Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumasankha Bwanji Zocita?

Kodi Mumasankha Bwanji Zocita?

“Pitilizani kuzindikila cifunilo ca Yehova.” —AEFESO 5:17.

NYIMBO: 69, 57

1. Ndi malamulo ena ati amene amapezeka m’Baibulo? Nanga kuwamvela kumatipindulitsa bwanji?

M’BAIBULO, muli malamulo omveka bwino amene Yehova watipatsa okamba zimene tiyenela kucita ndi zimene tiyenela kupewa. Mwacitsanzo, iye amatiuza kuti sitiyenela kulambila mafano, kuba, kuledzela, kapena kucita ciwelewele. (1 Akorinto 6:9, 10) Ndipo Mwana wa Yehova, Yesu, anapeleka lamulo lacindunji kwa otsatila ake lakuti: “Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani. Ndipo dziŵani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mateyu 28:19, 20) Zonse zimene Yehova ndi Yesu amatiuza kucita zimatipindulitsa. Malamulo a Yehova amatiphunzitsa mmene tiyenela kudzisamalila ndiponso mmene tingasamalilile mabanja athu. Amatithandiza kuti tikhale athanzi ndi osangalala. Koposa zonse, tikamvela malamulo a Yehova, kuphatikizapo lamulo lakuti tizilalikila, iye adzakondwela kwambili ndipo adzatidalitsa.

2, 3. (a) N’cifukwa ciani Baibulo silipeleka malamulo pankhani zina? (b) Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

2 Pali nkhani zina zimene Baibulo silipeleka lamulo mwacindunji. Mwacitsanzo, m’Baibulo mulibe malamulo amene amafotokoza mwacindunji zovala zimene tiyenela kuvala. Zimenezi zionetsa kuti Yehova ndi wanzelu kwambili. Ngakhale kuti anthu padziko lonse amavala zovala za masitaelo osiyanasiyana, ndipo mafashoni amasintha m’kupita kwa nthawi, mfundo za m’Baibulo sizisintha. Kuonjezela pamenepo, m’Baibulo mulibe malamulo acindunji onena za nchito zimene tiyenela kugwila kapena zosangulutsa zimene tiyenela kusankha. Silitiuza mwatsatanetsane zimene tiyenela kucita kuti tikhale athanzi. Yehova walola munthu aliyense kudzisankhila, ndipo walolanso mitu ya mabanja kusankhila mabanja ao.

3 Ngati tifuna kupanga cosankha cacikulu cimene cidzakhudza umoyo wathu ndipo m’Baibulo mulibe lamulo lokhudza nkhaniyo, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi Yehova adzamva bwanji ndikasankha kucita zimenezi? Kodi adzasangalala ndi zilizonse zimene ndingasankhe malinga ngati siziphwanya malamulo a m’Baibulo? Ndingatsimikize bwanji kuti adzasangalala ndi zosankha zanga?’

ZOSANKHA ZATHU ZIMATIKHUDZA NDIPONSO ZIMAKHUDZA ANTHU ENA

4, 5. Kodi zosankha zathu zingatikhudze bwanji? Nanga zingakhudze bwanji anthu ena?

4 Anthu ena amacita ciliconse cimene aganiza. Koma ife timafuna kucita zinthu zokondweletsa Yehova. Motelo, tisanapange cosankha, tiyenela kuganizila zimene Baibulo limakamba ndi kutsatila zimenezo. Mwacitsanzo, kudzela m’Baibulo, Mulungu watiuza mmene tiyenela kuonela magazi, ndipo timamvela zimenezo. (Genesis 9:4; Machitidwe 15:28, 29) Tingapemphe Yehova kuti atithandize kupanga zosankha zimene zidzam’kondweletsa.

5 Zosankha zathu zimakhudza umoyo wathu. Kusankha zinthu mwanzelu kudzatithandiza kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Koma kusankha zinthu mopanda nzelu kungaononge ubwenzi wathu ndi iye. Zimene timasankha zingakhudzenso anthu ena. Sitifuna kucita zinthu zimene zingakhumudwitse abale athu kapena kufooketsa cikhulupililo cao. Sitifunanso kuyambitsa mavuto pakati pa abale mumpingo. Conco kupanga zosankha zabwino n’kofunika kwambili.—Ŵelengani Aroma 14:19; Agalatiya 6:7.

