Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 18

Cikondi na Cilungamo Mumpingo Wacikhristu

Cikondi na Cilungamo Mumpingo Wacikhristu

“Musaleke kunyamulilana zolemetsa. Mukatelo mudzakhala mukukwanilitsa cilamulo ca Khristu.”—AGAL. 6:2.

NYIMBO 12 Mulungu Wamkulu, Yehova

ZA M’NKHANI INO *

1. Kodi ni mfundo ziŵili ziti zimene sitikayikila?

YEHOVA MULUNGU nthawi zonse amakonda atumiki ake, ndipo adzapitilizabe kuwakonda. Iye amakondanso cilungamo. (Sal. 33:5) Conco, sitikayikila mfundo ziŵili izi: (1) Cimamuŵaŵa kwambili Yehova akaona atumiki ake akucitilidwa zinthu mopanda cilungamo, ndiponso (2) Adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika, ndipo anthu oipa alandila cilango cowayenelela. M’nkhani yoyamba pa nkhani zinayizi, zofotokoza cikondi na cilungamo ca Yehova, * tinaphunzila kuti Cilamulo cimene Mulungu anapatsa Aisiraeli kupitila mwa Mose, cinazikidwa pa cikondi. Cilamulo cimeneco cinali kulimbikitsa anthu kucita zinthu mwacilungamo ndi anthu onse, maka-maka anthu osatetezeka. (Deut. 10:18) Cilamuloco cinaonetsanso kuti Yehova amakonda kwambili atumiki ake.

2. Kodi tidzakambilana mafunso ati?

2 Cilamulo ca Mose cinatha mu 33 C.E., pamene mpingo wacikhristu unakhazikitsidwa. Kodi izi zinatanthauza kuti Akhristu sadzakhala na cilamulo cozikidwa pa cikondi komanso colimbikitsa cilungamo? Kutalitali! Akhristu anapatsidwa cilamulo catsopano. M’nkhani ino, coyamba tikambilana zimene cilamulo catsopano cimeneci cimaphatikizapo. Kenako, tiyankha mafunso aya: N’cifukwa ciani tikamba kuti cilamulo cimeneci n’cozikidwa pa cikondi? N’cifukwa ciani tikambanso kuti cimalimbikitsa cilungamo? Nanga anthu amene ali na udindo pansi pa cilamulo cimeneci, ayenela kucita bwanji zinthu ndi ena?

KODI “CILAMULO CA KHRISTU” CIMAPHATIKIZAPO CIANI?

3. Kodi “cilamulo ca Khristu” cochulidwa pa Agalatiya 6:2 cimaphatikizapo ciani?

3 Ŵelengani Agalatiya 6:2. Akhristu ali pansi pa “cilamulo ca Khristu.” Yesu sanalembe m’ndandanda wa malamulo amene ophunzila ake afunika kutsatila. Koma anawapatsa malangizo, malamulo, na mfundo zimene afunika kutsatila muumoyo wawo. “Cilamulo ca Khristu” cimaphatikizapo zonse zimene Yesu anaphunzitsa. Kuti mucidziŵe bwino cilamulo cimeneci, ganizilani mfundo zotsatilazi.

4-5. Kodi Yesu anali kuwaphunzitsa bwanji anthu? Ndipo ni liti pamene anawaphunzitsa?

4 Kodi Yesu anali kuwaphunzitsa bwanji anthu? Coyamba, anali kuwaphunzitsa mwa zokamba zake. Uthenga umene anali kuwauza unali wogwila mtima cifukwa anali kuphunzitsa anthu coonadi ponena za Mulungu na colinga ca moyo. Anali kuwaphunzitsanso kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo udzacotsapo mavuto onse amene anthu timakumana nawo. (Luka 24:19) Yesu anali kuphunzitsanso anthu mwa zocita zake. Inde, mwa citsanzo cake, anaphunzitsa otsatila ake mmene anafunikila kukhalila.—Yoh. 13:15.

5 Ni liti pamene Yesu anaphunzitsa anthu? Anacita izi panthawi ya utumiki wake padziko lapansi. (Mat. 4:23) Iye anaphunzitsanso otsatila ake pambuyo poukitsidwa kwa akufa. Mwacitsanzo, anaonekela kugulu la ophunzila ake, mwina oposa 500, na kuwapatsa lamulo lakuti ‘akaphunzitse anthu.’ (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 15:6) Monga mutu wa mpingo, Yesu atabwelela kumwamba, anapitiliza kupeleka malangizo kwa ophunzila ake. Mwacitsanzo, ca m’ma 96 C.E., Khristu analamula mtumwi Yohane kuti apeleke uphungu na cilimbikitso kwa Akhristu odzozedwa.—Akol. 1:18; Chiv. 1:1.

