Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 21

Buku la Chivumbulutso—Mmene Likukhudzila Tsogolo Lanu

Buku la Chivumbulutso—Mmene Likukhudzila Tsogolo Lanu

“Ame! Bwelani, Ambuye Yesu.”—CHIV. 22:20.

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Ni cisankho cofunika citi cimene anthu onse ayenela kupanga?

 MASIKU ANO, anthu ayenela kupanga cisankho cofunika kwambili: Aliyense ayenela kusankha, kaya kukhala kumbali ya Yehova Mulungu wolamulila wa cilengedwe conse, kapena kukhala pansi pa ulamulilo wa mdani wankhanza, Satana Mdyelekezi. Palibe zokamba kuti ine sin’dzakhala kumbali iliyonse. Cisankho cimene adzapanga cidzakhudza tsogolo lawo. (Mat. 25:31-33, 46) Pa “cisautso cacikulu,” iwo adzaikidwa cizindikilo ca cipulumutso kapena ca ciwonongeko.—Chiv. 7:14; 14:9-11; Ezek. 9:4, 6.

2. (a) Kodi Aheberi 10:35-39 imatilimbikitsa kucita ciyani? (b) Kodi buku la Chivumbulutso lingatithandize bwanji?

2 Ŵelengani Aheberi 10:35-39. Ngati munasankha kucilikiza ulamulilo wa Yehova, munapanga cisankho canzelu. Ndipo mufunitsitsa kuthandiza ena kusankha mwanzelu. Kuti mucite zimenezi, mungaseŵenzetse mfundo za m’buku la Chivumbulutso. Buku lapadela limeneli limaonetsa zimene zidzacitikila anthu otsutsana na Yehova. Cina, limafotokoza madalitso amene anthu ocilikiza mokhulupilika ulamulilo wa Mulungu adzapeza. Tingacite bwino kumaŵelenga mfundo za coonadi zofunika kwambili zimenezi. Kucita izi kudzatithandiza kupitilizabe kutumikila Yehova. Kuwonjezela apo, tingaseŵenzetse zimene taphunzilazo pothandiza ena kupanga cisankho canzelu, na kumamatila ku zimene asankhazo.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilane mafunso aya: Kodi awo amene amacilikiza ulamulilo wa Mulungu awasungila madalitso otani? Kumbali ina, n’ciyani cidzacitikile awo amene asankha kucilikiza cilombo cofiila kwambili cochulidwa m’buku la Chivumbulutso?

MADALITSO AMENE ANTHU OKHULUPILIKA ADZAPEZA

4. Ni gulu liti limene mtumwi Yohane anaona lili pamodzi na Yesu kumwamba?

4 M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona magulu aŵili a anthu amene amacilikiza ulamulilo wa Yehova, ndipo iwo analandila madalitso a moyo wosatha. M’gulu loyamba muli anthu 144,000. (Chiv. 7:4) Iwo amatengedwa padziko lapansi kuti akapange boma, kapena kuti Ufumu kumwamba pamodzi na Yesu. Limodzi naye adzalamulila dziko lapansi. (Chiv. 5:9, 10; 14:3, 4) M’masomphenya, Yohane anawaona ataimilila na Yesu kumwamba pa Phili la Ziyoni.—Chiv. 14:1.

5. N’ciyani cidzacitikila otsalila a 144,000 posacedwa?

5 Kuyambila m’nthawi ya atumwi, anthu masauzande akhala akusankhidwa kuti akhale m’gulu la 144,000. (Luka 12:32; Aroma 8:17) Komabe, Yohane anauzidwa kuti ni otsalila a 144,000 ocepa cabe amene adzakhala na moyo padziko lapansi m’masiku otsiliza. “Otsala” amenewa adzaikidwa “cidindo” cothela pa cisautso cacikulu, kuonetsa kuti avomelezedwa na Yehova. (Chiv. 7:2, 3; 12:17) Ndiyeno, pa nthawi ya cisautso cacikulu, otsalila amenewo adzatengedwa kupita kumwamba kuti akakhale na odzozedwa anzawo, amene anamwalila ali okhulupilika. Kumeneko adzalamulila na Yesu mu Ufumu wa Mulungu.—Mat. 24:31; Chiv. 5:9, 10.

6-7. (a) Ni gulu laciŵili liti limene Yohane anaona? Nanga tiphunzilapo ciyani zokhudza gululi? (b) N’cifukwa ciyani otsalila a 144,000 komanso a khamu lalikulu ayenela kuyembekezela mwacidwi kukwanilitsidwa kwa Chivumbulutso caputala 7?

