Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tizithetsa Mikangano Mwamtendele

Tizithetsa Mikangano Mwamtendele

“Sungani mtendele pakati panu.”—MALIKO 9:50.

NYIMBO: 39, 77

1, 2. Ndi mikangano yotani imene inalembedwa m’buku la Genesis? Nanga n’cifukwa ciani kuphunzila zimenezo n’kothandiza?

KODI munayamba mwaganizilapo za mikangano imene inalembedwa m’Baibulo? Tikangoŵelenga macaputala ocepa a Genesis, timamva kuti Kaini anapha Abele (Genesis 4:3-8); Lameki anapha mnyamata amene anam’menya (Genesis 4: 23); Abusa a Abulahamu anakangana ndi abusa a Loti (Genesis 13:5-7); Hagara anacitila cipongwe Sara, ndipo Sara anakwiila Abulahamu (Genesis 16:3-6); Isimaeli analimbana ndi aliyense, ndipo aliyense analimbana naye.—Genesis 16:7-12.

2 N’cifukwa ciani mikangano imeneyi inalembedwa m’Baibulo? Cifukwa cakuti tikhoza kuphunzilapo kanthu pa zitsanzo za anthu opanda ungwilo amenewa amene anakanganapo ndi anthu ena. Ifenso ndife opanda ungwilo, ndipo tikakumana ndi mavuto ngati amenewo, tikhoza kutengela zitsanzo zabwino za m’Baibulo ndi kupewa kutengela zitsanzo zoipa. (Aroma 15:4) Kucita zimenezi kudzatithandiza kukhala mwamtendele ndi anthu ena.

3. Kodi tiphunzila ciani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tiphunzila cifukwa cake tiyenela kuthetsa mikangano kapena kusamvana, ndi mmene tingacitile zimenezo. Tiphunzilanso mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize kuthetsa kusamvana kuti tikhalebe paubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso anthu ena.

N’CIFUKWA CIANI ATUMIKI A MULUNGU AYENELA KUTHETSA MIKANGANO?

4. Ndi mzimu wotani umene wafala padziko lonse? Nanga pakhala zotsatilapo zotani?

4 Satana ndiye amacititsa anthu kugaŵikana ndi kukangana. Takamba zimenezi cifukwa m’munda wa Edeni, Satana anakamba kuti anthufe sitiyenela kuuzidwa zocita ndi Mulungu, koma tiyenela kucita zimene tifuna. (Genesis 3:1-5) Komabe, tikaona mmene dzikoli lilili masiku ano, timaona kuti maganizo otelo amabweletsa mavuto. Anthu ambili safuna kuuzidwa zocita ndi wina aliyense. Iwo ndi odzikuza, odzikonda, ampikisano, ndipo sadela nkhawa zakuti zocita zao zingakhumudwitse ena. Kukhala ndi mzimu umenewo kumayambitsa mikangano. Baibulo limatilangiza kuti ngati timakwiya msanga, tidzayamba kukangana kwambili ndi anthu ndipo tidzacita macimo ambili.—Miyambo 29:22.

5. Kodi Yesu anauza ophunzila ake kuti ayenela kucita ciani pakabuka mikangano?

5 Pamene Yesu anali kulalikila pa Phili, anaphunzitsa ophunzila ake kuti ayenela kukhala mwamtendele ndi kupewa mikangano ngakhale ataona kuti zinthu sizingawayendele bwino akacita zimenezo. Mwacitsanzo, iye anawauza kuti ayenela kukhala okoma mtima. Anawauzanso kuti ayenela kukhala mwamtendele ndi ena, kuthetsa mkwiyo, kuthetsa mikangano mwamsanga, ndi kukonda adani ao.—Mateyu 5:5, 9, 22, 25, 44.

6, 7. (a) N’cifukwa ciani kuthetsa mikangano mwamsanga n’kofunika? (b) Ndi mafunso otani amene anthu onse a Yehova ayenela kudzifunsa?

6 Masiku ano, timalambila Yehova mwa kupemphela, kulalikila, ndi kupita kumisonkhano. Ngati tilephela kukhazikitsa mtendele ndi abale athu, Yehova sadzakondwela ndi kulambila kwathu. (Maliko 11:25) Kuti tikhale mabwenzi a Yehova, tiyenela kukhululukila ena.—Ŵelengani Luka 11:4; Aefeso 4:32.

