Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 20

Buku la Chivumbulutso—Cimene Cidzacitikila Adani a Mulungu

Buku la Chivumbulutso—Cimene Cidzacitikila Adani a Mulungu

“Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Ciheberi amachedwa Haramagedo.”—CHIV. 16:16.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Malinga na buku la Chivumbulutso, kodi Satana akucita ciyani kwa anthu a Mulungu?

 BUKU la Chivumbulutso limaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba, komanso kuti Satana anaponyedwa padziko lapansi. (Chiv. 12:1-9) Izi zitacitika, kumwamba kunakhala mtendele. Koma Satana anabweletsa mavuto aakulu pa ife. Cifukwa ciyani? Cifukwa ni wokwiya na anthu amene amatumikila Yehova mokhulupilika pano padziko lapansi, ndipo amawaukila.—Chiv. 12:12, 15, 17.

2. N’ciyani cingatithandize kukhalabe osasunthika?

2 N’ciyani cingatithandize kukhalabe osasunthika Satana akamatiukila? (Chiv. 13:10) Cingatithandize ni kudziŵa zimene zidzacitika m’tsogolomu. Mwacitsanzo, m’buku la Chivumbulutso, mtumwi Yohane anafotokoza ena mwa madalitso amene tidzalandila posacedwa. Limodzi mwa madalitsowo n’lakuti adani onse a Mulungu adzawonongedwa. Tiyeni tsopano tikambilane zimene buku la Chivumbulutso limanena zokhudza adani amenewa, na zimene zidzawacitikile.

ADANI A MULUNGU AMAFOTOKOZEDWA “MWA ZIZINDIKILO”

3. Ni zizindikilo zina ziti zochulidwa m’buku la Chivumbulutso?

3 Vesi loyamba la Chivumbulutso, limatiuza kuti zimene tiŵelenge m’bukuli zafotokozedwa “mwa zizindikilo,” kutanthauza m’mawu ophiphilitsa. (Chiv. 1:1) Conco, adani a Mulungu amafotokozedwa mophiphilitsa. M’bukuli timaŵelenga za zilombo zingapo. Mwacitsanzo, pali “cilombo [cimene] cikutuluka m’nyanja.” Cili na “nyanga 10 ndi mitu 7.” (Chiv. 13:1) Pambuyo pake, “cilombo cina cikutuluka pansi pa dziko lapansi.” Cilomboci cimalankhula ngati cinjoka, ndipo cimapangitsa “moto kugwela padziko lapansi kucokela kumwamba.” (Chiv. 13:11-13) Kenako, tikuonanso cilombo cina cosiyana, cimene ni “cofiila kwambili.” Pa cilomboci pakwela hule. Zilombo zolusa zitatu zimenezi ziimila adani a Yehova Mulungu, amenenso akhala akutsutsa Ufumu wake kwa zaka zambili-mbili. Motelo, m’pofunikila kwambili kuti tiwadziŵe adaniwo.—Chiv. 17:1, 3.

ZILOMBO ZINAYI ZIKULU-ZIKULU

Zikutuluka “m’nyanja.”(Dan. 7:1-8, 15-17) Zilombozi ziimila maulamulilo amphamvu padziko lapansi, amene zocita zawo zakhala zikukhudza mwapadela anthu a Mulungu kuyambila m’nthawi ya Danieli. (Onani ndime 4, 7)

4-5. Kodi lemba la Danieli 7:15-17, limatithandiza bwanji kudziŵa tanthauzo la zizindikilo za m’buku la Chivumbulutso?

4 Kuti tiwadziŵe adani amenewo, coyamba tiyenela kudziŵa zimene zilombo zolusa komanso hule zimaimila. Baibo ndiyo yokha ingatithandize kudziŵa zimene zimaimila. Zizindikilo zambili zochulidwa m’buku la Chivumbulutso zinafotokozedwapo kale m’mabuku ena a m’Baibo. Mwacitsanzo, mneneli Danieli analota maloto. M’malotowo, anaona ‘zilombo zinayi zikulu-zikulu zikutuluka m’nyanja.’ (Dan. 7:1-3) Iye anafotokoza kuti zilombo zinayi zikulu-zikulu zimenezi ziimila “mafumu” anayi, kapena kuti maboma. (Ŵelengani Danieli 7:15-17.) Kufotokoza momveka bwino kumeneku kutithandiza kudziŵa kuti zilombo zochulidwa m’Chivumbulutso ziyenela kuti ziimilanso maulamulilo andale.

