NKHANI YOPHUNZILA 19
Cikondi na Cilungamo M’dziko Loipali
“Inu sindinu Mulungu wokondwela ndi zoipa, palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu ngakhale kwa kanthawi kocepa.”—Sal. 5:4.
NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu
ZA M’NKHANI INO *
1-3. (a) Malinga na Salimo 5:4-6, kodi Yehova amamvela bwanji na zoipa zilizonse? (b) N’cifukwa ciani tingakambe kuti kucitila ana zolaula n’kosemphana na “cilamulo ca Khristu”?
YEHOVA MULUNGU amazonda khalidwe lililonse loipa. (Ŵelengani Salimo 5:4-6.) Iye amadana kwambili na khalidwe locitila ana zolaula. Khalidwe limeneli n’loipa ndiponso n’lonyansa kwambili! Mofanana ndi Yehova, ife Mboni zake timadana nalo khalidwe limeneli, ndipo sitimalilekelela mumpingo.—Aroma 12:9; Aheb. 12:15, 16.
2 Kucitila mwana zolaula mwanjila ina iliyonse n’kosemphana kwambili na “cilamulo ca Khristu.” (Agal. 6:2) N’cifukwa ciani takamba conco? Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, cilamulo ca Khristu, kutanthauza zonse zimene Yesu anaphunzitsa mwa mawu na zocita zake, n’cozikidwa pa cikondi ndipo cimalimbikitsa cilungamo. Popeza ife Akhristu oona timatsatila cilamulo cimeneci, timayesetsa kucita zinthu ndi ana m’njila yakuti azidziona kukhala otetezeka komanso okondedwa. Koma kucitila mwana zolaula n’kudzikonda, n’kupanda cilungamo, ndipo kumapangitsa mwanayo kudziona kuti ni wosatetezeka ndiponso kuti anthu samukonda.
3 Comvetsa cisoni n’cakuti khalidwe locitila ana zolaula ni mlili umene wafala padziko lonse. Ngakhale Akhristu oona akhudzidwa na vutoli. N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa cakuti “anthu oipa ndi onyenga” aculuka padzikoli, ndipo ena angaloŵe mumpingo. (2 Tim. 3:13) Kuwonjezela apo, anthu ena mumpingo agonja ku zilakolako zathupi mpaka kufika pocitila ana zolaula. Tsopano tiyeni tikambilane cifukwa cake kucitila ana zolaula ni chimo lalikulu. Pambuyo pake, tidzakambilana mmene akulu amasamalila milandu ya macimo akulu-akulu, kuphatikizapo chimo la kucitila ana zolaula. Cinanso, tidzaona mmene makolo angatetezele ana awo kwa anthu ocitila ana zolaula. *
KUCITILA MWANA ZOLAULA NI CHIMO LALIKULU KWAMBILI
4-5. N’cifukwa ciani kucitila mwana zolaula ni kum’cimwila?
4 Kucitila mwana zolaula kumakhala na zotulukapo zoipa komanso zokhalitsa. Zimenezi zimapweteka kwambili mwanayo ndi anthu amene amam’konda, monga acibanja ndiponso abale na alongo mumpingo. Kucitila ana zolaula ni chimo lalikulu kwambili.
5 N’kucimwila mwanayo. * Ni chimo kucitila munthu wina nkhanza. Nkhani yotsatila idzaonetsa kuti izi n’zimene munthu wocitila mwana zolaula amacita. Inde, amavulaza mwanayo kwambili. Mwacitsanzo, mwana amakhulupilila na kudalila munthu wacikulile. Ndiye ngati munthu wacikulileyo wacitila mwanayo zolaula, mwana uja amakhumudwa na kusiya kum’khulupilila. Amadziona kuti ni wosatetezeka. Ana afunika kuwateteza ku nkhanza imeneyi, ndipo ana amene anacitilidwapo zolaula afunika kuwalimbikitsa na kuwathandiza.—1 Ates. 5:14.
6-7. N’cifukwa ciani tikamba kuti kucitila mwana zolaula n’kucimwila mpingo na boma?