6-7. (a) Kodi ziphunzitso za Yesu zinalembedwa kuti? (b) Kodi timamvela bwanji cilamulo ca Khristu?

6 Kodi zimene Yesu anaphunzitsa zinalembedwa kuti? Zinalembedwa m’mabuku anayi a Uthenga Wabwino. Mabukuwa amafotokoza zinthu zambili zimene Yesu anakamba na kucita ali pano padziko lapansi. Mabuku ena onse a m’Malemba Acigiliki Acikhristu amatithandiza kudziŵa bwino maganizo a Khristu pankhani zosiyana-siyana. Zili conco cifukwa cakuti analembedwa ndi amuna ouzilidwa na mzimu woyela, amene anali na “maganizo a Khristu.”—1 Akor. 2:16.

7 Zimene tiphunzilapo: Zimene Yesu anaphunzitsa n’zothandiza m’mbali zonse za moyo wathu. Conco, cilamulo ca Khristu cimakhudza mmene timacitila zinthu kunyumba, kunchito, kusukulu na mumpingo. Timaphunzila cilamulo cimeneci mwa kuŵelenga Malemba Acigiriki Acikhristu na kuwasinkha-sinkha. Ndipo timamvela cilamulo cimeneci mwa kukhala na umoyo wogwilizana na malangizo, malamulo ndi mfundo zopezeka m’Malemba amenewo. Ngati timvela cilamulo ca Khristu, ndiye kuti tikumvela Yehova Mulungu wathu wacikondi, amene ni Gwelo la zonse zimene Yesu anaphunzitsa.—Yoh. 8:28

CILAMULO COZIKIDWA PA CIKONDI

8. Kodi maziko a cilamulo ca Khristu n’ciani?

8 Ngati nyumba ni yomangidwa pa maziko olimba, anthu okhalamo amaona kuti ni otetezeka. Mofananamo, anthu amene amamvela cilamulo cokhala na maziko olimba, amakhala otetezeka. Ndipo cilamulo ca Khristu n’cozikidwa pa maziko olimba kwambili a cikondi. N’cifukwa ciani takamba conco?

Pamene ticita zinthu mwacikondi ndi ena, ndiye kuti tikumvela “cilamulo ca Khristu” (Onani ndime 9-14) *

9-10. Ni zitsanzo ziti zimene zionetsa kuti Yesu anali kucita zinthu cifukwa cokonda anthu? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

9 Coyamba, Yesu anali kusonkhezeledwa na cikondi m’zocita zake zonse. Kucitila ena cifundo ni njila imodzi yoonetsela kuti timawakonda. Cifundo n’cimene cinasonkhezela Yesu kuphunzitsa makamu a anthu, kucilitsa odwala, kudyetsa anjala, na kuukitsa akufa. (Mat. 14:14; 15:32-38; Maliko 6:34; Luka 7:11-15) Olo kuti kucita izi kunali kumuwonongela nthawi yoculuka na mphamvu, Yesu anaikabe zofuna za ena patsogolo pa zofuna zake. Koposa zonse, iye anaonetsa cikondi cacikulu mwa kupeleka moyo wake cifukwa ca ife.—Yoh. 15:13

10 Zimene tiphunzilapo: Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu. Tingatengelenso citsanzo cake mwa kuyesetsa kuonetsa cifundo kwa anthu a m’gawo lathu. Ngati tiyesetsa kulalikila anthu na kuwaphunzitsa uthenga wabwino cifukwa cowamvela cifundo, ndiye kuti tikumvela cilamulo ca Khristu.

11-12. (a) N’ciani cimaonetsa kuti Yehova amatikonda kwambili? (b) Kodi tingatengele bwanji cikondi ca Yehova?

11 Caciŵili, Yesu anaonetsa cikondi ca Atate ake. Pautumiki wake, Yesu anaonetsa bwino cikondi cacikulu cimene Yehova ali naco pa olambila ake. Imodzi mwa mfundo zimene Yesu anaphunzitsa inali yakuti: Atate wathu wakumwamba amaona kuti aliyense wa ife ni wamtengo wapatali komanso wofunika kwambili. (Mat. 10:31) Yehova ni wofunitsitsa kulandila nkhosa yosocela imene yalapa na kubwelela mumpingo wake. (Luka 15:7, 10) Iye anaonetsanso cikondi pa ife mwa kupeleka Mwana wake monga dipo lotiwombola.—Yoh. 3:16.

