Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 22

Onetsani Kuti Mumayamikila Cuma Cosaoneka

Onetsani Kuti Mumayamikila Cuma Cosaoneka

“[Ikani maso anu] pa zinthu zosaoneka, . . . Pakuti zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.”​—2 AKOR. 4:18.

NYIMBO 45 Kusinkha-sinkha kwa Mtima Wanga

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yesu anakamba ciani ponena za cuma ca kumwamba?

PALI cuma cina cimene sicioneka. Ndipo cuma cosaoneka ndico camtengo wapatali kwambili. Pa ulaliki wake wa pa phili, Yesu anakamba za cuma ca kumwamba cimene n’camtengo wapatali kwambili kuposa cuma cakuthupi. Kenako anakamba kuti: “Kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:19-21) Anthufe timafuna-funa cinthu cimene timaona kuti n’cofunika kwambili kapena camtengo wapatali. Timaunjika ‘cuma cathu kumwamba’ mwa kuyesetsa kukhala na mbili yabwino kwa Mulungu, kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi. Yesu anakamba kuti cuma cimeneci sicingawonongeke kapena kubedwa.

2. (a) Kodi pa 2 Akorinto 4:17, 18, Paulo anatilimbikitsa kuika maso athu pa ciani? (b) Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kuika maso athu pa zinthu zosaoneka.’ (Ŵelengani 2 Akorinto 4:17, 18.) Zinthu zosaoneka zimenezo ni cuma cimene cimaphatikizapo madalitso amene tidzalandila m’dziko latsopano la Mulungu. M’nkhani ino, tikambilana mphatso zinayi zimene ni cuma camtengo wapatali cimene tili naco. Mphatso zake ni izi: Ubwenzi na Mulungu, pemphelo, thandizo la mzimu woyela wa Mulungu, komanso thandizo la Yehova, Yesu, na angelo pa nchito yathu yolalikila. Tikambilananso mmene tingaonetsele kuti timayamikila cuma cosaoneka cimeneci.

UBWENZI NA YEHOVA

3. Kodi cuma cosaoneka camtengo wapatali kwambili kuposa zonse n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani n’zotheka kwa ife kupeza cuma cimeneci?

3 Cuma cosaoneka camtengo wapatali kwambili cimene tili naco, ni ubwenzi wathu na Yehova Mulungu. (Sal. 25:14) Kodi zimatheka bwanji Mulungu woyela kukhala pa ubwenzi ndi anthu ocimwa? Zimatheka cifukwa nsembe ya dipo la Yesu ‘inacotsa ucimo wa dziko,’ kapena kuti wa anthu. (Yoh. 1:29) Yehova asanapeleke dipo, anadziŵilatu kuti colinga cake copulumutsa anthu kupitila mwa Yesu sicidzalepheleka. Pa cifukwa cimeneci, zinali zotheka Mulungu kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene anali na moyo Khristu asanabwele kudzatifela.—Aroma 3:25.

4. Ni anthu ena ati amene anali mabwenzi a Mulungu Yesu asanabwele padziko lapansi?

4 Ganizilani za anthu ena amene anali mabwenzi a Mulungu, Khristu asanabwele padziko lapansi. Abulahamu anali munthu wa cikhulupililo colimba kwambili. Patapita zaka zoposa 1,000 kucokela pamene Abulahamu anamwalila, Yehova anamucha “bwenzi [lake].” (Yes. 41:8) Izi zionetsa kuti olo munthu afe, Yehova amamuonabe kuti ni bwenzi lake. Conco, m’maso mwa Yehova, Abulahamu akali moyo. (Luka 20:37, 38) Munthu wina wa m’nthawi yakale amene anali bwenzi la Mulungu ni Yobu. Pamene angelo onse anasonkhana kumwamba, Yehova anakamba monyadila za Yobu. Anakamba kuti Yobu anali “munthu wopanda colakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.” (Yobu 1:6-8) Nanga bwanji za Danieli, amene anatumikila Yehova mokhulupilika m’dziko la anthu osalambila Mulungu kwa zaka pafupi-fupi 80? Kodi Yehova anali kumuona bwanji? Katatu konse angelo anauza Danieli, amene panthawiyo anali wokalamba, kuti anali “wokondedwa kwambili” kwa Mulungu. (Dan. 9:23; 10:11, 19) Sitikayikila kuti Yehova amacita kulaka-laka nthawi pamene adzaukitsa mabwenzi ake amene anamwalila.—Yobu 14:15.

