Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 21

Musasoceletsedwe na “Nzelu za M’dzikoli”

Musasoceletsedwe na “Nzelu za M’dzikoli”

“Kwa Mulungu nzelu za m’dzikoli n’zopusa.”—1 AKOR. 3:19.

NYIMBO 98 Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu

ZA M’NKHANI INO *

1. Kodi Mawu a Mulungu amatipatsa ciani?

YEHOVA ndiye Mlangizi wathu Wamkulu. Kaya tikumane na vuto lotani, iye amatilongoza njila yothetsela vutolo. (Yes. 30:20, 21) Mawu ake amatipatsa nzelu zofunikila kuti tikhale “oyenelela bwino ndi okonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:17) Ngati titsatila malangizo a m’Baibo muumoyo wathu, timakhala anzelu kwambili kuposa anthu amene amayendela ‘nzelu za dzikoli.’—1 Akor. 3:19; Sal. 119:97-100.

2. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Monga tidzaonela m’nkhani ino, nthawi zambili nzelu za dziko zimaoneka zokopa cifukwa ca zilakolako zaucimo zimene timakhala nazo. Conco, cingakhale cosavuta kutengela maganizo a anthu a m’dzikoli na zocita zawo. M’pake kuti Baibo imaticenjeza kuti: “Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.” (Akol. 2:8) M’nkhani ino, tikambilana mabodza aŵili amene Satana amafalitsa. Tiona mmene anthu anayambila kukhulupilila mabodza amenewo. Pokambilana mbali iliyonse, tionanso umboni woonetsa kuti nzelu za dziko n’zopusa, koma nzelu za m’Mawu a Mulungu ni zapamwamba kwambili.

KUSINTHA KWA MAGANIZO A ANTHU PANKHANI YA KUGONANA

3-4. Ca kumayambililo kwa zaka za m’ma 1900, kodi maganizo a anthu ku America anasintha bwanji pa nkhani ya kugonana?

3 Ca kumayambililo kwa zaka za m’ma 1900, maganizo a anthu ku America anasintha pankhani ya kugonana. M’zaka za kumbuyoko, anthu ambili anali kukhulupilila kuti kugonana ni kwa anthu amene ali pabanja. Ndipo nkhani zokhudza kugonana sizinali kukambidwa pagulu. Koma kenako zinthu zinasintha. Anthu analeka kutsatila mfundo zimenezi, ndipo ambili anayamba kucita zinthu motayilila.

4 M’zaka za m’ma 1920, makhalidwe a anthu na maganizo awo pankhani ya kugonana anasintha kwambili. Katswili wina anati: “Nkhani za kugonana zinayamba kupezeka kwambili m’zosangalatsa zosiyana-siyana monga m’mafilimu, m’maseŵelo, m’nyimbo, m’mabuku a nthano, ndi pa zotsatsa malonda.” M’zaka zimenezo, kavinidwe kanakhala konyanyula kwambili, ndipo anthu ambili anayamba kuvala motayilila. Izi n’zogwilizana na zimene Baibo inakamba ponena za masiku otsiliza, kuti anthu adzakhala “okonda zosangalatsa.”—2 Tim. 3:4.

Anthu a Yehova sakopeka na khalidwe lotayilila la anthu a m’dzikoli (Onani ndime 5) *

5. Kodi makhalidwe a anthu anasintha bwanji kuyambila m’zaka za m’ma 1960?

5 M’zaka za m’ma 1960, vikwati vongothaŵitsana vinaculuka, ndiponso khalidwe la mathanyula (kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha) linafala. Kuwonjezela apo, kusudzulana popanda zifukwa zomveka kunafala kwambili. Cinanso, m’mafilimu anayamba kuonetselatu poyela zakugonana. M’zaka zaposacedwapa, taona mavuto osiyana-siyana amene abwela cifukwa ca makhalidwe otayilila amenewa. Mwacitsanzo, katswili wina anakamba kuti “khalidwe lotayilila pankhani zakugonana limene lafala kwambili m’dzikoli,” ndilo labweletsa mavuto monga kutha kwa maukwati, mabanja a kholo limodzi, kupwetekedwa mtima, kukonda kutamba zamalisece, na mavuto ena ngati amenewa. Ndipo kuculuka kwa matenda opatsilana monga a AIDS, ni umboni winanso woonetsa kuti nzelu za dzikoli n’zopusa.—2 Pet. 2:19.