6 N’kucimwila mpingo. Ngati wina mumpingo wacitila mwana zolaula, amabweletsa citonzo pampingo. (Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12) Kutonzetsa mpingo wonse n’kuwalakwila kwambili Akhristu okhulupilika mamiliyoni amene amayesetsa “kumenya mwamphamvu nkhondo yacikhulupililo.” (Yuda 3) Ife Mboni za Yehova sitilola kuti munthu woipa amene salapa apitilize kukhala mumpingo kapena kuipitsa mbili yabwino ya gulu la Mulungu.
7 N’kucimwila boma. Akhristu amalamulidwa ‘kumvela olamulila akuluakulu.’ (Aroma 13:1) Timaonetsa kuti ndife omvela mwa kutsatila malamulo a m’dziko limene tikhala. Ngati wina mumpingo waphwanya lamulo la boma, monga loletsa kucitila mwana zolaula, ndiye kuti wacimwila boma. (Yelekezelani na Machitidwe 25:8) Ngakhale kuti si udindo wa akulu kuonetsetsa kuti anthu akutsatila malamulo a boma, iwo sateteza kapena kuikila kumbuyo munthu wocitila ana zolaula kuti asalandile cilango. (Aroma 13:4) Iye amakolola zimene anafesa.—Agal. 6:7.
8. Kodi Yehova amaona bwanji ngati munthu wacimwila mnzake?
8 Koposa zonse, n’kucimwila Mulungu. (Sal. 51:4) Munthu akacimwila mnzake, ndiye kuti wacimwilanso Yehova. Ganizilani zimene zinali kucitika m’nthawi ya Cilamulo ca Mose. Cilamuloco cinakamba kuti ngati munthu walanda mnzake zinthu kapena kumubela mwacinyengo, ndiye kuti ‘wacita zinthu mosakhulupilika kwa Yehova.’ (Lev. 6:2-4) Conco, n’zoonekelatu kuti ngati wina mumpingo wacitila mwana zolaula, kumene ni kum’landa ufulu wake wokhala motetezeka, ndiye kuti wacita zinthu mosakhulupilika kwa Mulungu. Munthu wotelo amabweletsa citonzo cacikulu pa dzina la Yehova. Conco, kwa ife sitingakambile mwina koma kuti khalidwe lonyansa locitila mwana zolaula ni chimo lalikulu pamaso pa Mulungu.
9. Ni malangizo ati a m’Malemba amene gulu la Yehova lakhala likupeleka kwa zaka zambili? Nanga n’cifukwa ciani?
9 Kwa zaka zambili, gulu la Yehova lakhala likupeleka malangizo oculuka a m’Malemba pa nkhani yocitila ana zolaula. Mwacitsanzo, magazini a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! akhala akufotokoza zimene anthu amene anacitilidwapo zolaula angacite kuti alimbane na vuto lokhalitsa la kuvutika maganizo. Magaziniwa akhalanso akufotokoza mmene ena angathandizile anthu amenewa na kuwalimbikitsa, ndiponso mmene makolo angatetezele ana awo. Akulu alandila malangizo oculuka komanso omveka bwino a mmene angasamalile mlandu wa chimo locitila mwana zolaula. Ndipo gulu lapitiliza kupeleka malangizo atsopano kwa akulu pankhani imeneyi. Limacita izi pofuna kuonetsetsa kuti akulu akusamalila milandu imeneyi mogwilizana na cilamulo ca Khristu.
KUWELUZA MILANDU YA MACIMO AKULU-AKULU
10-12. (a) Posamalila mlandu wa chimo lalikulu, kodi akulu amakumbukila ciani? Nanga amakhala na nkhawa zotani? (b) Mogwilizana na Yakobo 5:14, 15, kodi akulu amayesetsa kucita ciani?
10 Akulu akamasamalila milandu ya macimo akulu-akulu, amakumbukila kuti cilamulo ca Khristu cimafuna kuti azicita zinthu mwacikondi na gulu la nkhosa, na kuti azicita zoyenela na zolungama pamaso pa Mulungu. Pa cifukwa cimeneci, iwo akamva kuti winawake wacita chimo lalikulu, amakhala na nkhawa zingapo. Nkhawa yaikulu imene amakhala nayo ni yofuna kuteteza dzina lopatulika la Mulungu. (Lev. 22:31, 32; Mat. 6:9) Nkhawa ina yaikulu imene amakhala nayo ni yofuna kuteteza umoyo wa uzimu wa abale na alongo mumpingo. Amafunanso kuthandiza aliyense amene wavulazidwa na chimo lalikulu limene wina wacita.