Kodi njila zina zimene tingaonetsele kuti timayamikila cuma cosaoneka n’ziti? (Onani ndime 5) *

5. Kodi munthu amafunika kucita ciani kuti akhale pa ubwenzi wolimba na Yehova?

5 Masiku ano, anthu mamiliyoni ali pa ubwenzi wolimba na Yehova. Tidziŵa zimenezi cifukwa anthu ambili padzikoli, amuna, akazi, ndi ana, amacita zinthu zoonetsa kuti alidi mabwenzi a Mulungu. Baibo imakamba kuti Yehova “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miy. 3:32) Zimakhala zotheka kwa ife kukhala pa ubwenzi na Yehova cifukwa cokhulupilila nsembe ya dipo la Yesu. Cifukwa ca dipo limeneli, Yehova amatilola kudzipatulila kwa iye na kubatizika. Tikacita zinthu zofunika zimenezi, timaloŵa m’gulu la Akhristu mamiliyoni odzipatulila komanso obatizika, amene ali pa ubwenzi wolimba na Yehova, Mulungu wamkulu-kulu m’cilengedwe conse!

6. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwayi wokhala pa ubwenzi na Mulungu?

6 Tingaonetse bwanji kuti timaona kuti ubwenzi wathu na Mulungu ni wamtengo wapatali? Abulahamu na Yobu anakhalabe okhulupilika kwa Mulungu kwa zaka zoposa 100. Nafenso tifunika kukhalabe okhulupilika olo kuti tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali m’dziko loipali. Mofanana na Danieli, tifunika kuona ubwenzi wathu na Mulungu kukhala wofunika kwambili kuposa moyo wathu. (Dan. 6:7, 10, 16, 22) Ndi thandizo la Yehova, tingathe kupilila mayeselo alionse amene tingakumane nawo n’kukhalabe pa ubwenzi wolimba na iye.—Afil. 4:13.

MPHATSO YA PEMPHELO

7. (a) Kulingana na Miyambo 15:8, kodi Yehova amamvela bwanji na mapemphelo athu? (b) Nanga amayankha bwanji mapemphelo athu?

7 Mphatso ina yosaoneka imene tili nayo ni pemphelo. Mabwenzi apamtima amakonda kuuzana zakukhosi komanso mmene akumvelela. N’zimenenso timacita na bwenzi lathu Yehova. Iye amakamba nase kupitila m’Mawu ake. Ndipo kupitila m’Mawu akewo, amatiuza maganizo ake ndiponso mmene amamvelela. Ise timakamba naye kupitila m’pemphelo. Pamene tipemphela, tingamuuze zimene zili mumtima mwathu komanso mmene tikumvelela. Yehova amakondwela kumvetsela mapemphelo athu. (Ŵelengani Miyambo 15:8.) Kuwonjezela apo, monga Bwenzi lacikondi, amayankha mapemphelo athu. Nthawi zina amayankha mwamsanga. Koma nthawi zina tingafunike kupemphela mobweleza-bweleza. Olo zikhale conco, sitikayikila kuti adzatiyankha pa nthawi yake ndiponso m’njila yoyenela. Nthawi zina, Mulungu angatiyankhe mosiyana na mmene tinali kuganizila. Mwacitsanzo, m’malo mothetsa vuto limene tikukumana nalo, angatipatse nzelu na mphamvu kuti tikwanitse ‘kupilila.’—1 Akor. 10:13.

(Onani ndime 8) *

8. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso ya pemphelo?

