Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 18

Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?

Kodi Mudzapunthwa Cifukwa ca Yesu?

“Wodala amene sapeza cokhumudwitsa mwa ine.”—MAT. 11:6.

NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ciani cimene ciyenela kuti cinakudabwitsani pamene kwa nthawi yoyamba munayesa kuuzako ena uthenga wa m’Baibo?

KODI mukumbukila nthawi yoyamba pamene munazindikila kuti mwapeza coonadi? Ziphunzitso za m’Baibo zimene munali kuphunzila zinali zosavuta kumva komanso zomveka bwino. Munali kuganiza kuti aliyense adzakondwela kuphunzila zimene imwe munayamba kukhulupilila. Munali otsimikiza kuti uthenga wa m’Baibo udzawathandiza kukhala na umoyo wabwino palipano, komanso kukhala na ciyembekezo ca tsogolo labwino. (Sal. 119:105) Conco, mwacimwemwe munali kuuzako mabwenzi na acibale anu onse mfundo za coonadi zimene munapeza. Koma n’ciani cinacitika? Munadabwa kuti ambili anakana zimene munali kuwauza.

2-3. N’cifukwa ciani unyinji wa anthu m’nthawi ya Yesu unam’kana?

2 Tonsefe sitiyenela kudabwa ngati ena akana uthenga umene timalalikila. M’nthawi ya Yesu, unyinji wa anthu unam’kana ngakhale kuti anacita zozizwitsa zambili zoonetsa kuti Mulungu anali naye. Mwacitsanzo, Yesu anaukitsa Lazaro—cozizwitsa cimene ngakhale anthu omutsutsa sakanakana. Ngakhale n’telo, atsogoleli aciyuda sanalandile Yesu monga Mesiya. Iwo anafuna ngakhale kupha onse aŵili, Yesu na Lazaro!—Yoh. 11:47, 48, 53; 12:9-11.

3 Yesu anadziŵa kuti anthu ambili adzakana kukhulupilila kuti iye ni Mesiya. (Yoh. 5:39-44) Iye anauza gulu la ophunzila a Yohane M’batizi kuti: “Wodala amene sapeza cokhumudwitsa mwa ine.” (Mat. 11:2, 3, 6) N’cifukwa ciani ambili anam’kana Yesu?

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino na yotsatila, tidzakambilana zifukwa zake ambili m’zaka za zana loyamba sanam’khulupilile Yesu. Tidzaonanso cifukwa cake ambili masiku ano amakana uthenga wathu. Ndipo cofunika kwambili, tidzaphunzila cifukwa cake tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba mwa Yesu kuti tisapunthwe.

(1) KUMENE YESU ANAKULILA

Ambili anapunthwa cifukwa ca kumene Yesu anakulila. Kodi zinthu zofanana na zimenezi zikuwapunthwitsa bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 5) *

5. N’cifukwa ciani ena anaganiza kuti Yesu sanali Mesiya wolonjezedwayo?

5 Ambili anapunthwa cifukwa ca kumene Yesu anakulila. Iwo anali kudziŵa kuti Yesu ni mphunzitsi waluso kwambili, komanso amacita zozizwitsa. Koma kwa iwo, iye anali cabe mwana wa kalipentala wosauka. Ndipo anali wocokela ku Nazareti, mzinda umene unali kuonedwa kuti ni wotsika. Ngakhale Natanayeli amene anakhala wophunzila wa Yesu, poyamba anati: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” (Yoh. 1:46) N’kutheka kuti Natanayeli sanali kuukonda mzinda umene Yesu anali kukhala. Kapena anali kuganizila za ulosi wa pa Mika 5:2, umene unakambilatu kuti Mesiya adzabadwila ku Betelehemu, osati ku Nazareti.

