Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 19

“Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi Yamapeto

“Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi Yamapeto

M’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwela idzayamba kukankhana nayo [mfumu ya kumpoto].”​—DAN. 11:40.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi maulosi a m’Baibo amatithandiza kudziŵa ciani?

KODI n’ciani cidzacitikila anthu a Yehova posacedwapa? Si zovuta kudziŵa yankho lake. Maulosi a m’Baibo amafotokoza zocitika zikulu-zikulu zimene zicitike posacedwapa, zomwe zidzakhudza aliyense wa ife. M’Baibo muli ulosi wina umene umatithandiza kudziŵa zimene maboma ena amphamvu kwambili padzikoli adzacita. Ulosiwo uli pa Danieli caputa 11. Ndipo umafotokoza za mafumu aŵili olimbana, amene amachedwa mfumu ya kumpoto komanso mfumu ya kum’mwela. Mbali yaikulu ya ulosiwu inakwanilitsidwa kale. Conco, sitikayikila kuti mbali yotsala nayonso idzakwanilitsidwa.

2. Kulingana na Genesis 3:15 komanso Chivumbulutso 11:7 na 12:17, ni mfundo zofunika ziti zimene tiyenela kukumbukila poŵelenga ulosi wa Danieli?

2 Kuti timvetsetse ulosi wa pa Danieli caputa 11, tifunika kukumbukila kuti ulosiwu umakamba za olamulila na maboma okhawo amene zocita zawo zinakhudza anthu a Mulungu mwacindunji. Atumiki a Mulungu ni ocepa kwambili poyelekezela ndi anthu onse padzikoli. Nanga n’cifukwa ciani maboma amakonda kuwazunza? Cifukwa colinga cacikulu ca Satana na onse amene ali kumbali yake ni kuwononga anthu amene amatumikila Yehova na Yesu. (Ŵelengani Genesis 3:15 na Chivumbulutso 11:7; 12:17.) Kuti timvetsetse ulosi wa m’buku la Danieli, tifunikanso kuonetsetsa kuti ukugwilizana na maulosi ena a m’Mawu a Mulungu. Ndipo popanda kuyelekezela ulosi wa Danieli na mavesi ena a m’Baibo, sitingathe kuumvetsetsa.

3. Tikambilana ciani m’nkhani ino komanso m’nkhani yotsatila?

3 Tili na mfundo zimenezi m’maganizo, tiyeni lomba tikambilane lemba la Danieli 11:25-39. Pokambilana, tiona kuti ni maulamulilo ati amene anali mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela kucokela mu 1870 mpaka mu 1991. Tionanso cifukwa cake tiyenela kusintha kamvedwe kathu ka mbali inayake ya ulosi umenewu. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana Danieli 11:40–12:1. Tidzafotokoza lembali mogwilizana na kamvedwe kathu katsopano, ndipo tidzaona zimene mbali imeneyi ya ulosi imatiuza ponena za zocitika kuyambila m’ma 1990 mpaka pankhondo ya Aramagedo. Pamene muŵelenga nkhani ziŵilizi, mungacite bwino kuonanso chati yakuti “Mafumu Olimbana M’nthawi Yamapeto.” Koma coyamba, tifunika kudziŵa kuti mafumu aŵili okambidwa mu ulosiwu ni ati.

MMENE TINGADZIŴILE MFUMU YA KUMPOTO NA MFUMU YA KUM’MWELA

4. Ni zinthu zitatu ziti zimene zimatithandiza kudziŵa mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela?

4 Maina akuti “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwela,” kale anali kugwilitsidwa nchito pokamba za maulamulilo amphamvu andale amene anali kumpoto na kum’mwela kwa dziko la Isiraeli. N’cifukwa ciani takamba conco? Onani zimene mngelo amene anapeleka uthengawu kwa Danieli anakamba. Anati: “Ndabwela kudzakuthandiza kuzindikila zimene zidzagwela anthu a mtundu wako m’masiku otsiliza.” (Dan. 10:14) Kuyambila kale mpaka kudzafika pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Aisiraeli akuthupi ndiwo anali anthu a Mulungu. Koma kungocokela nthawiyo, Yehova anapeleka umboni woonekelatu wakuti anali kuona kuti ophunzila a Yesu okhulupilika ndiwo anthu ake. Conco, mbali yaikulu ya ulosi wa pa Danieli caputa 11, imakamba za otsatila a Khristu osati za Aisiraeli akuthupi. (Mac. 2:1-4; Aroma 9:6-8; Agal. 6:15, 16) M’kupita kwa nthawi, maulamulilo kapena kuti maboma oimila mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akusintha-sintha. Ngakhale n’telo, pali mbali zina zimene sizinasinthe. Coyamba, zocita za mafumu amenewa zinakhudza kwambili anthu Mulungu. Caciŵili, zimene mafumuwa anacitila anthu a Mulungu zinaonetsa kuti anali kuzonda Mulungu woona, Yehova. Cacitatu, mafumu aŵiliwa anali kulimbilana ulamulilo.

