Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 22

Khalani na Cizoloŵezi Cabwino Coŵelenga

Khalani na Cizoloŵezi Cabwino Coŵelenga

“Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”—AFIL. 1:10.

NYIMBO 35 ‘Tsimikizilani Zinthu Zofunika Kwambili’

ZA M’NKHANI INO *

1. N’cifukwa ciani ena sakonda kuŵelenga?

MASIKU ANO, pamafunika khama kwambili kuti munthu apeze zofunikila muumoyo. Abale athu ambili amaseŵenza kwa maola oculuka, kuti apeze zosoŵa za mabanja awo. Enanso ambili amathela maola oculuka patsiku, poyenda kunchito na pobwelako. Palinso abale na alongo ambili amene amaseŵenza nchito zolemetsa, kuti akwanitse kusamalila mabanja awo. Pofika panyumba, abale na alongo olimbika pa nchito amenewa, amakhala olema ngako! Popeza amakhala olema, cimakhala covuta kuti aŵelenge.

2. Kodi ni nthawi yanji imene mumapeza mpata woŵelenga?

2 Ngakhale zili conco, mfundo ni yakuti tifunika kupeza nthawi yoŵelenga mozama Mawu a Mulungu na mabuku athu. Ubwenzi wathu na Yehova komanso ciyembekezo cathu ca moyo wosatha, zimadalila pa kucita zimenezi. (1 Tim. 4:15) Ena amauka m’mamaŵa tsiku lililonse na kuyamba kuŵelenga, panthawi imene kulibe congo, pamenenso maganizo awo ali okhazikika bwino. Enanso amapatula nthawi yocepa madzulo pamene kuli bata kuti aŵelenge na kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu.

3-4. Kodi panakhala kusintha kotani pankhani ya kuculuka kwa mabuku amene timalandila? Nanga cifukwa cake n’ciani?

3 Mosakayikila, mukugwilizana nayo mfundo yakuti kupeza nthawi yoŵelenga n’kofunika. Koma kodi n’ziti makamaka zimene tiyenela kuŵelenga? Mwina mungakambe kuti, ‘Pali zambili zofunika kuŵelenga. Nimalephela kuŵelenga zonse.’ Abale na alongo ena amakwanitsa kudya cakudya cauzimu conse cimene timalandila. Koma ena ambili sakwanitsa kupeza nthawi yocita zimenezi. Bungwe Lolamulila lidziŵa vuto limeneli. Ndiye cifukwa cake posacedwapa, bungweli linagamula zocepetsako ciŵelengelo ca mabuku na nkhani zimene amafalitsa pa Intaneti.

4 Mwacitsanzo, tsopano sitifalitsanso Buku Lapachaka la Mboni za Yehova, cifukwa cakuti zocitika zambili zolimbikitsa zimafalitsidwa pa jw.org®, komanso pa mapulogilamu apamwezi a JW Broadcasting®. Ndipo magazini a Nsanja ya Mlonda yogaŵila na Galamuka!, tsopano amafalitsidwa katatu cabe pacaka. Masinthidwe amenewa sanapangidwe n’colinga cakuti tizikhala na nthawi yoculuka yocita zinthu zakuthupi iyai. Koma anapangidwa pofuna kutithandiza kukhala na nthawi yokwanila yocita “zinthu zofunika kwambili.” (Afil. 1:10) Tsopano, tiyeni tikambilane mmene tingasankhile zinthu zofunika kuika patsogolo muumoyo. Tikambilananso zimene tingacite kuti tizipindula kwambili na zimene timaŵelenga.

SANKHANI ZOFUNIKA KUIKA PATSOGOLO MUUMOYO

5-6. N’zofalitsa ziti zimene tiyenela kuyesetsa kuziŵelenga mosamala?

5 Kodi n’zinthu ziti zimene tiyenela kuika patsogolo muumoyo wathu? Coyamba, ni kuŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Conco, tifunika kumapatula nthawi yocita zimenezi. Macaputa amene timaŵelenga mlungu na mlungu pa kuŵelenga Baibo kwa mpingo, lomba anacepetsedwa. Masinthidwe amenewa anapangidwa n’colinga cakuti tizikhala na nthawi yokwanila yosinkha-sinkha pa zimene timaŵelenga, ndi yofufuza mfundo zina. Conco, colinga cathu siciyenela kukhala kungotsiliza kuŵelenga macaputa a wikiyo. M’malomwake, tiyenela kulola uthenga wa m’Baibo kutifika pamtima, na kutithandiza kuyandikila kwambili Yehova.—Sal. 19:14.