8 Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila mphatso yamtengo wapatali imeneyi ya pemphelo? Njila imodzi ni mwa kulabadila malangizo a Yehova akuti: “Muzipemphela mosalekeza.” (1 Ates. 5:17) Iye satikakamiza kupemphela. Koma amalemekeza ufulu wathu wosankha, ndipo amatilangiza kuti “tizilimbikila kupemphela.” (Aroma 12:12) Conco, tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya pemphelo mwa kupemphela kaŵili-kaŵili tsiku lililonse. Ndipo pamene tipemphela, sitiyenela kuiŵala kumuyamikila Yehova na kum’tamanda.—Sal. 145:2, 3.

9. Kodi m’bale Chris amaliona bwanji pemphelo? Nanga imwe mumaliona bwanji?

9 Ngati tatumikila Yehova kwa zaka zambili ndipo taona mmene Yehova amayankhila mapemphelo athu, timayamba kuyamikila kwambili mphatso ya pemphelo. Mwacitsanzo, ganizilani za m’bale Chris amene wakhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 47. Iye anati: “Nimakondwela kupatula nthawi yopemphela kwa Yehova m’maŵa uliwonse. Zimakhala zokondweletsa kwambili kukamba na Yehova m’maŵa pamene dzuŵa likutuluka, kunja kukuoneka kokongola. Izi zimanisonkhezela kumuyamikila cifukwa ca mphatso zonse zimene amatipatsa, kuphatikizapo pemphelo. Madzulo nisanapite kukagona, nimayamba napemphela, ndipo cimakhala cokondweletsa kupita kukagona nili na cikumbumtima coyela.”

MPHATSO YA MZIMU WOYELA

10. N’cifukwa ciani tiyenela kuona kuti mzimu woyela wa Mulungu ni mphatso yamtengo wapatali?

10 Mphatso ina yosaoneka imene tiyenela kuiona kukhala yofunika kwambili ni mzimu woyela wa Mulungu. Yesu anatilangiza kuti tiyenela kupitiliza kupempha mzimu woyela kwa Mulungu. (Luka 11:9, 13) Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake potipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7; Mac. 1:8) Cifukwa ca mphamvu ya mzimu wa Mulungu, tingakwanitse kupilila mayeselo alionse amene tingakumane nawo.

(Onani ndime 11) *

11. Kodi mzimu woyela ungatithandize bwanji?

11 Mzimu woyela ungatithandize kukwanilitsa mautumiki amene tili nawo m’gulu la Mulungu. Ungatithandize kukulitsa maluso amene tili nawo. Conco, ngati zinthu zikutiyendela bwino mu utumiki wathu, timadziŵa kuti zimenezo zatheka kokha cifukwa ca thandizo la mzimu wa Mulungu.

12. Mogwilizana na Salimo 139:23, 24, kodi tingapemphe mzimu woyela kuti utithandize kucita ciani?

12 Njila ina imene timaonetsela kuti timaona mzimu woyela kukhala mphatso yamtengo wapatali, ni mwa kupempha Yehova kuti atipatse mzimuwo kuti utithandize kudziŵa maganizo kapena zilakolako zoipa zimene zili mu mtima mwathu. (Ŵelengani Salimo 139:23, 24.) Tikapempha zimenezi, Yehova poseŵenzetsa mzimu wake angatithandize kudziŵa maganizo na zilakolako zoipa zimene tili nazo. Ndipo tikadziŵa kuti tili na maganizo kapena cilakolako cinacake coipa, tiyenela kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake umene ungatithandize kuthetsa maganizo oipa kapena cilakolako coipaco. Tikatelo, tidzaonetsa kuti ndife otsimikiza mtima kupewa ciliconse cimene cingapangitse kuti Yehova aleke kutithandiza na mzimu wake woyela.—Aef. 4:30.