6. Kodi anthu amaonetsa bwanji kuti ali na maganizo a Satana pankhani ya kugonana?

6 Anthu m’dzikoli ali na maganizo a Satana pankhani ya kugonana. Iwo salemekeza mphatso ya kugonana ndi mphatso ya cikwati zimene Mulungu anapeleka. Conco, Satana mosakayikila amacita kudumpha, kukondwela akaona anthu akucita zimenezi. (Aef. 2:2) Anthu amene amacita zaciwelewele, amasukulutsa mphatso yabwino ya kubeleka imene Yehova anapeleka kwa anthu. Ndipo anthu otelo angataye mwayi wokalandila moyo wosatha.—1 Akor. 6:9, 10.

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA PANKHANI YA KUGONANA

7-8. Kodi Baibo imatilimbikitsa kukhala na maganizo ati oyenelela pankhani ya kugonana?

7 Anthu amene amayendela nzelu za dzikoli, amanena kuti malamulo a m’Baibo a makhalidwe abwino ni ovuta kuwatsatila. Iwo angafunse kuti, ‘Ngati Mulungu amafuna kuti tikhale odziletsa, n’cifukwa ciani anatilenga na cilakolako ca kugonana?’ Anthu amafunsa funso limeneli cifukwa cokhala na maganizo olakwika akuti munthu afunika kucita ciliconse cimene mtima wake wafuna. Koma zimene Baibo imakamba n’zosiyana kwambili na zimenezi. Imaphunzitsa kuti Yehova anatilemekeza ife anthu mwa kutipatsa mphamvu yolamulila zilakolako zathu. (Akol. 3:5) Kuwonjezela apo, Yehova anapeleka mphatso ya cikwati, cimene ni makonzedwe omwe amatipatsa mwayi wokhutilitsa cilakolako ca kugonana m’njila yolemekezeka. (1 Akor. 7:8, 9) Mwamuna na mkazi akakwatilana, amakhala na mwayi wosangalala na mphatso ya kugonana, popanda kukhala na nkhawa imene anthu aciwelewele amakhala nayo.

8 Mosiyana na nzelu za dzikoli, Baibo imatilimbikitsa kukhala na maganizo oyenelela pankhani ya kugonana. Imakamba kuti kugonana kumabweletsa cisangalalo. (Miy. 5:18, 19) Komabe, Baibo imakambanso kuti: “Aliyense wa inu akhale woyela mwa kudziwa kulamulila thupi lake m’njila yoyela kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, osati mwa cilakolako cosalamulilika ca kugonana, ngati cimene anthu a mitundu ina osadziwa Mulungu ali naco.”—1 Ates. 4:4, 5.

9. (a) Kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900, kodi anthu a Yehova analimbikitsidwa bwanji kutsatila mfundo zapamwamba za m’Baibo za makhalidwe abwino? (b) Ni malangizo anzelu ati amene ali pa 1 Yohane 2:15, 16? (c) Malinga n’zimene zili pa Aroma 1:24-27, ni makhalidwe oipa ati amene tiyenela kupewa?

9 Kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900, anthu oipa anafika pamlingo wosathanso “kuzindikila makhalidwe abwino.” Koma atumiki a Yehova sanatengele maganizo ocita zinthu motayilila amenewo. (Aef. 4:19) M’malomwake, iwo anayesetsa kutsatila miyezo ya Yehova. Nsanja ya Mlonda ya May 15, 1926, inakamba kuti “mwamuna kapena mkazi afunika kukhala wodziletsa, woyela m’maganizo na m’zocita zake, maka-maka pocita zinthu na munthu amene si mwamuna kapena mkazi wake.” Mosasamala kanthu za makhalidwe oipa amene anali kucitika panthawiyo, atumiki a Yehova anali kutsatila mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino za m’Baibo. (Ŵelengani 1 Yohane 2:15, 16.) Ndithudi! Ndife oyamikila kwambili kukhala na Mawu a Mulungu! Timayamikilanso Yehova potipatsa cakudya cauzimu ca panthawi yake, cimene cimatithandiza kupewa kutengela maganizo a dzikoli pankhani ya kugonana. *Ŵelengani Aroma 1:24-27.

