NKHANI YOPHUNZILA 13
NYIMBO 127 Mtundu wa Munthu Amene Niyenela Kukhala
Mungatsimikize Bwanji Kuti Yehova Amakondwela Nanu?
“Ndimakondwela nawe.”—LUKA 3:22.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene mungagonjetsele maganizo akuti Yehova sakondwela nanu.
1. Kodi ena mwa alambili okhulupilika a Yehova amavutika na maganizo otani?
N’ZOLIMBIKITSA zedi kudziŵa kuti Yehova amakonda gulu lonse la anthu ake! Baibo imati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe, nthawi zina ena amalefuka moti amafika podzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amakondwela nane?’ Ena mwa alambili okhulupilika a Yehova ochulidwa m’Baibo anavutikapo na maganizo otelo.—1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11.
2. Kodi Yehova amakondwela na anthu otani?
2 Baibo imakamba momveka bwino kuti anthu opanda ungwilo angapeze ciyanjo ca Yehova. Motani? Mwa kukhulupilila Yesu Khristu na kubatizika. (Yoh. 3:16) Mwa kutelo, timaonetsa poyela kuti tinalapa macimo athu, komanso kuti tinapanga lonjezo kwa Mulungu lakuti tidzacita cifunilo cake. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amakondwela ngati tapanga masitepe amenewa kuti tikhale naye pa ubale. Kuwonjezela apo, amakondwela nafe ngati tipitiliza kucita zonse zimene tingathe posunga lumbilo lathu la kudzipatulila. Ndipo amationa kukhala mabwenzi ake a pamtima.—Sal. 25:14.
3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?
3 Koma n’cifukwa ciyani anthu ena nthawi zina amamva kuti Mulungu sakondwela nawo? Kodi Yehova amaonetsa motani kuti amakondwela nafe? Ndipo kodi Mkhristu angacite ciyani kuti akhale wotsimikiza kuti Mulungu amakondwela naye?
CIFUKWA CAKE ENA AMAONA KUTI MULUNGU SAKONDWELA NAWO
4-5. Kodi tingakhale otsimikiza za ciyani ngakhale kuti nthawi zina tingazione acabe-cabe?
4 Ena a ife takhala tikuvutika na maganizo odziona kukhala osanunkha kanthu kuyambila tili ana. (Sal. 88:15) M’bale wina dzina lake Adrián anati: “Nthawi zonse n’nali kudziona wacabe-cabe. Nikumbuka kuti nili mwana n’nali kupemphela kuti banja lathu likakhalemo m’Paradaiso. Koma n’nali wotsimikiza kuti sin’nali woyenela kukapezekamo.” Tony, amene sanakulile m’banja la Mboni anati: “Makolo anga sanali kuniuzako kuti amanikonda, kapena kuti amaninyadila. N’nali kuona kuti palibe cabwino cimene n’nali kucita.”
5 Ngati nafenso nthawi zina timavutika na maganizo odziona wacabe-cabe, tizikumbukila kuti Yehova anatikokela kwa iye mwa kufuna kwake. (Yoh. 6:44) Amaona zabwino mwa ife, zimene ife sitingaone. Ndipo amaudziŵa bwino mtima wathu. (1 Sam. 16:7; 2 Mbiri 6:30) Conco tiyenela kukhulupilila akatiuza kuti ndife a mtengo wapatali.—1 Yoh. 3:19, 20.
6. Kodi Paulo anamva bwanji pa macimo amene anapanga m’mbuyomo?
6 Ena a ife tisanaphunzile coonadi, tinacitapo zinthu zimene ngakhale pali pano timadziimba nazo mlandu. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupilika amalimbanabe na zifooko. Kodi mtima wanu umakuimbani mlandu? Ngati n’telo, pezani cilimbikitso podziŵa kuti atumiki okhulupilika a Yehova amakumananso na vuto limeneli. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anadziona wolephela atakumbukila zophophoya zake. (Aroma 7:24) N’zoona kuti iye anali atalapa macimo ake na kubatizika. Ngakhale n’telo, ponena za iye mwini, anati anali “wamng’ono kwambili mwa atumwi onse,” komanso kuti anali “wocimwa kwambili.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15.
7. Tizikumbukila ciyani za macimo athu akale?
7 Atate wathu wa kumwamba analonjeza kutikhululukila macimo athu tikalapa. (Sal. 86:5) Conco ngati talapa macimo athu, tizikhulupilila mawu ake, na kukhala otsimikiza kuti watikhululukila.—Akol. 2:13.