11 Kuwonjezela apo, ngati wolakwayo ni m’bale kapena mlongo ndipo ni wolapa, nkhawa ya akulu imakhala yofuna kum’thandiza kukonzanso ubwenzi wake na Yehova. (Ŵelengani Yakobo 5:14, 15.) Ngati Mkhristu wagonja ku cilakolako coipa na kucita chimo lalikulu, ndiye kuti ni wodwala mwauzimu. Izi zitanthauza kuti salinso pa ubwenzi wabwino na Yehova. * M’lingalilo lauzimu, akulu ali ngati madokotala. Iwo amacita zonse zimene angathe kuti ‘acilitse wodwalayo [kapena kuti wocimwayo].’ Uphungu wa m’Malemba umene angamupatse, ungamuthandize kukonzanso ubwenzi wake na Mulungu. Koma izi zingatheke kokha ngati munthuyo ni wolapadi.—Mac. 3:19; 2 Akor. 2:5-10.
12 Conco, akulu ali na udindo waukulu kwambili. Iwo amazikonda kwambili nkhosa zimene Mulungu anaziika m’manja mwawo. (1 Pet. 5:1-3) Akulu amafuna kuti abale na alongo azidziona kukhala otetezeka mumpingo. Ndiye cifukwa cake amacitapo kanthu mwamsanga ngati amva kuti winawake mumpingo wacita chimo lalikulu, kuphatikizapo kucitila mwana zolaula. Ganizilani mafunso amene ali kumayambililo kwa ndime 13, 15, na 17 m’nkhani ino.
13-14. Kodi akulu amatsatila malamulo a boma okanena kupolisi ngati munthu winawake wacitila mwana zolaula? Fotokozani.
13 M’maiko ena, malamulo a boma amafuna kuti munthu akanene kupolisi ngati pacitika mlandu wocitila mwana zolaula. Kodi akulu amatsatila malamulo amenewa? Inde amatsatila. Ndipo amayesetsa kucita zimenezo. (Aroma 13:1) Malamulo amenewo si osemphana na malamulo a Mulungu. (Mac. 5:28, 29) Conco, akulu akamva kuti winawake wacitila mwana zolaula, mwamsanga amafunsila malangizo ku ofesi ya nthambi kuti adziŵe zimene angacite potsatila malamulo a boma ofuna kukanena kupolisi.
14 Akulu amauza wocitilidwa zolaulayo na makolo ake, kuphatikizapo ena amene aidziŵa nkhaniyo kuti ali na ufulu wokanena kupolisi za mlanduwo. Koma bwanji ngati wolakwayo ni wa mumpingo, ndipo Mkhristu wina wakanena za mlanduwo, kenako nkhaniyo n’kufalikila m’delalo? Kodi Mkhristu amene anapita kukanena ayenela kudziimba mlandu kuti watonzetsa dzina la Mulungu? Ayi. Wocitila mwana zolaulayo ndiye ali na mlandu wotonzetsa dzina la Mulungu.
15-16. (a) Malinga na 1 Timoteyo 5:19, n’cifukwa ciani pamafunika mboni zosacepela ziŵili kuti akulu apange komiti yaciweluzo? (b) N’ciani cimene akulu amacita akamvela kuti wina wake mumpingo anacitila mwana zolaula?
15 Akulu mumpingo asanapange komiti yaciweluzo, amafuna kuti pakhale mboni zosacepela ziŵili zotsimikizila colakwa. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti amatsatila miyezo yapamwamba ya m’Baibo ya cilungamo. Ngati munthu sanavomeleze kuti anacita colakwa, pamafunika mboni ziŵili zotsimikizila colakwaco kuti akulu akhale na mphamvu zopanga komiti yaciweluzo. (Deut. 19:15; Mat. 18:16; ŵelengani 1 Timoteyo 5:19.) Kodi izi zitanthauza kuti pafunika mboni ziŵili zotsimikizila colakwa kuti munthu akanene kupolisi mlandu wocitila mwana zolaula? Ayi. Kukanena mlandu wophwanya lamulo la boma sikulila kuti pakhale mboni ziŵili.