KUSINTHA KWA MAGANIZO A ANTHU PANKHANI YA KUDZIKONDA

10-11. Kodi Baibo inakambilatu kuti n’ciani cimene cidzacitika m’masiku otsiliza?

10 Baibo inakambilatu kuti m’masiku otsiliza, anthu adzakhala “odzikonda.” (2 Tim. 3:1, 2) Conco, n’zosadabwitsa kuti dzikoli limalimbikitsa anthu kukhala na mzimu wodzikonda. Buku lina linakamba kuti m’zaka za m’ma 1970, “mabuku a malangizo anaculuka kwambili.” Ena mwa mabuku amenewo anali “kulimbikitsa anthu kuti ayenela kudzidziŵa bwino, kudziona ngati salakwa, komanso kudzinyadila.” Mwacitsanzo, ganizilani cabe zimene buku lina linakamba. Linati: “Ufunika kudzikonda cifukwa ndiwe munthu wokongola kwambili, wosangalatsa, komanso wofunika kwambili kuposa munthu wina aliyense.” Bukulo linali kulimbikitsa anthu kukhala na “maganizo akuti munthu afunika kudzisankhila yekha zocita, malinga n’zimene aona kuti n’zabwino ndi zom’komela.”

11 Kodi mfundo imeneyi ni yacilendo? Iyai. Ni yofanana ndi imene Satana anauza Hava. Anamuuza kuti ‘adzafanana ndi Mulungu. Adzadziwa zabwino ndi zoipa.’ (Gen. 3:5) Masiku ano, anthu ambili amadziona kukhala apamwamba kwambili, moti amaona kuti palibe munthu aliyense angawauze zocita, ngakhale Mulungu amene. Maganizo amenewa amaonekela kwambili ndi mmene anthu amatengela cikwati.

Mkhristu amaika zofuna za anzake patsogolo, makamaka za mkazi kapena mwamuna wake (Onani ndime 12) *

12. Kodi dzikoli limalimbikitsa anthu kuti aziciona bwanji cikwati?

12 Baibo imakamba kuti mwamuna na mkazi wake afunika kulemekezana, na kulemekeza malumbilo awo a cikwati. Imalimbikitsa okwatilanawo kuona cikwati kukhala mgwilizano wacikhalile. Imati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Koma anthu amene amayendela nzelu za dziko amalimbikitsa okwatilana kuona cikwati m’njila yosiyana na imeneyi. Iwo amati aliyense m’cikwati afunika kusumika maganizo pa zofuna zake. Buku lina lokamba za kusudzulana linati: “M’miyambo ina ya cikwati, pocita malumbilo, anthu analeka kukamba kuti adzakhala limodzi kwa ‘nthawi yonse imene adzakhala ndi moyo.’ M’malomwake, amacita lumbilo locepa mphamvu lakuti adzakhala limodzi kwa ‘nthawi yonse imene adzakhala okondana.’” Kuona cikwati mopepuka kumeneku kwapangitsa kuti maukwati ambili asile. Ndipo izi zapweteketsa mtima anthu ambili. Conco, n’zoonekelatu kuti maganizo osalemekeza cikwati amene anthu ali nawo m’dzikoli si anzelu.

13. Fotokozani cifukwa cimodzi cimene Yehova amazondela anthu onyada.

13 Baibo imati: “Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.” (Miy. 16:5) N’cifukwa ciani Yehova amanyansidwa ndi anthu onyada? Cifukwa cimodzi n’cakuti anthu onyada, kapena amene amalimbikitsa khalidwe lodzikonda, amakhala odzikuza ngati Satana. Iye anali kudziŵa bwino kuti Yesu na amene Mulungu anam’seŵenzetsa polenga zinthu zonse. Ndiye tangoganizani! Satana anafika polakalaka kuti Yesuyo amugwadile na kumulambila. Ŵati kudzikuza kwake ŵati! (Mat. 4:8, 9; Akol. 1:15, 16) Mtima wodzikuza ngati umenewu, umene anthu ali nawo ni umboni wakuti nzelu za dziko n’zopusadi pamaso pa Mulungu.