6. N’ciani cingatithandize kupanga zosankha zabwino?

6 N’ciani cingatithandize kupanga zosankha mwanzelu ngati Baibulo silikamba mwacindunji zimene tiyenela kucita? M’malo mocita zimene ife tiona kuti n’zoyenela, tiyenela kuganizilapo mozama ndi kusankha zinthu zokondweletsa Yehova. Tikacita zimenezo, iye adzatidalitsa.—Ŵelengani Salimo 37:5.

KODI YEHOVA AFUNA KUTI NDICITE CIANI?

7. Ngati m’Baibulo mulibe lamulo lacindunji pankhani ina yake, kodi tingadziŵe bwanji zimene Yehova afuna kuti ticite?

7 Tingadziŵe bwanji cosankha cimene cidzakondweletsa Yehova? Lemba la Aefeso 5:17 limatilangiza kuti: “Pitilizani kuzindikila cifunilo ca Yehova.” Ngati m’Baibulo mulibe lamulo lacindunji lokhudza nkhani ina yake, tiyenela kuzindikila, kapena kumvetsetsa zimene Yehova afuna kuti ticite. Kodi tingacite bwanji zimenezo? Mwa kupemphela kwa Mulungu ndi kulola mzimu wake woyela kutitsogolela.

8. Kodi Yesu anazindikila bwanji zimene Yehova anali kufuna kuti iye acite? Pelekani citsanzo.

8 Yesu anali kuzindikila zimene Yehova anali kufuna kuti iye acite. Mwacitsanzo, pamene khamu la anthu linali ndi njala, Yesu anapemphela ndi kudyetsa khamulo m’njila yozizwitsa. Anacita izi maulendo aŵili. (Mateyu 14:17-20; 15:34-37) Koma pamene anali ndi njala m’cipululu, Mdyelekezi anamuuza kuti asandutse miyala kukhala mkate, koma iye anakana. (Ŵelengani Mateyu 4:2-4.) Yesu anali kuwadziŵa bwino Atate ake. Anadziŵanso kuti Yehova sangakondwele ngati iye wagwilitsila nchito mzimu woyela pofuna kukwanilitsa zofuna zake. Iye anadziŵa kuti Atate ake adzamuthandiza ndi kum’patsa cakudya panthawi yabwino.

9, 10. N’ciani cingatithandize kusankha zinthu mwanzelu? Pelekani citsanzo.

9 Mofanana ndi Yesu, tingapange zosankha zabwino ngati timadalila Yehova. Baibulo limakamba kuti: “Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako. Usamadzione kuti ndiwe wanzelu. Uziopa Yehova ndi kupatuka pa coipa.” (Miyambo 3:5-7) Tikamaphunzila Baibulo ndi kudziŵa mmene Yehova amaonela zinthu, tidzadziŵanso zimene iye afuna kuti ticite pa cocitika ciliconse. Izi zidzatithandiza kupanga zosankha zom’kondweletsa ndi kutsatila citsogozo cake.—Ezekieli 11:19.

10 Tiyelekezele kuti mkazi wokwatiwa akugula zinthu m’sitolo, kenako waona nsapato zabwino kwambili. Koma nsapatozo ndi zodula kwambili. Ngakhale kuti mwamuna wake palibe, iye adziŵa mmene mwamuna wakeyo angamvelele ngati wagula nsapato zodula. N’ciani cam’thandiza kudziŵa zimenezo? Iye wakhala m’cikwati kwa nthawi yaitali, ndipo adziŵa kuti mwamuna wake amafuna kuti iwo azigwilitsila nchito ndalama mosamala. Mofananamo, tikamvetsetsa maganizo a Yehova ndi kuona zimene anacita m’mbuyomu, tidzadziŵanso zimene afuna kuti ticite pankhani zosiyanasiyana.

TINGADZIŴE BWANJI MMENE YEHOVA AMAONELA ZINTHU?

11. Ndi mafunso ati amene tingadzifunse pamene tiŵelenga Baibulo kapena kucita phunzilo laumwini? (Onani Bokosi lakuti “ Mukamaphunzila Baibulo, Muzidzifunsa Kuti.”)