16 Akulu akamvela kuti wina mumpingo anacitila mwana zolaula, coyamba amayesetsa kutsatila malamulo a boma ofuna kukanena nkhaniyo kupolisi. Kenako, amafufuza za nkhaniyo potsatila malangizo a m’Baibo. Ngati munthuyo wakana kuti anacitila mwana zolaula, akulu amamvetsela umboni wa anthu ena amene adziŵa zimene zinacitikazo. Kuti komiti ya ciweluzo ipangidwe, pamafunika kukhala mboni ziŵili—yoimba mlandu munthuyo, na ina yotsimikizila mlanduwo, kapena milandu ina yocitila ana zolaula imene munthuyo anacitapo. * Ngati sipanapezeke mboni yaciŵili, sizitanthauza kuti mlanduwo ni wabodza ayi. Ngati mboni ziŵili zotsimikizila colakwaco sizinapezeke, akulu amazindikila kuti munthuyo akhoza kukhala kuti anacitadi colakwa cacikulu, cimene cinavulaza ena na kuwakhumudwitsa. Conco, iwo amapitiliza kutonthoza na kulimbikitsa anthu olakwilidwawo. Kuwonjezela apo, pofuna kuteteza mpingo, akulu amakhala chelu na munthu wodziŵika kuti amacitila ana zolaula.—Mac. 20:28.
17-18. Fotokozani udindo wa komiti yaciweluzo.
17 Kodi udindo wa komiti yaciweluzo ni wotani? Liwu lakuti “yaciweluzo” silitanthauza kuti akulu amagamula ngati munthu wolakwa ni woyenela kupatsidwa cilango na boma kapena ayi. Iwo amadziŵa kuti si udindo wawo kuonetsetsa kuti anthu akutsatila malamulo a boma, ndipo amasiyila boma udindo umenewu. (Aroma 13:2-4; Tito 3:1) Akulu amaweluza m’lingalilo lakuti amapenda kuti aone ngati munthu ni woyenelela kukhalabe mumpingo kapena ayi.
18 Akulu akakhala pa komiti yaciweluzo, udindo wawo ni kusamalila mbali yauzimu, kapena kuti yokhudza kulambila. Mwa kuseŵenzetsa Malemba, iwo amapenda ngati munthu wocitila mwana zolaula ni wolapa kapena ayi. Ngati ni wosalapa, amacotsedwa, ndipo cilengezo cimapelekedwa kumpingo. (1 Akor. 5:11-13) Koma ngati ni wolapa, angathe kukhalabe mumpingo. Ngakhale n’telo, akulu amamuuza kuti sangayenelele kutumikila pa udindo uliwonse mumpingo, kapena kupatsidwa utumiki uliwonse wapadela, kwa zaka zambili ngakhale kwa moyo wake wonse. Pofuna kuteteza ana, akulu angacenjeze mwamseli makolo amene ali ndi ana ang’ono-ang’ono mumpingo, kuti afunika kukhala chelu ngati anawo ali pafupi na munthuyo. Pamene akuluwo akucenjeza makolo, ayenela kupewa kuulula maina a anthu amene anacitilidwapo zolaula na munthuyo.
MMENE MUNGATETEZELE ANA ANU
19-22. Kodi makolo angacite ciani kuti ateteze ana awo kwa anthu ocitila ana zolaula? (Onani cithunzi pacikuto.)
19 N’ndani ali na udindo woteteza ana? Ni makolo. * Ana anu ni mphatso yamtengo wapatali, “colowa cocokela kwa Yehova.” (Sal. 127:3) Ni udindo wanu kuwateteza. Kodi mungacite ciani kuti muteteze ana anu kwa anthu amene amacitila ana zolaula?
20 Coyamba, idziŵeni bwino nkhani ya kucitila ana zolaula. Dziŵani mtundu wa anthu amene amacitila ana zolaula, na zimene amakonda kucita pofuna kunyengelela ana. Khalani chelu ndi anthu kapena mikhalidwe imene ingaike ana anu paciopsezo. (Miy. 22:3; 24:3) Kumbukilani kuti nthawi zambili, amene amacitila ana zolaula amakhala anthu amene anawo amawadziŵa na kuwadalila.
