NKHANI YOPHUNZILA 20
Kulimbikitsa Amene Anacitilidwapo Zolaula
“Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 AKOR. 1:3, 4.
NYIMBO 134 Ana ni Mphatso Zimene Mulungu Amaikiza kwa Makolo
ZA M’NKHANI INO *
1-2. (a) N’citsanzo citi cimene cionetsa kuti mwacibadwa anthu amafuna kutonthozedwa na kuti ali na luso lotonthoza ena? (b) Kodi ana ena amavulala motani?
MWACIBADWA, ife anthu timafuna kutonthozedwa. Ndipo tili na luso lapadela lotha kutonthoza ena. Mwacitsanzo, ngati mwana poseŵela wagwa na kudzivulaza, amathamangila kwa amayi kapena atate ake, uku akulila. Ngakhale kuti makolowo sangathe kupoletsa cilondaco, akhoza kum’tonthoza mwanayo. Angamunyamule, kum’pukuta misozi kwinaku akumuuza kuti, pepa! Kenako angamufunse zimene zacitika, ndipo pambuyo pake angamuike mankhwala pa cilondaco kapena kumangapo kansalu. Pasanapite nthawi itali, mwanayo amaleka kulila, ndipo angafike ngakhale poyambilanso kuseŵela. M’kupita kwa nthawi, cilondaco cimapola.
2 Koma nthawi zina, ana amavulala koopsa. Mwacitsanzo, ana ena amacitilidwa zolaula. Mwana angacitilidwe zolaula kamodzi, kapena kambili-mbili kwa zaka zoculuka. Mulimonsemo, kucitila mwana zolaula ni kumuvulaza kwambili, ndipo izi zingapangitse kuti akhale wovutika maganizo kwa nthawi yaitali. Nthawi zina, wocitila mwana zolaula angagwidwe na kupatsiwa cilango. Koma nthawi zina, wolakwayo angaoneke monga wazemba cilango. Ngakhale wolakwayo atalangidwa, mwana amene anacitilidwa zolaula angapitilize kuvutika na zotulukapo zake ngakhale atakula.
3. Malinga n’zimene 2 Akorinto 1:3, 4 imakamba, n’ciani cimene Yehova amafuna? Nanga m’nkhani ino tidzakambilana mafunso ati?
3 Ngati Mkhristu anacitilidwapo zolaula ali mwana, ndipo akali kuvutika maganizo, kodi tingamuthandize bwanji? (Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.) N’zoonekelatu kuti Yehova amafuna kuti nkhosa zake zizisamalidwa mwacikondi, na kutonthozedwa zikakumana na mavuto. Conco, tiyeni tikambilane mafunso atatu aya: (1) N’cifukwa ciani anthu amene anacitilidwapo zolaula afunika kutonthozedwa? (2) Kodi n’ndani angawatonthoze? (3) Tingawatonthoze bwanji mowafika pamtima?
CIFUKWA CAKE AFUNIKA KUTONTHOZEDWA
4-5. (a) N’cifukwa ciani kukumbukila kuti mwana ni wosiyana kwambili na munthu wamkulu n’kofunika? (b) Kodi kucitila mwana zolaula kungakhudze bwanji mmene amaonela ena?
4 Anthu ena amene anacitilidwapo zolaula ali ana angafunikilebe citonthozo ngakhale kuti papita zaka zambili. Cifukwa ciani? Kuti timvetse cifukwa cake, tifunika kukumbukila kuti ana ni osiyana kwambili na anthu akulu-akulu. Nthawi zambili mwana akacitilidwa zinthu zankhanza, amakhudzidwa m’njila yosiyana kwambili na mmene munthu wamkulu angakhudzidwile. Ganizilani zitsanzo izi:
5 Mwacibadwa, ana amakhulupilila anthu amene amawalela na kuwasamalila, ndipo amakhala nawo pa ubwenzi wolimba. Mgwilizano wotelo umapangitsa ana kudziona kukhala otetezeka. Kuwonjezela apo, umawathandiza kuti ayambe kukhulupilila anthu ena amene amawakonda. (Sal. 22:9) Zacisoni n’zakuti kambili, amene amacitila mwana zolaula ni anthu amene amakhala naye panyumba, monga abale ake eni-eni kapena anthu ena amene amamvana kwambili na banjalo. Mwana akacitilidwa zolaula na munthu amene amam’khulupilila, zimakhala zovuta kuti azikhulupilila anthu ena, ngakhale patapita zaka zambili.
