Kodi Mudziŵa?
Kodi m’nthawi za m’Baibo anthu anali kugwilitsila nchito gumbwa kupanga ngalawa?
AMBILI amadziŵa kuti m’nthawi za makedzana, anthu ku Iguputo anali kuseŵenzetsa kwambili gumbwa kupangila mapepala olembapo. Agiriki na Aroma, anali kulemba pa mapepala a gumbwa. * Koma ambili sadziŵa kuti gumbwa anali kumugwilitsilanso nchito kupangila ngalawa.
Zaka zoposa 2,500 zapitazo, mneneli Yesaya analemba kuti anthu okhala “m’cigawo ca mitsinje ya ku Itiyopiya” anatumiza “nthumwi zake panyanja, m’ngalawa zoyenda pamadzi zopangidwa ndi gumbwa.” Pambuyo pake, mneneli Yeremiya analosela kuti mzinda wa Babulo ukadzaukilidwa na Amedi na Aperisiya, iwo adzatentha “ngalawa zagumbwa” za Ababulo kuti asakathaŵe.—Yes. 18: 1, 2; Yer. 51:32.
Baibo ni mawu ouzilidwa a Mulungu. Conco n’zosadabwitsa kwa anthu okonda kuŵelenga Baibo mozama, kuti zimene ofukula zakale apeza, zionetsa kuti gumbwa anali kugwilitsidwadi nchito popanga ngalawa m’nthawi za m’Baibo. (2 Tim. 3:16) Kodi anapeza zotani? Akatswili ofukula zinthu zakale, anapeza maumboni ambili oonetsa kuti anthu ku Iguputo anali kuseŵenzetsa gumbwa kupangila ngalawa.
KODI NGALAWA ZAGUMBWA ZINALI KUPANGIDWA MOTANI?
Zogoba zopakidwa utoto zopezeka m’manda a Aiguputo, zionetsa mmene anali kusonkhanitsila gumbwa na kupanga ngalawa. Anthu anali kudula gumbwa n’kupanga mitolo, ndiyeno mitoloyo anali kuimanga pamodzi zolimba. Mapesi a gumbwa ali na makona atatu. Conco akamangidwa pamodzi mothina bwino, mapesiwo amapanga mtolo wolimba kwambili. Malinga na buku lakuti A Companion to Ancient Egypt, ngalawa zopangidwa na gumbwa zinali kukhala zazitali kukwana mamita 17, ndipo mbali iliyonse inali kukwana nkhafi 10 kapena 12.
N’CIFUKWA CIANI OPANGA NGALAWA ANALI KUSEŴENZETSA GUMBWA?
Gumbwa anali kupezeka mosavuta m’mbali mwa mtsinje wa Nile. Kuwonjezela apo, ngalawa zagumbwa zinali zosavuta kupanga. Ngakhale pamene anthu anayamba kuseŵenzetsa kwambili mitengo popanga ngalawa zikulu-zikulu, cioneka kuti asodzi, komanso osaka nyama, anapitiliza kuseŵenzetsa gumbwa popanga ngalawa zing’ono-zing’ono.
Kwa nthawi yaitali, anthu anali kuseŵenzetsa ngalawa zagumbwa. Malinga n’kunena kwa mlembi wina wacigiriki, dzina lake Plutarch, amene anakhalako pakati pa zaka za zana loyamba mpaka laciŵili C.E, ena anali kuseŵenzetsabe ngalawa zagumbwa panthawiyo.
^ ndime 3 Gumbwa amapezeka m’madambo, ndiponso m’maiŵe. Comelaci cikhoza kutalika pafupifupi mamita 5, ndipo tsinde la phesi lake likhoza kukula masentimita pafupi-fupi 15.