Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pindulani Mokwanila ndi Cakudya Cakuuzimu Cimene Yehova Amapeleka

Pindulani Mokwanila ndi Cakudya Cakuuzimu Cimene Yehova Amapeleka

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino.”—YESAYA 48:17.

NYIMBO: 117, 114

1, 2. (a) Kodi Mboni za Yehova zimaliona bwanji Baibulo? (b) Ndi mbali iti ya m’Baibulo imene mumakonda kwambili?

IFE Mboni za Yehova timalikonda kwambili Baibulo. Limatitonthoza ndiponso kutipatsa ciyembekezo ndi malangizo othandiza. (Aroma 15:4) Si buku la nzelu za anthu, koma ndi “mau a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.

2 Mosakaikila, aliyense wa ife ali ndi mbali inayake m’Baibulo imene amakonda kwambili. Ena amakonda mabuku a Uthenga Wabwino cifukwa m’Malembawo Yesu anaonetsa makhalidwe okhumbilika a Yehova. (Yohane 14:9) Ena amakonda mabuku a maulosi monga la Chivumbulutso, limene limakamba “zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwapa.” (Chivumbulutso 1:1) Ena amalimbikitsidwa kwambili akaŵelenga Masalimo, ndipo ena amasangalala kuŵelenga malangizo othandiza a m’buku la Miyambo. N’zoonekelatu kuti Baibulo ndi buku lothandiza kwa munthu aliyense.

3, 4. (a) Kodi zofalitsa zathu timaziona bwanji? (b) Chulani zofalitsa zimene zimalembedwela anthu osiyanasiyana.

3 Cifukwa cakuti timakonda Baibulo, timakondanso zofalitsa zathu zimene ndi zozikidwa pa Mau a Mulungu. Zofalitsa zonse zimene timalandila monga mabuku, mabulosha, ndi magazini zimacokela kwa Yehova. Zimatithandiza kukhalabe bwenzi lake ndiponso kukhala ndi cikhulupililo colimba.—Tito 2:2.

4 Zofalitsa zathu zambili amalembela Mboni za Yehova zonse. Komabe, pali zofalitsa zina zimene amalembela anthu monga acinyamata kapena makolo. Nkhani zambili ndi mavidiyo amene ali pa webusaiti yathu amakonzela anthu amene si Mboni za Yehova. Zofalitsa zosiyanasiyana zimenezo zimaonetsa kuti Yehova akukwanilitsa lonjezo lake lakuti adzapeleka malangizo ambili kwa anthu onse.—Yesaya 25:6.

5. Kodi Yehova amakondwela ndi ciani?

5 Ambili a ife timafuna titakhala ndi nthawi yoculuka yoŵelenga Baibulo ndi zofalitsa zathu. Koma zimativuta kupeza nthawi yoŵelenga zofalitsa zonse zimene talandila. Komabe, Yehova amakondwela kwambili ngati tigwilitsila nchito nthawi yathu mwanzelu mwa kuŵelenga ndi kuphunzila Baibulo ndi zofalitsa zathu. (Aefeso 5:15, 16) Koma pali cizoloŵezi coipa cimene tiyenela kuyesetsa kupewa. Kodi ndi cizoloŵezi cotani?

6. N’ciani cingatilepheletse kupindula ndi cakudya cakuuzimu cimene Yehova amapeleka?

6 Ngati sitisamala tingayambe kuganiza kuti mbali zina za m’Baibulo kapena zofalitsa zina sizitikhudza. Mwacitsanzo, kodi timacita bwanji ngati mbali ina ya m’Baibulo sigwilizana ndi zocitika za paumoyo wathu? Kapena bwanji ngati sitili mbali ya gulu la anthu amene anawalembela cofalitsaco? Kodi timangoŵelenga nkhaniyo mwa patalipatali kapena kupewelatu kuiŵelenga? Ngati timacita conco, tikhoza kuphonya mfundo zina zimene zingatipindulitse. Kodi tingapewe bwanji cizoloŵezi cimeneci? Tisaiŵale kuti cakudya conse cakuuzimu cimacokela kwa Yehova. M’Baibulo timaŵelenga kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino.” (Yesaya 48:17) M’nkhani ino, tikambilana mfundo zitatu zimene zingatithandize kuti tizipindula ndi cakudya cakuuzimu cimene Yehova amatipatsa.