6. N’cifukwa ciani kucitila ana zolaula ni nkhanza yosaneneka?
6 Ana sangathe kudziteteza okha, ndipo kuwacita zolaula ni nkhanza yosaneneka. Kugona mwana kapena kucita naye zinthu zina zokhudza kugonana, kukali zaka zambili kuti afike pamsikhu woti n’kukwatila kapena kukwatiliwa, ni kumuwononga kwambili. Kucita izi kungapangitse kuti mwanayo akhale na maganizo olakwika pankhani ya kugonana. Kungapangitsenso kuti azidziona monga wacabe-cabe, ndiponso kuti asamakhulupilile anthu ena.
7. (a) N’cifukwa ciani n’zosavuta kwa munthu wa zolinga zoipa kunyengelela mwana mpaka kumucita zolaula? Nanga angamuuze mabodza otani? (b) Kodi mabodza amenewo angamukhudze bwanji mwanayo?
7 Ana amakhala osakhwima m’kaganizidwe kawo, ndipo sakwanitsa kusiyanitsa cabwino na coipa. Sadziŵa ngozi. (1 Akor. 13:11) Conco, zimakhala zosavuta kwa anthu oipa amene amacitila ana zolaula kuwanyengelela. Anthuwo amauza ana mabodza oipa kwambili. Mwacitsanzo, angauze mwana kuti iye ndiye wapangitsa kuti amucite zolaula, komanso kuti safunika kuulula zimene zacitikazo. Mwinanso angamuuze kuti olo akanene, anthu sadzam’khulupilila kapena kumuthandiza. Kapena angamuuzenso kuti kugonana kwa mwana ndi munthu wamkulu ni njila yabwino-bwino yoonetsela kuti anthuwo amakondanadi. Mabodza amenewa amapotoza maganizo a mwana, ndipo pangatenge zaka zambili kuti awongolele kaganizidwe kake. Mwanayo angakule na maganizo odziona kuti ni wodetsedwa, komanso wosayenela kukondedwa kapena kutonthozedwa ndi anthu ena.
8. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Yehova angathe kupeleka citonthozo kwa anthu amene anacitilidwapo zolaula?
8 Conco, n’zosadabwitsa kuti anthu amene anacitilidwapo zolaula amavutika kwa nthawi yaitali. Kucitila mwana zolaula ni mcitidwe woipa kwambili! Kufala kwa khalidwe limeneli ni umboni woonekelatu wakuti tikukhala m’masiku otsiliza, nthawi imene anthu ambili ni “osakonda acibale awo,” ndipo ‘anthu oipa ndi onyenga akuipilaipilabe.’ (2 Tim. 3:1-5, 13) Satana ali na ziwembu zoipa kwambili! Ndipo zimakhala zokhumudwitsa kuona anthu akucita zinthu zokondweletsa Mdyelekezi. Komabe, Yehova ni wamphamvu kwambili kuposa Satana ndi anthu ake. Iye adziŵa bwino macenjela a Satana. Ndife otsimikiza kuti Yehova adziŵa bwino mavuto onse amene timapitamo, ndipo angathe kutitonthoza. Ndife odala kuti timatumikila “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse, kuti tithe kutonthoza amene ali m’masautso amtundu uliwonse, cifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.” (2 Akor. 1:3, 4) Koma kodi Yehova amaseŵenzetsa ndani popeleka citonthozo?
N’NDANI ANGAWATONTHOZE?
9. Mogwilizana na mawu a Mfumu Davide a pa Salimo 27:10, kodi Yehova amacita ciani ngati ana asiyidwa na makolo awo?
9 Anthu amene anasiyidwa na makolo awo, kapena amene anacitilidwapo zolaula na abululu awo kapena anthu ena amene amamvana nawo, angafunikile kwambili citonthozo. Wolemba Salimo Davide, anadziŵa kuti Yehova ndiye gwelo lodalilika la citonthozo. (Ŵelengani Salimo 27:10.) Davide anali na cikhulupililo cakuti Yehova amasamalila anthu amene asiyidwa na okondedwa awo. Kodi Yehova amacita bwanji zimenezi? Amaseŵenzetsa atumiki ake okhulupilika. Akhristu anzathu ni banja lathu lauzimu. Mwacitsanzo, Yesu anakamba kuti anthu amene anali kulambila Yehova pamodzi naye anali abale ake, alongosi ake, na amayi ake.—Mat. 12:48-50.