8-9. Tingagonjetse bwanji maganizo akuti sitingakwanitse kukondweletsa Yehova?
8 Tonse timafuna kucita zimene tingathe potumikila Yehova. Komabe, ena amaona kuona kuti sangakwanitse kucita zambili kuti amukondweletse. Mlongo wina dzina lake Amanda anati: “Nimaganiza kuti kupatsa Mulungu zabwino koposa kumatanthauza kucita zoculuka nthawi zonse pom’tumikila. Conco nthawi zambili nimayesetsa kucita zoculuka kuposa zimene ningakwanitse. Ndipo nikalephela kuzikwanilitsa, nimaganiza kuti kwa Yehova ndine wolephela.”
9 Ndiye, tingagonjetse motani maganizo odziona kuti sitingakwanitse kukondweletsa Yehova? Kumbukilani kuti Yehova si wokhwimitsa zinthu. Satiyembekezela kucita zoculuka kuposa zimene tingakwanitse. Amayamikila zilizonse zimene timam’patsa, malinga n’zimene tingakwanitse. Komanso, muziganizila zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo amene anatumikila Yehova na mtima wawo wonse. Ganizilani za Paulo. Iye anatumikila mokangalika kwa zaka, anayenda mitunda itali-itali, ndipo anakhazikitsa mipingo. Koma zinthu zinasintha pa umoyo wake, ndipo sanathenso kulalikila monga kale. Kodi Mulungu analeka kukondwela naye? Ayi. Iye anapitiliza kucita zonse zimene akanatha, ndipo Yehova anamudalitsa. (Mac. 28:30, 31) Mofananamo, zimene timapatsa Yehova sizingafanane nthawi zonse. Nthawi zina zingaculuke, nthawi zina zingacepe. Koma cofunika kwambili kwa iye, ni cimene timacitila zimenezo. Tiyeni tsopano tikambilane mmene Yehova amaonetsela kuti amakondwela nafe.
MMENE YEHOVA AMAONETSELA KUTI AMAKONDWELA NAFE?
10. Ni motani mmene “tingamvele” mawu a Yehova otiuza kuti amakondwela nafe? (Yoh. 16:27)
10 Kupitila m’Baibo. Yehova amafuna-funa mipata yoonetsa anthu kuti amawakonda, komanso kuti amakondwela nawo. Malemba amakamba nthawi ziŵili pomwe Iye anauza Yesu kuti ni Mwana wake wokondedwa, ndiponso kuti amakondwela naye. (Mat. 3:17; 17:5) Kodi mungakonde kumva Yehova akukuuzani kuti amakondwela nanu? Yehova sakamba nafe mwacindunji masiku ano, koma amatelo kupitila m’Mawu ake. Timamva mawu a Yehova otitsimikizila kuti amakondwela nafe tikaŵelenga mawu a Yesu opezeka m’Mauthenga Abwino. (Ŵelengani Yohane 16:27.) Yesu anatengela bwino kwambili makhalidwe a Atate wake. Cotelo, tikamaŵelenga mawu a Yesu oonetsa kuti anali kuwakonda otsatila ake opanda ungwilo koma okhulupilika, zimakhala ngati tikumumva Yehova akutiuza mawu amenewo.—Yoh. 15:9, 15.
11. N’cifukwa ciyani kukumana na mavuto si umboni wa wakuti Yehova analeka kukondwela nafe? (Yakobo 1:12)
11 Kupitila m’zocita zake. Yehova ni wofunitsitsa kupeleka thandizo kwa ife, monga kutithandiza kupeza zofunikila za paumoyo. Koma nthawi zina, Iye angalole kuti tikumane na mavuto monga zinalili kwa munthu wolungama Yobu. (Yobu 1:8-11) Kukumana na mavuto si umboni wakuti Mulungu analeka kukondwela nafe. M’malo mwake, kumatipatsa mwayi woonetsa kuzama kwa cikondi cathu pa Mulungu, komanso kukula kwa cidalilo cathu mwa iye. (Ŵelengani Yakobo 1:12.) Ndipo pamene akutithandiza kupilila, m’pamene timaona kuti amatikonda kwambili, komanso kuti amasamala za ife.