6 N’zinthu zina ziti zimene tiyenela kuŵelenga mosamala? Tiyenela kukonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda na Phunzilo la Baibo la Mpingo, komanso nkhani zina za mumsonkhano wa Umoyo na Utumiki Wathu. Tiyenelanso kumaŵelenga magazini onse a Nsanja ya Mlonda na Galamuka! amene timalandila.

7. Kodi tifunika kugwa mphwayi ngati sitikwanitsa kuŵelenga na kutamba zonse zimene zimatulutsidwa pa webusaiti yathu na pa JW Broadcasting?

7 Koma mwina mungakambe kuti, ‘Nanga bwanji za mavidiyo na nkhani zambili-mbili zimene zimatulutsidwa pa webusaiti yathu ya jw.org, na pa JW Broadcasting? Niona kuti zinthu zofunika kuŵelenga na kutamba n’zoculuka kwambili.’ Cabwino, ganizilani izi: M’lesitilanti mumakhala zakudya zambili-mbili zopatsa thanzi ndi zamitundu-mitundu. Zakudyazo zimakhala zoculuka kwambili cakuti makasitoma sangakwanitse kudyako zakudya zonse. Conco, amasankhapo zakudya zocepa cabe zimene angakwanitse kudya. Mofananamo, ngati simukwanitsa kuŵelenga nkhani kapena kutamba mavidiyo onse amene timalandila pa Intaneti, musagwe mphwayi. Ŵelengani na kutamba zimene mungakwanitse. Tsopano tiyeni tikambilane zimene tiyenela kucita poŵelenga, komanso zimene tingacite kuti tizipindula kwambili na zimene timaŵelenga.

KUŴELENGA NI NCHITO

8. Tingacite ciani pokonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda? Nanga kucita zimenezi kudzatipindulitsa bwanji?

8 Pamene tiŵelenga, tifunika kukhala na colinga cophunzila mfundo inayake yofunika. Sitifunika kungoŵelenga mothamanga nkhani yophunzila na kuconga mayankho. Mwacitsanzo, pokonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, coyamba ŵelengani mbali yakuti Za M’nkhani Ino, imene imapezeka kuciyambi kwa nkhaniyo. Ndiyeno, pendani mutu wa nkhaniyo, tumitu twatung’ono na mafunso obwelelamo. Kenako, ŵelengani nkhaniyo modekha bwino komanso mosamala. Pamene muŵelenga, ganizilani mfundo yaikulu m’ndime iliyonse. Nthawi zambili mfundo yaikulu m’ndime imakhala m’ciganizo coyamba ca ndimeyo. Kudziŵa mfundo yaikulu m’ndime kudzakuthandizani kuona kumene nkhaniyo ikuloŵela. Pamene muŵelenga nkhaniyo, ganizilaninso mmene ndime iliyonse igwilizanilana na kamutu kakang’ono komanso mfundo yaikulu m’nkhaniyo. Ikani cizindikilo pa mawu aliwonse amene simuwadziŵa, kapena pa mfundo imene mufuna kuifufuza mowonjezeleka kuti muimvetsetse.

9. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuŵelenga mosamala malemba pokonzekela Nsanja ya Mlonda? Nanga tingacite bwanji zimenezi? (b) Malinga n’zimene Yoswa 1:8 imakamba, kodi tikaŵelenga malemba tiyenelanso kucita ciani?

9 Kuphunzila Nsanja ya Mlonda pa misonkhano, kumatithandiza kumvetsetsa Baibo. Conco, pokonzekela muziŵelenga mosamala malemba, maka-maka amene adzaŵelengedwa ku Nyumba ya Ufumu pocita phunzilolo. Mukaŵelenga lemba, ganizilani mmene mawu a palembalo akucilikizila mfundo ya m’ndimeyo. Komanso, sinkha-sinkhani pa malemba amene mwaŵelenga, ndipo ganizilani mmene mungaseŵenzetsele mfundo zimene mwaphunzila pa malembawo.—Ŵelengani Yoswa 1:8.

Makolo, phunzitsani ana anu mmene angacitile phunzilo laumwini (Onani ndime 10) *

10. Mogwilizana na Aheberi 5:14, n’cifukwa ciani makolo pa kulambila kwa pabanja ayenela kuphunzitsa ana awo mocitila phunzilo laumwini ndi mofufuzila nkhani?

