Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 19

Olungama Palibe Cowakhumudwitsa

Olungama Palibe Cowakhumudwitsa

“Okonda cilamulo canu amapeza mtendele woculuka, ndipo palibe cowakhumudwitsa.”—SAL. 119:165.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi wolemba wina anakamba ciani? Nanga tikambilane ciani m’nkhani ino?

MASIKU ano, anthu mamiliyoni amakamba kuti amakhulupilila Yesu, koma satsatila zimene iye anaphunzitsa. (2 Tim. 4:3, 4) Ndiye cifukwa cake, wolemba wina anati: “Pakati pathu masiku ano pakanakhala munthu wokamba zinthu mofanana na mmene Yesu anali kukambila . . . , kodi tikanam’kana monga mmene anthu anakanila Yesu zaka 2000 zapitazo? . . . Yankho losapita m’mbali n’lakuti: Inde, tikanam’kana.”

2 Ambili m’zaka za zana loyamba anamva zimene Yesu anali kuphunzitsa, ndipo anaona zozizwitsa zimene anali kucita, koma anakana kum’khulupilila. Cifukwa ciani? M’nkhani yapita tinakambilana zifukwa zinayi zimene zinapangitsa anthu kupunthwa na zimene Yesu anakamba na kucita. Tsopano tiyeni tikambilane zifukwa zina zinayi. Pokambilana, tione cifukwa cake anthu masiku ano amakana otsatila a Yesu, ndiponso tione zimene tingacite kuti tipewe kupunthwa.

(1) YESU ANALIBE TSANKHO

Ambili anapunthwa cifukwa ca anthu amene Yesu anali kuyanjana nawo. Kodi zinthu ngati zimenezi zingapunthwitsenso bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 3) *

3. Kodi Yesu anasankha kucita ciani cimene cinapangitsa kuti ena akhumudwe?

3 Ali padziko lapansi, Yesu anali kuyanjana na anthu a zikhalidwe zonse. Iye anali kudya pamodzi na anthu olemela ndiponso aulamulilo. Koma analinso kuceza kwambili na anthu osauka, komanso opondelezedwa. Kuwonjezela apo, iye anali kucitila cifundo anthu amene anali kuonedwa ngati “ocimwa.” Anthu ena odzilungamitsa anakhumudwa na zimene Yesu anacita. Iwo anafunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ocimwa?” Poyankha funso limeneli Yesu anawauza kuti: “Anthu athanzi safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Ine sindinabwele kudzaitana anthu olungama, koma ocimwa kuti alape.”—Luka 5:29-32.

4. Malinga na ulosi wa Yesaya, kodi Ayuda anayenela kuyembekezela ciani zokhudza Mesiya?

4 Kodi Malemba amati ciani? Kukali zaka Mesiya asanabwele, mneneli Yesaya anafotokoza kuti iye adzakanidwa na anthu a m’dziko. Ulosiwo unati: “Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa . . . Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake. Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.” (Yes. 53:3) Mesiya anali kudzakanidwa na “anthu.” Conco Ayuda a m’nthawi ya atumwi anafunika kuyembekezela kuti Yesu adzakanidwa.

5. Kodi anthu ambili masiku ano amawaona bwanji otsatila a Yesu?

5 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Atsogoleli ambili acipembedzo amakondwela kulandila anthu m’mipingo yawo, omwe ni ochuka, olemela, komanso amene dzikoli limawaona kuti ni anzelu. Iwo amalandila anthu amenewa, ngakhale kuti mamembala atsopanowo ali na umoyo, komanso makhalidwe osagwilizana na mfundo za Mulungu. Atsogoleli acipembedzo amodzi-modziwo, amaona atumiki a Yehova amene ni akhama komanso a makhalidwe abwino kukhala otsika cifukwa si ochuka m’dzikoli. Monga Paulo anakambila, Mulungu anasankha anthu amene amaoneka ngati ‘acabecabe.’ (1 Akor. 1:26-29) Komabe, kwa Yehova, atumiki ake onse okhulupilika ni a mtengo wapatali.

6. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu, malinga na mmene anakambila pa Mateyu 11:25, 26?

6 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? (Ŵelengani Mateyu 11:25, 26.) Musatengele mmene dzikoli limaonela anthu a Mulungu. Dziŵani kuti Yehova amaseŵenzetsa cabe anthu odzicepetsa kucita cifunilo cake. (Sal. 138:6) Ndipo ganizilani kuculuka kwa zinthu zimene wacita mwa kuseŵenzetsa anthu amene dziko limawaona kuti ni opanda nzelu kapena osaphunzila.

(2) YESU ANAVUMBULA ZIPHUNZITSO ZABODZA

7. N’cifukwa ciani Yesu anachula Afarisi kuti onyenga? Nanga kodi iwo anacita ciani?

7 Yesu molimba mtima anadzudzula miyambo yonyenga ya cipembedzo ya m’nthawi yake. Mwacitsanzo, iye anavumbula cinyengo ca Afarisi, amene anali kusamala kwambili za kasambidwe kawo ka m’manja kuposa kusamalila makolo awo. (Mat. 15:1-11) Ophunzila a Yesu ayenela kuti anadabwa na zimene iye anakamba. Ndiye cifukwa cake anamufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?” Yesu anayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinabzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa. Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleli akhungu. Cotelo ngati munthu wakhungu akutsogolela wakhungu mnzake, onse awili adzagwela m’dzenje.” (Mat. 15:12-14) Yesu sanalole maganizo olakwika a atsogoleli acipembedzo kumulepheletsa kulankhula coonadi.

8. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti si ziphunzitso zonse zimene n’zovomelezeka kwa Mulungu?

8 Yesu anavumbulanso ziphunzitso zabodza za cipembedzo. Iye sanakambe kuti ziphunzitso zonse za cipembedzo n’zovomelezeka kwa Mulungu. M’malomwake, anakamba za anthu ambili amene adzakhala pa msewu wotakasuka wopita ku ciwonongeko, pamene ocepa cabe adzakhala pa msewu wopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:13, 14) Anakamba momveka bwino kuti ena adzaoneka monga otumikila Mulungu, koma m’ceni-ceni sam’tumikila. Iye anacenjeza kuti: “Cenjelani ndi aneneli onyenga amene amabwela kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.”—Mat. 7:15-20.

Ambili anapunthwa cifukwa cakuti Yesu anadzudzula ziphunzitso na miyambo yabodza. Kodi zinthu ngati zimenezi zingapunthwitsenso bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 9) *

9. Ni ziphunzitso zina ziti zabodza za cipembedzo zimene Yesu anavumbula?

9 Kodi Malemba amati ciani? Ulosi wa m’Baibo unakambilatu kuti kudzipeleka kwambili pa nyumba ya Yehova kudzamudya Mesiya. (Sal. 69:9; Yoh. 2:14-17) Kudzipeleka kumeneko, kunasonkhezela Yesu kuvumbula miyambo na ziphunzitso zabodza za cipembedzo. Mwacitsanzo, Afarisi anali kukhulupilila kuti moyo sumafa, koma Yesu anaphunzitsa kuti akufa ali m’tulo. (Yoh. 11:11) Asaduki sanali kukhulupilila kuti akufa adzauka. Koma Yesu anaukitsa bwenzi lake Lazaro. (Yoh. 11:43, 44; Mac. 23:8) Afarisi anali kuphunzitsa kuti zonse za kutsogolo kwa munthu zinakonzedwelatu na mphamvu ina yake kapena Mulungu. Koma Yesu anaphunzitsa kuti anthu angasankhe okha kutumikila Mulungu kapena ayi.—Mat. 11:28.