12 Zimene tiphunzilapo: Kodi tingatengele bwanji cikondi ca Yehova? (Aef. 5:1, 2) Tiyenela kuona abale na alongo athu kukhala ofunika kwambili. Tiyenelanso kulandila mwacimwemwe “nkhosa yosocela” imene yabwelela kwa Yehova. (Sal. 119:176) Timaonetsanso kuti timakonda abale na alongo athu mwa kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu powathandiza akakumana na mavuto. (1 Yoh. 3:17) Tikamacitila ena zinthu mwacikondi, timaonetsa kuti timamvela cilamulo ca Khristu.

13-14. (a) Malinga ndi Yohane 13:34, 35, kodi Yesu anawalamula ciani otsatila ake? Nanga n’cifukwa ciani limeneli ni lamulo latsopano? (b) Kodi timaonetsa bwanji kuti timamvela lamulo latsopano limeneli?

13 Cacitatu, Yesu analamula otsatila ake kuti ayenela kuonetsana cikondi codzimana. (Ŵelengani Yohane 13:34, 35.) Lamulo la Yesu limeneli n’latsopano cifukwa cakuti, mosiyana na Cilamulo ca Mose, lamuloli limafuna kuti tizikonda okhulupilila anzathu monga mmene Yesu anatikondela. Izi zitanthauza kuti tiyenela kukhala na cikondi codzimana. * Tifunika kukonda abale na alongo athu kuposa mmene timadzikondela ife eni. Tiyenela kuwakonda kwambili mpaka kufika poti n’kuwafela, ngati mmene Yesu anacitila.

14 Zimene tiphunzilapo: Tingaonetse bwanji kuti timamvela lamulo latsopano? Tingacite izi mwa kudzimana zinthu zina m’malo mwa abale na alongo athu. Ndife okonzeka ngakhale kupeleka moyo wathu kaamba ka iwo. Kuwonjezela apo, ndife okonzeka kudzimana zinthu zina zazing’ono. Mwacitsanzo, ngati nthawi zambili timayesetsa kuthandiza m’bale kapena mlongo wacikulile na mayendedwe opita kumisonkhano, ndiye kuti tikumvela cilamulo ca Khristu. Tingaonetsenso kuti timamvela cilamulo ca Khristu mwa kukhala okonzeka kudzimana zinthu zimene timakonda, n’colinga cakuti tikondweletse wokondedwa wathu. Mwinanso tingatenge chuti kunchito kuti ticilikize pa nchito yothandiza anthu okhudzidwa na tsoka la zacilengedwe. Tikamacita zimenezi, timathandizanso kuti aliyense mumpingo azidziona kuti ni wotetezeka.

CILAMULO CA KHRISTU CIMALIMBIKITSA CILUNGAMO

15-17. (a) Kodi zocita za Yesu zinaonetsa bwanji kuti amakonda cilungamo? (b) Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu?

15 M’Baibo, liwu lakuti “cilungamo” limatanthauza kucita zinthu zimene Mulungu amaona kuti n’zoyenela, komanso kuzicita mopanda tsankho. N’cifukwa ciani tikamba kuti cilamulo ca Khristu cimalimbikitsa cilungamo?

Yesu anali kulemekeza akazi na kucita nawo zinthu mokoma mtima, kuphatikizapo amene anali kuoneka onyozeka m’maso mwa ena (Onani ndime 16) *

16 Coyamba, ganizilani mmene zocita za Yesu zinaonetsela kuti iye amakonda cilungamo. M’masiku a Yesu, atsogoleli a cipembedzo ca Ciyuda anali kuzonda anthu amene sanali Ayuda. Anali kuona Ayuda wamba monga osanunkha kanthu. Kuwonjezela apo, sanali kulemekeza akazi. Koma Yesu anali kucita zinthu ndi anthu onse mwacilungamo na mopanda tsankho. Iye analola ngakhale anthu a mitundu ina, amene anali na cikhulupililo mwa iye kuti azimutsatila. (Mat. 8:5-10, 13) Yesu anali kulalikila kwa anthu onse, kaya olemela kapena osauka. (Mat. 11:5; Luka 19:2, 9) Iye sanali kucita zinthu mwaukali kapena mwankhanza ndi akazi. Koma anali kuwalemekeza na kuwakomela mtima. Anali kucita zimenezi ngakhale kwa akazi amene anthu anali kuwaona kuti ni onyozeka.—Luka 7:37-39, 44-50.