5. Kodi padzikoli panali mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela kuyambila m’caka ca 100 C.E. mpaka mu 1870? N’cifukwa ciani mwayankha conco?

5 Panthawi inayake m’zaka za m’ma 100 C.E., Akhristu ambili onyenga analoŵa mumpingo wacikhristu. Iwo anayamba kuphunzitsa ziphunzitso zabodza na kuphimba coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Kucokela nthawiyo mpaka kufika mu 1870, padziko lapansi panalibe gulu la atumiki a Mulungu. Akhristu onyenga anaculuka mumpingo wacikhristu monga namsongole, moti zinali zovuta kwambili kudziŵa Akhristu oona. (Mat. 13:36-43) N’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi n’kofunika? Cifukwa zionetsa kuti mafumu kapena maboma amene analamulila kuyambila m’caka ca 100 C.E. mpaka mu 1870, sangakhale mfumu ya kumpoto kapena mfumu ya kum’mwela. Zili conco cifukwa panthawiyi panalibe gulu la anthu a Mulungu limene akanaliukila. * Koma pambuyo pa caka ca 1870, mafumu aŵili amenewa, ya kumpoto na ya kum’mwela, anaonekelanso. Tidziŵa bwanji zimenezi?

6. Ni liti pamene anthu a Mulungu anayambanso kusonkhanitsidwa monga gulu? Fotokozani.

6 Kuyambila mu 1870, anthu a Mulungu anayambanso kusonkhanitsidwa monga gulu. M’caka cimeneci, M’bale Charles T. Russell na anzake anapanga kagulu ka ophunzila Baibo. M’bale Russell na anzakewo ndiwo anali mthenga amene ananenedwelatu kuti ‘adzakonza njila’ Ufumu wa Mesiya usanakhazikitsidwe. (Mal. 3:1) Apa tsopano atumiki oona a Mulungu anaonekelanso. Kodi panthawiyo panali maulamulilo amphamvu padziko lonse amene zocita zawo zikanakhudza kwambili atumiki a Mulungu? Ganizilani mfundo zotsatilazi.

KODI MFUMU YA KUM’MWELA NDANI?

7. Ndani anali mfumu ya kum’mwela kucokela mu 1870 mpaka mkati mwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse?

7 Pofika m’caka ca 1870, dziko la Britain linali kulamulila dela lalikulu kwambili kuposa dziko lina lililonse, ndiponso linali na gulu la asilikali lamphamvu kwambili pa dziko lonse. Mu ulosi wa Danieli, dzikoli likuimilidwa na nyanga yaing’ono imene inagonjetsa nyanga zina zitatu. Nyanga zitatuzo ziimila dziko la France, Spain, na Netherlands. (Dan. 7:7, 8) Dziko la Britain ndilo linali mfumu ya kum’mwela kuyambila mu 1870 mpaka mkati mwa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. Panthawi imodzi-modziyo, dziko la America linakhala lolemela kwambili padziko lonse, ndipo linayamba kupanga mgwilizano wamphamvu na dziko la Britain.

8. M’masiku otsiliza ano, ni maiko ati amene akhala akulamulila monga mfumu ya kum’mwela?

8 Panthawi ya Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse, Britain na America anamenya nkhondo mogwilizana, cakuti ulamulilo wawo unakhala wamphamvu kwambili. Panthawiyo, maikowa anagwilizana kwambili, ndipo anapanga ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America. Monga mmene ulosi wa Danieli unakambila, mfumuyi inasonkhanitsa “gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.” (Dan. 11:25) M’nthawi yonse ya masiku otsiliza, maiko a Britain na America ndiwo akhala akulamulila monga mfumu ya kum’mwela. * Nanga ni boma liti limene linali kulamulila monga mfumu ya kumpoto?