5 Lomba, tiyeni tikambilane zina mwa zizindikilo zochulidwa m’buku la Chivumbulutso. Pokambilana, tione mmene Baibo itithandizile kudziŵa tanthauzo la zizindikilo zimenezo. Tiyamba mwa kukambilana zilombo zolusa zimene zikuonekela motsatizana. Coyamba, tiona zimene zilombozo zimaimila. Kenaka, tione zimene zidzacitikila zilombozo. Ndipo cothela, tikambilane mmene zocitikazo zimatikhudzila.

ADANI A MULUNGU ADZIŴIKA

CILOMBO CA MITU 7

Cikutuluka “m’nyanja” ndipo cili na mitu 7, nyanga 10, komanso zisoti 10 zacifumu. (Chiv. 13:1-4) Cikuimila maulamulilo onse andale amene akhala akulamulila anthu mpaka pano. Mitu 7 iimila maulamulilo 7 amphamvu padziko lonse amene mwapadela akhala akutsutsa anthu a Mulungu. (Onani ndime 6-8)

6. Kodi cilombo ca mitu 7 cochulidwa pa Chivumbulutso 13:1-4 ciimila ciyani?

6 Kodi cilombo ca mitu 7 ciimila ciyani? (Ŵelengani Chivumbulutso 13:1-4.) Tikuona kuti cilombo cimeneci cili na maonekedwe a kambuku, koma mapazi a cimbalangondo, pakamwa pa mkango, ndipo cili na nyanga 10. Amenewa ndiwonso maonekedwe a zilombo zinayi zochulidwa m’buku la Danieli caputala 7. Koma cilombo ca m’buku la Chivumbulutso cili na maonekedwe onse a zilombo zinayi za m’buku la Danieli. Cilombo cimeneci siciimila boma limodzi, kapena ufumu wa padziko lonse. Cimachulidwa kuti cili na ulamulilo “pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, cinenelo ciliconse ndi dziko lililonse.” Conco, ciyenela kuti cili na ulamulilo waukulu kuposa boma lililonse palokha. (Chiv. 13:7) Cilombo cimeneci ciyenela kuti cikuimila maboma onse amphamvu amene akhala akulamulila anthu kuyambila kale-kale. *Mlal. 8:9.

7. Kodi mutu uliwonse wa cilombo ca mitu 7 uimila ciyani?

7 Kodi mutu uliwonse wa cilombo ca mitu 7 uimila ciyani? Chivumbulutso caputala 17 imatithandiza kupeza yankho, cifukwa imafotokoza cifanizilo ca cilombo cochulidwa pa Chivumbulutso caputala 13. Pa Chivumbulutso 17:10 pamati: “Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kocepa.” Pa maboma onse amene Satana wakhala akuseŵenzetsa, maboma 7 okha ndiwo anali ngati “mitu” ya cilombo cifukwa anali amphamvu kwambili. Awa ni maulamulilo amphamvu padziko lonse amene akhala akuvutitsa kwambili anthu a Mulungu. Podzafika m’nthawi ya mtumwi Yohane, maboma asanu anali atalamulila kale. Mabomawo ni Iguputo, Asiriya, Babulo, Mediya na Perisiya, komanso Girisi. Ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa nambala 6 wa Roma, unali ukali kulamulilabe Yohane atalandila vumbulutso. Nanga ni boma liti limene linakhala ulamulilo wamphamvu wa padziko lonse wa nambala 7 komanso wothela?

8. Kodi mutu wa nambala 7 wa cilombo uimila ciyani?

8 Monga tionele, maulosi a m’buku la Danieli amatithandiza kudziŵa zimene mutu wa cilombo wa nambala 7 komanso wothela umaimila. Ni ulamulilo uti wamphamvu wa padziko lonse umene wakhala ukulamulila m’nthawi ino ya mapeto, kapena kuti “m’tsiku la Ambuye”? (Chiv. 1:10) Ni mgwilizano wa dziko la United Kingdom komanso America, kapena kuti ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America. Conco, tingati ndiwo mutu wa nambala 7 wa cilombo colusa cochulidwa pa Chivumbulutso 13:1-4.