10 M’pomveka kuti makolo amafuna kuti kulambila kwawo kwa pabanja kuzikhala nthawi yokondweletsa kwa ana awo. N’zoona kuti makolo afunika kukonzekela bwino pulogilamu ya kulambila kwa pabanja. Koma sikuti wiki iliyonse afunika kukonza zocita zinthu zinazake zapadela kapena zokondweletsa pa pulogilamuyi. Pa Kulambila kwa Pabanja, tingaonelele pulogilamu yapamwezi ya JW Broadcasting, ndipo mwa apo na apo tingacite zinthu zinazake zapadela, monga kupanga cifanizilo ca cingalawa ca Nowa. Komabe, kuphunzitsa ana mmene angacitile phunzilo laumwini n’kofunikanso kwambili. Mwacitsanzo, tiyenela kuwaphunzitsa mokonzekelela misonkhano, kapena mofufuzila mayankho pa mafunso amene anzawo angawafunse kusukulu. (Ŵelengani Aheberi 5:14.) Ngati ana ali na cizoloŵezi coŵelenga kunyumba, amakhala amvetseli achelu ku misonkhano yampingo, yadela, kapena yacigawo, kumene nthawi zina sikukhala mavidiyo. Koma kutalika kwa nthawi imene mungaŵelenge limodzi na mwana kumadalila msinkhu wa mwanayo na cibadwa cake.

11. N’cifukwa ciani kuphunzitsa maphunzilo athu a Baibo mocitila phunzilo laumwini n’kofunika kwambili?

11 Nawonso maphunzilo athu a Baibo, tifunika kuwaphunzitsa mmene angacitile phunzilo laumwini. Tikangoyamba kuphunzila nawo, timakondwela tikaona kuti aconga mayankho m’buku lawo pokonzekela phunzilo la Baibo, kapena pokonzekela misonkhano ya mpingo. Koma tifunikanso kuwaphunzitsa mmene angafufuzile nkhani zosiyana-siyana, ndi mmene angacitile phunzilo laumwini lopindulitsa. Tikacita zimenezi, ndiye kuti akakumana na vuto linalake, sadzathamangila kukafunsa malangizo kwa ena mumpingo. M’malomwake, adzakwanitsa kudzipezela okha malangizo othandiza pa vuto lawo, mwa kufufuza m’mabuku athu.

MUZIŴELENGA NA COLINGA

12. Kodi n’zolinga ziti zimene mungakhale nazo pamene muŵelenga?

12 Ngati simukonda zoŵelenga-ŵelenga, mwina mungaganize kuti n’zosatheka kusangalala poŵelenga. Koma n’zotheka kusangalala. Yambani mwa kuŵelenga kwa nthawi yocepa. Ndiyeno muziwonjezela pang’ono-pang’ono nthawi yoŵelenga. Kuwonjezela apo, khalani na colinga. Colinga canu cacikulu ciyenela kukhala kulimbitsa ubwenzi wanu na Yehova. Koma mungakhalenso na zolinga zina zing’ono zing’ono, monga kufufuza yankho pafunso limene winawake anakufunsani, kapena kufufuza mfundo zothandiza pa vuto limene muli nalo.

13. (a) Fotokozani zimene mwana wa sukulu angacite kuti akwanitse kuteteza cikhulupililo cake kusukulu. (b) Kodi mungaseŵenzetse bwanji malangizo a pa Akolose 4:6?

13 Mwacitsanzo, kodi ndinu wacicepele amene muli pasukulu? Mwina anzanu a m’kilasi amakuvutitsani cifukwa cakuti simuimbako nawo nyimbo ya fuko. Mungafune kucilikiza mfundo za m’Baibo pankhaniyi. Koma mwina mumaona kuti simungakwanitse kucita zimenezo. Conco, mungafunike kuŵelenga mosamala za nkhaniyo. Mungakhale na zolinga ziŵili izi (1) kulimbitsa cikhulupililo canu cakuti sitifunika kukhala mbali ya dziko, na (2) kukulitsa luso lanu loteteza coonadi. (Yoh. 17:16; 1 Pet. 3:15) Coyamba, dzifunseni kuti, ‘Kodi anzanga anakamba zotani pocilikiza mfundo yakuti kuimba nyimbo ya fuko n’kofunika?’ Ndiyeno, mwa kuseŵenzetsa mabuku athu, fufuzani mosamala za nkhaniyi. Musadele nkhawa kwambili kuti mwina anzanuwo sadzakhutila na mfundo zimene mwakonzekela. Dziŵani kuti anthu ambili amaimba nyimbo ya fuko, cabe cifukwa cakuti munthu winawake amene iwo amam’lemekeza anawauza kuti afunika kuimba. Ngati mwapeza mfundo imodzi cabe kapena ziŵili, mungakwanitse kupeleka mayankho okhutilitsa pa mafunso amene munthu woona mtima angakhale nawo.—Ŵelengani Akolose 4:6.