Kodi mumakhululukila ena mwamsanga?

7 Yehova amafuna kuti atumiki ake onse azikhululukilana ndi kukhala mwamtendele. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimakhululukila ena mwamsanga? Kodi ndimakonda kukhala ndi Akristu anzanga?’ Ngati mwaona kuti muyenela kuongolela kuti muzikhululukila ena, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kucita zimenezo. Atate wathu wakumwamba adzayankha mapemphelo ocokela pansi pamtima amenewo.—1 Yohane 5:14, 15.

MUZINYALANYAZA ZOLAKWA ZA ENA

8, 9. Tiyenela kucita ciani munthu wina akatikhumudwitsa?

8 Tonse ndife opanda ungwilo, conco tiyenela kuyembekezela kuti nthawi ina iliyonse munthu akhoza kukamba kapena kucita zinthu zimene zingatikhumudwitse. (Mlaliki 7:20; Mateyu 18:7) Ngati zakhala conco, kodi mudzacita ciani? Tingatengele phunzilo pa cocitika cotsatilaci: Mlongo wina atafika kuphwando, anapatsa moni abale aŵili. Koma m’bale mmodzi pa aŵiliwo anakhumudwa cifukwa ca mmene mlongoyo anam’patsila moni. Abalewo atakhala okhaokha, m’bale amene anakhumudwa anayamba kudandaula za mlongoyo. Komabe, m’bale winayo anam’kumbutsa kuti mlongoyo watumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka 40 ngakhale kuti akukumana ndi mavuto ambili. Iye anam’tsimikizila kuti mlongoyo sanacitile dala pofuna kum’khumudwitsa. Ndiyeno m’bale wokhumudwayo anakamba kuti, “Mwakamba zoona.” Kenako anasankha kungonyalanyaza zimene zinacitikazo.

9 Kodi tiphunzilapo ciani pa cocitika cimeneci? Ngati munthu wina wake watilakwila, tingasankhe kucitapo kanthu kapena kum’khululukila. Munthu wacikondi amakhululukila ena. (Ŵelengani Miyambo 10:12; 1 Petulo 4:8.) Ngati ‘tinyalanyaza colakwa,’ Yehova amakondwela kwambili. (Miyambo 19:11; Mlaliki 7:9) Conco ngati munthu wina wakamba kapena wacita cinacake cimene cakukhumudwitsani, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndiyenela kumangoganizila za cocitika cimeneci kapena ndiiŵaleko cabe?’

10. (a) Kodi mlongo wina anacita ciani anthu ena atamunena? (b) Ndi lemba liti limene linathandiza mlongoyo kukhalabe wosangalala?

10 Ngati anthu ena atinena, cingakhale covuta kunyalanyaza zokamba zao. Mvelani zimene zinacitikila mpainiya wina amene tam’patsa dzina lakuti Lucy. Ena mumpingo anali kukamba mau oipa okhudza mmene anali kucitila utumiki wake ndi mmene anali kugwilitsila nchito nthawi yake. Mlongo Lucy atamva zimenezo, anakhumudwa kwambili cakuti anapempha nzelu kwa abale ofikapo. Kodi zinakhala bwanji pambuyo pake? Iye anakamba kuti io anagwilitsila nchito Baibulo ndipo anam’thandiza kuti aleke kuganizila kwambili zoipa zimene ena anakamba ndi kuyamba kuganizila kwambili za Yehova. Analimbikitsidwa ataŵelenga lemba la Mateyu 6:1-4 (Ŵelengani.) Lemba limeneli linam’kumbutsa kuti kukondweletsa Yehova ndico cinthu cofunika kwambili. Conco anasankha kunyalanyaza mau oipa amene anthuwo anakamba. Masiku ano, ngakhale ena akambe mau oipa okhudza utumiki wake, iye amakhalabe wosangalala cifukwa codziŵa kuti akucita zimene angakwanitse kuti akondweletse Yehova.