6 Pambuyo poona gulu lakumwamba, Yohane anaona “khamu lalikulu.” Mosiyana na a 144,000, khamu limeneli palibe angathe kuliŵelenga. (Chiv. 7:9, 10) Tiphunzilapo ciyani zokhudza iwo? Yohane anauzidwa kuti: “Amenewa ndi amene atuluka m’cisautso cacikulu, ndipo acapa mikanjo yawo ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:14) Likadzapulumuka cisautso cacikulu, “khamu lalikulu” limeneli lidzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi, ndipo lidzapindula na madalitso osaneneka.—Sal. 37:9-11, 27-29; Miy. 2:21, 22; Chiv. 7:16, 17.

7 Kaya tinasankhidwa kuti tikapite kumwamba kapena kukhala padziko lapansi, kodi timakhulupilila kuti tidzaona kukwanilitsidwa kwa Chivumbulutso caputala 7? Inde, tiyenela kukhulupilila. Iyi idzakhala nthawi yokondweletsa kwambili ku magulu onse aŵili a atumiki a Mulungu. Pa nthawiyo, tidzakhala na cimwemwe codzaza tsaya poona kuti tinasankha kucilikiza ulamulilo wa Yehova. Kodi buku la Chivumbulutso limatiuzanso ciyani za cisautso cacikulu?—Mat. 24:21.

CIMENE CIDZACITIKILA ANTHU OTSUTSANA NA MULUNGU

8. Kodi cisautso cacikulu cidzayamba bwanji? Nanga anthu ambili adzacita ciyani?

8 Monga tinaonela m’nkhani yapita, posacedwa magulu andale adzaukila Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga. (Chiv. 17:16, 17) Kuukila kumeneko kudzakhala ciyambi ca cisautso cacikulu. Kodi izi zidzapangitsa anthu ambili-mbili kusankha kutumikila Yehova? Ayi. M’malo mwake, Chivumbulutso caputala 6 imati pa nthawi yovuta imeneyo, anthu amene satumikila Yehova adzafuna-funa citetezo ku maboma a dzikoli komanso mabungwe a zamalonda, amene amawayelekezela na mapili. Popeza anthuwo sadzaiima kumbali ya Ufumu wa Mulungu, Yehova adzawaona kuti ni otsutsa.—Luka 11:23; Chiv. 6:15-17.

9. Kodi anthu a Yehova adzakhala osiyana motani na anthu onse pa cisautso cacikulu? Nanga n’ciyani cidzacitika kwa iwo?

9 Ndithudi, atumiki a Yehova okhulupilika adzakhala osiyana kwambili na anthu a m’dzikoli pa nthawi yovuta ya cisautso cacikulu imeneyo. Ni okhawo amene padziko lapansi azidzatumikila Yehova Mulungu, na kukana kucilikiza “cilombo.” (Chiv. 13:14-17) Cifukwa cokhalabe okhulupilika, adzaputa mkwiyo wa anthu otsutsana na Yehova. Zotulukapo n’zakuti, mgwilizano wa mitundu udzaukila anthu a Mulungu padziko lonse lapansi. Kuukila koopsa kumeneku kunanenedwelatu mwaulosi kuti kuukila kwa Gogi wa Magogi.—Ezek. 38:14-16.

10. Malinga na Chivumbulutso 19:19-21, kodi Yehova adzacita ciyani anthu ake akadzaukilidwa?

10 Kodi Yehova adzacita ciyani na kuukila koopsa kumeneku? Iye anatiuza kuti: “Mkwiyo wanga udzatulukila m’mphuno mwanga.” (Ezek. 38:18, 21-23) Chivumbulutso caputala 19 imakamba zimene zidzatsatilapo. Yehova adzatumiza Mwana wake kuti akateteze anthu ake, na kuwononga adani awo. Pa kuwononga kumeneko, Yesu adzakhala pamodzi na ‘magulu ankhondo akumwamba,’ omwe ni angelo okhulupilika komanso a 144,000. (Chiv. 17:14; 19:11-15) Kodi nkhondo imeneyi idzakhala na zotulukapo zotani? Anthu onse otsutsana na Yehova pamodzi na mabungwe awo adzawonongedwa kothelatu.—Ŵelengani Chivumbulutso 19:19-21.

