MBILI YANGA
“Naphunzila Zambili kwa Ena!”
USIKU wina kuli mdima wandiweyani, ife asilikali a ku France, tinali pa msasa wathu ku mapili m’dziko la Algeria, apo n’kuti nkhondo itafika pacimake mu Algeria. Na mfuti yanga m’manja, n’nali nekha paulonda kumbuyo kwa mulu wa matumba a mcenga. Mwadzidzidzi, n’nangomva tswa! tswa! tswa! mapazi a cina cake cikuyenda. Thupi langa linauma gwa! na mantha. N’nali wamng’ono panthawiyo, ndipo sin’nali kufuna kupha munthu kapena kuphedwa. Conco, n’nafuula kuti: “Mulungu wanga! n’thandizeni!”
Cocitika cocititsa mantha cimeneco cinasintha umoyo wanga, cifukwa cinakhala ciyambi cofuna kudziŵa za Mlengi. Koma n’sanakusimbileni zimene zinacitika pambuyo pake usikuwo, lekani nikufotokozelenkoni zocitika za paubwana wanga, zimene zinasintha maganizo na mtima wanga kuti niyambe kufuna kudziŵa za Mulungu.
ZIMENE N’NAPHUNZILA KWA ATATE NILI MWANA
N’nabadwa mu 1937, ku Guesnain, m’tauni ya migodi kumpoto kwa France. Kucokela kwa atate amene anali kugwila nchito yokumba malasha amiyala, n’naphunzila kufunika kogwila nchito molimbika. N’natengelanso atate pankhani yoonetsetsa kuti cilungamo cikucitika. Ndipo izi zinali kuwalimbikitsa kucita zinthu moimilako anyanchito anzawo amene anali kugwila nchito m’mikhalidwe yovuta kwambili. Poyesetsa kuti zinthu zikhaleko bwino, atate analoŵa m’tumabungwe tomenyela maufulu a ogwila nchito, komanso kumacita nawo masitalaka. Atate analinso wokwiya na cinyengo ca ansembe m’dela lathu. Ambili a iwo anali kukhala umoyo wawofuwofu. Ngakhale n’telo, anali kupempha cakudya na ndalama kwa anthu ogwila nchito pamgodi, amene anali kuvutika kupeza zofunikila pa umoyo. Atate anali kunyansidwa kwambili na makhalidwe a
ansembe cakuti sananiphunzitse zacipembedzo, ndipo sitinali kuyesa n’komwe kukambilana za Mulungu.Pamene n’nali kukula, nanenso n’nayamba kudana nazo zopanda cilungamo. Kupanda cilungamo kumeneko, kunaphatikizapo tsankho limene ena anali kucitila anthu obwela kudzakhala m’dziko la France. N’nali kukonda kuseŵela mpila pamodzi na ana a anthu obwela kudzakhala m’dzikoli. Cina, amayi anali ocokela ku dziko la Poland, osati m’dziko la France. N’nali kufunitsitsa kuti anthu azikhala mwamtendele popanda kusankhana mitundu, komanso kucitilidwa zinthu mofanana na wina aliyense.
N’NAYAMBA KUGANIZILA KWAMBILI ZA UMOYO WANGA
Mu 1957 n’nalembedwa usilikali. Izi n’zimene zinapangitsa kuti nipezeke ku mapili a ku Algeria, usiku uja umene nafotokoza poyamba. Pambuyo pofuula kuti, “Mulungu wanga! n’thandizeni!” n’naona bulu wakuchile, osati msilikali wacidani. Mtima unakhala pansi kuti ziii! Ngakhale n’telo, cocitika cija komanso nkhondo zinanipangitsa kuganizila kwambili tanthauzo la moyo. N’cifukwa ciani tili na moyo? Kodi Mulungu amasamala za ife? Kodi tidzakhalako pa mtendele wokhalitsa?
Patapita nthawi, nili pa chuti kunyumba kwa makolo anga, n’nakumana na Mboni ya Yehova. Ananipatsa Baibo ya ci French yacikatolika yochedwa La Sainte Bible, limene n’nayamba kuliŵelenga n’tabwelela ku Algeria. Mawu amene ananikhudza mtima kwambili ni a pa Chivumbulutso 21:3, 4. Pamati: “Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu. . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” * Mawu amenewa ananidabwitsa. Mu mtima n’nati: ‘Kodi izi zingathekedi?’ Panthawiyo n’nali kudziŵa zocepa kwambili za Mulungu na Baibo.
N’tatsiliza maphunzilo a usilikali mu 1959, n’nakumana na wa Mboni dzina lake François, amene ananiphunzitsa zinthu zambili kucokela m’Baibo. Mwacitsanzo, iye ananionetsa kucokela m’Baibo kuti Mulungu ali na dzina lakuti Yehova. (Sal. 83:18) Ananifotokozelanso kuti Yehova adzabweletsa cilungamo padziko lapansi, adzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso, komanso kuti mawu a pa Chivumbulutso 21:3, 4 adzakwanilitsidwa.
Ziphunzitso zimenezo zinali zomveka bwino ndipo zinanikhudza mtima. Koma nanenso n’nakwiyila kwambili ansembe, ndipo n’nali kufuna kuwadzudzula cifukwa cophunzitsa zinthu zimene si za m’Baibo! Cioneka kuti panthawiyo n’nali kutengelabe maganizo a atate ndipo n’nali wosaleza mtima. N’nali na mtima wofuna kucitapo kanthu nthawi yomweyo!
M’bale François na anzanga ena atsopano a Mboni, ananithandiza kukhala woleza mtima. Iwo anafotokoza kuti nchito yathu monga Akhristu si kuweluza, koma kupeleka ciyembekezo mwa kuwauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Imeneyi ndiyo nchito imene Yesu anagwila komanso imene anapatsa otsatila ake kuti aigwile. (Mat. 24:14; Luka 4:43) N’nafunikanso kuphunzila kukamba na anthu mokoma mtima komanso mosamala, mosayang’ana pa zimene amakhulupilila. Baibo imakamba kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu, koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.”—2 Tim. 2:24.
Miy. 19:14.
N’napanga masinthidwe ofunikila, ndipo n’nabatizika kukhala Mboni ya Yehova mu 1959 pa msonkhano wadela. Kumeneko n’nakumana na mlongo wina wacitsikana dzina lake Angèle amene n’nakopeka naye. N’nayamba kumuyendela mwa kumasonkhanako ku mpingo kwawo, ndipo tinakwatilana mu 1960. Kukamba zoona, ni mkazi wabwino kwambili, ndipo ni mphatso yanga yamtengo wapatali yocokela kwa Yehova.—N’NAPHUNZILA ZAMBILI KWA AMUNA ANZELU ACIYAMBAKALE
Kwa zaka zambili, naphunzila zinthu zofunika kwa abale anzelu aciyambakale. Limodzi mwa maphunzilo ofunika kwambili ni ili: Kuti tikwanitse kucita bwino utumiki wovuta, tiyenela kukhala odzicepetsa na kuseŵenzetsa malangizo anzelu a pa Miyambo 15:22, amene amati: “Aphungu akaculuka [zolingalila] zimakwanilitsidwa.”
Mu 1964 n’nayamba kuona kukwanilitsidwa kwa mawu ouzilidwa amenewa. M’caka cimeneco n’nayamba kutumikila monga woyang’anila dela, kucezela mipingo na kulimbikitsa abale mwauzimu. Komabe, panthawiyo n’nali na zaka 27 ndipo sin’nali kudziŵa zambili. Conco, n’nali kulakwitsa zinthu zina. Koma n’nali kuyesetsa kutengapo phunzilo. Koposa zonse, n’naphunzila zinthu zofunika kwambili kwa “aphungu” oyenelela amenenso ni aciyambakale.
Nikumbukila cocitika cina n’tangokhala woyang’anila dela. N’tapita kukacezela mpingo wina wake ku Paris, m’bale wina wokhwima mwauzimu ananipempha kuti tikambilaneko pang’ono mwamseli. Poyankha n’nati, “Zili bwino.”
M’baleyo ananifunsa kuti, “M’bale Louis, kodi dokotala amathandiza ndani, odwala kapena anthu athanzi?”
Poyankha n’nati, “odwala.”
Iye anati: “Mwayankha bwino. Koma naona kuti mumakonda kuceza kwambili na anthu amene akucita bwino mwauzimu, mwacitsanzo, woyang’anila mpingo. Mumpingo mwathu muli abale na alongo ambili amene ni olefuka, atsopano, kapena amanyazi. Iwo angayamikile kwambili kupatula nthawi yoceza nawo ngakhale kupita kukadya cakudya ku nyumba zawo.”
Uphungu wa m’bale ameneyo unali wothandiza komanso wofunika kwambili. Cikondi cake pa nkhosa za Yehova cinanikhudza mtima kwambili. Conco ngakhale kuti zinali zovuta kuvomeleza kuti sin’nali kucita bwino pa mbali imeneyi, mwamsanga n’nayamba kuseŵenzetsa malangizo amene iye ananipatsa. Niyamikila Yehova pokhala na abale ngati amenewa.
Miyambo 15:22—kufunsila malangizo kwa ena. N’nafunsila malangizo kwa amuna okhwima mwauzimu amene anali kudziŵa bwino nkhani ya zakudya. Ena mwa iwo anali ogulitsa nyama, alimi a ndiwo zamasamba, odziŵa kuphika, komanso odziŵa zogula-gula. Tonse capamodzi tinakwanitsa kugwila nchito yovuta kwambili imeneyo.
Mu 1969 na mu 1973, n’naikidwa kukhala woyang’anila Dipatimenti ya Utumiki wa Cakudya pamisonkhano ya maiko iŵili m’dela la Colombes, mu mzinda wa Paris. Pamsonkhano wa mu 1973, anthu pafupi-fupi 60,000 anafunika kupatsidwa cakudya kwa masiku asanu! Kukamba zoona, n’nali na nkhawa. Apanso, cinsinsi cinagona pa mfundo ya paMu 1973, ine na mkazi wanga anatiitana kukatumikila pa Beteli ku France. Utumiki woyamba umene n’napatsidwa kumeneko unalinso wovuta. N’nafunika kutumiza zofalitsa kwa abale athu ku dziko la Cameroon, ku Africa, kumene nchito yathu inali yoletsedwa kucokela mu 1970 mpaka mu 1993. Apanso n’nakhala na nkhawa kwambili. M’bale wina amene anali kuyang’anila nchitoyo ku France atazindikila zimenezi ananilimbikitsa kuti: “Abale athu ku Cameroon akufunikila kwambili cakudya cauzimu. Tiyeni tiwapatse cakudya!” Ndipo tinawapatsadi.
N’napanga maulendo ambili opita ku maiko ocita malile na dziko la Cameroon kukakumana na akulu ocokela ku dzikolo. Amuna olimba mtima komanso ocenjela amenewo, ananithandiza kupanga makonzedwe ofunikila kuti tizipeleka cakudya cauzimu nthawi zonse ku dziko la Cameroon. Yehova anadalitsa khama lathu. Ndipo kwa zaka ngati 20, anthu ake m’dzikolo sanaphonyepo ngakhale magazini imodzi ya Nsanja ya Mlonda, komanso cofalitsa ca pamwezi cimene panthawiyo cinali kuchedwa Utumiki Wathu wa Ufumu.
N’NAPHUNZILA ZAMBILI KWA MKAZI WANGA WOKONDEKA
Kucokela pamene tinangokhala pa cibwenzi, n’naona makhalidwe auzimu a mlongo Angèle. Makhalidwe amenewo anadzaonekela bwino kwambili
mu umoyo wathu wabanja. Mwacitsanzo, m’madzulo pambuyo pa cikwati cathu, iye ananipempha kuti nipemphele kwa Yehova za cikhumbo cathu cofuna kum’tumikila mokwanila monga banja. Yehova anayankha pemphelo limenelo.Angèle ananithandizanso kudalila kwambili Yehova. Mwacitsanzo, pamene tinapemphedwa kukatumikila pa Beteli mu 1973, n’nazengeleza cifukwa n’nali kukonda kwambili nchito ya m’dela. Koma Angèle ananikumbutsa kuti tinapatulila miyoyo yathu kwa Yehova. Iye ananiuza kuti tiyenela kucita zilizonse zimene gulu lake latipempha kucita. (Aheb. 13:17) Mfundo imeneyi inali yosatsutsika! Conco tinapita ku Beteli. Pa umoyo wathu wonse monga banja, mkazi wanga wathandizila kwambili kulimbitsa cikwati cathu komanso kuti tizipanga zosankha zabwino, cifukwa ni munthu wozindikila, woganiza bwino, ndiponso woona zinthu mwauzimu.
M’zaka zathu zaukalamba, Angèle wapitilizabe kukhala mkazi wabwino kwambili, komanso wonicilikiza. Mwacitsanzo, kuti tikwanitse kuloŵako masukulu a zaumulungu amene ambili amacitika mu Cizungu, ine na Angèle tinayamba kuyesetsa kuphunzila citunduco kuti ticidziŵe bwino. Zimenezo zinaphatikizapo kuyamba kusonkhana ku mpingo wa Cizungu ngakhale kuti panthawiyo tinali m’zaka za m’ma 70. Cifukwa ca maudindo anga ambili monga ciwalo ca Komiti ya Nthambi ya France, kuphunzila citundu cina kunali kovuta. Koma tinali kuthandizana na mkazi wanga. Tsopano tili m’zaka za m’ma 80, ndipo tikupitiliza kukonzekela misonkhano yathu ya mpingo mu Cizungu na mu ci French. Timayesetsanso kutengako mbali mmene tingathele pamisonkhano, komanso mu ulaliki pamodzi na mpingo wathu. Yehova wadalitsa khama lathu kuti tiphunzile Cizungu.
Mu 2017, tinalandila dalitso lina lapadela. Ine na Angèle tinakhala na mwayi woloŵa Sukulu ya Ziwalo za Komiti ya Nthambi na Akazi Awo, imene imacitikila ku Likulu la Maphunzilo la Watchtower ku Patterson, mu mzinda wa New York.
Kukamba zoona, Yehova ni mlangizi wamkulu. (Yes. 30:20) Conco n’zosadabwitsa kuti anthu ake, acikulile na acicepele amalandila maphunzilo abwino koposa! (Deut. 4:5-8) Naona kuti acicepele omvela Yehova, komanso omvela abale na alongo aciyambakale, amapita patsogolo mwauzimu, ndipo amakula bwino. Miyambo 9:9 imatikumbutsa kuti: “Peleka malangizo kwa munthu wanzelu ndipo adzawonjezela nzelu zake. Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiliza kuphunzila.”
Nthawi zina, nimakumbukila tsiku loopsa lija ku mapili a ku Algeria zaka pafupi-fupi 60 zapitazo. Panthawiyo, sin’nali kudziŵa kuti nidzakhala na umoyo wacimwemwe wotele. Naphunzila zambili kwa ena! Kukamba zoona, Yehova wapatsa ine na mkazi wanga, umoyo wabwino kwambili komanso wokhutilitsa. Conco, tatsimikiza mtima kupitilizabe kuphunzila kucokela kwa Atate wathu wakumwamba, ndiponso kwa abale na alongo anzelu aciyambakale ndipo amam’konda.
^ ndime 11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.