12. Tiphunzilapo ciyani pa cocitika ca m’bale Dmitrii?
12 Ganizilani citsanzo ca m’bale wa ku Asia dzina lake Dmitrii. Nchito inam’thela, ndipo sanapeze ina kwa miyezi yambili. Conco, anayamba kuthela nthawi yoculuka mu utumiki. Mwa kutelo, pofuna anaonetsa cidalilo cake mwa Yehova. Panapita miyezi yambili koma anali asanapezebe nchito. Kenako anadwala matenda aakulu moti anali kungokhala cogona. Kaamba ka zimenezi, iye anayamba kudziona kuti sanali mwamuna wabwino komanso tate wabwino, ndipo anayamba kukaikila ngati Yehova anali kukondwelabe naye. Ndiyeno tsiku lina, mwana wake wamkazi anamulembela mawu a pa Yesaya 30:15 akuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.” Ndiyeno anawauza kuti, “Atate, mukamva kulefuka, muzikumbukila lemba limeneli.” M’bale Dmitrii anazindikila kuti na thandizo la Yehova, banja lake silinasoŵe cakudya, zovala, komanso pokhala. Kenako anati, “N’nali kungofunikila kukhala wosatekeseka, na kupitiliza kudalila Mulungu.” Ngati inunso mukukumana na vuto ngati limeneli, khalani na cidalilo cakuti Yehova amasamala za inu, komanso kuti adzakuthandizani kupilila.
13. Kodi Yehova angaseŵenzetse ndani potionetsa kuti amakondwela nafe? Ndipo angacite motani zimenezo?
13 Kupitila mwa alambili anzathu. Yehova amagwilitsa nchito alambili anzathu potionetsa kuti amakondwela nafe. Mwacitsanzo, angapangitse ena kutiuza mawu acilimbikitso tikavutika maganizo. Izi n’zimene zinacitikila mlongo wina ku Asia pomwe anali wopsinjika maganizo. Iye anacotsedwa nchito, kenako anadwala matenda aakulu. Pamwamba pa izi, mwamuna wake anacita chimo lalikulu, ndipo anacotsedwe pa ukulu. Mlongoyo anati, “Sin’namvetse cifukwa cake zonsezi zinali kunicitikila. N’naganiza kuti mwina n’nalakwitsa cina cake, ndipo Yehova ananifulatila.” Cotelo iye anacondelela Yehova kuti am’thandize kuona kuti akali kum’kondabe. Kodi Mulungu anayankha motani pempho lakelo? Iye anati, “Akulu mumpingo anakamba nane, ndipo ananitsimikizila kuti Yehova amanikonda.” Patapita nthawi, iye anapemphanso Yehova kuti am’thandize kuona kuti akali kukondwela naye. Iye anati, “Tsiku limenelo n’nalandila kalata kucokela kwa gulu la abale na alongo mu mpingo. Pomwe n’nali kuŵelenga mawu awo otonthoza, n’naona kuti Yehova anamvela pemphelo langa.” Inde, nthawi zambili Yehova amationetsa kuti amakondwela nafe kupyolela m’mawu olimbikitsa a anthu ena.—Sal. 10:17.
14. Ni njila inanso iti imene Yehova amaonetsela kuti amakondwela nafe?
14 Yehova amaonetsanso kuti amakondwela nafe mwa kuseŵenzetsa okhulupilila anzathu kutipatsa uphungu pakakhala pofunikila. Mwacitsanzo, m’zaka za zana loyamba, Yehova anauzila mtumwi Paulo kulembela okhulupilila anzake makalata okwanila 14. M’makalata amenewo, Paulo mwacikondi anapatsa alambili anzake uphungu wosapita m’mbali. N’cifukwa ciyani Yehova anauzila Paulo kuphatikizamo uphungu umenewo m’makalata ake? Cifukwa Yehova ni Tate wabwino, ndipo “amadzudzula mwana amene amakondwela naye.” (Miy. 3:11, 12) Conco tikapatsidwa uphungu wa m’Baibo, tiziuona kuti ni umboni wakuti Mulungu amatikonda, m’malo moganiza kuti watikwiyila. (Aheb. 12:6) N’ciyaninso cina cimaonetsa kuti Mulungu amakondwela nafe?