10. Kodi mtumwi Paulo anakamba ciani pofotokoza nchito yake monga mkulu mumpingo?
10 Ganizilani citsanzo ici coonetsa mmene mpingo ungakhalile monga banja lathu. Mtumwi Paulo anali mkulu wokhulupilika komanso wodzipeleka kwambili. Iye anapeleka citsanzo cabwino, moti anauzilidwa kuuza Akhristu anzake kuti azitengela citsanzo cake monga mmene iyenso anali kutsanzilila Khristu. (1 Akor. 11:1) Onani zimene Paulo panthawi ina anafotokoza ponena za nchito yake monga mkulu mumpingo. Iye anati: “Tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalilila ana ake.” (1 Ates. 2:7) Masiku anonso, akulu okhulupilika amakamba mokoma mtima na modekha pamene akupeleka citonthozo ca m’Malemba kwa anthu ofunikila cilimbikitso.
11. N’ciani cionetsa kuti si akulu okha amene angapeleke citonthozo kwa anthu amene anacitilidwapo zolaula?
11 Kodi ni akulu okha amene angapeleke citonthozo kwa anthu amene anacitilidwapo zolaula? Iyai. Tonsefe tili na udindo ‘wolimbikitsana’ wina na mnzake. (1 Ates. 4:18) Alongo acikulile kuuzimu angathandize kwambili polimbikitsa alongo amene anacitilidwapo zolaula. N’cifukwa cake ngakhale Yehova Mulungu amadziyelekezela na mayi amene akutonthoza mwana wake. (Yes. 66:13) M’Baibo muli zitsanzo za azimayi amene anatonthoza anthu omwe anali kukumana na mavuto. (Yobu 42:11) Ndithudi! Yehova amakondwela kwambili kuona alongo akupeleka citonthozo kwa alongo anzawo, amene akuvutika maganizo. Nthawi zina, mkulu mmodzi kapena aŵili, mosamala angapemphe mlongo wina wacikulile kuuzimu, kuti akalimbikitse na kutonthoza mlongo amene akuvutika maganizo cifukwa cakuti anacitilidwapo zolaula. *
KODI TINGAWATONTHOZE BWANJI?
12. Kodi tiyenela kupewa kucita ciani?
12 Komabe, pothandiza m’bale kapena mlongo amene anacitilidwapo zolaula, tiyenela kupewa kufunsitsitsa zinthu zimene mwini wakeyo safuna kufotokoza. (1 Ates. 4:11) Nanga tingawathandize bwanji anthu amene akufunikila citonthozo? Tiyeni tikambilane mfundo zisanu za m’Baibo za mmene tingawatonthozele.
13. Malinga n’zimene 1 Mafumu 19:5-8 imakamba, kodi mngelo wa Yehova anam’citila ciani Eliya? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?
13 Citani zinthu zinazake zimene zingamulimbikitse. Pamene mneneli Eliya anali kuthaŵa adani ake amene anafuna kumupha, anavutika maganizo kwambili cakuti anafika polakalaka kufa. Yehova anatumiza mngelo wamphamvu kuti akamulimbikitse. Mngeloyo anapatsa Eliya thandizo limene anali kufunikila. Anamupatsa cakudya cothuma na kum’limbikitsa kuti adye. (Ŵelengani 1 Mafumu 19:5-8.) Nkhaniyi itiphunzitsa mfundo yofunika yakuti, nthawi zina kucitila munthu zinthu zazing’ono koma zoonetsa kukoma mtima, kungam’limbikitse kwambili munthuyo. Mwina mungamukonzeleko kacakudya, kumupatsa kamphatso, kapena kum’lembela kalata yolimbikitsa. Kucita izi kungathandize m’bale kapena mlongo wosautsika mtima kuzindikila kuti timamukonda na kum’ganizila. Ngati tiona kuti sitingakwanitse kukambilana na Mkhristuyo zinthu zimene mwina zingamucotsele ulemu kapena kumupweteka maganizo, tingamuthandize mwa kucita zinthu ngati zimene tachulazi.
