Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 19

Buku la Chivumbulutso—Mmene Limakukhudzilani

Buku la Chivumbulutso—Mmene Limakukhudzilani

“Wodala ndi munthu amene amaŵelengela ena mokweza . . . mawu a ulosi umenewu.”—CHIV. 1:3.

NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. N’cifukwa ciyani tiyenela kucita cidwi na buku la Chivumbulutso?

 KODI wina anakupemphamponi kuti muone mapikica a munthu wina wake? Pamene muyang’ana mapikicawo, mukuona kuti anthu ambili simuŵadziŵa. Koma pikica ina yakucititsani cidwi kwambili. Cifukwa ciyani? Cifukwa inu mulipo pa pikicayo. Pamene mukuiyang’anitsitsa, mukuyesa kukumbukila malo komanso nthawi imene munaijambulila. Cina, mukuyesa kuona ngati pali ena amene mwadziŵa pa pikicayo. Mwacionekele, pikicayo ni yofunika ngako kwa inu.

2 Buku la Chivumbulutso ili monga pikica imeneyo. Cifukwa ciyani takamba conco? Cifukwa coyamba n’cakuti buku la m’Baibo limeneli analembela ife. Pa vesi loyamba pamati: “Chivumbulutso copelekedwa ndi Yesu Khristu, cimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwapa.” (Chiv. 1:1) Conco, zimene zinalembedwa m’bukuli sizinalembedwele anthu onse, koma analembela ife atumiki a Mulungu odzipatulila. Pokhala anthu a Mulungu, sitiyenela kudabwa poona kuti tikutengako mbali pokwanilitsa maulosi a m’buku locititsa cidwi limeneli. M’mawu ena tingati, “tilipo pa pikicayo.”

3-4. Malinga na buku la Chivumbulutso, ni liti pamene maulosi ake anayamba kukwanilitsika? Nanga zimenezi ziyenela kupangitsa aliyense wa ife kucita ciyani?

3 Cifukwa caciŵili n’cokhudza nthawi imene maulosi amenewa anayamba kukwanilitsika. Mtumwi Yohane wokalamba anaizindikila nthawiyo pamene anati: “Mwa mzimu, ndinapezeka kuti ndili m’tsiku la Ambuye.” (Chiv. 1:10) Pamene Yohane analemba mawu amenewo ca m’ma 96 C.E., ‘tsiku la Ambuye’ linali likali kutali. (Mat. 25:14, 19; Luka 19:12) Koma malinga na ulosi wa m’Baibo, tsikulo linayamba mu 1914 pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba. Conco, kuyambila mu 1914, maulosi a m’buku la Chivumbulutso amenenso amakhudza anthu a Mulungu, anayamba kukwanilitsika. Ndithudi, tikukhala “m’tsiku la Ambuye.”

4 Cifukwa tikukhala m’nthawi yapadela imeneyi, tiyenela kukhala chelu kwambili potsatila uphungu wacikondi wa pa Chivumbulutso 1:3 wakuti: “Wodala ndi munthu amene amaŵelengela ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu, komanso amene akusunga zolembedwamo, pakuti nthawi yoikidwilatu ili pafupi.” Zoonadi, tiyenela ‘kuŵelenga mokweza,’ ‘kumvela mawu a ulosi umenewu,’ na ‘kuwasunga.’ Kodi ena mwa mawu amene tiyenela kumvela ni ati?

ONETSETSANI KUTI KULAMBILA KWANU N’KOVOMELEZEKA

5. Kodi buku la Chivumbulutso lionetsa bwanji kufunika kodzipenda kuti tione ngati kulambila kwathu n’kovomelezeka kwa Yehova?

5 Caputala coyamba ca Chivumbulutso, cimationetsa kuti Yesu adziŵa bwino zonse zimene zikucitika m’mipingo ya anthu ake. (Chiv. 1:12-16, 20; 2:1) Iye anaonetsa bwino zimenezi m’mauthenga amene analembela mipingo 7 ya ku Asia Minor. M’mauthengawo, iye anapatsa Akhristu oyambilila amenewo malangizo acindunji owathandiza kuona ngati kulambila kwawo kunali kovomelezeka kwa Yehova. Ndipo zimene anakamba m’mauthengawo zigwilabe nchito kwa anthu onse a Mulungu masiku ano. Kodi tiphunzilapo ciyani? Mtsogoleli wathu Yesu Khristu, adziŵa bwino mmene uzimu wathu ulili. Tili pansi pa uyang’anilo wa Yesu, ndipo iye amaona zonse. Adziŵa zimene tiyenela kucita kuti Yehova apitilize kutiyanja. Kodi Yesu anapeleka malangizo otani amene tiyenela kumvela masiku ano?

6. (a) Malinga na mawu a Yesu a pa Chivumbulutso 2:3, 4, kodi mpingo wa ku Aefeso unali na vuto lotani? (b) Nanga tiphunzilapo ciyani?

