Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kufatsa—Kodi Khalidweli Limatipindulitsa Bwanji?

Kufatsa—Kodi Khalidweli Limatipindulitsa Bwanji?

Sara * anati, “Mwacibadwa ndine wamanyazi, komanso nimadzikayikila. Conco, sinimasuka kukhala na munthu wodzimvela ndiponso woumilila maganizo ake. Koma nimamasuka kwambili kukhala na munthu wofatsa komanso wodzicepetsa. Nimamasuka kumufotokozela mmene nimvelela ndiponso mavuto anga. Umu ni mmene mabwenzi anga alili. Ni ofatsa komanso odzicepetsa.”

Zimene Sara anakamba zionetsa kuti cimakhala cosavuta anthu kumasuka nafe tikakhala ofatsa. Khalidwe la kufatsa limakondweletsanso Yehova. Mawu ake amatilangiza kuti: “Valani . . . kufatsa.” (Akol. 3:12) Kodi kufatsa n’kutani? Kodi Yesu anaonetsa bwanji khalidwe la kufatsa? Nanga khalidweli lingatithandize bwanji kukhala na umoyo wacimwemwe?

KODI KUFATSA N’KUTANI?

Kufatsa ni khalidwe limene munthu amakhala nalo ngati ali na mtima wodekha. Munthu wofatsa amakhala waubwenzi komanso wokoma mtima pocita zinthu na ena. Iye amakhalabe wodekha komanso wodziletsa ngati ena amucitila zinthu zokhumudwitsa.

Liwu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kufatsa” linali kugwilitsidwa nchito pokamba za mahosi a kusanga amene anthu anali kugwila n’kuyamba kuŵeta. Hosi ya kusanga akamaisunga panyumba, inali kukhalabe na mphamvu zambili, koma anali kuiphunzitsa kudziletsa poseŵenzetsa mphamvuzo. Mofananamo, munthu akakhala wofatsa sikuti ni wofooka. Koma ni wolimba. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa munthu wofatsa amakwanitsa kupondeleza zizoloŵezi zake zaucimo kuti akhalebe pa mtendele na ena.

Mwina mumtima tingakambe kuti, ‘Mwacibadwa, si ndine munthu wofatsa.’ Popeza tikhala m’dziko limene anthu ambili ni odzimvela komanso osaleza mtima, cingakhale covuta kwa ife kuonetsa khalidwe la kufatsa. (Aroma 7:19) Motelo, pamafunika khama kuti tikhale ofatsa. Koma mzimu woyela wa Yehova udzatithandiza kupitiliza kuyesetsa kukulitsa khalidweli. (Agal. 5:22, 23) N’cifukwa ciani tiyenela kuyesetsa kukulitsa khalidwe la kufatsa?

Anthu amamasuka nase tikakhala ofatsa. Monga anakambila Sara, amene tamugwila mawu m’nkhani ino, anthufe timamasuka kwambili kukhala na munthu wofatsa. Yesu ni citsanzo cabwino kwambili pankhaniyi. Anali wofatsa komanso wokoma mtima kwambili. (2 Akor. 10:1) Ngakhale ana amene sanali kumudziŵa, anali kumasuka naye.—Maliko 10:13-16.

Kufatsa kumatiteteza pamodzi ndi anthu amene timakhala nawo. Tikakhala ofatsa, sitikhumudwa msanga kapena kucita zinthu mwaukali wina akatiputa. (Miy. 16:32) Izi zimatiteteza kuti tisadziimbe mlandu pambuyo pake cifukwa cocita zinthu zokhumudwitse ena, maka-maka amene timawakonda. Kuwonjezela apo, kufatsa kumapindulitsa anthu amene tikhala nawo, cifukwa tikakhala ofatsa, timapewa kucita zinthu zimene zingawakhumudwitse kapena kuwavulaza.

CITSANZO CABWINO KWAMBILI PANKHANI YA KUFATSA

Yesu anali kucita zinthu mofatsa ndi anthu onse, olo kuti anali na maudindo aakulu komanso anali kukhala wotangwanika. M’nthawi yake, anthu ambili anali kulimbana na mavuto osiyana-siyana ndiponso anali olemedwa moti anali kufunika kutsitsimulidwa. Anthuwo ayenela kuti anatonthozedwa kwambili Yesu atawauza kuti: “Bwelani kwa ine . . . ndipo mudzatsitsimulidwa.”—Mat. 11:28, 29.

