NKHANI YOPHUNZILA 11
NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza
Mungalimbikilebe Kutumikila Yehova Ngakhale Mutagwilitsidwa Mwala
“Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana cifukwa ca dzina langa.”—CHIV. 2:3.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
N’zotheka kutumikilabe Yehova mokhulupilika olo tikumane na zogwilitsa mwala.
1. Timasangalala na madalitso otani cifukwa cokhala m’gulu la Yehova?
NDIFE odalitsika cotani nanga kukhala m’gulu la Yehova pa nthawi ino yovuta ya masiku otsiliza! Pomwe mavuto a m’dzikoli akuwonjezeleka, Yehova watipatsa banja lauzimu la abale na alongo ogwilizana. (Sal. 133:1) Amatithandiza kukhala na mabanja ogwilizana. (Aef. 5:33–6:1) Amatipatsanso nzelu na kuzindikila kuti tikhale na mtendele wa mumtima.
2. Kodi tiyenela kucita ciyani? Ndipo cifukwa ciyani?
2 Komabe, tiyenela kulimbikila kuti tipitilize kutumikila Yehova mokhulupilika. Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi zina tingakhumudwe na zophophonya za ena. Cina, tingakhumudwe na zophophonya zathu, maka-maka ngati talakwitsa cina cake mobweleza-bweleza. Komabe, tiyenela kulimbikilabe kutumikila Yehova ngati (1) Mkhristu mnzathu watikhumudwitsa (2) tagwilitsidwa mwala mu ukwati wathu, komanso (3) ngati takhumudwa na zophophonya zathu. M’nkhani ino, tikambilana zocitika zimenezi, ciliconse pa cokha. Pa cocitika ciliconse, tikambilanenso zimene tingaphunzile kwa munthu wokhulupilika wochulidwa m’Baibo.
LIMBIKILANIBE KUTUMIKILA YEHOVA MKHRISTU MNZANU AKAKUKHUMUDWITSANI
3. Kodi anthu a Yehova amakumana na vuto lotani?
3 Vuto. Abale na alongo ena ali na cibadwa cimene sitikondwela naco. Ena angatigwilitse mwala, kapena kuticitila zinthu mosatiganizila. Ndipo amene akutsogolela angalakwitse zina zake. Zocitika zimenezi zingapangitse ena kukaikila ngati ili ni gulu la Mulungu. M’malo mopitiliza kutumikila Mulungu “mogwilizana” pamodzi na abale na alongo, ena amasiya kugwilizana na amene awakhumudwitsa, ndipo ena amafika poleka kusonkhana. (Zef. 3:9) Kodi n’canzelu kucita zimenezi? Onani zimene tingaphunzile kwa munthu wochulidwa m’Baibo amene anakumana na vuto lofanana na limeneli.
4. Kodi mtumwi Paulo anakumana na zotani?
4 Citsanzo ca m’Baibo. Mtumwi Paulo anali kudziŵa kuti abale na alongo ake anali opanda ungwilo. Mwacitsanzo, atangokhala Mkhristu abale na alongo sanakhulupilile kuti wasinthadi. (Mac. 9:26) Patapita nthawi, ena anali kumunenela zoipa zimene zinamuipitsila mbili. (2 Akor. 10:10) Paulo anaona mkulu akucita zolakwika zimene mwina zinakhumudwitsa ena. (Agal. 2:11, 12) Ndipo mmodzi wa mabwenzi ake apamtima, Maliko, anamugwilitsapo fuwa la moto. (Mac. 15:37, 38) Paulo sanalole ciliconse mwa zocitika zimenezi kumulepheletsa kugwilizana na amene anamulakwila. M’malo mwake, anapitilizabe kuona abale na alongo ake moyenela, ndipo anakhalabe wokangalika mu utumiki wa Yehova. N’ciyani cinam’thandiza?