21 Caciŵili, khalani na cizoloŵezi cokambilana momasuka ndi ana anu. (Deut. 6:6, 7) Izi ziphatikizapo kumvetsela mwachelu zimene anawo akukamba. (Yak. 1:19) Kumbukilani kuti kaŵili-kaŵili ana amaopa kufotokoza ngati acitilidwa zolaula. Amaopa kuti ena sadzawakhulupilila. Komanso, akhoza kukhala kuti munthuyo anawaopseza kuti asakaulule zimene zinacitikazo. Mukazindikila kuti pali cina cake cimene sicili bwino, m’funseni mafunso mosamala kuti mudziŵe zimene zinacitika. Ndipo mvetselani moleza mtima pamene akufotokoza.
22 Cacitatu, phunzitsani ana anu. Phunzitsani ana anu mfundo zokhudza kugonana malinga na msinkhu wawo. Aphunzitseni zimene anganene kapena kucita ngati munthu wina afuna kuwagwila malo obisika. Gwilitsilani nchito malangizo amene gulu la Mulungu lakhala likupeleka pankhani ya mmene makolo angatetezele ana awo.—Onani bokosi yakuti “Dziphunzitseni Nokha Komanso Phunzitsani Ana Anu.”
23. Kodi khalidwe locitila ana zolaula timaliona bwanji? Nanga nkhani yokonkhapo idzayankha funso liti?
23 Ife Mboni za Yehova timaona kuti kucitila ana zolaula ni chimo lalikulu kwambili komanso khalidwe lonyansa. Popeza timatsatila cilamulo ca Khristu, sitiikila kumbuyo anthu amene amacitila ana zolaula kuti asalandile cilango. Koma kodi tingawathandize bwanji abale na alongo amene anacitilidwapo zolaula? Nkhani yokonkhapo idzayankha funso limeneli.
NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna
^ ndime 5 M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingatetezele ana kwa anthu amene amacitila ana zolaula. Tidzaphunzila mmene akulu amatetezela mpingo, na mmene makolo angatetezele ana awo.
^ ndime 3 MAWU OFOTOKOZEDWA: Tikanena kuti kucitila mwana zolaula, titanthauza kuti munthu wamkulu wagwilitsila nchito mwana kukhutilitsa cilakolako cake ca kugonana. Zingaphatikizepo kugona naye, kumugona mkamwa kapena kumbuyo, kum’sisita malisece, maŵele, kapena matako, kapenanso kumucita zinthu zina zosayenela. Nthawi zambili ana amene amacitilidwa zolaula na atsikana, koma palinso anyamata ambili amene amacitilidwa nkhanza zimenezi. Cinanso, ngakhale kuti ambili amene amacitila ana zolaula ni amuna, palinso akazi ena amene amacita zimenezi.
^ ndime 5 MAWU OFOTOKOZEDWA: M’nkhani ino na yotsatila, mawu akuti “wocitilidwa zolaula” atanthauza munthu amene wacitilidwa zolaula ali mwana. Taseŵenzetsa mawu amenewa pofuna kumveketsa bwino mfundo yakuti mwanayo anam’vulaza na kum’pondeleza, komanso kuti iye si wolakwa.
^ ndime 11 Ngati munthu ni wodwala mwauzimu, sizitanthauza kuti safunika kupatsidwa cilango. Iye amakhalabe na mlandu pa zosankha zake na zocita zake zoipa, ndipo Yehova adzamuweluza mogwilizana na zocita zakezo.—Aroma 14:12.
^ ndime 16 Akulu sapempha mwana wocitilidwa zolaula kuti akhalepo pamene akukambilana na munthu amene anam’cita zolaula. Iwo angapemphe kholo lake kapena munthu wina amene mwanayo anamuuza nkhaniyo kuti awafotokozele zimene zinacitika. Mwa ici, amapewa kuwonjezela kuvutika maganizo kwa mwanayo pa zimene zinacitikazo.
^ ndime 19 Malangizo opita kwa makolo amene ali m’nkhani ino, apitanso kwa anthu ena amene ali na udindo wosamalila ana aang’ono.