Kodi tingacite ciani kuti tikhale ofatsa monga Yesu? Tiyenela kumaŵelenga Mawu a Mulungu kuti tidziŵe mmene Yesu anali kucitila zinthu ndi anthu, komanso mmene anali kucitila zinthu panthawi zovuta. Tikatelo, tidzayesetsa kucita zinthu mofatsa ngati Yesu pamene takumana na zovuta. (1 Pet. 2:21) Tsopano onani zinthu zitatu zimene zinathandiza Yesu kukhala wofatsa.

Yesu anali wodzicepetsa zeni-zeni. Iye anakamba kuti anali “wofatsa ndi wodzicepetsa.” (Mat. 11:29) Baibo imachula makhalidwe aŵiliwa pamodzi cifukwa kufatsa kumagwilizana kwambili na kudzicepetsa. (Aef. 4:1-3) N’cifukwa ciani takamba conco?

Kudzicepetsa kumatithandiza kuti tisamadzione apamwamba ndiponso kuti tisamakwiye msanga ena akatikambila zoipa. Mwacitsanzo, kodi Yesu anacita ciani pamene anthu anam’nena kuti anali “wosusuka ndi wokonda kwambili vinyo”? Sanakwiye. Koma analola zocita zake kuonetsa poyela kuti zokamba za anthuwo zinali zabodza. Ndipo mofatsa iye anati, “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.”—Mat. 11:19.

Ngati munthu wina wakunenani cifukwa ca khungu lanu, kumene munakulila, kapena cifukwa cakuti ndimwe mkazi kapena mwamuna, bwanji osayesetsa kucita zinthu mofatsa? M’bale Peter wa ku South Africa, amene ni mkulu mu mpingo anati: “Ngati wina wanikhumudwitsa nimadzifunsa kuti, ‘Kodi Yesu akanacita ciani pamenepa?’” Anakambanso kuti: “Naphunzila kusadziona wapamwamba kuposa ena.”

Yesu anali kudziŵa kuti anthu ni opanda ungwilo. Ophunzila a Yesu anali kufuna kucita zabwino, koma nthawi zina cifukwa copanda ungwilo anali kulephela kucita zimene anali kufunazo. Mwacitsanzo, usiku wakuti aphedwa maŵa, Yesu anapempha Petulo, Yakobo, na Yohane kuti asagone n’colinga cakuti azimulimbikitsa. Koma iwo analephela kucita zimenezi. Yesu anadziŵa kuti “mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:40, 41) Iye sanakhumudwe na zimene atumwiwo anacita cifukwa anali kudziŵa kuti anali opanda ungwilo.

Mlongo Mandy anali kukonda kupeza ena zifukwa. Koma lomba amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu ca kufatsa. Iye anati: “Nimayesetsa kukumbukila kuti tonse ndise opanda ungwilo ndiponso nimayesetsa kuona makhalidwe abwino mwa ena, monga mmene Yehova amacitila.” Kukhala wacifundo komanso kukumbukila kuti anthu ni opanda ungwilo kunathandiza Yesu kukhala wofatsa pocita zinthu ndi anthu. Ngati titengela citsanzo cake, na ise tidzatha kucita zinthu mofatsa na ena.

Yesu anali kusiya zonse m’manja mwa Mulungu. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anapilila zinthu zopanda cilungamo. Mwacitsanzo, anthu anali kumunyoza, kumuzunza, ndiponso sanali kumumvetsetsa. Ngakhale zinali telo, anakhalabe wofatsa cifukwa anali “kudzipeleka kwa iye amene amaweluza molungama.” (1 Pet. 2:23) Yesu anali kudziŵa kuti Atate wake wakumwamba adzamuthandiza kupilila, komanso kuti panthawi yake yoyenela, adzalanga anthu amene anali kumucitila zinthu mopanda cilungamo.

Tikacita zinthu mokhumudwa cifukwa ca zopanda cilungamo zimene ena aticitila, tingawonjezele vuto. Ndiye cifukwa cake Malemba amati: “Mkwiyo wa munthu subala cilungamo ca Mulungu.” (Yak. 1:20) Tingakhale na zifukwa zomveka zokwiyila, koma popeza ndife opanda ungwilo, mkwiyo ungatipangitse kucita zinthu mosaganiza bwino.

Mlongo wina ku Germany, dzina lake Cathy, anali na maganizo akuti, ‘Ngati sucitapo kanthu kuti udziteteze, palibe angakuteteze.’ Mlongoyu anasintha maganizo amenewa pamene anaphunzila kudalila Yehova. Iye anati: “Sinicita kufunika kukhala wokonzeka nthawi zonse kuti nidziteteze. Wina akanilakwila, nimacita zinthu mofatsa podziŵa kuti Yehova adzathetsa zoipa zonse m’dzikoli.” Conco, ngati anthu ena anakucitilani zinthu zopanda cilungamo, dalilani Mulungu monga mmene Yesu anacitila. Mukatelo, mudzakwanitsa kukhalabe wofatsa.

“ODALA NDI ANTHU AMENE ALI OFATSA”

Kodi kufatsa kumatithandiza bwanji pamene zinthu zili zovuta?

Yesu anaonetsa kuti kukhala wofatsa kumathandiza kwambili kuti munthu akhale wacimwemwe. Anati: “Odala [acimwemwe] ndi anthu amene ali ofatsa.” (Mat. 5:5) Onani mmene kufatsa kumathandizila m’mbali zotsatilazi.

Kufatsa kumathandiza ngati anthu asemphana maganizo m’banja. M’bale Robert wa ku Australia anati: “N’nakambapo mawu ambili okhumudwitsa kwa mkazi wanga cifukwa cokwiya. Koma vuto n’lakuti ukakamba mawu okhumudwitsa, sungawabweze. Cinaniŵaŵa ngako kuona mmene mawuwo anakhumudwitsila mkazi wanga.”

“Tonsefe timapunthwa nthawi zambili” pa mawu, ndipo mawu okambidwa mosaganiza bwino angasokoneze mtendele m’banja. (Yak. 3:2) Zaconco zikacitika, kufatsa kumatithandiza kukhalabe odekha na kulamulila lilime lathu.—Miy. 17:27.

M’bale Robert anayesetsa kuphunzila kucita zinthu modekha ndiponso modziletsa. Kodi pakhala zotulukapo zotani? M’baleyo anati: “Masiku ano, nikasemphana maganizo na mkazi wanga, nimayesetsa kumumvetsela mosamala, kukamba modekha, na kupewa kukhumudwa. Tsopano ine na mkazi wanga timagwilizana kwambili.”

Kufatsa kumatithandiza kukhala bwino na ena. Anthu amene amakonda kukwiya msanga amakhala na mabwenzi ocepa. Koma kufatsa kumatithandiza “kusunga umodzi wathu . . . mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.” (Aef. 4:2, 3) Mlongo Cathy amene tam’gwilapo kale mawu, anati: “Kufatsa kwanithandiza kuti nizicita zinthu mwamtendele na munthu aliyense, ngakhale anthu amene ni ovuta kucita nawo zinthu.”

Kufatsa kumatithandiza kukhala na mtendele wa mumtima. Baibo imagwilizanitsa “nzelu yocokela kumwamba” na khalidwe la kufatsa komanso mtendele. (Yak. 3:13, 17) Munthu wofatsa amakhala na “mtima wodekha.” (Miy. 14:30) Martin amene anayesetsa kukulitsa khalidwe la kufatsa, anati: “Tsopano ndine wololela, ndipo nili na mtendele waukulu wa mumtima na cimwemwe coculuka.”

Kukamba zoona, si copepuka munthu kukhala wofatsa. Pamafunika khama. Mwacitsanzo, m’bale wina anati: “Kukamba moona mtima, mpaka lomba nimapsa mtima kwambili nthawi zina.” Koma Yehova, amene amatilangiza kukhala ofatsa, adzatithandiza kukulitsa khalidwe limeneli. (Yes. 41:10; 1 Tim. 6:11) Iye ‘adzamalizitsa kutiphunzitsa,’ ndiponso ‘adzatilimbitsa.’ (1 Pet. 5:10) Monga Paulo, m’kupita kwa nthawi, tidzatengela “kufatsa ndi kukoma mtima kwa Khristu.”—2 Akor. 10:1.

^ ndime 2 Maina ena asinthidwa.