CILOMBO CA NYANGA ZIŴILI NGATI MWANA WA NKHOSA

Cikutuluka “pansi pa dziko lapansi” ndipo cimalankhula “ngati cinjoka.” Cilomboci cimapangitsa “moto kugwela padziko lapansi kucokela kumwamba,” komanso cimacita zizindikilo ngati “mneneli wonyenga.” (Chiv. 13:11-15; 16:13; 19:20) Pokhala cilombo ca nyanga ziŵili komanso mneneli wonyenga, ulamulilo wa Britain na America umasoceletsa anthu na kuwauza “kupanga cifanizilo” ca “cilombo” ca mitu 7 na nyanga 10. (Onani ndime 9)

9. Kodi cilombo ca “nyanga ziŵili ngati mwana wa nkhosa” ciimila ciyani?

9 Chivumbulutso caputala 13 imatiuzanso kuti mutu wa nambala 7 umenewu, kutanthauza ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America, ndiwo umaimilidwanso na cilombo ca “nyanga ziŵili ngati mwana wa nkhosa, koma cinayamba kulankhula ngati cinjoka.” Cilombo cimeneci ‘cimacitanso zizindikilo zazikulu, moti cimapangitsa ngakhale moto kugwela padziko lapansi kucokela kumwamba anthu akuona.’ (Chiv. 13:11-15) Macaputala 16 na 19 a Chivumbulutso amafotokoza kuti cilomboci ni “mneneli wonyenga.” (Chiv. 16:13; 19:20) Nayenso Danieli anachula zofanana na zimenezi, pamene anati ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America ‘udzawononga zinthu zambili.’ (Dan. 8:19, 23, 24) Izi n’zimene zinacitika pa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Akatswili a sayansi a ku Britain na America, anagwilizana popanga mabomba aŵili amene anaphulitsidwa ku Japan kuti athetse nkhondoyo. Mwa kutelo, ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America, unapangitsa “moto kugwela padziko lapansi kucokela kumwamba.”

CILOMBO COFIILA KWAMBILI

Wokwela pa cilomboci ni hule, limene ni Babulo Wamkulu. Cilomboci cikufotokozedwa kuti ni mfumu ya nambala 8. (Chiv. 17:3-6, 8, 11) Poyamba, hule limenelo likulamulila cilomboco, koma pambuyo pake cikumuwononga. Hulelo liimila ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. Cilombo ciimila bungwe la United Nations, limene limacilikiza ndale padziko lonse. (Onani ndime 10, 14-17)

10. Kodi “cifanizilo ca cilombo” ciimila ciyani? (Chivumbulutso 13:14, 15; 17:3, 8, 11)

10 Cotsatila, tikuonanso cilombo cina. Maonekedwe a cilomboci alinganako na cilombo ca mitu 7 cija, kungoti n’cofiila kwambili. Cimachedwa kuti “cifanizilo ca cilombo” ndipo cimafotokozedwa kuti ni “mfumu ya 8.” * (Ŵelengani Chivumbulutso 13:14, 15; 17:3, 8, 11.) “Mfumu” imeneyi imanenedwa kuti inalipo ndiyeno n’kuzimililika, kenako n’kudzaonekelanso. Izi n’zimene zinacitika ndendende na bungwe la United Nations, limene limacilikiza ndale padziko lonse lapansi. Poyamba, linali kuchedwa bungwe la League of Nations. Koma bungweli linazimililika pa Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Kenako, linadzaonekelanso na dzina lina lakuti United Nations.

11. Kodi zilombo zandale zimatuntha anthu kucita ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani sitiyenela kuziopa?

11 Kupitila m’mauthenga awo abodza, zilombo zandale kapena kuti maboma, zimatuntha anthu kutsutsa Yehova na anthu ake. Mophiphilitsa, iwo amasonkhanitsila “mafumu a dziko lonse lapansi” ku nkhondo ya Aramagedo, imene ni “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chiv. 16:13, 14, 16) Koma sitiyenela kuopa cifukwa Mulungu wathu wamkulu Yehova, adzacitapo kanthu mwamsanga kuti apulumutse amene amacilikiza ulamulilo wake.—Ezek. 38:21-23.

12. N’ciyani cidzacitikila zilombo zonse?

12 N’ciyani cidzacitikila zilombo zonse? Chivumbulutso 19:20 imayankha kuti: “Cilomboco cinagwidwa limodzi ndi mneneli wonyenga uja, amene anacita zizindikilo pamaso pa cilomboco. Zizindikilo zimenezi anasoceletsa nazo olandila cizindikilo ca cilombo ndi olambila cifanizilo cake. Adakali amoyo, onse aŵili anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.” Conco, pamene mabomawa akulamulilabe, Mulungu adzawaononga kwamuyaya.