11 Tingadziŵe bwanji mmene Yehova amaonela zinthu? Cinthu cofunika kwambili cimene tingacite ndi kuŵelenga ndi kuphunzila Baibulo nthawi zonse. Pamene ticita zimenezi, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi izi zindiphunzitsa ciani ponena za Yehova? N’cifukwa ciani Iye anacita zinthu mwanjila imeneyi?’ Ndipo mofanana ndi Davide, tiyenelanso kupempha Yehova kuti atithandize kum’dziŵa bwino. Davide analemba kuti: “Ndidziŵitseni njila zanu, inu Yehova. Ndiphunzitseni kuyenda m’njila zanu. Ndiyendetseni m’coonadi canu ndi kundiphunzitsa, pakuti inu ndinu Mulungu wa cipulumutso canga. Ciyembekezo canga cili mwa inu tsiku lonse.” (Salimo 25:4, 5) Ngati taphunzila cinacake cokhudza Yehova, tiyenela kuganizila mmene tingagwilitsile nchito zimene taphunzilazo. Tikhoza kuona mmene tingazigwilitsile nchito m’banja, ku nchito, ku sukulu, kapena mu ulaliki. Tikatelo, cidzakhala copepuka kudziŵa zimene Yehova afuna kuti ticite.

Kuti tidziŵe mmene Yehova amaonela zinthu tiyenela kuŵelenga ndi kuphunzila Baibulo nthawi zonse

12. Kodi zofalitsa zathu ndi misonkhano zingatithandize bwanji kudziŵa mmene Yehova amaonela zinthu?

12 Cina cimene cingatithandize kudziŵa mmene Yehova amaonela zinthu, ndi kumvetsela mwachelu zimene gulu lake limaphunzitsa kucokela m’Baibulo. Mwacitsanzo, ngati tifuna kupanga cosankha pankhani inayake, buku la Cingelezi lakuti Watch Tower Publications Index, ndi Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, angatithandize kudziŵa maganizo a Yehova pankhaniyo. Tingapindulenso pamene tipezeka pamisonkhano yacikristu, kumvetsela mosamala, kupeleka ndemanga, ndi kusinkhasinkha zimene taphunzila. Kucita zimenezi kudzatithandiza kuyamba kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Zotsatilapo zake n’zakuti, tidzayamba kupanga zosankha zom’kondweletsa, ndipo iye adzatidalitsa.

MUZIGANIZILA MMENE YEHOVA AMAONELA ZINTHU MUSANAPANGE COSANKHA

13. Pelekani citsanzo coonetsa kuti kudziŵa mmene Yehova amaonela zinthu kungatithandize kupanga zosankha mwanzelu.

13 Tiyeni tikambilane citsanzo ndi kuona mmene tingapangile zosankha mwanzelu ngati tiganizila zimene Yehova afuna. Mwina mukufuna kucita upainiya. Mwasintha zinthu zina ndi zina paumoyo wanu kuti muzithela nthawi yaitali mu ulaliki. Koma mukali kukaikila ngati mudzakhaladi osangalala mukakhala ndi ndalama zocepa ndiponso katundu wocepa. N’zoona kuti Baibulo silikamba kuti tiyenela kukhala mpainiya kuti titumikile bwino Yehova. Tikhoza kupitiliza kum’tumikila mokhulupilika ngakhale ndife ofalitsa cabe. Komabe, Yesu anakamba kuti Yehova amadalitsa anthu amene amadzipeleka cifukwa ca Ufumu. (Ŵelengani Luka 18:29, 30.) Baibulo limakambanso kuti Yehova amasangalala kwambili ngati ticita zimene tingathe kuti tim’tamande, ndipo afuna kuti tizim’tumikila mosangalala. (Salimo 119:108; 2 Akorinto 9:7) Tikapemphelela zinthu zimenezi ndi kuzisinkhasinkha, tidzapanga cosankha mwanzelu, ndipo Yehova adzatidalitsa.

14. Kodi mungadziŵe bwanji ngati sitayilo inayake ya zovala ndi yovomelezeka kwa Yehova?

14 Tiyeni tikambilanenso citsanzo cina: Mwina mumakonda kwambili zovala za sitaelo inayake, koma mudziŵa kuti ena mumpingo angakhumudwe ngati mwavala zovalazo. Ndipo Baibulo silikambapo ciliconse pa sitaelo ya zovalazo. Kodi mungadziŵe bwanji zimene Yehova afuna? Baibulo limati: “Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenela, povala mwaulemu ndi mwanzelu, osati kudzikongoletsa ndi masitayilo omangila tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali. Koma azidzikongoletsa mogwilizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenela kudzikongoletsela. Azidzikongoletsa ndi nchito zabwino.” (1 Timoteyo 2:9, 10) Malangizo amenewa angathandize atumiki onse a Yehova, kuphatikizapo amuna. Ngati ndife odzicepetsa, tidzaganizila mmene ena angamvelele akaona mmene tavalila. Komanso cifukwa cokonda abale athu, tidzapewa kuwakhumudwitsa. (1 Akorinto 10:23, 24; Afilipi 3:17) Ngati tiganizila zimene Baibulo limakamba ndi zimene Yehova amafuna, tidzapanga zosankha zimene zidzam’kondweletsa.

15, 16. (a) Kodi Yehova amamvela bwanji tikamaganizila zaciwelewele? (b) Tikafuna kusankha zosangulutsa, tingadziŵe bwanji zimene zimakondweletsa Yehova? (c) Kodi tiyenela kucita bwanji tikafuna kupanga zosankha zazikulu?

15 Baibulo limaonetsa kuti Yehova amakhumudwa kwambili ngati tiganizila zinthu zoipa kapena kuzicita. (Ŵelengani Genesis 6:5, 6) N’zoonekelatu kuti Yehova safuna kuti tiziganizila za ciwelewele. Kukamba zoona, ngati tipitiliza kuganizila zinthu zimenezi, mpata ukapezeka tingazicite. M’malomwake, Yehova afuna kuti tiziganizila zinthu zoyela ndiponso zabwino. Ponena za nzelu za Yehova, wophunzila Yakobo analemba kuti, “coyamba, ndi yoyela, kenako yamtendele, yololela, yokonzeka kumvela, yodzaza ndi cifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda cinyengo.” (Yakobo 3:17) Conco, Baibulo limaphunzitsa kuti tiyenela kupewa zosangulutsa zilizonse zimene zingaticititse kuganizila kapena kulakalaka zinthu zoipa. Ndipo ngati timvetsetsa bwinobwino zimene Yehova amakonda ndi zimene amadana nazo, cidzakhala copepuka kusankha bwino mabuku, mafilimu, kapena magemu. Sitidzacita kupempha ena kuti atiuze zocita.

16 Ngati tifuna kusankha zocita pankhani inayake, pangakhale zosankha zingapo zimene tingapange patokha zovomelezeka kwa Yehova. Koma ngati ndi nkhani yaikulu, tingacite bwino kufunsila kwa mkulu kapena kwa m’bale kapena mlongo wofikapo kuti atithandize. (Tito 2:3-5; Yakobo 5:13-15) Komabe, sitiyenela kuuza munthuyo kuti atipangile cosankha. M’malomwake, tiyenela kuganizila mosamala mfundo za m’Baibulo ndi kudzipangila cosankha.(Aheberi 5:14) Mtumwi Paulo anati: “Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.”—Agalatiya 6:5.

17. Kodi timapindula bwanji tikapanga zosankha zimene zimakondweletsa Yehova?

17 Ngati tipanga zosankha zimene zimakondweletsa Yehova, tidzamuyandikila, ndipo iye adzatikonda ndi kutidalitsa. (Yakobo 4:8) Ndiyeno cikhulupililo cathu mwa Yehova cidzalimba kwambili. Conco, tiyeni tizisinkhasinkha zimene timaŵelenga m’Baibulo kuti tidziŵe zimene amafuna. N’zoona kuti sitingadziŵe zonse zokhudza Yehova. (Yobu 26:14) Koma ngati tiyesetsa kuphunzila zambili zokhudza iye, tidzakhala anzelu ndipo tidzapanga zosankha zabwino. (Miyambo 2:1-5) Maganizo a anthu amasinthasintha, koma Yehova sasintha. Wamasalimo anati: “Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale. Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.” (Salimo 33:11) Kukamba zoona, ngati tiphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela, tidzasankha zinthu mwanzelu ndipo tidzacita zinthu zom’kondweletsa.