ZIMENE MUNGACITE NGATI MULEPHELA KUNYALANYAZA COLAKWA

11, 12. (a) Kodi Mkristu ayenela kucita ciani akaona kuti Mkristu mnzake ‘ali naye cifukwa’? (b) Kodi tiphunzilapo ciani tikaona mmene Abulahamu anathetsela mkangano? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 “Tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yakobo 3:2) Tiyelekezele kuti m’bale kapena mlongo winawake wakhumudwa cifukwa ca zimene munakamba kapena kucita. Kodi muyenela kucita ciani? Yesu anakamba kuti: “Conco ngati wabweletsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba, ndipo ukabwelako, peleka mphatso yako.” (Mateyu 5:23, 24) Conco, muyenela kukambilana ndi m’bale wanu. Pokambilana, colinga canu cikhale kukhazikitsa mtendele. Muyenela kuvomeleza kulakwa kwanu m’malo moimba mlandu mnzanuyo. Cofunika kwambili ndi kukhala pamtendele ndi abale anu.

Tiyenela kukhala ndi colinga cokhazikitsa mtendele ndi abale athu

12 Baibulo limaonetsa kuti atumiki a Mulungu angakhalebe pamtendele ngakhale kuti pali kusamvana. Mwacitsanzo, Abulahamu ndi Loti, onse anali ndi ziŵeto zambili, ndipo abusa ao anayamba kukangana cifukwa ca kucepa kwa malo odyetselako ziŵeto. Abulahamu anafuna kukhalabe pamtendele ndi Loti, conco anam’patsa mwai wosankha malo abwino. (Genesis 13:1, 2, 5-9) Cimeneci ndi citsanzo cabwino cimene tiyenela kutengela. Kodi Abulahamu anavutika cifukwa copatsa Loti malo abwino? Ayi ndithu. Patangopita nthawi yocepa, Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzam’patsa zoculuka kuposa zimene analuza. (Genesis 13:14-17) Kodi tiphunzilapo ciani? Ngakhale titaluza zinazake pofuna kukhazikitsa mtendele, Yehova adzatidalitsa. [1]—Onani mau akumapeto.

13. Kodi woyang’anila wina anacita ciani atauzidwa mau oipa? Nanga mwaphunzilapo ciani pa citsanzo cake?

13 Mvelani citsanzo ca masiku ano. M’bale wina amene anaikidwa kukhala woyang’anila watsopano wa dipatimenti ina pa msonkhano, anatumila foni m’bale wina ndi kum’pempha ngati angakonde kutumikila m’dipatimenti imeneyo. M’baleyo anayankha mau oipa ndi kuzimitsa foni cifukwa anali wokhumudwa ndi zimene woyang’anila wakale wa dipatimentiyo anam’citila. Woyang’anila watsopanoyo sanakhumudwe. Ngakhale zinali conco, iye sananyalanyaze zimene zinacitika. Patapita ola limodzi, anatumilanso m’baleyo ndi kum’pempha kuti akakumane kuti akakambilane. Mlungu wotsatila, abalewo anakumana pa Nyumba ya Ufumu, ndipo pambuyo popemphela kwa Yehova, anakambilana kwa ola limodzi. M’bale amene anakhumudwa uja anafotokoza zimene zinacitika pakati pa iye ndi woyang’anila wakale. Woyang’anila watsopanoyo anamvetsela mokoma mtima ndi kukambilana naye malemba olimbikitsa. Zotsatilapo zake n’zakuti abalewo anakhazikitsa mtendele ndipo anaseŵenzela pamodzi pamsonkhano. M’baleyo amayamikila kwambili cifukwa woyang’anilayo anakambilana naye mokoma mtima ndiponso mwacikondi.

KODI MUYENELA KUUZAKO AKULU?

14, 15. (a) Ndi pa zocitika ziti pamene tingagwilitsile nchito malangizo amene ali pa Mateyu 18:15-17? (b) Ndi masitepe atatu ati amene Yesu anakamba? Nanga tiyenela kukhala ndi colinga cotani pamene tiwatsatila?