5. N’ciyani cinam’thandiza Paulo kukhululukila abale na alongo ake? (Akolose 3:13, 14) (Onaninso cithunzi.)
5 Paulo anali kuwakonda abale na alongo ake. Cikondi cake pa abale cinamulimbikitsa kuika maganizo ake pa makhalidwe awo abwino, osati pa zophophonya zawo. Cikondi cinamulimbikitsanso kucita zimene iye mwini analemba pa Akolose 3:13, 14. (Ŵelengani.) Onani mmene anacitila zimenezo pa nkhani ya Maliko. Ngakhale kuti Maliko anamusiya Paulo pa ulendo wake woyamba wa umishonale, iye sanamusungile cakukhosi. Patapita nthawi, Paulo analemba kalata ku mpingo wa ku Kolose. M’kalatamo iye anatamanda Maliko kuti anali wanchito mnzake komanso, wapamtima pake ‘amene anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Cina, Paulo ali m’ndende ku Roma anapempha kuti Maliko adzam’thandize. (2 Tim. 4:11) N’zoonekelatu kuti Paulo sanatope nawo abale na alongo ake, anakhalabe mabwenzi ake. Kodi tiphunzila ciyani kwa Paulo?
6-7. N’ciyani cingatithandize kupitilizabe kukonda Akhristu anzathu ngakhale kuti nthawi zina amalakwitsa? (1 Yohane 4:7)
6 Phunzilo. Yehova amafuna kuti tipitilize kuwaonetsa cikondi abale na alongo athu. (Ŵelengani 1 Yohane 4:7.) M’bale kapena mlongo akacita nafe mopanda cikondi, tizikumbukila kuti sicinali colinga cake. Amafunitsitsa kucita zimene Mulungu amafuna, koma wangocita zinthu mosaganiza bwino. (Miy. 12:18) Yehova amawakonda alambili ake, ngakhale kuti nthawi zina amalakwitsa. Amapitilizabe kukhala bwenzi lathu tikalakwitsa; ndipo satisungila cakukhosi. (Sal. 103:9) M’pofunika kwambili kuti tizitengela citsanzo ca Atate wathu wa kumwamba pa nkhani ya kukhululuka!—Aef. 4:32–5:1.
7 Kumbukilaninso kuti pamene mapeto akuyandikila, m’pamene tiyenela kukhala ogwilizana kwambili na abale na alongo athu. Tikuyembekezela kudzazunzidwa m’tsogolo, moti tingafike pomangidwa cifukwa ca cikhulupililo cathu. Izi zikadzacitika, tidzafunikila abale na alongo athu kuposa n’kale lonse. (Miy. 17:17) Ganizilani zimene zinacitikila m’bale Josep, a mkulu ku Spain. Iye na abale ena anamangidwa cifukwa cosatengako mbali pa nkhondo. Iye anati: “Cinali capafupi kukhumudwila Mkhristu mnzathu cifukwa cokhala pamodzi nthawi zonse. Tinangofunikila kukhala ololelana na kukhululukilana mocokela pansi pamtima. Izi zinatithandiza kukhala ogwilizana, komanso kutetezana. Tinazingidwa na akaidi ena osatumikila Yehova. Nthawi ina, n’nadzipweteka dzanja, ndipo ananiika citute. Conco sin’nali kukwanitsa kucita zinthu panekha. M’bale wina ndiye anali kuwacha zovala na kunisamalila m’njila zina. N’naona cikondi ceniceni pa nthawi imene n’nali kucifunikiladi.” Conco tikasemphana maganizo, m’pofunika kwambili kuti tikambilane na kubwezeletsa mtendele pali pano!