13. Kodi Akhristu amakumana na vuto lotani kucokela ku maboma a dzikoli?

13 Kodi izi zitanthauza ciyani kwa ife? Pokhala Akhristu, tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa Mulungu na Ufumu wake. (Yoh. 18:36) Kuti ticite zimenezi, tiyenela kusakhalila mbali m’ndale za dzikoli. Komabe, kusakhalila mbali kumeneku kungakhale kovuta kwambili cifukwa maboma a dzikoli, amatikakamiza kuti tiziwacilikiza m’mawu komanso m’zocita. Aja amene amagonja ku cikakamizo cawo amalandila cizindikilo ca cilombo. (Chiv. 13:16, 17) Ndipo aliyense amene walandilako cizindikiloco, amataya ciyanjo ca Yehova, komanso sadzapeza moyo wosatha. (Chiv. 14:9, 10; 20:4) Conco, n’kofunika kwambili kuti aliyense wa ife azipewa zandale, olo am’kakamize motani.

MAPETO OCITITSA MANYAZI A HULE LALIKULU

14. Kodi mtumwi Yohane anaona cinthu codabwitsa citi malinga na Chivumbulutso 17:3-5?

14 Mtumwi Yohane anati ‘anadabwa kwambili’ na cina cake cimene anaona. Kodi anaona ciyani? Anaona mkazi atakwela pa cimodzi mwa zilombo zoopsa zija. (Chiv. 17:1, 2, 6) Mkaziyo amamuonetsa kuti ni “hule lalikulu,” ndipo amachedwa “Babulo Wamkulu.” Iye amacita “dama” na “mafumu a dziko lapansi.”—Ŵelengani Chivumbulutso 17:3-5.

15-16. Kodi “Babulo Wamkulu” ndani? Nanga tidziŵa bwanji?

15 Kodi “Babulo Wamkulu” ndani? Mkaziyu saimila mabungwe andale cifukwa amanenedwa kuti amacita ciwelewele na atsogoleli andale. (Chiv. 18:9) Ndipo iye amayesetsa kutsogolela olamulila amenewa, pokwela pa msana pawo mophiphilitsa. Komanso, mkaziyu saimila mabungwe amalonda adyela a dziko ili la Satana. M’mavesi ena m’buku la Chivumbulutso, mabungwewo amachedwa “amalonda oyenda-yenda a padziko lapansi.”—Chiv. 18:11, 15, 16.

16 M’Baibo, mawu akuti “hule” angatanthauze anthu amene amati amatumikila Mulungu, koma amacita zinthu zokhudza kupembedza mafano, kapena kupalana ubwenzi na dziko. (Ezek. 16:2, 35, 36; Yak. 4:4) Mosiyana na zimenezi, awo amene amalambila Mulungu mokhulupilika amachulidwa kuti ‘oyela’ kapena kuti “anamwali.” (2 Akor. 11:2; Chiv. 14:4) Babulo wakale anali cimake ca kulambila konyenga. Conco, tingati Babulo Wamkulu aimila kulambila kulikonse konyenga. Mkaziyu ni ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga.—Chiv. 17:5, 18; onani nkhani yakuti, “Kodi Babulo Wamkulu N’ciyani?” Nkhaniyi mungaipeze pa webusaiti ya jw.org ku Chichewa.

17. N’ciyani cidzacitikila Babulo Wamkulu?

17 N’ciyani cidzacitikila Babulo Wamkulu? Chivumbulutso 17:16, 17 imayankha funsoli motele: “Nyanga 10 waziona zija, komanso cilombo, zimenezi zidzadana nalo hulelo. Zidzalisakaza ndi kulisiya lamalisece. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto. Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zicite monga mwa maganizo ake.” Inde, Yehova adzasonkhezela mitundu ya anthu kuti iseŵenzetse cilombo cofiila kwambili, cimene ni bungwe la United Nations, kuti iukile ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga, na kuuwononga kothelatu.—Chiv. 18:21-24.