17 Zimene tiphunzilapo: Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kucita zinthu mopanda tsankho ndi ena, na kulalikila kwa anthu onse ofuna kumvetsela uthenga wabwino, mosasamala kanthu kuti ni olemela kapena osauka, kapenanso kuti ni acipembedzo canji. Amuna acikhristu amatsatila citsanzo ca Yesu mwa kucita zinthu mwaulemu na akazi. Tikamacita zimenezi, ndiye kuti tikumvela cilamulo ca Khristu.

18-19. Kodi Yesu anaphunzitsa ciani ponena za cilungamo? Nanga tiphunzilapo ciani pa zimene anaphunzitsa?

18 Caciŵili, ganizilani zimene Yesu anaphunzitsa anthu ponena za cilungamo. Iye anaphunzitsa otsatila ake mfundo zimene zinawathandiza kucita zinthu mwacilungamo ndi anthu ena. Mwacitsanzo, ganizilani za mfundo yocitila ena zabwino imene Yesu anakamba. (Mat. 7:12) Tonse timafuna kuti anthu ena aziticitila zinthu mwacilungamo. Conco, nafenso tifunika kucita zinthu mwacilungamo ndi ena. Tikatelo, iwonso adzalimbikitsidwa kucita nafe zinthu mwacilungamo. Nanga bwanji ngati anthu ena aticitila zinthu mopanda cilungamo? Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti zinthu zikakhala conco, ayenela kukhala na cidalilo cakuti Yehova ‘adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa iwo, amene amafuulila kwa iye usana ndi usiku.’ (Luka 18:6, 7) Apa tinganene kuti Yesu anali kutitsimikizila kuti Mulungu wathu wacilungamo, amaona masautso amene timakumana nawo masiku otsiliza ano, ndipo adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika pa nthawi yake yoyenela.—2 Ates. 1:6.

19 Zimene tiphunzilapo: Tikamatsatila mfundo zimene Yesu anaphunzitsa, tidzayamba kucita zinthu mwacilungamo ndi anthu ena. Ndipo ngati tikuvutika cifukwa cakuti anthu ena aticitila zinthu mopanda cilungamo m’dziko la Satanali, tidzalimbikitsidwa podziŵa kuti Yehova adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika.

KODI AMENE ALI NA UDINDO AYENELA KUCITA BWANJI NDI ENA?

20-21. (a) Kodi amene ali na udindo ayenela kucita bwanji ndi ena? (b) Kodi mwamuna angaonetse bwanji cikondi codzimana? Nanga tate ayenela kucita bwanji ndi ana ake?

20 Malinga na cilamulo ca Khristu, kodi amene ali na udindo ayenela kucita bwanji zinthu ndi ena? Popeza cilamuloci cinazikidwa pa cikondi, iwo afunika kulemekeza anthu amene amawayang’anila. Afunikanso kucita nawo zinthu mwacikondi. Ayenela kukumbukila kuti Khristu amafuna kuti tizicita zinthu mwacikondi nthawi zonse.

21 M’banja. Mwamuna ayenela kukonda mkazi wake “monga mmene Khristu anakondela mpingo.” (Aef. 5:25, 28, 29) Mwamuna ayenela kutengela Khristu mwa kukhala na cikondi codzimana. Ndipo angaonetse kuti ali na cikondi cotelo mwa kuika zofuna za mkazi wake patsogolo pa zofuna zake. Amuna ena zimawavuta kuonetsa cikondi cimeneci, mwina cifukwa cakuti anakulila m’dela limene anthu sakonda kucitila ena zinthu mwacilungamo komanso mwacikondi. Amuna amenewa zingawavute kuleka zizoloŵezi zoipa zimene angakhale nazo. Koma afunika kuyesetsa kusintha. Akatelo, adzaonetsa kuti amamvela cilamulo ca Khristu. Ngati mwamuna amaonetsa cikondi codzimana kwa mkazi wake, mkaziyo amam’lemekeza. Ndipo tate amene amakondadi ana ake, amapewa kuwacitila nkhanza anawo kaya mwa zokamba kapena zocita zake. (Aef. 4:31) M’malomwake, amacita zinthu zoonetsa kuti amawakonda, ndipo izi zimathandiza kuti anawo aziona kuti ni otetezeka. Tate amene amacita zinthu mwanjila imeneyi, ana ake amam’konda na kum’dalila.

22. Mogwilizana ndi 1 Petulo 5:1-3, kodi “nkhosa” za mumpingo ni za ndani? Nanga nkhosazo ziyenela kusamalidwa bwanji?

22 Mumpingo. Akulu afunika kukumbukila kuti “nkhosa” za mumpingo si zawo. (Yoh. 10:16; ŵelengani 1 Petulo 5:1-3.) Mawu akuti “gulu la nkhosa za Mulungu” ndi akuti “colowa cocokela kwa Mulungu,” amakumbutsa akulu kuti nkhosazo ni za Yehova. Iye amafuna kuti nkhosa zake zizisamalidwa mwacikondi ndi mokoma mtima. (1 Ates. 2:7, 8) Akulu amene amatumikila ena mwacikondi monga abusa, Yehova amakondwela nawo. Ndipo nawonso abale na alongo amawalemekeza na kuwakonda.

23-24. (a) Kodi akulu ali na udindo wotani poweluza mlandu wa munthu amene wacita colakwa cacikulu mumpingo? (b) Nanga amaganizila ciani poweluza mlandu wotelo?

23 Kodi akulu ali na udindo wotani poweluza mlandu wa munthu amene wacita chimo lalikulu? Udindo wawo ni wosiyana na udindo umene oweluza komanso akulu aciisiraeli anali nawo m’nthawi ya Cilamulo ca Mose. M’Cilamulo ca Mose, oweluza komanso akulu sanali kuweluza cabe milandu yokhudzana ndi kulambila. Anali kuweluzanso milandu ina yosakhudzana kweni-kweni na kulambila. Koma m’cilamulo ca Khristu, ngati munthu wacita colakwa, udindo wa akulu ni kusamalila mbali yokhudza kulambila ya mlanduwo. Akulu mumpingo amazindikila kuti mololedwa na Mulungu, olamulila a dziko ndiwo ali na udindo woweluza milandu munthu akaphwanya malamulo a boma. Udindo wawo uphatikizapo kupeleka cilango kwa munthu amene wacita colakwa, mwina mwa kumulipilitsa kapena kumuika m’ndende.—Aroma 13:1-4.

24 Kodi akulu amasamalila bwanji mlandu wa munthu amene wacita colakwa cacikulu mumpingo? Iwo amapenda mosamala nkhaniyo pogwilitsila nchito Malemba, ndipo kenako amapanga cigamulo. Akulu amakumbukila kuti cilamulo ca Khristu n’cozikidwa pa cikondi. Conco, cifukwa ca cikondi, amayesetsa kuganizila zimene angacite kuti athandize aliyense mumpingo amene wakhudzidwa na colakwaco. Cinanso, mwacikondi akulu amayesetsa kupenda kuti aone ngati wolakwayo ni wolapa. Ndipo amaganizilanso zimene angacite kuti amuthandize kukonzanso ubwenzi wake na Yehova.

25. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

25 Ndithudi! Ndife oyamikila kwambili kaamba ka cilamulo ca Khristu. Tonse tikamayesetsa kumvela cilamulo cimeneci, aliyense mumpingo amadziona kukhala wokondedwa, wofunika, na wotetezeka. Komabe, tikukhala m’dziko limene ‘anthu oipa . . . akuipilaipilabe.’ (2 Tim. 3:13) Conco, tifunika kukhala maso. Kodi mpingo wacikhristu ungaonetse bwanji cilungamo ca Mulungu pa milandu yocitila ana zolaula? M’nkhani yotsatila, tidzayankha funso limeneli.

NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova

^ ndime 5 Nkhani ino na ziŵili zotsatila, zili m’gulu la nkhani zinayi zofotokoza cifukwa cake ndife otsimikiza kuti Yehova ni Mulungu wacikondi komanso wacilungamo. Iye amafuna kuti anthu ake azicitilidwa zinthu mwacilungamo, ndipo amatonthoza anthu amene amacitilidwa zinthu mopanda cilungamo m’dziko loipali.

^ ndime 1 Onani nkhani yakuti “Cikondi na Cilungamo M’nthawi ya Aisiraeli,” mu Nsanja ya Mlonda ya February 2019.

^ ndime 13 MAWU OFOTOKOZEDWA: Cikondi codzimana cimatisonkhezela kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu. Timakhala okonzeka kudzimana zinthu zina kuti tithandize anthu ena.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Yesu akuyang’ana mkazi wamasiye amene mwana wake mmodzi yekha wamwamuna wamwalila. Atagwidwa na cifundo, iye aukitsa mnyamatayo.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Yesu ali pa cakudya m’nyumba ya Mfarisi dzina lake Simoni. Mkazi wina, amene mwina ni hule, wanyowetsa mapazi a Yesu na misozi yake, wapukuta mapaziwo na tsitsi lake na kuwapaka mafuta. Simoni akuipidwa na zocita za mkaziyo, koma Yesu akumuikila kumbuyo mkaziyo.