10. N’cifukwa ciani ambili amakhumudwa na ziphunzitso zathu?

10 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Ambili amakhumudwa cifukwa cakuti ziphunzitso zathu za m’Baibo, zimavumbula ziphunzitso zabodza za cipembedzo. Atsogoleli acipembedzo amaphunzitsa nkhosa zawo kuti Mulungu amalanga anthu oipa ku helo. Iwo amaseŵenzetsa ciphunzitso cabodza cimeneci kuti azitha kulamulila anthu awo. Ife atumiki a Yehova, amene timalambila Mulungu wacikondi, timavumbula ciphunzitso cabodza cimeneci. Atsogoleli acipembedzo amaphunzitsanso kuti moyo sumafa. Timavumbula kuti ciphunzitso cimeneci, cinacokela ku cikunja. Ndipo ciphunzitso cimeneci cikanakhala coona kuuka kwa akufa kukanakhala kosafunikila. Ndipo mosiyana na ciphunzitso ca zipembedzo zambili cakuti Mulungu analembelatu za tsogolo lathu, ife timaphunzitsa kuti munthu ali na ufulu ndipo angasankhe kutumikila Mulungu. Kodi atsogoleli acipembedzo amatani tikawavumbula kuti amaphunzitsa zabodza? Nthawi zambili amakwiya ngako!

11. Malinga na mawu a Yesu apa Yohane 8:45-47, kodi Mulungu amafuna kuti anthu ake azicita ciani?

11 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Ngati timakonda coonadi tifunika kumvela na kukhulupilila mawu a Mulungu. (Ŵelengani Yohane 8:45-47.) Mosiyana na Satana Mdyelekezi, ife timaima zolimba m’coonadi. Timapewa kucita ciliconse cosagwilizana na zimene timakhulupilila. (Yoh. 8:44) Mulungu amafuna kuti anthu ake ‘azinyansidwa ndi coipa’, na kugwilitsitsa cabwino,’ monga mmene Yesu anacitila.—Aroma 12:9; Aheb. 1:9.

(3) YESU ANAZUNZIDWA

Ambili anapunthwa cifukwa ca imfa ya Yesu pa mtengo. Kodi zinthu ngati zimenezi zingapunthwitsenso bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 12) *

12. N’cifukwa ciani Ayuda ambili anam’kana Yesu poona mmene anafela?

12 N’ciani cina cinapangitsa Ayuda kum’kana Yesu? Paulo anati: “Ife timalalikila za Khristu amene anapacikidwa. Kwa Ayuda, cimeneci ndi cinthu cokhumudwitsa.” (1 Akor. 1:23) N’cifukwa ciani Ayuda ambili anakhumudwa na mmene Yesu anafela? Kwa iwo, imfa ya Yesu pa mtengo wozunzikilapo inam’pangitsa kuoneka monga munthu wocita zoipa komanso wocimwa, osati Mesiya.—Deut. 21:22, 23.

13. Kodi aja amene anakana Yesu analephela kuzindikila ciani?

13 Ayuda ena amene anam’kana Yesu, analephela kuzindikila kuti iye anali wosalakwa, anaimbidwa mlandu wabodza, ndiponso kuti anacitilidwa zinthu mopanda cilungamo. Amene anali kuweluza mlandu wa Yesu anapotoza cilungamo. Khoti yapamwamba ya Ayuda inangoweluza nkhani ya Yesu mmangu-mmangu, moti sanatsatilenso ndondomeko ya kaweluzidwe ka milandu. (Luka 22:54; Yoh. 18:24) M’malo momvetsela na kupenda maumboni mosakondela pa mlandu wa Yesu, oweluza amene ndiwo “anali kufunafuna umboni wonama kuti amunamizile mlandu Yesu ndi kumupha.” Izi zitalepheleka, mkulu wa ansembe anapangitsa Yesu kukamba zinthu zakuti zim’palamulitse. Kucita izi kunali kosemphana kwambili na malamulo ovomelezeka a kaweluzidwe ka mlandu. (Mat. 26:59; Maliko 14:55-64) Ndipo pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa kwa akufa, oweluza opanda cilungamo amenewo analipila asilikali aciroma amene anali kulondela manda ake “ndalama zasiliva zambili.” Iwo anacita izi kuti afalitse nkhani ya bodza yofotokoza cifukwa cake Yesu munalibe m’manda.—Mat. 28:11-15.

14. Kodi Malemba analosela ciani ponena za imfa ya Mesiya?

14 Kodi Malemba amati ciani? Ngakhale kuti Ayuda ambili m’nthawi ya Yesu sanali kuyembekezela kuti Mesiya adzafunika kufa, onani zimene zinaloseledwa m’Malemba: “Anakhuthula moyo wake mu imfa ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ocimwa. Iye ananyamula chimo la anthu ambili ndipo analowelelapo kuti athandize olakwa.” (Yes. 53:12). Conco, Ayudawo analibe cifukwa cokanila Yesu pamene anaphedwa monga kuti anali wocimwa.

15. Kodi a Mboni za Yehova amaimbidwa milandu yotani imene yapangitsa ena kuwakana?

15 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde! Yesu anazengedwa mlandu na kuweluzidwa mopanda cilungamo, ndipo zopanda cilungamo zimenezi zimacitikilanso Mboni za Yehova. Onani zina mwa zitsanzo. Ku America, m’zaka za m’ma 1930 komanso m’ma 1940 m’makhoti munali milandu yambili yokhudza ufulu wathu wolambila Mulungu. Zinacita kuonekelatu kuti oweluza ena anali kuticitila tsankho. Mu mzinda wa Quebec ku Canada, a cipembedzo na a boma anacita zinthu mogwilizana kwambili potsutsa nchito yathu. Ofalitsa ambili anamangidwa cabe cifukwa couzako ena za Ufumu wa Mulungu. Mu ulamulilo wa Nazi ku Germany abale okhulupilika acinyamata ambili anaphedwa na ulamulilo wosaopa Mulungu umenewo. Ndipo m’zaka zaposacedwapa, ambili mwa abale na alongo ku Russia aimbidwa milandu na kuponyedwa m’ndende cifukwa cokamba za Baibo. A boma la Russia amaona kuti kucita zimenezi n’kukhala na “maganizo komanso makhalidwe opitilila muyeso.” Ngakhale Baibulo la Dziko Latsopano la ci Russia linaletsedwa ndipo akuti lili m’gulu la mabuku okhala na mfundo “zopitilila muyezo” cifukwa limaseŵenzetsa dzina lakuti Yehova.

16. Mogwilizana na 1 Yohane 4:1, n’cifukwa ciani sitiyenela kusoceletsedwa na nkhani zabodza zokhudza anthu a Yehova?

16 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Dziŵani zeni-zeni. Pa ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti ena ‘adzakunamizilani zoipa zilizonse.’ (Mat. 5:11) Satana ndiye gwelo la mabodza amenewa. Iye amasonkhezela otsutsa kufalitsa mabodza okhudza anthu okonda coonadi. (Chiv. 12:9, 10) Tiyenela kukaniza mabodza amene anthu otitsutsa amakamba. Tisalole kuti mabodza otelo atiwopseze kapena kufooketsa cikhulupililo cathu.—Ŵelengani 1 Yohane 4:1.

(4) YESU ANAPELEKEDWA NA KUSIYIDWA

Ambili anapunthwa cifukwa cakuti Yesu anapelekedwa na Yudasi. Kodi zinthu ngati zimenezi zingapunthwitsenso bwanji ena masiku ano? (Onani ndime 17-18) *

17. N’ciani cikanapangitsa ena kukhumudwa Yesu asanamwalile?

17 Atatsala pang’ono kufa, Yesu anapelekedwa na mmodzi wa atumwi ake 12. Mtumwi wina anakana Yesu katatu, ndipo atumwi ake ena anam’siya usiku wakuti aphedwa maŵa. (Mat. 26:14-16, 47, 56, 75) Yesu sanadabwe nazo zimenezo. Iye anacita kukambilatu kuti izi zidzacitika. (Yoh. 6:64; 13:21, 26, 38; 16:32) Poona zimenezi, ena akanapunthwa, n’kumaganiza kuti, ‘Ngati izi n’zimene atumwi a Yesu anacita, sinifuna kukhala m’gulu limenelo!’

18. Ni maulosi ati amene anakwanilitsika Yesu atatsala pang’ono kufa?

18 Kodi Malemba amati ciani? Kukali zaka mahandiledi, Yehova anaonetsa m’Mawu ake kuti Mesiya adzapelekedwa na ndalama 30 zasiliva. (Zek. 11:12, 13) Wom’pelekayo anali kudzakhala mmodzi wa mabwenzi apamtima a Yesu. (Sal. 41:9) Nayenso mneneli Zekariya analemba kuti: “Ipha m’busa ndipo nkhosa zake zibalalike.” (Zek. 13:7) M’malo mopunthwa na zocitika zimenezi, anthu oona mtima anayenela kulimbikitsidwa cifukwa coona kuti maulosi amenewa akukwanilitsidwa pa Yesu.

19. Kodi anthu oona mtima amadziŵa ciani?

19 Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. M’masiku athu ano, Mboni zina zocepa zodziŵika bwino zasiya coonadi, n’kukhala anthu ampatuko. Ndipo zayesa kupatutsa ena pa coonadi. Iwo amafalitsa nkhani zoipa, kupotoza coonadi, na kufalitsa mabodza okhudza Mboni za Yehova kupitila m’manyuzipepala, pa wailesi, pa TV, komanso pa intaneti. Koma anthu oona mtima sapunthwa. M’malomwake, iwo amadziŵa kuti Baibo inakambilatu kuti zotelezi zidzacitika.—Mat. 24:24; 2 Pet. 2:18-22.

20. Tingacite ciani kuti tipewe kupunthwa cifukwa ca aja amene aleka coonadi? (2 Tim. 4:4, 5)

20 Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Tifunika kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuphunzila mawu a Mulungu nthawi zonse, kupitiliza kupemphela, ndiponso kucita zambili m’nchito imene Yehova watipatsa. (Ŵelengani 2 Timoteyo 4:4, 5.) Tikakhala na cikhulupililo, sitidzakhala na nkhawa tikamvela nkhani zoipa zokhudza Mboni za Yehova. (Yes. 28:16) Cikondi cathu pa Yehova, pa Mawu ake, ndiponso pa abale athu cidzatithandiza kupewa kupunthwa cifukwa ca aja amene aleka coonadi

21. Ngakhale kuti unyinji wa anthu masiku ano umakana uthenga wathu, tingakhale wotsimikiza za ciani?

21 M’zaka za zana loyamba, ambili anapunthwa, ndipo anam’kana Yesu. Koma ena ambili anamulandila. Ena mwa iwo anali mmodzi wa oweluza m’Khoti Yapamwamba ya Ayuda, komanso ngakhale “ansembe ambilimbili.” (Mac. 6:7; Mat. 27:57-60; Maliko 15:43) Mofananamo, masiku ano anthu ofika mamiliyoni sanapunthwe. Cifukwa ciani? Cifukwa amadziŵa na kukonda mfundo za coonadi zopezeka m’Malemba. Mawu a Mulungu amakamba kuti: “Okonda cilamulo canu amapeza mtendele woculuka, ndipo palibe cowakhumudwitsa.”—Sal. 119:165.

NYIMBO 124 Tikhale Okhulupilika Nthawi Zonse

^ ndime 5 M’nkhani yapita, tinakambilana zifukwa zinayi zimene anthu anakanila Yesu m’nthawi yakale, na zimene iwo amakanila otsatila ake masiku ano. M’nkhani ino, tikambilananso zifukwa zina zinayi. Tionanso cifukwa cake anthu oona mtima amene amakonda Yehova sapunthwa.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu akudya cakudya pamodzi na Mateyu ndiponso okhometsa msonkho.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu akuthamangitsa amalonda mu kacisi.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yesu akum’nyamulitsa mtengo wozunzikilapo.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Yudasi akupeleka Yesu mwa kum’psompsona.