MFUMU YA KUMPOTO IONEKELANSO

9. Kodi mfumu ya kumpoto inaonekelanso liti? Nanga lemba la Danieli 11:25 linakwanilitsidwa bwanji?

9 Mu 1871, mfumu ina ya kumpoto inaonekela. Apa n’kuti papita caka cimodzi kucokela pamene m’bale Russell na anzake anapanga kagulu ka ophunzila Baibo. M’caka cimeneco, Otto von Bismarck anathandiza kwambili pokhazikitsa ulamulilo wamphamvu wa Germany. Wilhelm Woyamba ndiye anakhala mfumu yoyamba ya Germany, ndipo anasankha Bismarck kukhala nduna yaikulu yoyamba. * M’kupita kwa zaka, dziko la Germany linayamba kulamulila maiko ena a mu Africa komanso a ku nyanja ya Pacific. Germany anakula mphamvu kwambili moti anayamba kupikisana na dziko la Britain. (Ŵelengani Danieli 11:25) Dziko la Germany linakhazikitsa gulu lankhondo lalikulu kwambili komanso lamphamvu lotsala pang’ono kulingana na la Britain. Pankhondo yoyamba ya padziko lonse, Germany anaseŵenzetsa gulu limeneli la asilikali polimbana na adani ake.

10. Kodi ulosi wa pa Danieli 11:25b, 26 unakwanilitsidwa bwanji?

10 Ndiyeno, Danieli anakambilatu zimene zinali kudzacitikila Ulamulilo wa Germany na gulu lake la asilikali. Ulosiwo unakamba kuti mfumu ya kumpoto ‘sidzalimba.’ Cifukwa ciani? “Cifukwa adzamukonzela ciwembu. Anthu amene amadya zakudya zake zokoma ndi amene adzacititsa kuti iye athyoke.” (Dan. 11:25b, 26a) M’masiku a Danieli, anthu amene anali ‘kudya zakudya zokoma za mfumu’ anali akulu-akulu ‘otumikila mfumu.’ (Dan. 1:5) Kodi pamenepa ulosiwu ukamba za ndani? Ukamba za anthu a udindo wapamwamba mu Ufumu wa Germany, monga akulu-akulu a asilikali komanso alangizi a zankhondo. M’kupita kwa nthawi, amenewa anacititsa kuti ufumu wa Germany uthe mphamvu. * Ulosi wa Danieli sunakambe cabe za kutha mphamvu kwa ulamulilo wa Germany, koma unakambanso za mmene nkhondo ya pakati pa Germany na mfumu ya kum’mwela idzayendela. Pokamba za mfumu ya kumpoto, ulosiwo unati: “Pamenepo gulu lake lankhondo lidzagonja ngati kuti latengedwa ndi madzi osefukila, ndipo anthu ambili adzaphedwa.” (Dan. 11:26b) Monga mmene ulosiwo unakambila, pankhondo yoyamba ya padziko lonse, gulu la asilikali a Germany ‘linagonja ngati kuti latengedwa ndi madzi osefukila,’ moti ‘anthu ambili anaphedwa.’ Pankhondoyo panaphedwa anthu ambili kuposa amene anaphedwa pankhondo ina iliyonse kumbuyoko.

11. Kodi mafumu aŵili, ya kumpoto komanso ya kum’mwela, anacita ciani?

11 Pofotokoza zimene zinacitika Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse ili pafupi kuyamba, Danieli 11:27, 28 imakamba kuti mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela “azidzalankhula bodza patebulo limodzi.” Izi n’zimenedi zinacitika. Maiko a Germany na Britain anali kukambilana zakuti afuna mtendele, koma nkhondo imene inayamba mu 1914 inaonetselatu kuti zokamba zawozo zinali zabodza. Ulosi wa Danieli umakambanso kuti mfumu ya kumpoto idzadziunjikila “katundu woculuka.” Mogwilizana na ulosi umenewu, podzafika m’caka ca 1914, dziko la Germany linali litakhala dziko laciŵili lolemela kwambili padziko lonse. Ndiyeno, pokwanilitsa ulosi wa pa Danieli 11:29, na mbali yoyamba ya vesi 30, dziko la Germany linamenya nkhondo na mfumu ya kum’mwela, koma linagonjetsedwa.