18. Tingacite ciyani kuti tisacilikize Babulo Wamkulu m’njila ina iliyonse?

18 Kodi izi zitanthauza ciyani kwa ife? Tiyenela kupitiliza na “kupembedza koyela ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu wathu.” (Yak. 1:27) Tisalole ngakhale pang’ono kusonkhezeledwa na ziphunzitso zabodza, zikondwelelo zacikunja, makhalidwe oipa a ŵanthu, komanso macita-cita a zamizimu a Babulo Wamkulu. Cina, tipitilize kucenjeza anthu kuti ‘atuluke mwa iye,’ kuti asagaŵane naye macimo amene iye ali nawo kwa Mulungu.—Chiv. 18:4.

MDANI WAMKULU WA MULUNGU AWELUZIDWA

CINJOKA CACIKULU COFIILA

Satana ndiye amapatsa mphamvu cilombo. (Chiv. 12:3, 9, 13; 13:4; 20:2, 10) Pokhala mdani wamkulu wa Yehova, Satana adzaponyedwa kuphompho zaka 1,000. Pambuyo pake, adzaponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.” (Onani ndime 19-20)

19. Kodi “cinjoka cacikulu cofiila” ndani?

19 Buku la Chivumbulutso limachulanso za “cinjoka cacikulu cofiila.” (Chiv. 12:3) Cinjoka cimeneci cinacita nkhondo na Yesu komanso angelo ake. (Chiv. 12:7-9) Cinaukila anthu a Mulungu, na kupatsa mphamvu zilombo zandale. (Chiv. 12:17; 13:4) Kodi cinjoka cimeneci ndani? Ni “njoka yakale ija, amene ndi Mdyelekezi ndiponso Satana.” (Chiv. 12:9; 20:2) Iye ndiye amalamulila adani onse a Yehova.

20. N’ciyani cidzacitikila cinjokaco?

20 N’ciyani cidzacitikila cinjokaco? Chivumbulutso 20:1-3 imafotokoza kuti mngelo adzaponya Satana m’phompho, imene idzakhala ngati ndende kwa iye. Pa nthawi yonse imene adzakhala m’ndendeyo, Satana ‘sadzasoceletsanso mitundu ya anthu kufikila zitatha zaka 1,000.’ Potsilizila pake, iye na ziŵanda zake adzaponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.” Izi zitanthauza kuti iwo adzawonongedwa kothelatu. (Chiv. 20:10) Tangoganizilani mmene zinthu zidzakhalile popanda Satana na ziŵanda zake. Imeneyi idzakhala nthawi yokondweletsa ngako!

21. N’cifukwa ciyani tingakondwele na zimene timaŵelenga m’buku la Chivumbulutso?

21 Ha! n’zolimbikitsa cotani nanga kudziŵa tanthauzo la zizindikilo zochulidwa m’buku la Chivumbulutso. Tawadziŵa adani a Yehova, na zimene zidzawacitikila. Ndithudi, “wodala ndi munthu amene amaŵelengela ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu.” (Chiv. 1:3) Adani a Mulungu akadzawonongedwa, kodi anthu okhulupilika adzalandila madalitso otani? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yothela pa nkhani zino zogwilizana.

NYIMBO 23 Ulamulilo wa Yehova Wayamba

^ Buku la Chivumbulutso limagwilitsa nchito zizindikilo povumbula adani a Mulungu. Buku la Danieli limatithandiza kudziŵa tanthauzo la zizindikilo zimenezo. M’nkhani ino, tiona mmene maulosi ena ochulidwa m’buku la Danieli, amagwilizanilana na maulosi a m’Chivumbulutso. Izi zidzatithandiza kudziŵa adani a Mulungu. Kenaka, tikambilane cimene cidzacitikila adaniwo.

^ Cina cimene cionetsa kuti cilombo ca mitu 7 ciimila maboma onse, n’cakuti cili na “nyanga 10.” M’Baibo, nambala ya 10 nthawi zambili imaimila cinthu cokwana kapena kuti cathunthu.

^ Mosiyana na cilombo coyamba, cifanizilo cimeneci cilibe zisoti zacifumu ku nyanga zake. (Chiv. 13:1) Izi zili conco cifukwa ‘cikutuluka mwa mafumu 7 aja,’ ndipo cimapatsidwa mphamvu kucokela kwa mafumuwo.—Onani nkhani yakuti, “Kodi Cilombo Cofiila Kwambili Comwe Cimachulidwa M’caputala 17 ca Chivumbulutso Cimaimila Ciyani?” Nkhaniyi mungaipeze pa webusaiti ya jw.org ku Chichewa.