13. Kodi tingacite ciani kuti tiziyamikila kwambili mphatso ya mzimu woyela?

13 Kodi tingacite ciani kuti tiziyamikila kwambili mphatso ya mzimu woyela? Tiyenela kumaganizila zimene mzimuwo ukucita masiku ano. Yesu asanapite kumwamba, anauza ophunzila ake kuti: “Mzimu woyela ukadzafika pa inu, mudzalandila mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Izi n’zimenedi zikucitika masiku ano. Cifukwa ca thandizo la mzimu woyela, atumiki a Yehova oposa 8.5 miliyoni ocokela kulikonse padzikoli, asonkhanitsidwa kukhala gulu la Yehova. Kuwonjezela apo, tili m’paradaiso wauzimu cifukwa mzimu wa Mulungu umatithandiza kukulitsa makhalidwe abwino, monga cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa, komanso kudziletsa. Awa ni “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22, 23) Ndithudi! Mzimu woyela ni mphatso yamtengo wapatali!

KUSEŴENZELA PAMODZI NA YEHOVA, YESU, KOMANSO ANGELO

14. Kodi ndani amatithandiza pamene tigwila nchito yolalikila?

14 Tili na cuma cina cosaoneka, cimene ni mwayi ‘wogwila nchito limodzi’ na Yehova, Yesu, ndiponso angelo. (2 Akor. 6:1) Timaseŵenzela nawo limodzi pamene tikugwila nchito yolalikila. Paulo pokamba za iyemwini komanso za anthu ena amene amagwila nchitoyi, anati: “Ndife anchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Tikamagwila nchito yolalikila, timakhalanso anchito anzake a Yesu. Kumbukilani kuti iye atalamula otsatila ake kuti, “pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga,” anakambanso kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mat. 28:19, 20) Nanga kodi angelo amatithandiza bwanji? Iwo amatitsogolela pamene tikulengeza “uthenga wabwino wosatha . . . kwa anthu okhala padziko lapansi.” Kunena zoona, umenewu ni mwayi waukulu!—Chiv. 14:6.

15. Fotokozani citsanzo ca m’Baibo coonetsa mbali yaikulu imene Yehova amacita pa nchito yathu yolalikila.

15 Ni madalitso otani amene timapeza pa nchito yolalikila cifukwa ca thandizo la Yehova, Yesu, na angelo? Pamene tilalikila uthenga wa Ufumu, mbewu zina za coonadi zimagwela pa nthaka yabwino na kukula. (Mat. 13:18, 23) Ndani amene amacititsa kuti mbewu za coonadi zimenezi zikule na kubala zipatso? Yesu anakamba kuti palibe munthu amene angakhale wotsatila wake “akapanda kukokedwa ndi Atate” wake. (Yoh. 6:44) Ndipo m’Baibo muli citsanzo cofotokoza mwacindunji za munthu amene anakokedwa na Yehova. Kumbukilani zimene zinacitika pamene Paulo analalikila gulu la azimayi kunja kwa mzinda wa Filipi. Onani zimene Baibo imakamba ponena za mmodzi wa azimayiwo, dzina lake Lidiya. Imati: “Yehova anatsegula kwambili mtima wake kuti achele khutu ku zimene Paulo anali kunena.” (Mac. 16:13-15) Mofanana na Lidiya, anthu ena mamiliyoni akokedwa na Yehova.

16. Ndani ayenela kutamandidwa ngati zinthu zikutiyendela bwino mu ulaliki?

16 Kodi ndani kweni-kweni amene amacititsa kuti zinthu zitiyendele bwino mu ulaliki? Paulo anayankha funso limeneli polembela kalata Akhristu a mu mpingo wa ku Korinto. Iye anati: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa. Cotelo wobzala kapena wothilila sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.” (1 Akor. 3:6, 7) Tiyenela kutengela citsanzo ca Paulo mwa kutamanda Yehova nthawi zonse ngati ulaliki ukutiyendela bwino.

17. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwayi ‘wogwila nchito limodzi’ na Yehova, Yesu, ndiponso angelo?

