEZA CIYANI?

18. Kodi mungadzifunse mafunso ati?

18 Kodi mwakonzeka kukabatizika? Ndinu mungapeleke yankho. Koma zingakuthandizeni kwambili mutadzifunsa kuti, ‘Kodi niyembekeza ciyani?’ (Mac. 8:36) Kumbukilani zifukwa zitatu zimene takambilana. Coyamba, mumacikonda coonadi na cilungamo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimafunitsitsa kudzakhalapo na moyo panthawi imene aliyense azidzakamba coonadi, komanso kucita cilungamo?’ Caciŵili, mumam’konda Yesu Khristu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimafuna Mwana wa Mulungu kukhala Mfumu yanga, komanso kutengela citsanzo cake?’ Cacitatu komanso coposa zonse, mumam’konda Yehova. Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimafuna kukondweletsa mtima wa Yehova pom’tumikila monga Mulungu wanga?’ Ngati yankho lanu pa mafunso amenewa ni lakuti inde, mulekelanji kubatizika?—Mac. 16:33.

19. N’cifukwa ciyani simuyenela kuzengeleza kubatizika? Fotokozani citsanzo. (Yohane 4:34)

19 Ngati mukudodoma kubatizika, onani fanizo ili limene Yesu anafotokoza. (Ŵelengani Yohane 4:34.) Iye anati kucita cifunilo ca Atate wake kuli ngati cakudya. Cifukwa ciyani? Cifukwa cakudya cimatipindulila kwambili. Yesu anali kudziŵa kuti ciliconse cimene Yehova angatiuze kucita n’copindulitsa kwa ife. Yehova sangafune kuti ticite cinthu cimene cingativulaze. Kodi Yehova amafuna kuti inuyo mubatizike? Inde. (Mac. 2:38) Conco, mungakhale na cidalilo cakuti kumvela lamulo lakuti mubatizike kungakupindulileni. Ngati simuzengeleza kudya cakudya cimene mumakonda kwambili, nanji kubatizika?

20. Kodi tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

20 N’cifukwa ciyani ena amazengeleza kubatizika? Ambili angayankhe kuti, “Sinili wokonzeka.” Dziŵani kuti kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika, ni cisankho cabwino koposa cimene mungapange. Conco, kukhala wokonzeka kuti mubatizike kumalila nthawi, kuganiza mofatsa, komanso khama. Koma ngati mufunitsitsadi kutenga sitepe imeneyi, kodi mungacite ciyani palipano kuti mukhale wokonzeka kukabatizika? Funsoli tidzaliyankha m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova

a Ubatizo ni sitepe yofunika kwambili kwa wophunzila Baibo aliyense. N’ciyani cingalimbikitse wophunzila Baibo kutenga sitepe imeneyi? Ni cikondi. Koma kukonda ciyani komanso ndani? M’nkhani ino, tikambilane mayankho a mafunso amenewa, na mmene umoyo wathu ungakhalile tikabatizika.