14. Kodi tingaphunzilepo ciani pa nkhani ya Eliya?
14 Thandizani munthu wovutika maganizo kukhala womasuka ndi kuona kuti ni wotetezeka. Palinso mfundo ina imene tingaphunzilepo pankhani ya Eliya. Mozizwitsa, Yehova anapatsa mneneliyo thandizo lofunikila kuti akwanitse kuyenda ulendo wautali mpaka kukafika ku Phili la Horebe. Mwina Eliya anaona kuti anali wotetezeka pamene anafika ku dela lakutali limenelo, kumene Yehova anacitila pangano ndi anthu ake zaka mahandiledi angapo kumbuyoko. Iye ayenela kuti anaona kuti kumene anathaŵilako kunali kutali kwambili, cakuti adani ake amene anafuna kumupha sakanakwanitsa kufikako. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tikafuna kulimbikitsa munthu amene anacitilidwapo zolaula, coyamba tifunika kum’thandiza kuona kuti ni wotetezeka. Akulu ayenela kukumbukila kuti anthu amasiyana-siyana. Mwacitsanzo, mlongo wina wovutika maganizo angaone kuti ni wotetezeka komanso angakhale womasuka ngati akulu akambilana naye ali kunyumba kwake, kwinaku akumwa zozizilitsa kukhosi, kusiyana na kukambilana naye m’Nyumba ya Ufumu. Koma mlongo wina angakhale womasuka ku Nyumba ya Ufumu osati kunyumba kwake.
15-16. Kodi kumvetsela mosamala kumaphatikizapo kucita ciani?
15 Muzimvetsela mosamala. Baibo imapeleka malangizo omveka bwino akuti: “Munthu aliyense akhale wofulumila kumva, wodekha polankhula.” (Yak. 1:19) Kodi mumamvetsela mosamala pamene ena akamba? Mwina tingaganize kuti kumvetsela mosamala kumatanthauza cabe kukhala phee, kwinaku tikuyang’ana munthu amene akamba nafe. Koma zoona zake n’zakuti kumvetsela mosamala kumaphatikizapo zambili. Mwacitsanzo, patapita nthawi Eliya anakhuthulila Yehova nkhawa zake, ndipo Yehova anamvetsela mokoma mtima. Yehova anazindikila kuti Eliya anali na mantha, ndipo anali kudziona monga anali yekha-yekha. Anali kuganizanso kuti zonse zimene anacita pa utumiki wake zinangopita pacabe. Mwacikondi, Yehova anamuthandiza kuthetsa nkhawa zake. Iye anaonetsa kuti anali kumvetsela mosamala pamene Eliya anali kukamba.—1 Maf. 19:9-11, 15-18.
1 Akor. 13:4, 7.
16 Kodi tingaonetse bwanji kuti tikumvetsela mwacifundo pamene m’bale kapena mlongo akamba nafe? Nthawi zina, tingakambe mawu ocepa osankhidwa bwino oonetsa mmene nkhaniyo yatikhudzila. Mwacitsanzo, tingakambe kuti: “Pepani, cinaipa kwambili! Zimene anacitazo ni nkhanza yaikulu!” Mwina mungafunse m’bale kapena mlongo wopwetekedwa mtimayo funso limodzi kapena aŵili kuti mumvetsetse zimene akamba. Mungamufunse kuti, “Nifuna nione ngati namvetsetsa. Kodi mutanthauza kuti . . . ?” kapena kuti, “Pa zimene mwakamba, namva ngati mutanthauza kuti . . . Kodi n’telodi?” Kukamba mawu ngati amenewa kungathandize munthuyo kuona kuti mukumvetseladi mosamala, ndipo mufunadi kumvetsetsa zimene akukamba.—17. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala woleza mtima ndi “wodekha polankhula”?
17 Koma mufunika kukhalabe “wodekha polankhula.” Mukafuna kum’patsa malangizo kapena kuwongolela maganizo ake, musam’dule mawu. Dekhani! Pamene Eliya anali wopanikizika maganizo, anakhuthulila Yehova nkhawa zake, ndipo anakamba moonetsa kuti zimene zinacitikazo zinamuŵaŵa kwambili. Pambuyo polimbikitsidwa na Yehova, Eliya anam’khuthulilanso Yehova nkhawa zake, ndipo anakamba mawu ofanana ndi amene anakamba poyamba. (1 Maf. 19:9, 10, 13, 14) Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tiphunzilapo kuti nthawi zina, munthu wopwetekedwa mtima angafunike kufotokoza mobweleza-bweleza mmene akumvelela. Tifunika kutengela citsanzo ca Yehova mwa kumumvetsela moleza mtima. Tiyenela kumuonetsa cifundo cacikulu, m’malo mofulumila kumuuza mmene angathetsele vuto lake.—1 Pet. 3:8.