MALANGIZO OTHANDIZA KUTI TIZIPINDULA POŴELENGA BAIBULO

7. N’cifukwa ciani tiyenela kuŵelenga Baibulo tili ndi maganizo oyenela?

7 Muziŵelenga muli ndi maganizo oyenela. N’zoona kuti mbali zina za m’Baibulo anazilembela anthu ena kapena gulu lina lake. Komabe, Baibulo limakamba mosapita m’mbali kuti, “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Ndiye cifukwa cake tiyenela kuona Malemba onse kukhala ofunika kwambili pamene tiŵelenga Baibulo. M’bale wina amakumbukila kuti pa nkhani imodzi ya m’Baibulo amakwanitsa kuphunzilapo zinthu zambili. Zimenezi zimam’thandiza kudziŵa mfundo zina zimene sizidziŵika mwamsanga. Conco tisanayambe kuŵelenga Baibulo, tiyenela kupempha Yehova kuti atithandize kukhala ndi maganizo oyenela, tingam’pemphe kuti atipatse nzelu kuti timvetsetse zinthu zimene afuna kuti tidziŵe.—Ezara 7:10; ŵelengani Yakobo 1:5.

Kodi mumapindula mokwanila pamene muphunzila Baibulo? (Onani ndime 7)

8, 9. (a) Ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa tikamaŵelenga Baibulo? (b) Kodi ziyeneletso zimene akulu Acikristu ayenela kukwanilitsa zimatiuza ciani ponena za Yehova?

8 Muzidzifunsa mafunso. Mukamaŵelenga Baibulo, muziima pang’ono ndi kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zindiphunzitsa ciani ponena za Yehova? Kodi mfundo zimenezi ndingazigwilitsile nchito bwanji paumoyo wanga? Nanga ndingazigwilitsile nchito bwanji pothandiza anthu ena?’ Tikasinkhasinkha ndi kupeza mayankho a mafunso amenewa tidzapindula kwambili poŵelenga Baibulo. Tiyeni tikambilane citsanzo cimodzi. Baibulo limafotokoza ziyeneletso zina zimene akulu ayenela kukwanilitsa. (Ŵelengani 1 Timoteyo 3:2-7.) Komabe, ambili a ife sindife akulu, conco tingaganize kuti mfundo zimenezi sizingatithandize m’njila iliyonse. Tiyeni tikambilane mafunso atatu amene tachula pamwambapa kuti tione mmene ziyeneletso zimenezo zingatithandizile.

9 “Kodi izi zindiphunzitsa ciani ponena za Yehova?” Yehova anatipatsa m’ndandanda wa ziyeneletso za akulu. Iye afuna kuti abale amene azisamalila mpingo azikwanilitsa miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino. Zimenezi zionetsa kuti mpingo ndi wamtengo wapatali kwa Yehova. Baibulo limakamba kuti anaugula ndi “magazi a Mwana wake weniweni.” (Machitidwe 20:28) Conco Yehova amafuna kuti akulu azikhala citsanzo cabwino, ndipo io adzayankha mlandu kwa iye cifukwa ca mmene amacitila ndi anthu a mumpingo. Mulungu amafuna kuti tizidzimva kukhala otetezeka pansi pa ulamulilo wao. (Yesaya 32:1, 2) Pamene tiŵelenga ziyeneletso zimenezi, timaona kuti Yehova amatisamaliladi.

Yehova amafuna kuti aliyense wa ife akhale wololela ndiponso woganiza bwino

10, 11. (a) Pamene tiŵelenga ziyeneletso za akulu, kodi tingazigwilitsile nchito bwanji pa umoyo wathu? (b) Nanga ndingazigwilitsile nchito bwanji pothandiza anthu ena?

10 “Kodi mfundo izi ndingazigwilitsile nchito bwanji pa umoyo wanga?” Ngati ndinu mkulu, muyenela kuŵelenga m’ndandanda wa ziyeneletso umenewu, ndipo ngati mwaona pamene muyenela kuongolela, muyenela kucita zimenezo mwamsanga. Ngati ‘mukuyesetsa kuti mukhale woyang’anila,’ onetsetsani kuti mukukwanilitsa ziyeneletso zimenezi mmene mungathele. (1 Timoteyo 3:1) Koma Akristu onse angatengelepo phunzilo pa ziyeneletso zimenezi. Mwacitsanzo, Yehova amafuna kuti aliyense wa ife akhale wololela ndiponso woganiza bwino. (Afilipi 4:5; 1 Petulo 4:7) Ngati akulu ndi zitsanzo zabwino “kwa gulu la nkhosa,” tingaphunzile kwa io ndi ‘kutsanzila cikhulupililo cao.’—1 Petulo 5:3; Aheberi 13:7.