17 Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwayi ‘wogwila nchito limodzi’ na Yehova, Yesu, ndiponso angelo? Tingatelo mwa kuyesetsa kusakila mipata youzako ena uthenga wabwino. Pali njila zambili zolalikilila uthenga wabwino. Mwacitsanzo, tingacite ulaliki ‘wapoyela komanso wa kunyumba ndi nyumba.’ (Mac. 20:20) Ofalitsa ena ambili amakondanso kulalikila mwamwayi. Akakumana na munthu, amam’patsa moni mwaubwenzi na kuyesa kuyambitsa makambilano. Ngati munthuyo waonetsa cidwi, mwaluso amayamba kukambilana naye uthenga wabwino wa Ufumu.

(Onani ndime 18) *

18-19. (a) Kodi timathilila bwanji mbewu za coonadi? (b) Fotokozani citsanzo ca mmene Yehova anathandizila wophunzila Baibo wina.

18 Monga “anchito anzake a Mulungu,” tikafesa mbewu za coonadi, tiyenelanso kumazithilila. Ngati munthu waonetsa cidwi, tiyenela kuyesetsa kucita ulendo wobwelelako, kapena tingapemphe wina kuti akakambilanenso naye munthuyo n’colinga coyambitsa phunzilo la Baibo. Pamene wophunzila akupita patsogolo, timakondwela kuona Yehova akumuthandiza kusintha maganizo na mtima wake.

19 Ganizilani za m’bale Raphalalani wa ku South Africa. Asanakhale Mboni, anali sing’anga. Atayamba kuphunzila Baibo, anakondwela kwambili na zimene anali kuphunzila. Koma zinali zovuta kwambili kwa iye kulabadila zimene Baibo imakamba zakuti sitiyenela kulankhula ndi anthu akufa. (Deut. 18:10-12) Pang’ono-pang’ono, iye analola kuti Mulungu amuthandize kusintha maganizo ake. Ndipo m’kupita kwa nthawi, analeka using’anga olo kuti ndiyo nchito imene inali kum’thandiza kupeza zofunikila mu umoyo. M’bale Raphalalani, amene lomba ali na zaka 60, anati: “Nimayamikila kwambili kuti Mboni za Yehova zinanithandiza m’njila zambili. Mwacitsanzo, zinanithandiza kupeza nchito. Koposa zonse, nimayamikila Yehova ponithandiza kusintha umoyo wanga, moti tsopano nili na mwayi wogwila nawo nchito yolalikila, monga Mboni yobatizika.”

20. Kodi imwe mudzayesetsa kucita ciani?

20 M’nkhani ino, takambilana mphatso zinayi zimene ni cuma cosaoneka. Koma camtengo wapatali kwambili pa mphatso zimenezi, ni mwayi wokhala pa ubwenzi wolimba na Yehova. Zili conco cifukwa ubwenzi umenewu, ni umene umatithandiza kupindula na mphatso zina monga pemphelo, thandizo la mzimu woyela, komanso thandizo la Yehova, Yesu, na angelo pa nchito yolalikila. Tiyeni tiziyesetsa kukulitsa mtima woyamikila kaamba ka mphatso zosaoneka zimenezi. Ndipo tisaleke kuyamikila Yehova, amene ni Bwenzi lathu labwino kwambili.

NYIMBO 145 Mulungu Analonjeza Paradaiso

^ ndime 5 M’nkhani yapita, tinakambilana za mphatso zingapo zooneka zimene Mulungu anatipatsa. M’nkhani ino, tikambilana za cuma cosaoneka kapena kuti mphatso zosaoneka. Tikambilananso mmene tingaonetsele kuyamikila cuma cimeneco. Nkhaniyi itithandizanso kuti tiziyamikila kwambili Yehova Mulungu, Gwelo la cuma cimeneci.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (1) Pamene mlongo akuyang’ana zacilengedwe, akusinkha-sinkha za ubwenzi wake na Yehova.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (2) Mlongoyo akupemphela kwa Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima kuti akwanitse kulalikila.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (3) Mzimu woyela wathandiza mlongoyo kucita ulaliki wamwayi molimba mtima.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (4) Mlongoyo akutsogoza phunzilo la Baibo kwa munthu uja amene anamulalikila mwamwayi. Mlongo mmodzi-modziyo akuthandizidwa na angelo pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila.