NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA May 2020

Magazini ino ili na nkhani zophunzila kuyambila pa July 6–August 2, 2020.

“Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi Yamapeto

Nkhani Yophunzila 19: Wiki ya July 6-12, 2020. Tikuona umboni woonetsa kuti ulosi wa Danieli wokamba za “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela” ukupitiliza kukwanilitsidwa. Tidziŵa bwanji zimenezi? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kuumvetsetsa ulosi umenewu?

Mafumu Aŵili Olimbana M’nthawi Yamapeto

Mbali zina za ulosi wokamba mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela zimafanana na maulosi ena. Kodi maulosi amenewa aonetsa bwanji kuti dziko loipali latsala pang’ono kuwonongedwa?

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndani Masiku Ano?

Nkhani yophunzila 20: Wiki ya July 13-19, 2020. Kodi “mfumu ya kumpoto” ndani masiku ano? Nanga idzawonongedwa bwanji? Kudziŵa mayankho pa mafunso amenewa kungalimbitse cikhulupililo cathu, komanso kungatithandize kukonzekela mayeselo amene tidzakumana nawo posacedwa.

Kodi Mumayamikila Mphatso Zimene Mulungu Anakupatsani?

Nkhani yophunzila 21: Wiki ya July 20-26, 2020. Nkhani ino itithandiza kuyamikila kwambili Yehova komanso zina mwa mphatso zimene iye anatipatsa. Itithandizanso kudziŵa mmene tingakambile ndi anthu amene amakayikila zakuti kuli Mulungu.

Onetsani Kuti Mumayamikila Cuma Cosaoneka

Nkhani yophunzila 22: Wiki ya July 27–August 2, 2020. M’nkhani yapita, tinakambilana za mphatso zingapo zooneka zimene Mulungu anatipatsa. M’nkhani ino, tikambilana za cuma cosaoneka kapena kuti mphatso zosaoneka. Tikambilananso mmene tingaonetsele kuyamikila cuma cimeneco. Nkhaniyi itithandizanso kuti tiziyamikila kwambili Yehova Mulungu, Gwelo la cuma cimeneci.