11 “Nanga ndingazigwilitsile nchito bwanji pothandiza anthu ena?” Tingagwilitsile nchito m’ndandanda wa ziyeneletso za akulu kuti tithandize ophunzila Baibulo athu ndi anthu ena a cidwi kudziŵa mmene akulu Acikristu amasiyanilana ndi atsogoleli a zipembedzo zina. Ziyeneletso zimenezi zidzatithandiza kukumbukila nchito yaikulu imene akulu amacita mumpingo, ndipo tidzayamba kuwalemekeza kwambili. (1 Atesalonika 5:12) Ndipo ngati tiwalemekeza kwambili, m’pamenenso amasangalala kwambili ndi utumiki wao.—Aheberi 13:17.

12, 13. (a) Ndi kufufuza kotani kumene tingacite pogwilitsila nchito zofufuzila zimene tili nazo? (b) Kambani citsanzo coonetsa mmene kufufuza kungatithandizile kudziŵa mfundo zobisika.

12 Muzifufuza. Pamene tiphunzila Baibulo, tingacite bwino kupeza mayankho a mafunso awa:

  • Ndani analemba mbali ya Baibulo imeneyi?

  • Ndi kuti kumene anailembela? Nanga anailemba liti?

  • Ndi zocitika zapadela ziti zimene zinali kucitika pamene bukuli linali kulembedwa?

Mayankho a mafunso amenewa angatithandize kumvetsa mfundo zimene sitingazidziŵe mwamsanga.

13 Mwacitsanzo, lemba la Ezekieli 14:13, 14 limati: “Ngati dziko landicimwila pocita zosakhulupilika, ndidzalitambasulila dzanja langa n’kuthyola ndodo zake zimene amakolowekapo mikate yoboola pakati. Komanso ndidzalitumizila njala ndipo ndidzapha anthu ndi ziŵeto m’dzikolo. ‘Amuna atatu awa: Nowa, Danieli ndi Yobu, akanakhala m’dzikolo, io okhao akanapulumutsa miyoyo yao cifukwa cokhala olungama,’ watelo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” Ngati tafufuza pankhani imeneyi, tikhoza kuona kuti Ezekieli analemba mau amenewa pafupifupi zaka 612 Kristu asanabwele. Panthawi imeneyo, panali patapita zaka zambili Nowa ndi Yobu atafa kale, koma Yehova anali kukumbukilabe kukhulupilika kwao. Komabe, Danieli anali akali moyo. Zikuoneka kuti anali ndi zaka pafupifupi 20 pamene Yehova anakamba kuti anali olungama mofanana ndi Nowa ndi Yobu. Kodi tiphunzilapo ciani? Yehova amaona atumiki ake onse okhulupilika kuti ndi amtengo wapatali, kuphatikizapo acinyamata.—Salimo 148:12-14.

PINDULANI NDI ZOFALITSA ZOSIYANASIYANA ZIMENE MUMALANDILA

14. Kodi zofalitsa zimene zimalembedwela acinyamata zingawathandize bwanji? Nanga ena zingawathandize bwanji? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

14 Zofalitsa za Acinyamata. Taphunzila kuti tingapindule ndi mbali zonse za Baibulo. Mofananamo, tingapindule ndi zofalitsa zonse zimene gulu lathu limafalitsa. Tiyeni tikambilaneko zitsanzo zocepa. M’zaka zaposacedwapa, Yehova watipatsa zofalitsa zambili zokhudza acinyamata. [1] (Onani mau akumapeto.) Malangizo a m’zofalitsa zimenezi, amawathandiza kulimbana ndi mavuto a kusukulu ndiponso amene amakumana nao pamene akukula. Koma kodi tonse tingapindule bwanji mwa kuŵelenga nkhani ndi mabuku amenewa? Tikamaŵelenga nkhani zimenezi, timadziŵa mavuto amene acinyamata amakumana nao, ndipo timadziŵa mmene tingawathandizile ndi kuwalimbikitsa.