KULITSANI CIDWI CANU COŴELENGA

14-16. (a) Kodi mungacite ciani kuti muphunzile zambili zokhudza buku la m’Baibo limene simulidziŵa bwino? (b) Fotokozani mmene malemba a m’ndime 16 angakuthandizileni kumvetsetsa bwino buku la Amosi. (Onaninso bokosi Yakuti “ Muziyesetsa Kuona M’maganizo Mwanu Zimene Muŵelenga m’Baibo.”)

14 Tiyelekezele kuti pamsonkhano wotsatila tidzakambilana mfundo za m’buku limodzi mwa mabuku aulosi a m’Baibo, mwina limene simulidziŵa kweni-kweni. Coyamba, mungafunike kudziŵa bwino uthenga wa m’bukulo. Kodi mungacite bwanji zimenezi?

15 Dzifunseni kuti: ‘Kodi nidziŵa ciani za munthu amene analemba bukuli? Kodi anali ndani? Kodi anali kukhala kuti, nanga nchito yake inali yotani?’ Kudziŵa bwino umoyo wa wolembayo kungakuthandizeni kuzindikila cifukwa cake anaseŵenzetsa mawu kapena mafanizo amene ali m’bukulo. Pamene muŵelenga buku lililonse m’Baibo, onani mawu amene angakuthandizeni kudziŵa bwino umunthu wa wolembayo.

16 Cinanso, zingakhale zothandiza kudziŵa nthawi imene bukulo linalembedwa. Kuti mudziŵe, mungaone cakumapeto m’Baibulo la Dziko Latsopano, pa mbali yakuti “Mabuku a m’Baibulo ndi Tsatanetsatane Wake.” Kuwonjezela apo, mungaone chati ya aneneli na mafumu, m’Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu, peji 14-17. Ngati muŵelenga buku la m’Baibo la maulosi, mungacite bwino kufufuza mmene umoyo wa anthu unalili pamene bukulo linali kulembedwa. Kodi ni maganizo na makhalidwe oipa ati amene mneneliyo anafuna kuthandiza anthu kuwongolela? Ni anthu ati amene analipo m’nthawi ya mneneliyo? Kuti mumvetsetse mmene zinthu zinalili, mungafunike kufufuza zowonjezeleka m’mabuku ena a m’Baibo. Mwacitsanzo, kuti mudziŵe bwino mmene zinthu zinalili m’nthawi ya mneneli Amosi, mungaŵelenge mavesi a 2 Mafumu ndi 2 Mbiri, amene ali m’danga lapakati, pa Amosi 1:1. Kuwonjezela apo, mungaŵelengenso buku la Hoseya amene ayenela kuti analiko m’nthawi ya Amosi. Mabuku amenewa adzakuthandizani kumvetsetsa mmene umoyo unalili m’nthawi ya Amosi.—2 Maf. 14:25-28; 2 Mbiri 26:1-15; Hos. 1:1-11; Amosi 1:1.

POŴELENGA, MUZIDEKHA KUTI MUONE MFUNDO ZOBISIKA

17-18. Kodi kudekha poŵelenga kuti muone mfundo zobisika kumapangitsa bwanji phunzilo laumwini kukhala lokondweletsa? Poyankha, seŵenzetsani zitsanzo zili m’ndimezi kapena citsanzo canu.