6. M’nthawi ya Yesu, n’ciani cikanathandiza anthu kumuzindikila kuti iye ndiye Mesiya?

6 Kodi Malemba amati ciani? Mneneli Yesaya analosela kuti adani a Yesu adzalephela kuganizila “tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo” a Mesiya. (Yes. 53:8) Zambili zokhudza Mesiya zinali zitaloseledwa kale. Anthu amenewo akanapenda zonse zokhudza Yesu, akanadziŵa kuti iye anabadwila ku Betelehemu, komanso kuti anali mbadwa ya Mfumu Davide. (Luka 2:4-7) Conco, malo amene Yesu anabadwilako anali ogwilizana na ulosi wa pa Mika 5:2. Nanga kodi vuto linali ciani? Anthu anafulumila kumuweluza Yesu m’maganizo awo asanadziŵe zonse zokhudza iye. Kaamba ka ici, iwo anapunthwa.

7. N’cifukwa ciani anthu ambili masiku ano amakana Mboni za Yehova?

7 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Ambili mwa anthu a Yehova ni osaukila. Anthu ambili amaona kuti iwo ni “anthu osaphunzila ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Ena amakamba kuti anthu a Mulungu sangaphunzitse Baibo cifukwa sanapite ku masukulu ochuka ophunzitsa za umulungu. Ena amaganiza kuti Mboni za Yehova ni “Cipembedzo ca ku America,” ngakhale kuti m’ceni-ceni Mboni za Yehova zambili sizikhala ku America. Enanso amauzidwa kuti Mboni za Yehova sizikhulupilila Yesu. Kwa zaka zambili, anthu akhala akutinena kuti ife anthu a Yehova timacilikiza “cikomyunizimu,” ndife “akazitape a dziko la America,” komanso kuti ndife “anthu a maganizo na makhalidwe opitilila muyeso.” Cifukwa cakuti anthu amene amauzidwa nkhani zimenezi sadziŵa zeni-zeni, amakhumudwa nafe.

8. Malinga na Machitidwe 17:11, kodi anthu ayenela kucita ciani ngati afuna kudziŵa atumiki a Mulungu masiku ano?

8 Kodi munthu angacite ciani kuti asapunthwe? Anthu ayenela kupenda mosamala kuti adziŵe zoona zeni-zeni. Izi n’zimene wolemba Uthenga Wabwino Luka anatsimikiza kucita. Iye anayesetsa kufufuza “zinthu zonse mosamala kwambili kucokela pa ciyambi.” Anafuna kuti oŵelenga ‘adziŵe bwino-bwino kuti zinthu zimene’ anamvela zokhudza Yesu n’zodalilika. (Luka 1:1-4) Ayuda okhala mu mzinda wakale wa Bereya anali monga Luka. Iwo atamva uthenga wabwino wokhudza Yesu kwa nthawi yoyamba, anafufuza m’Malemba a Ciheberi kuti atsimikizile ngati zimene anali kuuzidwa zinalidi zoona. (Ŵelengani Machitidwe 17:11.) Mofananamo, anthu masiku ano ayenelanso kupenda mosamala kuti adziŵe zoona zeni-zeni. Ayenela kulinganiza zimene amaphunzitsidwa na anthu a Mulungu na zimene Malemba amakamba. Ayenelanso kuidziŵa bwino mbili yamakono ya anthu a Yehova. Akacita zimenezi, sadzalola tsankho kapena zokamba za anthu kuwacititsa khungu.

(2) YESU ANAKANA KUCITA ZOZIZWITSA ZODZIONETSELA

Ambili anapunthwa cifukwa cakuti Yesu anakana kucita zozizwitsa zodzionetsela. Kodi zinthu zofanana na zimenezi zikuwapunthwitsa bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 9-10) *

9. N’ciani cinacitika Yesu atakana kuonetsa cizindikilo cocokela kumwamba?

9 Anthu ena m’nthawi ya Yesu sanakhutile na ziphunzitso zake zocititsa cidwi. Iwo anali kufuna zowonjezeleka. Anamuuza kuti adzakhulupilila kuti iye ni Mesiya ngati awaonetsa “cizindikilo cocokela kumwamba.” (Mat. 16:1) Mwina anamuuza zimenezi cifukwa cosamvetsa bwino lemba la Danieli 7:13, 14. Komabe, nthawi ya Yehova yokwanilitsa ulosi umenewo inali isanakwane. Zimene Yesu anali kuphunzitsa zinayenela kukhala zokwanila kuti iwo akhulupilile kuti iye ni Mesiya. Koma pamene iye anakana kuwapatsa cizindikilo cimene anali kufuna, anthuwo anapunthwa.—Mat. 16:4.

10. Kodi Yesu anakwanilitsa bwanji zimene Yesaya analemba zokhudza Mesiya?

10 Kodi Malemba amati ciani? Ponena za Mesiya, mneneli Yesaya analemba kuti: “Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.” (Yes. 42:1, 2) Yesu anali kucita utumiki wake modzicepetsa osati modzionetsela. Iye sanamange akacisi odzionetsela ndipo sanavale zovala zapamwamba zacipembedzo kapena kulamula kuti anthu azimuchula na maina audindo a cipembedzo. Pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu kuti aphedwe, iye anakana kukondweletsa Mfumu Herode mwa kumuonetsa cizindikilo. (Luka 23:8-11) Yesu anali kucita zozizwitsa. Koma colinga cake cacikulu cinali kulalikila uthenga wabwino. Iye anauza ophunzila ake kuti, “[Ici] ndico colinga cimene ndinabwelela.”—Maliko 1:38.

11. Kodi anthu ena ali na maganizo olakwika ati masiku ano?

11 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Masiku ano, anthu ambili amakondwela na machalichi akulu-akulu okhala na zithunzi zamtengo wapamwamba, atsogoleli acipembedzo okhala na maudindo apamwamba, komanso miyambo yosagwilizana na mfundo za m’Baibo. Koma anthu amene amapita ku machalichi amaphunzila zocepa ponena za Mulungu na colinga cake. Aja amene amapezeka ku misonkhano yathu yacikhristu, amaphunzila zimene Yehova amafuna kwa ife na mmene angacitile zinthu mogwilizana na cifunilo cake. Nyumba zathu za Ufumu n’zaukhondo ndipo si zokongoletsedwa mwapamwamba. Amene amatsogolela savala zovala zapamwamba kapena kuchulidwa na maina audindo. Mawu a Mulungu ndiwo maziko a zimene timaphunzitsa na kukhulupilila. Ngakhale n’telo, ambili masiku ano amakhumudwa cifukwa amaganiza kuti kalambilidwe kathu n’kocititsa ulesi. Ndipo zimene timaphunzitsa zimasiyana na zimene iwo amafuna kumva.

12. Mogwilizana na mmene Aheberi 11:1, 6 yafotokozela, kodi cikhulupililo cathu ciyenela kuzikidwa pa ciani?

12 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma kuti: “Munthu amakhala ndi cikhulupililo cifukwa ca zimene wamva. Ndipo zimene wamvazo zimacokela m’mawu onena za Khristu.” (Aroma 10:17) Conco timalimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Malemba, osati mwa kucitako miyambo yacipembedzo yosagwilizana na malemba, olo kuti ioneke yokondweletsa kwambili m’maso mwathu. Tifunika kukhala na cikhulupililo colimba cozikidwa pa cidziŵitso colongosoka cifukwa “popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” (Ŵelengani Aheberi 11:1, 6.) Conco, sitifunika kucita kuona cizindikilo capadela cocokela kumwamba kuti tikhulupilile kuti tapeza coonadi. Kupenda mosamala ziphunzitso za m’Baibo zolimbitsa cikhulupililo n’kokwanila kuti tikhutile na kucotsa zikayikilo zilizonse zimene tingakhale nazo.

(3) YESU SANATSATILE MIYAMBO YAMBILI YA AYUDA

Ambili anapunthwa cifukwa cakuti Yesu anakana kutsatila ina mwa miyambo yawo. Kodi zinthu zofanana na zimenezi zikuwapunthwitsa bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 13) *

13. N’ciani cinapangitsa anthu ambili kumuimba mlandu Yesu?

13 M’nthawi ya Yesu, ophunzila a Yohane M’batizi anadabwa cifukwa ophunzila a Yesu sanali kusala kudya. Yesu anafotokoza kuti panalibe cifukwa cosalila kudya cifukwa iye anali akali na moyo. (Mat. 9:14-17) Ngakhale n’telo, Afarisi na otsutsa ena anamuimba mlandu Yesu cifukwa sanali kutsatila miyambo yawo. Iwo anakwiya pamene Yesu anasankha kucilitsa odwala pa Sabata. (Maliko 3:1-6; Yoh. 9:16) Anali kukamba kuti amalemekeza Sabata, koma anali kuona kuti palibe vuto kucita malonda m’kacisi. Iwo anakwiya kwambili Yesu atawadzudzula kaamba ka zimenezo. (Mat. 21:12, 13, 15) Ndipo pamene Yesu anali kulalikila anthu m’sunagoge ku Nazareti, anthuwo anakwiya kwambili iye atapeleka zitsanzo zokhudza mbili ya Aisiraeli, zimene zinavumbula kuti iwo anali anthu odzikonda komanso opanda cikhulupililo. (Luka 4:16, 25-30) Anthu ambili anapunthwa cifukwa Yesu sanacite zimene iwo anali kuyembekezela.—Mat. 11:16-19.

14. N’cifukwa ciani Yesu anadzudzula miyambo ya anthu yosemphana na Malemba?

14 Kodi Malemba amati ciani? Yehova kupitila mwa mneneli Yesaya anati: “Anthu awa ayandikila kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha koma mtima wawo auika kutali ndi ine, ndiponso amangophunzila malamulo a anthu n’kumaganiza kuti kucita zimenezo ndiye kundiopa.” (Yes. 29:13) Panali poyenela Yesu kudzudzula miyambo ya anthu yosagwilizana na Malemba. Anthu amene anali kuona kuti malamulo opangidwa na anthu ni ofunika kwambili kuposa Malemba, anakana Yehova komanso Mesiya amene anatumidwa na iye.

15. N’cifukwa ciani anthu ambili masiku ano sazikonda Mboni za Yehova?

15 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Ambili amakwiya cifukwa cakuti Mboni za Yehova sizicita nawo miyambo yosagwilizana na Malemba, monga kukondwelela masiku akubadwa, na Khrisimasi. Ena amakalipa akaona kuti Mboni za Yehova sizicitako zikondwelelo za dziko lawo, kapena cifukwa sizitsatila miyambo ya malilo yosemphana na Mawu a Mulungu. Aja amene amakhumudwa pa zifukwa zimenezi, amakhulupilila na mtima wonse kuti amalambila Mulungu movomelezeka. Koma sangamukondweletse ngati amakonda kwambili miyambo ya dziko kuposa ziphunzitso zomveka bwino za m’Baibo.—Maliko 7:7-9.

16. Malinga na Salimo 119:97, 113, 163-165, kodi tiyenela kucita ciani? Nanga tiyenela kupewa ciani?

16 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Tiyenela kukonda kwambili malamulo a Yehova na mfundo zake. (Ŵelengani Salimo 119:97, 113, 163-165.) Ngati timam’konda Yehova, tidzakana miyambo iliyonse yosam’kondweletsa. Sitidzalola ciliconse kusokoneza cikondi cathu pa Yehova.

(4) YESU SANATHETSE MAVUTO A ZANDALE

Ambili anapunthwa cifukwa cakuti Yesu sanafune kuloŵelela m’zandale. Kodi zinthu zofanana na zimenezi zikuwapunthwitsa bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 17) *

17. Malinga n’zimene anthu anali kuyembekezela, n’cifukwa ciani ambili anam’kana Yesu?

17 Ena m’nthawi ya Yesu, anali kufuna kusintha ulamulilo wa boma. Iwo anali kuyembekezela kuti Mesiya adzawamasula ku ulamulilo wopondeleza wa Aroma. Koma pamene iwo anayesa kuika Yesu kukhala mfumu yawo, iye anakana. (Yoh. 6:14, 15) Ena, kuphatikizapo ansembe, anali na nkhawa yakuti Yesu akasintha zinthu pa nkhani za ndale, adzakwiyitsa Aroma amene anapatsa atsogoleli amenewo mphamvu na ulamulilo. Nkhawa zokhudza ndale zimenezo zinapangitsa Ayuda ambili kukana Yesu.

18. Ni maulosi a m’Baibo ati okhudza Mesiya amene ambili anawanyalanyaza?

18 Kodi Malemba amati ciani? Ngakhale kuti maulosi ambili anakambilatu kuti Mesiya pamapeto pake adzapambana nkhondo, maulosi ena anaonetsa kuti adzafunika kufa coyamba kaamba ka macimo athu. (Yes. 53:9, 12) Nanga n’cifukwa ciani Ayuda anali kuyembekezela zinthu zolakwika zokhudza Mesiya? Ambili m’nthawi ya Yesu ananyalanyaza ulosi uliwonse umene sunawapatse ciyembekezo cothetsa mavuto awo panthawiyo.—Yoh. 6:26, 27.

19. N’cifukwa ciani ambili amakana uthenga wathu masiku ano?

19 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Ambili masiku ano amakhumudwa nafe cifukwa cakuti sititengako mbali m’zandale. Iwo amafuna kuti tizivotako pa masankho. Komabe, timadziŵa kuti tikasankha mtsogoleli waumunthu kuti azitilamulila, ndiye kuti tikukana Yehova. (1 Sam. 8:4-7) Anthu amaona kuti tiyenela kumanga masukulu, zipatala, komanso kucita zinthu zina zothandiza anthu. Iwo amakana uthenga wathu cifukwa timasumika maganizo athu pa nchito yolalikila, osati pa kuthetsa mavuto amene ali padzikoli.

20. Mogwilizana na zimene Yesu anakamba pa Mateyu 7:21-23, kodi colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala ciani?

20 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? (Ŵelengani Mateyu 7:21-23.) Colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala pa kugwila nchito imene Yesu anatilamula. (Mat. 28:19, 20) Tisatengeke na zandale kapena kutangwanika pofuna kuyesa kuthetsa mavuto a m’dzikoli. Timakonda anthu, ndipo timasamala za mavuto awo. Koma tidziŵa kuti njila yabwino yothandizila anansi athu, ni mwa kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu ndiponso mwa kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova.

21. Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

21 M’nkhani ino, takambilana zopunthwitsa zinayi zimene zinapangitsa anthu ambili kukana Yesu m’zaka za zana loyamba, komanso zimene zingapangitse ena masiku ano kukana otsatila a Yesu. Koma kodi izi ndiye zinthu zokha zimene tiyenela kupewa? Iyai. M’nkhani yotsatila, tidzakambilananso zopunthwitsa zina zinayi zimene zinapangitsa anthu ambili kukana Yesu. Tiyeni tiziyesetsa kuti tisapunthwe, ndiponso tikhalebe na cikhulupililo colimba.

NYIMBO 56 Khulupilila Coonadi Iwe Mwini

^ ndime 5 Ngakhale kuti Yesu anali Mphunzitsi waluso kuposa anthu onse amene anakhalako padziko lapansi, anthu ambili m’nthawi yake anam’kana. Cifukwa ciani? M’nkhani ino, tikambilana zifukwa zinayi. Tidzaonanso cifukwa cake ambili masiku ano, amakhumudwa na zimene otsatila oona a Yesu amakamba na kucita. Ndipo cofunika kwambili, tidzaphunzila cifukwa cake tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba mwa Yesu kuti tisapunthwe.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Filipo alimbikitsa Natanayeli kuti akumane na Yesu.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu alalikila uthenga wabwino.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu akucilitsa munthu wopuwala dzanja pamene otsutsa akuona.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu akupita ku phili ali yekha-yekha.