LIMBIKILANIBE KUTUMIKILA YEHOVA NGAKHALE MUTAONA KUTI MUNAGWILITSIDWA MWALA MU UKWATI WANU
8. Ni vuto lanji limene anthu okwatilana amakumana nawo?
8 Vuto. Ukwati ulionse umakhala na mavuto ake. Baibo imakamba mosapita m’mbali kuti okwatilana adzakhala na “nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Cifukwa? Cifukwa ukwati umabweletsa pamodzi anthu aŵili opanda ungwilo, osiyana zikhalidwe, komanso a makonda osiyana. Nthawi zina angakhale kuti anthuwo anakulila kosiyana. Nthawi zinanso angaonetse tumsawu tumene tunali tobisika asanakwatilane. Zinthu ngati zimenezi zingabweletse kukwesana m’banja. M’malo movomeleza kuti ni opanda ungwilo, ndipo naonso amalakwitsa zinthu, ena amalata cala mnzawo wa mu ukwati pa mavuto amene akukumana nawo m’banja. Angafike mpaka poona kuti kusalana kapena kuthetsa ukwati ndiwo mankhwala. Kodi n’zoona kuti kusudzulana n’kumene kungathetse mavuto awo? b Tiyeni tiphunzile ku citsanzo ca mkazi wochulidwa m’Baibo amene anapilila mavuto adzaoneni m’banja lake.
9. Kodi Abigayeli anali mu vuto lotani?
9 Citsanzo ca m’Baibo. Abigayeli anali mkazi wa Nabala, munthu amene Baibo imakamba kuti anali wa nkhanza, komanso wa khalidwe loipa kwambili. (1 Sam. 25:3) Mwacionekele, zinali zovuta kwa Abigayeli kukhala na mwamuna ameneyu. Kodi Abigayeli mwayi anali nawo woonjoka ku ukwati umenewu? Mwayi umenewu unam’tsegukila pamene Davide, mfumu ya m’tsogolo ya Isiraeli, ananyamuka kuti akaphe Nabala cifukwa comunyoza pamodzi na anyamata ake. (1 Sam. 25:9-13) Cinali capafupi kwa Abigayeli kungothaŵa kuti Davide akwanilitse colinga cake. M’malo mwake, analoŵelelapo na kupempha Davide kuti asamuphe Nabala. (1 Sam. 25:23-27) Anacitilanji zimenezi?
10. N’cifukwa ciyani Abigayeli anakhalabe mu ukwati wovuta wotelo?
10 Abigayeli anali kumukonda ngako Yehova, ndipo anali kulemekeza miyeso yake pa nkhani ya ukwati. Mosakaikila anali kudziŵa zimene Yehova ananena kwa Adamu na Hava pamene anayambitsa ukwati woyamba. (Gen. 2:24) Abigayeli anali kudziŵa kuti Yehova anali kuona ukwati kukhala wopatulika. Anali kufuna kukondweletsa Yehova, ndipo izi ziyenela kuti ndiye zinamulimbikitsa kucita zonse zotheka kuti apulumutse a m’banja lake kuphatikizapo mwamuna wake. Anacitapo kanthu mwamsanga kuti Davide asaphe Nabala. Cina, anali wokonzeka kupepesa pa zimene sanalakwitse. Mosakaikila, Yehova anali kumukonda ngako mkazi wanzelu ameneyu, komanso wosadzikonda. Kodi mwamuna na mkazi, angaphunzile ciyani pa citsanzo ca Abigayeli?
11. (a) Kodi Yehova amayembekezela ciyani kwa okwatilana? (Aefeso 5:33) (b) Kodi mwaphunzila ciyani pa zimene Carmen anacita poteteza ukwati wake? (Onaninso cithunzi.)
11 Phunzilo. Yehova amafuna kuti anthu ali pa banja asungebe ukwati wawo banja lawo, ngakhale kuti mnzawoyo ni wovuta kukhala naye. Yehova amakondwela ngako ngati okwatilana amayesetsa kukambilana kuti athetse mavuto awo, akumaonetsana cikondi copanda dyela komanso ulemu. (Ŵelengani Aefeso 5:33.) Ganizilani citsanzo ici ca Carmen. Patangopita zaka 6 atakwatiliwa, iye anayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova, ndipo pambuyo pake anabatizika. Iye anati. “Mwamuna wanga sanakondwele nazo zimenezi. Anayamba kuona ngati Yehova akumulanda mkazi wake, poona kuti nikutayila nthawi pa zinthu zauzimu. Anali kunitukwana na kuniopseza kuti adzanisiya.” Ngakhale n’telo, Carmen anakhalabe mu ukwati umenewu. Kwa zaka 50, anali kuyesetsa kum’konda mwamuna wake na kumulemekeza. Ndiyeno ananena kuti: “M’kupita kwa zaka, n’naphunzila kukamba mwanzelu kwa mwamuna wanga. Podziŵa kuti ukwati ni wopatulika kwa Yehova, n’nacita zonse zimene nikanatha kuti niuteteze. Sin’nathetse ukwati wanga cifukwa nimakonda Yehova.” c Mukakumana na mavuto mu ukwati wanu, dziŵani kuti Yehova adzakucilikizani na kukuthandizani.
LIMBIKILANIBE KUTUMIKILA YEHOVA MUKAKHUMUDWA NA ZOPHOPHONYA ZANU
12. Kodi tingakhale na vuto lanji tikacita cimo lalikulu?
12 Vuto. Tikacita chimo lalikulu tingamve kukhala wacabe-cabe. Ngakhale Baibo imakamba kuti tikacita macimo aakulu timakhala na “mtima wosweka ndi wophwanyika.” (Sal. 51:17) M’bale wina dzina lake Robert, anakhala mtumiki wothandiza pambuyo poyesetsa molimbika kwa zaka zingapo. Koma mwa tsoka ilo, anagwela m’chimo lalikulu, moti anamva kuipa kuti wakhumudwitsa Yehova. Iye anati: “Cikumbumtima canga cinanipsinja ngati kuti ni nyumba imene yaniundumukila. Cinaniŵaŵa kwambili kuti zimenezi zacitika. N’napemphela kwa Yehova kwinaku nikusisima. Pa nthawiyo n’naona kuti Yehova sadzanimvetselanso konse. Ndipo n’naona kuti panali pomveka. Cifukwa n’namugwilitsa mwala.” Conco tikagonja ku mayeso na kucita chimo, mtima wathu woswekawo, umatiuza kuti Yehova watifulatila. (Sal. 38:4) Ngati munamvapo conco, ganizilani za munthu wina wokhulupilika wa m’Baibo, amene sanaleke kutumikila Yehova ngakhale atagwela m’chimo lalikulu.
13. Kodi Petulo anacita chimo lalikulu liti? Nanga n’ciyani cinamufikitsa ku chimo limenelo?
13 Citsanzo ca m’Baibo. Usiku wakuti Yesu aphedwa maŵa, mtumwi Petulo analakwitsa zinthu zingapo zimene zinamufikitsa ku chimo lalikulu. Coyamba, iye anaonetsa kudzidalila mopambanitsa. Anadzitama kuti adzakhalabe wokhulupilika ngakhale atumwi onse atamusiya Yesu. (Maliko 14:27-29) Caciŵili, ali m’munda wa Getsemane, Petulo mobweleza-bweleza analephela kukhalabe maso. (Maliko 14:32, 37-41) Kenako pamene kunabwela cigulu ca adani onyamula malupanga na zibonga kudzagwila Yesu, Petulo analapuka kuthaŵa. (Maliko 14:50) Pamapeto pake, katatu konse Petulo anamkana Yesu. Anafika ngakhale polumbila kuti sam’dziŵa. (Maliko 14:66-71) Kodi Petulo anatani atazindikila kukula kwa chimo lake? Anamva cisoni na kuyamba kulila. Mwina anathedwa nzelu cifukwa codziimba mlandu. (Maliko 14:72) Tangoganizilani cisoni cimene anamvela bwenzi lake Yesu ataphedwa. Ayenela kuti anadzimva kukhala wopanda pake.
14. N’ciyani cinathandiza Petulo kupitilizabe kutumikila Yehova? (Onani cithunzi pa cikuto.)
14 Petulo sanaleke kutumikila Yehova pa zifukwa zingapo. Iye sanadzipatule. M’malo mwake anapita kwa abale ake a kuuzimu, ndipo iwo anamutonthoza. (Luka 24:33) Kuwonjezela apo, Yesu ataukitsidwa anaonekela kwa Petulo, mwacionekele kuti amulimbikitse. (Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Pambuyo pake, Yesu anauza Petulo kuti adzalandila maudindo aakulu, m’malo momudzudzula pa zolakwa zake. (Yoh. 21:15-17) Petulo anadziŵa kuti anacita chimo lalikulu, koma sanataye mtima n’kudziona kuti ni wacabe-cabe. Iye analimbikilabe kucita zoyenela. Cifukwa ciyani? Cifukwa anali wotsimikiza kuti Mbuye wake, Yesu, sanamufulatile. Ndipo abale ake auzimu sanaleke kumulimbikitsa. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Petulo?
15. Kodi Yehova amafuna kuti tikhale otsimikiza za ciyani? (Salimo 86:5; Aroma 8:38, 39) (Onaninso cithunzi.)
15 Phunzilo. Yehova amafuna kuti tikhale otsimikiza kuti amatikonda, ndipo amafuna kutikhululukila. (Ŵelengani Salimo 86:5; Aroma 8:38, 39.) Tikacimwa timadziimba mlandu. N’cibadwa kutelo, ndipo n’zoyenela. Komabe, tisaganize kuti Yehova sangatikondenso, kapena kuti sangatikhululukile. M’malo mwake, tipemphe thandizo mwamsanga. Robert amene tam’chula uja anati: “N’nagwela m’chimo cifukwa codzidalila kuti ningakwanitse kugonjetsa mayeselo panekha.” Kenako, anazindikila kuti ayenela kukamba na akulu. Ndiyeno anati: “N’tangocita zimenezi, n’naona cikondi ca Yehova pa ine kudzela mwa iwo. Anacita nane mwacikondi, na kunitsimikizila kuti Yehova sananisiye.” Nafenso tikhale otsimikiza kuti Yehova amatikonda zedi. Ndipo amatikhululukila tikalapa macimo athu, tikapempha thandizo lake, komanso tikayesetsa kusabwelezanso colakwaco. (1 Yoh. 1:8, 9) Kukhala otsimikiza mtima koteleku kumatithandiza kulimbikilabe kutumikila Yehova ngakhale tikapunthwa kapena kugwa.
16. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciyani potumikila Yehova?
16 Yehova amayamikila kwambili kuyesetsa kwathu kuti tipitilizebe kum’tumikila m’masiku otsiliza ano ovuta. Na thandizo la Yehova n’zotheka kupitilizabe kum’tumikila ngakhale tikumane na zokhumudwitsa. Tingakulitse cikondi pa abale na alongo athu na kuwakhululukila akatilakwila. Tingaonetse kukula kwa cikondi cathu pa Mulungu, komanso pa makonzedwe ake a ukwati mwakucita zonse zotheka kuti tithetse mavuto alionse amene angabuke mu ukwati wathu. Ndipo tikacita cimo, tipemphe thandizo la Yehova, tikhulupilile kuti Iye amatikondadi, komanso kuti watikhululukiladi, ndipo tipitilizebe kum’tumikila. Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kuti tikapitiliza “kucita zabwino,” tidzalandila madalitso oculuka.—Agal. 6:9.
TINGALIMBIKILE BWANJI KUTUMIKILA YEHOVA NGATI . . .
-
wokhulupilila mnzathu watikhumudwitsa?
-
tagwilitsidwa mwala mu ukwati wathu?
-
takhumudwa na zophophonya zathu?
NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano
a Maina ena asinthidwa.
b Mawu a Mulungu salimbikitsa kusalana. Ndipo amakamba momveka bwino kuti kusalana sikupatsa munthu ufulu wokwatilanso. Komabe, pali mikhalidwe ina yovuta imene yapangitsa Akhristu ena kuganizila zosalana. Onani mfundo ya kumapeto 4 yakuti “Kusalana pa Ukwati” m’buku la Kondwelani na Moyo kwa Muyaya!
c Kuti muone citsanzo cina, onani vidiyo pa jw.org yakuti, Musasoceletsedwe na Mtendele Wabodza!—Darrel na Deborah Freisinger.