MAFUMU AŴILIWA AKHALA AKUZUNZA ANTHU A MULUNGU

12. Kodi mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela anacita ciani pankhondo yoyamba ya padziko lonse?

12 Kucokela mu 1914, mafumu aŵiliwa, ya kumpoto na ya kum’mwela, akhala akulimbana kwambili komanso kuzunza anthu a Mulungu. Mwacitsanzo, pankhondo yoyamba ya padziko lonse, maboma a Germany na Britain anazunza atumiki a Mulungu amene anakana kumenya nawo nkhondo. Boma la America linaponya m’ndende abale amene anali kutsogolela pa nchito yolalikila. Cizunzo cimeneci cinakwanilitsa ulosi wa pa Chivumbulutso 11:7-10.

13. N’ciani cimene mfumu ya kumpoto inacita m’zaka za m’ma 1930 komanso pankhondo yaciŵili ya padziko lonse?

13 M’zaka za m’ma 1930 komanso maka-maka pankhondo yaciŵili ya padziko lonse, mfumu ya kumpoto inazunza anthu a Mulungu mwankhanza kwambili. Cipani ca Nazi citayamba kulamulila Germany, Hitler na otsatila ake analetsa nchito ya anthu a Mulungu. Anthu otsutsawo anapha atumiki a Yehova pafupi-fupi 1,500, ndipo ena ofika m’masauzande anawatsekela m’ndende zacibalo. Ulosi wa Danieli unakambilatu kuti zimenezi zidzacitika. Mfumu ya kumpoto inaika ziletso pa atumiki a Mulungu kuti asakhale na ufulu wotamanda dzina la Yehova poyela. Mwa kucita izi, ‘inaipitsa malo opatulika’ ndiponso ‘inacotsa nsembe zoyenela kupelekedwa nthawi zonse.’ (Dan. 11:30b, 31a) Mtsogoleli wa dzikolo, dzina lake Hitler, anacita kulumbila kuti adzafafanizilatu Mboni za Yehova mu Germany.

MFUMU YATSOPANO YA KUMPOTO IONEKELA

14. Ndani anakhala mfumu ya kumpoto pambuyo pankhondo yaciŵili ya padziko lonse? Fotokozani.

14 Pambuyo pankhondo yaciŵili ya padziko lonse, boma la cikomyunizimu la Soviet Union linayamba kulamulila maiko amene linalanda kwa Germany. Boma la Soviet Union na maiko ogwilizana naye ndiwo anakhala mfumu ya kumpoto. Mofanana na ulamulilo wopondeleza wa Nazi, boma la Soviet Union linali kuzunza mwankhanza aliyense amene anali kulambila Mulungu woona mokhulupilika m’malo momvela zilizonse zimene boma lalamula.

15. Kodi mfumu ya kumpoto inacita ciani Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha?

15 Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha, posapita nthawi mfumu yatsopano ya kumpoto, kutanthauza Soviet Union na maiko ogwilizana naye, inayamba kuzunza anthu a Mulungu. Mogwilizana na ulosi wa pa Chivumbulutso 12:15-17, mfumu ya kumpoto imeneyi inaletsa nchito yolalikila komanso inathamangitsila ku Siberia anthu a Yehova ofika m’masauzande. M’nthawi yonse ya masiku otsiliza ano, mfumu ya kumpoto yakhala ‘ikulavula madzi ngati mtsinje’ kapena kuti kuzunza anthu a Mulungu pofuna kuletsa nchito yawo, koma yalephela. *

16. Kodi boma la Soviet Union linakwanilitsa bwanji ulosi wa pa Danieli 11:37-39?

16 Ŵelengani Danieli 11:37-39. Pokwanilitsa ulosi wa pa lembali, mfumu ya kumpoto inacita zinthu ‘mosaganizila Mulungu wa makolo ake.’ Kodi inacita bwanji zimenezi? Pofuna kuthetsa zipembedzo, boma la Soviet Union linapanga pulani inayake yomwe colinga cake cinali kulanda mphamvu zipembedzo. Kuyambila mu 1918, bomalo linakhazikitsa lamulo limene linapangitsa kuti m’kupita kwa nthawi, kumasukulu ana aziphunzitsidwa zakuti kulibe Mulungu. Nanga kodi mfumu ya kumpoto inapeleka bwanji “ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambili”? Boma la Soviet Union linawononga ndalama zambili-mbili popanga gulu la nkhondo lalikulu ndi la mphamvu kwambili, komanso popanga zida za nyukiliya masauzande oculuka kuti ulamulilo wake ukhale wamphamvu. M’kupita kwa nthawi, mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela, onse anakwanitsa kupanga zida zankhondo zambili zamphamvu zotha kupha anthu mabiliyoni!

MAFUMU OLIMBANAWO ANACITILA ZINTHU PAMODZI

17. Kodi “cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko” n’ciani?

17 Mfumu ya kumpoto inacilikiza mfumu ya kum’mwela m’njila inayake yapadela. Iwo ‘anaika pamalowo cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko.’ (Dan. 11:31) “Cinthu conyansa” cimeneco ni bungwe la United Nations.

18. N’cifukwa ciani Bungwe la United Nations limachulidwa kuti “cinthu conyansa”?

18 N’cifukwa ciani Bungwe la United Nations likuchulidwa kuti “cinthu conyansa”? Cifukwa bungweli limakamba kuti lingakwanitse kubweletsa mtendele padziko lonse, pamene m’ceni-ceni Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungakwanitse kucita zimenezi. Ulosiwu umakambanso kuti cinthu conyansa cimeneci ni “cobweletsa ciwonongeko,” cifukwa cakuti bungwe la United Nations ndilo lidzaukila zipembedzo zonama na kuziwononga.—Onani chati yakuti, “Mafumu Olimbana M’nthawi Yamapeto.”

N’CIFUKWA CIANI KUDZIŴA MBILI IMENEYI N’KOFUNIKA?

19-20. (a) N’cifukwa ciani mbili imene takambilanayi ni yofunika kuidziŵa bwino? (b) Tidzakambilana funso liti m’nkhani yotsatila?

19 Kudziŵa mbili imeneyi n’kofunika cifukwa ipeleka umboni wakuti kucokela mu 1870 mpaka mu 1991, ulosi wa Danieli wokamba za mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela unakwanilitsidwa. Conco, sitikayika konse kuti mbali yothela ya ulosiwu nayonso idzakwanilitsidwa.

20 Mu 1991, ulamulilo wa Soviet Union unatha. Nanga n’ndani amene akulamulila monga mfumu ya kumpoto masiku ano? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.

NYIMBO 128 Pilila Mpaka Mapeto

^ ndime 5 Tikuona umboni woonetsa kuti ulosi wa Danieli wokamba za “mfumu ya kumpoto” na “mfumu ya kum’mwela” ukupitiliza kukwanilitsidwa. N’cifukwa ciani sitikukayikila zimenezi? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kuumvetsetsa ulosiwu?

^ ndime 5 Pa cifukwa cimeneci, sitingakambenso kuti Mfumu Yaikulu ya Roma, Uleliya (wolamulila kuyambila mu 270-275 C.E.) anali “mfumu ya kumpoto.” Komanso, sitingakambe kuti Mfumukazi Zenobia (wolamulila kuyambila mu 267-272 C.E.) anali “mfumu ya kum’mwela.” Izi zasintha mfundo zimene zili m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! macaputa 13 na 14.

^ ndime 8 Onani bokosi yakuti, “Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America mu Ulosi wa m’Baibo.”

^ ndime 9 Mu 1890, Mfumu ya Germany Wilhelm II inacotsa Bismarck paudindo.

^ ndime 10 Anthu a udindo wapamwamba anacita zambili zimene zinapangitsa kuti boma la Germany lithe mphamvu. Mwacitsanzo, analeka kucilikiza mfumu, anali kuulula zinsinsi zokhudza nkhondo, komanso anakakamiza mfumu kuti itule pansi udindo.

^ ndime 15 Malinga na zimene Danieli 11:34 imakamba, kwa kanthawi mfumu ya kumpoto inaleka kuzunza Akhristu. Mwacitsanzo, izi zinacitika pamene ulamulilo wa Soviet Union unatha mu 1991.