MAUMBONI ENA OONETSA KUTI YEHOVA AMAKONDWELA NAFE
15. Kodi Yehova amapeleka mzimu wake woyela kwa ndani? Ndipo zimenezi ziyenela kutilimbikitsa kucita ciyani?
15 Yehova amapeleka mzimu wake woyela kwa amene amakondwela nawo. (Mat. 12:18) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi nimaonetsako zipatso za mzimu wa Mulungu mu umoyo wanga?’ Kodi mumaona kuti mwaphunzila kucita zinthu moleza mtima na ena kusiyana na mmene zinalili musanadziŵe Yehova? Pamene mukulitsa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala, mudzakhala otsimikiza kuti Yehova amakondwela nanu!—Onani mbali yakuti, “ Makhalidwe Amene Mzimu Woyela Umabala.”
16. Kodi Yehova amagwilitsa nchito ndani polalikila uthenga wabwino? Nanga zimenezi zikupangitsani kumva bwanji? (1 Atesalonika 2:4)
16 Yehova amapatsa anthu amene amakondwela nawo udindo wolalikila uthenga wabwino. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:4.) Onani mmene mlongo wina dzina lake Jocelyn anapindulila cifukwa cogaŵilako ena uthenga wabwino. Tsiku lina mlongoyu anauka ali wopsinjika maganizo. Iye anati, “N’nadzimva wosanunkha kanthu. Koma n’nali kucita upainiya, ndipo inali tsiku limene nimapita mu utumiki. Conco n’napemphela na kupita mu utumiki. M’maŵa umenewo mlongo Jocelyn anakumana na mayi wina wokoma mtima dzina lake Mary, amene anavomela kuyamba kuphunzila Baibo. Patapita miyezi, Mary ananena kuti anali kupemphela kwa Mulungu kuti am’thandize pomwe mlongo Jocelyn anagogoda pa citseko cake. Ataganizila za cocitikaci, mlongo Jocelyn anati, “N’namva monga Yehova akuniuza kuti, ‘Nimakondwela nawe.’” N’zoona kuti si onse angalandile uthenga umene timalalikila. Koma ndife otsimikiza kuti Yehova amakondwela tikacita zonse zimene tingathe pogaŵilako ena uthenga umenewu.
17. Mwaphunzila ciyani pa mawu a mlongo Vicky okhudza mphatso ya dipo? (Salimo 5:12)
17 Yehova amaseŵenzetsa mphamvu ya dipo kwa amene amakondwela nawo. (1 Tim. 2:5, 6) Koma bwanji ngati timaonabe kuti Yehova sakondwela nafe, ngakhale kuti timakhulupilila nsembe ya dipo, ndipo tinabatizika? Kumbukilani kuti mtima ni wonyenga. Koma tizim’khulupilila Yehova nthawi zonse. Amaona amene amakhulupilila nsembe ya dipo kukhala olungama, ndipo analonjeza kuti adzawadalitsa. (Ŵelengani Salimo 5:12; Aroma 3:26) Kusinkhasinkha za dipo kunathandiza mlongo wina dzina lake Vicky. Tsiku lina ataganizila mozama za dipo, anakamba kuti: “Yehova wakhala akunilezela mtima kwa nthawi yaitali. . . . Koma, zinali monga kuti ine nikumuuza kuti: ‘Cikondi canu n’cosakwanila kwa ine. Nsembe ya Mwana wanu siingakwanitse kuphimba macimo anga.’” Kuganizila mofatsa za mphatso ya dipo kunam’thandiza kuona kuti Yehova amamukonda. Kusinkhasinkha dipo kudzatithandiza nafenso kuzindikila kuti Yehova amatikonda, komanso kuti amakondwela nafe.
18. Tisakaikile za ciyani tikapitiliza kukonda Atate wathu wa kumwamba?
18 Ngakhale tiyesetse bwanji kugwilitsa nchito mfundo zomwe taphunzila m’nkhani ino, nthawi zina tingalefuke na kukaikila zakuti Yehova amakondwela nafe. Izi zikacitika, muzikumbukila kuti iye amakondwela na “onse omukonda.” (Yak. 1:12) Conco pitilizani kumuyandikila Yehova, na kuona mmene amaonetsela kuti amakondwela nanu. Ndipo musaiŵale kuti “Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Mac. 17:27.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
-
N’cifukwa ciyani ena amaona kuti Yehova sakondwela nawo?
-
Ni m’njila ziti zimene Yehova amaonetsela kuti amatikonda nafe?
-
N’ciyani cimatipatsa citsimikizo cakuti Mulungu amakondwela nafe?
NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu