Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 21

Yehova Adzakupatsani Mphamvu

Yehova Adzakupatsani Mphamvu

“Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.”—2 AKOR. 12:10.

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi Mboni zambili zimakumana na mavuto otani?

MTUMWI Paulo analimbikitsa Timoteyo kuphatikizapo ngakhale ife Akhristu tonse kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wathu. (2 Tim. 4:5) Tonsefe timayesetsa kutsatila malangizo a Paulo amenewa. Ngakhale n’telo, timakumana na zopinga. Abale na alongo ambili amafunika kucita kulimba mtima kuti agwile nchito yolalikila. (2 Tim. 4:2) Mwacitsanzo, ganizilani za abale amene amakhala m’maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa. Amalalikilabe ngakhale amadziŵa kuti angaponyedwe m’ndende!

2 Anthu a Yehova amakumana na mavuto ambili amene angawalefule. Mwacitsanzo, ambili amafunika kuseŵenza kwa maola ambili, cabe kuti apeze zofunikila za banja lawo. Amafuna kucita zambili mu ulaliki, koma amakhala olema podzafika kumapeto kwa mlungu. Ena amacita zocepa kwambili mu utumiki wawo cifukwa ali na matenda okhalitsa kapena ni okalamba. Iwo mwina angakhale kuti sacoka panyumba. Ndipo ena amavutika kwambili na maganizo odziona kuti ni osafunika. Mlongo Mary, * amene amakhala ku Middle East, anakamba kuti: “Nimacita kulimbikila kwambili kuti nicotse maganizo olefula cifukwa amanipangitsa kukhala wofooka kwambili. Pambuyo pake nimadziimba mlandu cifukwa zimanilanda nthawi na mphamvu zimene nikanaseŵenzetsa mu ulaliki.”

3. Kodi tikambilane ciani m’nkhani ino?

3 Mosasamala kanthu za mavuto amene tili nawo, Yehova angatipatse mphamvu zotithandiza kupilila mavuto athu na kupitiliza kum’tumikila malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wathu. Tisanayambe kukambilana mmene Yehova angatithandizile, tiyeni tione mmene iye analimbikitsila Paulo na Timoteyo kuti akwanilitse utumiki wawo mosasamala kanthu za mavuto amene anali kukumana nawo.

YEHOVA AMATIPATSA MPHAMVU KUTI TIKWANITSE KUGWILA NCHITO YOLALIKILA

4 Paulo anakumana na mavuto ambili. Iye anafunikila mphamvu maka-maka pamene anali kumenyedwa, kuponyedwa miyala, na kuikidwa m’ndende. (2 Akor. 11:23-25) Paulo anafotokoza poyela kuti nthawi zina anali kuvutika na maganizo olefula. (Aroma 7:18, 19, 24) Anapililanso vuto lina lokhudza thanzi limene linali monga “munga m’thupi,” ndipo anali wofunitsitsa kuti Mulungu amucotsele mungawo.—2 Akor. 12:7, 8.

N’ciani cinathandiza Paulo kukwanitsa kucita utumiki wake? (Onani ndime 5-6) *

5. Kodi Paulo anakwanitsa kucita ciani ngakhale kuti anali kukumana na mavuto?

5 Yehova anam’patsa mphamvu Paulo kuti apitilize kucita utumiki wake mosasamala kanthu za mavuto amene anakumana nawo. Ganizilani zimene Paulo anakwanitsa kucita. Mwacitsanzo, pamene anali m’ndende ya panyumba ku Roma, iye analalikila uthenga wabwino mokangalika kwa atsogoleli aciyuda komanso mwina kwa akulu-akulu a boma. (Mac. 28:17; Afil. 4:21, 22) Analalikilanso asilikali oteteza mfumu, na kucitila umboni kwa onse amene anali kubwela kudzamuona. (Mac. 28:30, 31; Afil. 1:13) Panthawi imodzimodziyo, Paulo analemba makalata ouzilidwa amene amapindulitsa Akhristu oona masiku ano. Kuwonjezela apo, citsanzo ca Paulo cinalimbikitsa mpingo wa ku Roma, ndipo cotulukapo cake cinali cakuti abale ake anaonetsa “kulimba mtima kowonjezeleka polankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.” (Afil. 1:14) Ngakhale kuti nthawi zina Paulo anali kulephela kucita zinthu zimene anali kufuna, iye anali kucita zimene angathe malinga na mmene mikhalidwe inalili. Ndipo izi zinathandiza “kupititsa patsogolo uthenga wabwino m’malo moulepheletsa.”—Afil. 1:12.

6. Malinga na 2 Akorinto 12:9, 10, n’ciani cinathandiza Paulo kukwanilitsa utumiki wake?

6 Paulo anazindikila kuti zonse zimene anacita potumikila Yehova zinatheka cifukwa ca mphamvu za Mulungu osati zake. Iye anadziŵa kuti mphamvu za Mulungu zinali ‘zokwanila pamene anali wofooka.’ (Ŵelengani 2 Akorinto 12:9, 10.) Kupitila mwa mzimu wake woyela, Yehova anapatsa Paulo mphamvu zomuthandiza kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wake, mosasamala kanthu za cizunzo, kuponyedwa m’ndende, komanso mavuto ena amene anakumana nawo.

N’ciani cinathandiza Timoteyo kukwanitsa kucita utumiki wake? (Onani ndime 7) *

7. Kodi Timoteyo anagonjetsa zopinga zotani kuti akwanitse kucita utumiki wake?

7 Timoteyo, mnzake wacicepele wa Paulo, nayenso anayenela kudalila mphamvu za Mulungu kuti akwanitse kucita utumiki wake. Iye anali kuyenda na Paulo pa maulendo atali-atali aumishonale. Kuwonjezela apo, Paulo analinso kutuma Timoteyo kukacezela mipingo na kuilimbikitsa. (1 Akor. 4:17) N’kutheka kuti Timoteyo anali kudzidelela. Mwina ndiye cifukwa cake Paulo anamulimbikitsa kuti: “Usalole kuti munthu aliyense akudelele poona kuti ndiwe wamng’ono.” (1 Tim. 4:12) Ndipo panthawiyo, Timoteyo anali na munga wake m’thupi—“kudwaladwala” (1 Tim. 5:23) Koma iye anadziŵa kuti mzimu wamphamvu woyela wa Yehova, udzamupatsa mphamvu zofunikila kuti alalikile uthenga wabwino komanso kuti atumikile abale ake.—2 Tim. 1:7.

TIMAPATSIDWA MPHAMVU KUTI TIKHALEBE OKHULUPILIKA PA MAVUTO

8 Masiku ano, Yehova amapatsa anthu ake “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti apitilize kum’tumikila mokhulupilika. (2 Akor. 4:7) Tiyeni tikambilane zinthu zinayi zimene Yehova watipatsa zomwe zingatilimbikitse na kutithandiza kukhalabe okhulupilika kwa iye: pemphelo, Baibo, mayanjano acikhristu, na utumiki wathu.

Yehova amatilimbikitsa kupitila m’pemphelo (Onani ndime 9)

9. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji?

9 Pemphelo limatilimbikitsa. Malinga na Aefeso 6:18, Paulo akutilangiza kuti tizipemphela kwa Mulungu “pa cocitika ciliconse.” Ndipo Mulungu adzatilimbikitsadi. M’bale Jonnie wa ku Bolivia analimbikitsidwa mwa njila imeneyi pamene anakumana na mavuto motsatizana-tsatizana. Mkazi wake na makolo ake onse aŵili anadwala kwambili panthawi imodzi. M’bale Jonnie anavutika kwambili kupeza zofunikila powasamalila onse atatu. Amayi ake anamwalila, ndipo panapita nthawi yaitali kuti mkazi wake na atate ake acile. Pofotokoza za nthawi yovuta imeneyo, m’bale Jonnie anakamba kuti, “Nikakhala wopanikizika maganizo kwambili, nthawi zonse cimene cinali kunithandiza ni kuchula zinthu mwacindunji m’pemphelo.” Yehova anapatsa m’bale Jonnie mphamvu zofunikila kuti apilile. M’bale Ronald, amene ni mkulu ku Bolivia anauzidwa kuti amayi ake ali na khansa. Iwo anamwalila pambuyo pa mwezi umodzi. N’ciani cinamuthandiza kupilila? Iye ananena kuti: “Kupemphela kwa Yehova kumanithandiza kumuuza zonse za kumtima kwanga na mmene nimvelela. Nidziŵa kuti amanimvetsa kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale ine amene.” Nthawi zina tingaone kuti mavuto atikulila msinkhu kapena sitingadziŵe zofunikila kuchula m’pemphelo. Koma Yehova amatipempha kuti tizipemphela kwa iye ngakhale pamene zativuta kufotokoza bwino-bwino mmene tikumvelela.—Aroma 8:26, 27.

Yehova amatilimbikitsa kupitila m’Baibo (Onani ndime 10)

10. Malinga na Aheberi 4:12, n’cifukwa ciani kuŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha pa zimene taŵelenga n’kofunika kwambili?

10 Baibo imatilimbikitsa. Paulo anali kudalila pa Malemba kuti amupatse mphamvu na citonthozo. Nafenso tingawadalile. (Aroma 15:4) Pamene tiŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, Yehova mwa mzimu wake, angatithandize kumvetsa bwino mmene Malemba angatithandizile. (Ŵelengani Aheberi 4:12.) M’bale Ronald amene tamuchula kumayambililo anati: “Niyamikila kuti n’nakulitsa cizoloŵezi coŵelenga Baibo usiku uliwonse. Nimasinkha-sinkha kwambili pa makhalidwe a Yehova na mmene amacitila zinthu mwacikondi na atumiki ake. Izi zimanithandiza kupezanso mphamvu.”

11. Kodi Baibo inamulimbikitsa bwanji mlongo wofeledwa?

11 Kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu kudzatithandiza kukhala na kapenyedwe koyenela malinga na mmene zinthu zili pa umoyo wathu. Ganizilani mmene Baibo inathandizila mkazi wamasiye wacisoni. M’bale wina amene ni mkulu anamulimbikitsa kuŵelenga buku la Yobu kuti apeze mfundo zothandiza. Ataŵelenga bukulo, poyamba anafulumila kuweluza Yobu cifukwa cokhala na maganizo olakwika. M’maganizo mwake anati: “Iwe Yobu! Usamangoganizila za mavuto ako cabe!” Koma kenako, anazindikila kuti iyenso maganizo ake anali ofanana kwambili ndi a Yobu. Izi zinamuthandiza kusintha kaganizidwe kake, ndipo anatha kupilila cisoni cotayikilidwa mwamuna wake.

Yehova amatilimbikitsa kupitila m’mayanjano acikhristu (Onani ndime 12)

12. Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji kupitila mwa alambili anzathu?

12 Mayanjano acikhristu amatilimbikitsa. Njila ina imene Yehova amalimbikitsila Akhristu ni kupitila mwa alambili anzawo. Paulo analemba kuti anali kulakalaka ‘kukalimbikitsana’ na abale na alongo ake auzimu. (Aroma 1:11, 12) Mlongo Mary amene tamuchula kumayambililo, amakondwela kukhala na mayanjano amenewa. Iye anati: “Yehova waseŵenzetsapo abale na alongo amene sanali kudziŵa ngakhale mavuto amene n’nali kukumana nawo. Iwo anali kukamba mawu olimbikitsa kapena kunitumizila khadi. N’zimene ine n’nali kufunikila. Zanithandizanso kukhala womasuka pofotokoza mavuto anga kwa alongo ena amene anakumanapo na mavuto monga anga. Ndipo nimaphunzilapo kanthu na mmene iwo anacitila. Nthawi zonse akulu amanithandiza kumva kuti ndine wofunika mu mpingo.”

13. Kodi tingalimbikitsane bwanji ku misonkhano ya mpingo?

13 Malo abwino kwambili olimbikitsilana ni ku misonkhano ya mpingo. Mukakhala kumisonkhano, bwanji osayamba ndinu kulimbikitsa ena mwa kukamba mawu acikondi ocokela pansi pa mtima, komanso oonetsa kuyamikila? Mwacitsanzo, misonkhano isanayambe mkulu wina dzina lake Peter, anauza mlongo amene mwamuna wake ni wosakhulupilila kuti: “N’zolimbikitsa kwambili kukuonani kuti mwabwela ku misonkhano. Nthawi zonse mumakonzekeletsa ana anu onse 6 kupelekapo ndemanga.” Maso a mlongoyo anadzala na misozi yoyamikila pamene anayankha kuti: “Ndipo nakondwela ngako kumva mawu olimbikitsa amenewo!”

Yehova amatilimbikitsa kupitila mu ulaliki (Onani ndime 14)

14. Kodi kugwila nchito yolalikila kumatithandiza motani?

14 Ulaliki umatilimbikitsa. Tikamauzako ena mfundo za coonadi ca m’Baibo, timatsitsimulidwa na kupezanso mphamvu kaya anthu amvele uthenga wathu kapena ayi. (Miy. 11:25) Mlongo wina dzina lake Stacy anadzionela yekha kuti ulaliki umakhaladi wolimbikitsa. Wa m’banja lawo atacotsedwa, iye anamva cisoni kwambili n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi pali zina zimene nikanacita kuti nithandize?’ Cinali covuta kwa mlongo Stacy kucotsa maganizo ake pa nkhani imeneyi. Kodi n’ciani cinam’thandiza pa vuto limeneli? Ulaliki! Pamene anali kugwila nchito yolalikila, iye anayamba kusumika maganizo ake pa anthu ofunikila thandizo m’gawo lake. Mlongo Stacy anati: “Pa nthawi imeneyo, Yehova ananipatsa phunzilo la Baibo limene linapita patsogolo mwamsanga. Zimenezo zinanilimbikitsa kwambili. Cimene canithandiza kwambili mu umoyo wanga ni kugwila nchito yolalikila.”