14 Kaŵilikaŵili, mikangano imene imayamba pakati pa Akristu iyenela kuthetsedwa mwam’seli. Komabe, nthawi zina zimavuta. Mikangano ina ingafunike kuti ena athandizileko malinga ndi zimene lemba la Mateyu 18:15-17 limakamba. (Ŵelengani.) ‘Chimo’ limene Yesu anachula palembali silitanthauza mkangano waung’ono wapakati pa Akristu. Tanena izi cifukwa Yesu anakamba kuti ngati wocimwa salapa pambuyo pakuti m’bale wake wakambilana naye, waitananso mboni, ndiponso abale a maudindo, ayenela kuonedwa monga “munthu wocokela mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.” Masiku ano, zimenezi zitanthauza kuti ayenela kucotsedwa mumpingo. Chimo limene Yesu anakamba lingaphatikizepo zinthu monga cinyengo kapena misece. Koma siliphatikizapo macimo monga dama, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, mpatuko, kapena kulambila mafano. Nthawi zonse macimo a mtundu umenewu afunika kusamalidwa ndi akulu.

Nthawi zina, tingafunike kukambilana ndi munthu kangapo kuti tikhazikitse mtendele (Onani ndime 15)

15 Yesu anapeleka malangizo amenewa pofuna kutiphunzitsa mmene tingathandizile Mkristu mnzathu mwacikondi. (Mateyu 18:12-14) Kodi tingatsatile bwanji uphungu umenewu? (1) Tiyenela kuyesetsa kukhazikitsa mtendele ndi m’bale wathu popanda kuloŵetsamo ena. Kuti ticite zimenezi tingafunike kukambilana naye maulendo angapo. Koma kodi tiyenela kucita ciani ngati talephela kukhazikitsa mtendele? (2) Tiyenela kupita kukakambilana ndi m’bale wathu pamodzi ndi munthu wina amene akuidziŵa bwino nkhaniyo kapena amene angatithandize. Ngati mwakwanitsa kukhazikitsa mtendele ndiye kuti ‘mwabweza m’bale wanuyo.’ Koma pokhapo ngati mwakambilana ndi m’bale wanu maulendo angapo ndipo mwalephela kukhazikitsa mtendele ndi pamene (3) mungauze akulu za vutolo.

16. N’ciani cionetsa kuti kutsatila malangizo a Yesu ndi njila yacikondi yothetsela mikangano ndiponso yothandiza?

16 Nthawi zambili sitingafunikile kugwilitsila nchito masitepe onse atatu amene ali pa Mateyu 18:15-17. Zimenezi n’zolimbikitsa. Takamba conco cifukwa nthawi zambili wolakwa amazindikila colakwa cake ndi kucitapo kanthu, ndipo pamakhala palibe cifukwa com’cotsela mumpingo. Zikatelo, wolakwilidwa ayenela kukhululukila m’bale wake kuti akhale nayenso pamtendele. Conco, malinga ndi malangizo a Yesu tikhoza kuona kuti sitiyenela kuuza akulu nkhaniyo mwamsanga. Tiyenela kuuza akulu pambuyo potsatila masitepe aŵili oyambilila, ndiponso ngati taona kuti munthuyo anatilakwiladi.

17. Kodi tidzalandila madalitso otani tikamayesetsa kukhala mwamtendele ndi ena?

17 Sitingapeweletu kukhumudwitsa ena cifukwa ndife opanda ungwilo. Wophunzila Yakobo analemba kuti: “Ngati wina sapunthwa pa mau, ameneyo ndi munthu wangwilo, ndipo akhoza kulamulilanso thupi lake lonse.” (Yakobo 3:2) Kuti tithetse kusamvana, tiyenela kucita zimene tingathe kuti ‘tifunefune mtendele ndi kuusunga.’ (Salimo 34:14) Ngati tiyesetsa kukhala mwamtendele ndi ena, tidzakhala paubwenzi wabwino ndi abale ndi alongo athu, ndipo tidzakhalabe ogwilizana. (Salimo 133:1-3) Koposa zonse, tidzakhala paubwenzi wolimba ndi Yehova, “Mulungu amene amapatsa mtendele.” (Aroma 15:33) Tidzasangalala ndi madalitso amenewa pokhapo ngati tithetsa mikangano mwamtendele.

^ [1] (ndime 12) Ena amene anathetsa mikangano mwamtendele ndi Yakobo, ndi Esau (Genesis 27:41-45; 33:1-11); Yosefe ndi abale ake (Genesis 45:1-15); Gidiyoni ndi a Efuraimu (Oweruza 8:1-3). Mungaganizilenso zitsanzo zina za m’Baibulo.