Akristu acikulile sayenela kuona kuti nkhani zimene amalembela acinyamata n’zosafunika kwa io

15. N’cifukwa ciani Akristu acikulile ayenela kuŵelenga zofalitsa zimene zimalembedwela acinyamata?

15 Akristu acikulile sayenela kuona kuti nkhani zimene amalembela acinyamata n’zosafunika kwa io. Mavuto ambili amene acinyamata amakumana nao olembedwa m’nkhani zimenezi amakhudza Akristu onse. Mwacitsanzo, tonse tiyenela kuteteza zikhulupililo zathu, kulamulila mtima wathu, kukaniza ziyeso, kupewa mabwenzi oipa, ndi zosangulutsa zoipa. Conco ngakhale kuti zofalitsa zimenezi analembela acinyamata, uthenga umene ulimo umacokela m’Baibulo, ndipo ungapindulitse Akristu onse.

16. Kodi zofalitsa zathu zimawathandiza bwanji acinyamata?

16 Zofalitsa zimene amalembela acinyamata zingawathandize kulimbitsa ubwenzi wao ndi Yehova. (Ŵelengani Mlaliki 12:1, 13.) Acikulile naonso angapindule ndi zofalitsa zimenezi. Mwacitsanzo, mu Galamukani! ya April 2009 muli nkhani yakuti, “Zimene Acinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingatani Kuti Kuŵelenga Baibulo Kuzindisangalatsa?” M’nkhani imeneyo muli malangizo ambili othandiza, ndipo muli kabokosi kamene munthu angadule ndi kukasunga kuti azikagwilitsila nchito pa phunzilo laumwini. Kodi pali acikulile amene anapindula ndi nkhani imeneyo? Mai wina amene ali pabanja, ndipo ali ndi ana, anakamba kuti kuŵelenga Baibulo kunali kumuvuta kwambili. Koma anagwilitsila nchito malangizo a m’nkhaniyo cakuti tsopano amasangalala poŵelenga Baibulo. Iye anakamba kuti amacita cidwi ndi mmene mabuku a m’Baibulo amagwilizanilana, ndipo amatha kuona m’maganizo mwake zimene akuŵelenga. Anakambanso kuti: “Masiku ano ndimasangalala kwambili kuŵelenga Baibulo kuposa kale.”

17, 18. Tingapindule bwanji ndi zofalitsa zogaŵila? Pelekani citsanzo.

17 Zofalitsa zogaŵila. Kuyambila mu 2008, takhala tikusangalala kwambili kuŵelenga Nsanja ya Mlonda yophunzila. Magazini imeneyi amalembela makamaka Mboni za Yehova, koma tilinso ndi magazini ena amene amalembela anthu onse. Kodi tingapindule bwanji ndi magazini amenewa? Kuti timvetsetse, tiyeni tikambilane citsanzo ici. Ngati mwaitanila munthu ku Nyumba ya Ufumu ndipo munthuyo wapezeka, mumakondwela kwambili. Pamene m’bale akamba nkhani mumaganizila mlendo wanuyo. Mumaganizila mmene mfundo zimene zikukambidwa zikumukhudzila ndi mmene zingasinthile umoyo wake. Zimenezi zimakulimbikitsani cakuti mumayamikila kwambili nkhani imeneyo.

18 Zinthu zofanana ndi zimenezi zingaticitikile ngati tiŵelenga zofalitsa zimene analembela anthu onse. Mwacitsanzo, Nsanja ya Mlonda yogaŵila ndi nkhani zimene zimapezeka pa jw.org zimafotokoza Baibulo pogwilitsila nchito mau osavuta kumvetsa. Pamene tiŵelenga nkhani zimenezi, timayamba kumvetsetsa coonadi ca m’Baibulo ndi kucikonda kwambili. Kuonjezela pamenepo, tingaphunzilenso njila zina zimene tingagwilitsile nchito pofotokozela ena zikhulupililo zathu mu utumiki. Komanso, magazini ya Galamukani! imalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti kuli Mlengi. Imatithandizanso kudziŵa mmene tingatetezele zikhulupililo zathu.—Ŵelengani 1 Petulo 3:15.

19. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila Yehova cifukwa ca zofalitsa zimene amatipatsa?

19 Kukamba zoona, Yehova watipatsa malangizo ambili kuti zinthu zitiyendele bwino. (Mateyu 5:3) Tiyeni tipitilize kuŵelenga ndi kucita zimene timaphunzila. Ngati ticita zimenezi, zinthu zidzatiyendela bwino, ndipo Yehova adzakondwela kudziŵa kuti timayamikila cakudya cakuuzimu cimene watipatsa.—Yesaya 48:17.

^ [1] (ndime 14) Zofalitsa zimenezo ziphatikizapo buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba ndi Laciŵili, ndiponso nkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,” zimene zimapezeka pa intaneti.