17 Pamene tiŵelenga Baibo, tifunika kukhala na cidwi cofuna kumvetsetsa zambili. Tinene kuti mukuŵelenga caputa 12 ca ulosi wa Zekariya, cimene cinakambilatu za imfa ya Mesiya. (Zek. 12:10) Ndiyeno, pamene mwafika m’vesi 12, mukupeza mfundo yakuti “banja la nyumba ya Natani” lidzalila kwambili cifukwa ca imfa ya Mesiya. M’malo mongoŵelenga mofulumila vesiyo, imani pang’ono na kudzifunsa kuti: ‘Kodi pali kugwilizana kwanji pakati pa banja la Natani na Mesiya? Kodi ningacite ciani kuti nidziŵe zambili za nkhaniyi?’ Ndiyeno, mukufufuza kuti mudziŵe zambili. Mukuona kuti pavesiyo pali lifalensi yotsogolela ku 2 Samueli 5:13, 14, pamene pamakamba kuti Natani anali mmodzi mwa ana a Mfumu Davide. Lifalensi ina ni Luka 3:23, 31, imene imakamba kuti Yesu anali mbadwa ya Natani, kupitila mwa Mariya. (Onani Nsanja ya Mlonda yogaŵila, ya No. 3, 2016, peji 9.) Kodi mfundo imeneyi si yocititsa cidwi? Mwacionekele, ambili a ife timadziŵa kuti Baibo inakambilatu kuti Yesu adzakhala mbadwa ya Davide. (Mat. 22:42) Koma Davide anali ndi ana aamuna oposa 20. Ndithudi, n’zocititsa cidwi kuona kuti pa ana 20 amenewo, Zekariya anacita kuchula banja la Natani kuti lidzalila imfa ya Yesu.

18 Ganizilani citsanzo cina ici. M’caputa coyamba ca Luka, timaŵelenga kuti mngelo Gabirieli anaonekela kwa Mariya, na kumuuza mfundo zina zocititsa cidwi zokhudza mwana amene anali kudzabeleka. Mngeloyo anati: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzachedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wacifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulila monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya.” (Luka 1:32, 33) Nthawi zambili, tikaŵelenga uthenga wa Gabirieli umenewu, timaika maganizo kwambili pa mfundo yakuti Yesu adzachedwa “Mwana wa Wam’mwambamwamba.” Koma onani kuti Gabirieli analoselanso kuti Yesu “adzalamulila monga Mfumu.” Kodi muganiza kuti Mariya anamvela bwanji atauzidwa zimenezi? Kodi Mariya anaganiza kuti zimene Gabirieli anakamba zinatanthauza kuti Yesu adzatenga malo a Mfumu Herode, kapena a wina amene adzaloŵe m’malo mwa Herodeyo? Yesu akanakhaladi Mfumu, sembe Mariya wakhala mayi wa Mfumu, ndipo banja lake lonse likanakhala kunyumba yacifumu. Koma palibe paliponse m’Baibo pamene paonetsa kuti Mariya anafunsa mngelo Gabirieli za nkhaniyi. Palibenso pamene pamakamba kuti Mariya anapempha kuti akakhale pamalo a pamwamba mu Ufumu, monga mmene ophunzila ena aŵili a Yesu anacitila. (Mat. 20:20-23) Ndithudi, mfundoyi imatithandiza kuona kuti Mariya anali mayi wodzicepetsa kwambili!

19-20. Mogwilizana na Yakobo 1:22-25 komanso 4:8, n’zolinga ziti zimene timakhala nazo poŵelenga Baibo?

19 Tizikumbukila kuti colinga cathu cacikulu coŵelengela Mawu a Mulungu na mabuku athu, ni kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova. Timafunanso kudziŵa bwino kuti ndife “munthu wotani,” ndiponso kuti ni masinthidwe otani amene tifunika kupanga kuti tikondweletse Mulungu. (Ŵelengani Yakobo 1:22-25; 4:8.) Conco, nthawi zonse tisanayambe kuŵelenga, tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyela. Tizim’pemphanso kuti atithandize kupindula mokwanila na zimene tiŵelenga, na kuti atithandize kudziŵa zimene tifunika kuwongolela.

20 Tiyeni tonse tikhale monga munthu wa Mulungu wochulidwa m’buku la Masalimo. Ponena za iye, Baibo imati: “Amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amawelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku. . . . Zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”—Sal. 1:2, 3.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

^ ndime 5 Yehova amatipatsa zinthu zambili zofunika kutamba na kuŵelenga. Nkhani ino idzakuthandizani kudziŵa mmene mungasankhile nkhani zakuti muphunzile. Ndipo muli malangizo othandiza a zimene mungacite kuti muzipindula kwambili na phunzilo lanu laumwini.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Makolo aphunzitsa ana awo kukonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale akuŵelenga za mneneli Amosi. Zithunzi-thunzi zimene zili kumbuyo kwake, zionetsa zimene m’baleyo akuona m’maganizo mwake, pamene aŵelenga na kusinkha-sinkha pa mavesi a m’Baibo okamba za Amosi.