18. Kodi kupemphela na munthu wovutika maganizo kungamulimbikitse bwanji?
18 Pemphelani naye mocokela pansi pa mtima. Ngati munthu ni wovutika maganizo kwambili, nthawi zina angalephele kupemphela. Angadzione kuti ni wosayenelela kupemphela kwa Yehova. Conco, pofuna kulimbikitsa munthu wotelo, tingapemphele naye pamodzi, ndipo tingachule dzina lake popemphela. Tingauze Yehova m’pemphelo kuti ife na mpingo wonse, timam’konda kwambili m’bale kapena mlongoyo. Tingapemphe Yak. 5:16.
Yehova kuti amutonthoze na kum’limbikitsa Mkhristuyo, amene ni nkhosa yake yamtengo wapatali. Pemphelo lotelo lingamulimbikitse kwambili.—19. N’ciani cingatithandize kukonzekela kukalimbikitsa munthu wovutika maganizo?
19 Kambani mawu otsitsimula komanso otonthoza. Tiyenela kusamala tisanakambe ciliconse. Kukamba mosaganizila kungam’khumudwitse munthu. Koma kukamba mokoma mtima kungamulimbikitse. (Miy. 12:18) Conco, pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kupeza mawu abwino, olimbikitsa, ndi otsitsimula. Kumbukilani kuti mawu alionse amene mungakambe, sangapose mphamvu ya mawu a Yehova opezeka m’Baibo.—Aheb. 4:12.
20. Kodi anthu ena amene anacitilidwapo zolaula amakhala na maganizo otani? Nanga tifunika kuwatsimikizila za ciani?
20 Munthu amene anacitilidwapo zolaula angafike podziona kuti ni wodetsedwa komanso wacabe-cabe. Angakhale na maganizo akuti anthu ena samukonda ndi kuti sangamukonde. Koma maganizo amenewa si oona ngakhale pang’ono. Conco, pogwilitsila nchito Malemba, m’tsimikizileni kuti Yehova amamukonda kwambili. (Onani mbali yakuti, “ Cilimbikitso ca m’Malemba.”) Kumbukilani mmene mngelo analimbikitsila mneneli Danieli mokoma mtima pamene anali wofooka komanso wosautsika mtima. Yehova anafuna kuti Danieli adziŵe kuti iye amamuona kuti ni wamtengo wapatali. (Dan. 10:2, 11, 19) Mofananamo, Yehova amaona abale na alongo athu ovutika maganizo kukhala amtengo wapatali kwambili.
21. Kodi anthu ocita zoipa amene safuna kulapa ali na tsogolo lotani? Nanga pali pano, ife tiyenela kuyesetsa kucita ciani?
21 Pamene titonthoza ena, timawathandiza kukumbukila kuti Yehova amawakonda. Ndipo tifunikanso kukumbukila kuti Yehova ni Mulungu wacilungamo. Ngati winawake anacitilidwapo zolaula, Yehova amaona zonse. Ndipo iye sadzalephela kupeleka cilango kwa anthu onse ocita zoipa amene salapa. (Num. 14:18) Koma pali pano, tiyeni ticite zonse zimene tingathe poonetsa cikondi kwa anthu amene anacitilidwapo zolaula. Ndipo n’zokondweletsa cotani nanga kudziŵa kuti kutsogolo, Yehova adzatonthoza kothelatu anthu onse amene amacitilidwa nkhanza na Satana komanso dziko lake. Posacedwa, zoŵaŵa zonse zimene tikukumana nazo zidzatha, ndipo sitidzazikumbukilanso.—Yes. 65:17.
NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse
^ ndime 5 Munthu amene anacitilidwapo zolaula ali mwana angavutike kwa zaka zambili cifukwa ca zotulukapo zake. M’nkhani ino, tidzakambilana cifukwa cake zili conco. Tidzakambilananso za amene ali pamalo abwino kutonthoza anthu otelo. Potsiliza, tidzakambilana njila zina zabwino zimene tingalimbikitsile anthu amene anacitilidwapo zolaula ali ana.
^ ndime 11 Munthu amene anacitilidwapo zolaula angasankhe kupita ku cipatala kuti akalandile cithandizo ngati afuna.
^ ndime 76 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mlongo wacikulile mwauzimu akutonthoza mlongo wovutika maganizo.
^ ndime 78 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Akulu aŵili apita kukalimbikitsa mlongo wosautsika mtima. Mlongoyo wapempha mlongo wacikulile uja kuti akhalepo pamene akuluwo akambilana naye.