15. Tiphunzilapo ciani pa zimene anakamba mlongo Mary?

15 Cifukwa ca mmene zinthu zilili pa umoyo wawo, ena angaone kuti sangakwanitse kucita zambili mu ulaliki. Ngati umu ni mmene mumamvelela, musaiŵale kuti Yehova amakondwela na zimene mumakwanitsa kucita. Ganizilaninso citsanzo ca mlongo Mary. Atasamukila ku dela la citundu cina, iye anali kuona kuti anali kucita zocepa kwambili. Iye anakamba kuti, “Kwa kanthawi, n’nali kukwanitsa cabe kupeleka ndemanga yacidule, kuŵelengako Baibo, kapena kungogaŵila kathilakiti mu ulaliki.” Cifukwa ca izi, anali kuona kuti sakucita bwino podziyelekezela na ena amene anali kukamba bwino citunduco. Komabe, anasintha kaganizidwe kake. Anayamba kukumbukila kuti Yehova angamuseŵenzetse mosasamala kanthu kuti sadziŵa kukamba bwino citunduco. Mlongo Mary anakamba kuti, “Mfundo za coonadi zopulumutsa miyoyo n’zosavuta kumva, ndipo ndizo zimasintha munthu.”

16. N’ciani cingathandize aja amene sakutha kucoka panyumba kupeza mphamvu?

16 Yehova amaona, ndipo amayamikila cikhumbo cathu cofuna kugwila nchito yolalikila, ngakhale pamene sitikutha kucoka panyumba. Iye angatitsegulile mipata yolalikila kwa obwela kudzatisamalila, madokotala, kapena manesi. Ngati tiyelekezela zimene timacita palipano na zimene tinali kucita kale, tingalefuke. Koma ngati tiona mmene Yehova akutithandizila palipano, tidzapeza mphamvu zotithandiza kupilila mayeso alionse mwacimwemwe.

17. Malinga na Mlaliki 11:6, n’cifukwa ciani tiyenela kupitiliza kulalikila ngakhale kuti sitiona zotulukapo zake pa nthawiyo?

17 Pa mbewu za coonadi zimene timabyala, sitidziŵa kuti n’ziti zimene zingamele na kukula. (Ŵelengani Mlaliki 11:6.) Mwacitsanzo, mlongo Barbara amene ali m’zaka za m’ma 80, nthawi zambili amacita ulaliki wa pafoni na wa makalata. Mu imodzi ya makalata ake, anaikamo Nsanja ya Mlonda ya March 1, 2014, ya mutu wakuti “Zimene Mulungu Wakucitilani.” Iye sanadziŵe kuti anatumiza kalatayo kwa okwatilana amene sanalinso Mboni za Yehova. Iwo anaŵelenga magaziniyo mobweleza-bweleza. Mwamuna anamvela monga kuti Yehova anali kukamba naye mwacindunji. Banjalo linayamba kupezeka ku misonkhano. Ndipo patapita zaka pafupifupi 27, iwo anakhalanso Mboni. Ganizilani cabe mmene mlongo Barbara analimbikitsidwila ataona zotulukapo zabwino pa kalata imodzi cabe!

Yehova amatilimbikitsa kupitila mu (1) pemphelo, (2) Baibo, (3) mayanjano acikhristu, komanso (4) ulaliki (Onani ndime 9-10, 12, 14)

18. Kodi tingacite ciani kuti tipindule na mphamvu za Mulungu?

18 Yehova amatipatsa mwayi waukulu wolandila mphamvu zake zoculuka. Tikamaseŵenzetsa zimene watipatsa monga pemphelo, Baibo, mayanjano acikhristu na ulaliki, timaonetsa kuti timakhulupilila m’mphamvu za Yehova zotithandiza, na kuti iye ni wofunitsitsadi kutelo. Tiyeni nthawi zonse tipitilize kudalila Atate wathu wakumwamba, amene amakondwela ‘kuonetsa mphamvu zake kwa anthu “amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.’—2 Mbiri 16:9.

NYIMBO 61 Patsogolo! Inu Mboni Zake

^ ndime 5 Tikukhala m’nthawi zovuta, koma Yehova amatipatsa thandizo lofunikila kuti tipilile. M’nkhani ino, tidzaona mmene Yehova anathandizila mtumwi Paulo na Timoteyo kupitiliza kum’tumikila ngakhale kuti anali kukumana na mavuto. Tidzakambilana zinthu zinayi zimene Yehova watipatsa pofuna kutithandiza kupilila masiku ano.

^ ndime 2 Dzina lasinthidwa.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene ali m’ndende paukaidi wosacoka panyumba ku Roma, Paulo akulemba makalata ku mipingo ingapo na kulalikila uthenga wabwino kwa anthu obwela kudzamuona.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Timoteyo akulimbikitsa abale pamene akucezela mipingo.