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA PANKHANI YA KUDZIKONDA

14. Kodi lemba la Aroma 12:3 limatithandiza bwanji kuti tizidziona moyenelela?

14 Baibo imatithandiza kuti tizidziona moyenelela. Imaonetsa kuti kudzikonda pamlingo woyenelela kulibe vuto. Mwacitsanzo, Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha,” kuonetsa kuti kudzikonda pa mlingo woyenelela kuli cabe bwino. (Mat. 19:19) Komabe, Baibo imaphunzitsa kuti sitiyenela kudziona monga ofunika kwambili kuposa ena. M’malomwake, imati: “Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”—Afil. 2:3; ŵelengani Aroma 12:3.

15. N’cifukwa ciani muona kuti uphungu wa m’Baibo woletsa kudzikuza ni wanzelu?

15 Masiku ano, anthu ambili amadziyesa anzelu. Anthu amenewa amaona kuti uphungu wa m’Baibo woletsa kudzikuza ni wopanda nzelu. Amakamba kuti kuona ena kuti ni okuposa, kungapangitse kuti anthu azikupondeleza. Koma kodi khalidwe lodzikonda, limene dziko la Satana limalimbikitsa, lakhala na zotulukapo zabwino? Kodi imwe muona bwanji? Kodi anthu odzikonda amakhala osangalala? Kodi amakhala na mabanja acimwemwe? Kodi amakhala na mabwenzi abwino? Kodi amakhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu? Malinga n’zimene mwaona, n’ciani cothandiza—kuyendela nzelu za dzikoli kapena kutsatila malangizo a m’Baibo?

16-17. Kodi ndife oyamikila kwambili kaamba ka ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

16 Kodi amene amatsatila malangizo a anthu odziŵika monga anzelu m’dzikoli, tingawayelekezele na ndani? Tingawayelekezele na munthu wapaulendo amene wasocela, ndipo akufunsa njila kwa mnzake amenenso wasocela. Yesu pokamba za anthu a m’nthawi yake, amene anali kudziona kuti ni “anzelu,” anati: “Iwo ndi atsogoleli akhungu. Cotelo ngati munthu wakhungu akutsogolela wakhungu mnzake, onse awili adzagwela m’dzenje.” (Mat. 15:14) Zoona, nzelu za m’dzikoli n’zopusadi kwa Mulungu!

Atumiki a Mulungu akusangalala poganizila umoyo wabwino umene akhala nawo potumikila Yehova (Onani ndime 17) *

17 Conco, n’zoonekelatu kuti malangizo anzelu a m’Baibo ni opindulitsa nthawi zonse “pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’cilungamo.” (2 Tim. 3:16) Ndife oyamikila kwambili kuti Yehova, kupitila m’gulu lake, amatiteteza kuti tisatengele nzelu za dzikoli. (Aef. 4:14) Cakudya cauzimu cimene iye amatipatsa, cimatilimbikitsa kupitiliza kutsatila mfundo za m’Baibo. Kunena zoona, ife tili na mwayi waukulu ngako wotsogoleledwa na malangizo anzelu komanso odalilika a m’Baibo!

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

^ ndime 5 Nkhani ino idzatithandiza kukhala na cikhulupililo colimba cakuti Yehova yekha ndiye Gwelo la malangizo odalilika. Cinanso, idzatithandiza kuona kuti ngati tiyendela nzelu za dziko, tingakumane na mavuto aakulu, koma ngati titsatila malangizo a m’Baibo, tidzapindula.

^ ndime 9 Mwacitsanzo, onani buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba, mutu 24 mpaka 26, na buku laciwili, mutu 4 na 5.

^ ndime 50 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Tiona banja la Mboni panthawi zosiyana-siyana muumoyo wawo. Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1960, m’bale na mkazi wake akulalikila.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’ma 1980, m’baleyo akusamalila mkazi wake wodwala, ndipo mwana wawo wamkazi wamng’ono akuona.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Lelo, m’baleyo na mkazi wake akuyang’ana zithunzi za umoyo wawo muutumiki wa Yehova. Mwana wawo wamkazi uja na banja lake akusangalala nawo pamodzi.