NKHONDO IKADZATHA, UKWATI

11. Ni cocitika capadela citi cothela cochulidwa m’buku la Chivumbulutso?

11 Tangoganizilani mmene anthu okhulupilika padziko lapansi adzamvelela adani a Mulungu akadzawonongedwa. Idzakhala nthawi yokondweletsa ngako! Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, kumwamba kudzakhala mfuu yaikulu yacisangalalo. Koma palinso cina cidzabweletsa cimwemwe cacikulu. (Chiv. 19:1-3) Ni “ukwati wa Mwanawankhosa,” umene ni cocitika cokondweletsa kwambili cothela cochulidwa m’buku la Chivumbulutso.—Chiv. 19:6-9.

12. Malinga n’kunena kwa Chivumbulutso 21:1, 2, kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzacitika liti?

12 Kodi ukwati umenewo udzacitika liti? Nkhondo ya Aramagedo isanayambe, onse a 144,000 adzakhala kumwamba. Komabe, imeneyo sidzakhala nthawi ya ukwati wa Mwanawankhosa. (Ŵelengani Chivumbulutso 21:1, 2.) Ukwati wa Mwanawankhosa udzacitika pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, adani onse a Mulungu akadzawonongedwa.—Sal. 45:3, 4, 13-17.

13. Kodi ukwati wa Mwanawankhosa utanthauza ciyani kwa oloŵetsedwamo?

13 Kodi ukwati wa Mwanawankhosa utanthauza ciyani kwa oloŵetsedwamo? Monga mmene ukwati umagwilizanitsila mwamuna na mkazi, ukwati wophiphilitsa umenewo udzagwilizanitsa Yesu Khristu Mfumu, na a 144,000 amene ni “mkwatibwi” wake. Cocitika capadela cimeneco cidzakhazikitsa boma latsopano limene lidzalamulila dziko lapansi zaka 1,000.—Chiv. 20:6.

MZINDA WAULEMELELO NA TSOGOLO LANU

Chivumbulutso caputala 21 imacitila cithunzi Yerusalemu Watsopano amene ‘akutsika kucokela kumwamba kwa Mulungu.’ Mu ulamulilo wa zaka 1,000. Yerusalemu ameneyu adzabweletsa madalitso oculuka pa anthu omvela. (Onani ndime 14-16)

14-15. Kodi Chivumbulutso caputala 21 imayelekezela a 144,000 na ciyani? (Onani cithunzi pacikuto.)

14 Cotsatila, Chivumbulutso caputala 21 imayelekezela a 144,000 na mzinda wokongola kwambili wochedwa “Yerusalemu Watsopano.” (Chiv. 21:2, 9) Mzinda umenewu uli na maziko a miyala 12, imene panalembedwa “maina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” N’cifukwa ciyani mfundoyi inakopa cidwi Yohane? Cifukwa anaona dzina lake litalembedwa pa umodzi mwa miyala imeneyo. Uwu ni mwayi waukulu kwambili!—Chiv. 21:10-14; Aef. 2:20.

15 Mzinda wophiphilitsa ulibe unzake wofanana nawo. Mzindawo uli na msewu waukulu wopangidwa na golide woyengedwa bwino, zipata 12 za ngale, ndipo zipupa na maziko ake anazikongoletsa na miyala ya mtengo wapatali, komanso miyeso yake yonse inali yolinganizidwa bwino lomwe. (Chiv. 21:15-21) Ngakhale n’conco, pali cina cake cimene sicikuoneka mu mzindawo. Onani zimene Yohane akutiuza: “Sindinaone kacisi mumzindawo, pakuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anali kacisi wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kacisi wake. Mzindawo sunafunikilenso kuwala kwa dzuŵa kapena kwa mwezi, pakuti ulemelelo wa Mulungu unauwalitsa, ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.” (Chiv. 21:22, 23) Amene amapanga Yerusalemu Watsopano azitha kuonana naye Yehova mwacindunji. (Aheb. 7:27; Chiv. 22:3, 4) Conco, Yehova na Yesu ndiwo kacisi mu mzinda umenewo.

Ndani adzapindula na zinthu zabwino zimene aziyelekezela na “mtsinje” komanso “mitengo”? (Onani ndime 16-17)

16. Kodi mtundu wa anthu udzapindula bwanji mu Ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu wa Zaka 1,000?

16 Odzozedwa amalimbikitsidwa kwambili akamasinkhasinkha za mzinda umenewo. Koma naonso amene ali na ciyembekezo ca padziko lapansi ayenela kucita cidwi na mzindawo. Mu Ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu wa Zaka 1,000, Yerusalemu Watsopano adzabweletsa madalitso oculuka. Yohane anaona madalitsowo akuyenda ngati “mtsinje wa madzi a moyo.” Ndipo kumbali zonse ziŵili za mtsinjewo kunali “mitengo ya moyo,” imene inali kutulutsa masamba “ocilitsila mitundu ya anthu.” (Chiv. 22:1, 2) Anthu onse amene adzakhalako pa nthawiyo adzapindula na zinthu zabwino zimenezo. Pang’ono-m’pang’ono anthu omvela adzakhala angwilo. Sikudzakhala matenda, zopweteka, komanso kulila.—Chiv. 21:3-5.

17. Malinga na Chivumbulutso 20:11-13, ndani adzapindula na Ulamulilo wa Zaka 1,000?

17 Ndani adzapindula na madalitso amenewo? Oyambilila ni khamu lalikulu lopulumuka Aramagedo, pamodzi na ana awo amene angadzabadwe m’dziko latsopano. Komanso, Chivumbulutso caputala 20 imakambanso kuti akufa adzauka. (Ŵelengani Chivumbulutso 20:11-13.) Anthu okhulupilika “olungama” amene anamwalila kale-kale, komanso “osalungama” amene analibe mwayi wokwanila wophunzila za Yehova, onse adzaukitsidwa n’kukhala na moyo pano padziko lapansi. (Mac. 24:15; Yoh. 5:28, 29) Kodi izi zitanthauza kuti anthu onse amene anafa adzaukitsidwa pa nthawi ya Ulamulilo wa Zaka 1,000? Ayi. Aja amene anakanatu mwadala mwayi wotumikila Yehova asanamwalile sadzaukitsidwa. Iwo anali na mwayi wophunzila za Yehova, koma anaonetsa kuti si oyenela kukhala na moyo m’Paladaiso padziko lapansi.—Mat. 25:46; 2 Ates. 1:9; Chiv. 17:8; 20:15.

MAYESO OTHELA

18. Kodi zinthu zidzakhala bwanji padziko lapansi kumapeto kwa zaka 1,000?

18 Kumapeto kwa zaka 1,000 anthu onse okhala padziko lapansi adzakhala angwilo. Palibe aliyense amene adzakhala na uchimo umene tinatengela kwa Adamu. (Aroma 5: 12) Tembelelo lobwela cifukwa ca uchimo wa Adamu lidzakhala litacotsedwapo kothelatu. Izi zikadzacitika, tidzakhala na “moyo” monga anthu angwilo kumapeto kwa zaka 1,000.—Chiv. 20:5.

19. N’cifukwa ciyani mayeso othela ni ofunika?

19 Tidziŵa kuti Yesu sanagonje ku mayeso a Satana ofuna kumuwonongela cikhulupililo cake. Iye anakhalabe wokhulupilika poyesedwa. Koma kodi anthu angwilo adzakhalabe okhulupilika Satana akadzapatsidwa mpata wakuti awayese? Aliyense adzadziyankhila yekha funso limeneli Satana akadzamasulidwa ku phompho kumapeto kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:7) Amene adzakhala okhulupilila pa mayeso othela amenewo, adzakhala na moyo kwamuyaya komanso ufulu weniweni. (Aroma 8:21) Koma amene amapandukila Mulungu, adzawonongedwa kwamuyaya pamodzi na Mdyelekezi komanso ziŵanda zake.—Chiv. 20:8-10.

20. Kodi mukumva bwanji ponena za maulosi ocititsa cidwi a m’buku la Chivumbulutso?

20 Kodi mukumva bwanji pambuyo pokambilana mwacidule mfundo za m’buku la Chivumbulutso? Kodi sizokondweletsa kuona kuti mukukwanilitsa nawo maulosi ocititsa cidwi amenewo? Kodi izi sizikupangitsani kuitanila ena kuti adzagwilizane nafe pa kulambila koyela? (Chiv. 22:17) Pamene mitima yathu ili yodzala na cimwemwe cifukwa ca zocitika za kutsogolo zokondweletsa, ndife ofunitsitsa kukamba mawu amene mtumwi Yohane anakamba akuti: “Ame! Bwelani, Ambuye Yesu.”—Chiv. 22:20.

NYIMBO 27 Ana a Mulungu Adzaonekela

[Mau apansi]

^ Ino ni nkhani yothela pa nkhani zogwilizana zokhudza buku la Chivumbulutso. Monga tionele m’nkhani ino, amene adzakhalabe okhulupilika kwa Yehova adzakhala na tsogolo labwino. Koma amene amatsutsa ulamulilo wa Mulungu mapeto awo adzakhala ocititsa manyazi.