6 Ŵelengani Chivumbulutso 2:3, 4. Tisaleke kukonda Yehova mmene tinali kum’kondela poyamba. Uthenga wa Yesu ku mpingo wa ku Aefeso unaonetsa kuti iwo anapilila zinthu zambili, komanso kuti anapitiliza kutumikila Yehova olo kuti anakumana na zovuta zosiyana-siyana. Ngakhale n’conco, iwo anasiya cikondi cimene anali naco poyamba. Anafunika kukulitsanso cikondi cawo cimeneco, cifukwa akanapanda kutelo, kulambila kwawo kukanakhala kosavomelezeka. Mofananamo, ifenso masiku ano tiyenela kucita zambili kuwonjezela pa kupilila. Tiyenela kupilila na zolinga zabwino. Mulungu wathu amacita cidwi na zimene timacita, komanso colinga cimene timacitila zimenezo. Mulungu amayang’ana pa zolinga zathu zom’tumikila, cifukwa amafuna kuti tizim’lambila kaamba kom’konda kwambili komanso kumuyamikila.—Miy. 16:2; Maliko 12:29, 30.

7. (a) Malinga n’kunena kwa Chivumbulutso 3:1-3, kodi Yesu anaupeza na vuto lotani mpingo wa Sade? (b) Nanga ife tiyenela kucita ciyani?

7 Ŵelengani Chivumbulutso 3:1-3. Tiyenela kupitiliza kukhala maso. Ofalitsa mu mpingo wa Sade anali na vuto losiyana. Ngakhale kuti poyamba anali okangalika kuuzimu, iwo anayamba kubwelela m’mbuyo muutumiki wawo kwa Mulungu. Ndiye cifukwa cake Yesu anawauza kuti ‘adzuke.’ Kodi pali cenjezo lotani kwa ife pamenepa? N’zoona kuti Yehova sadzaiŵala nchito zathu. (Aheb. 6:10) Ngakhale n’telo, sitiyenela kukhutila cabe na zimene tinacita muutumiki wa Yehova kumbuyoku. Olo kuti sitingacite zambili poyelekezela na kale, tiyenela kupitilizabe kukhala na zocita zambili “mu nchito ya Ambuye,” na kukhalabe maso mpaka mapeto.—1 Akor. 15:58; Mat. 24:13; Maliko 13:33.

8. Tiphunzilapo ciyani pa uthenga wopita kwa Akhristu a ku Laodikaya, wolembedwa pa Chivumbulutso 3:15-17?

8 Ŵelengani Chivumbulutso 3:15-17. Tiyenela kukhala acangu komanso odzipeleka na mtima wonse pa kulambila kwathu. Uthenga wa Yesu kwa Akhristu a ku Laodikaya, unaonetsa vuto limene anali nalo. Iwo anali “ofunda” pa kulambila kwawo. Cifukwa cakuti cangu cawo cinali citacepa, Yesu anawauza kuti anali ‘ovutika’ komanso ‘omvetsa cisoni.’ Iwo anafunika kukangalika kwambili pa kulambila Yehova. (Chiv. 3:19) Kodi tiphunzilapo ciyani pamenepa? Ngati cangu cathu cacepa, mankhwala ake ni kukulitsa mzimu woyamikila kwambili cuma cauzimu cimene tili naco. (Chiv. 3:18) Tisalole kuti kufuna-funa umoyo wofeŵa kutipangitse kukankhila zinthu zauzimu pambuyo.

9. Malinga na mauthenga a Yesu kwa Akhristu a ku Pegamo na Tiyatira, kodi tiyenela kupewa ciyani?

9 Tizipewa ziphunzitso za ampatuko. Yesu anadzudzula anthu ena amene anali kulimbikitsa magaŵano ku Pegamo. (Chiv. 2:14-16) Iye anayamikila Akhristu a ku Tiyatira cifukwa anapewa “zinthu zozama za Satana,” ndipo anawalimbikitsa ‘kugwila mwamphamvu’ coonadi. (Chiv. 2:24-26) Koma Akhristu ofooka kumeneko amene anayamba kutsatila ziphunzitso zabodza anafunika kusintha. Nanga bwanji ife masiku ano? Tizipewa ziphunzitso zosagwilizana na mfundo za Yehova. Ampatuko angaoneke “odzipeleka kwa Mulungu, koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe.” (2 Tim. 3:5) Cidzakhala copepuka kudziŵa na kupewa ziphunzitso zabodza, kokha ngati timaŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama.—2 Tim. 3:14-17; Yuda 3, 4.

10. N’ciyani cina cimene tiphunzilapo pa zimene Yesu anauza mpingo wa ku Pegamo na Tiyatira?

10 Tizipewa zaciwelewele za mtundu uliwonse. Kunalinso vuto lina ku Pegamo na Tiyatira. Yesu anadzudzula Akhristu a m’mipingo imeneyi cifukwa anali kucita zaciwelewele. (Chiv. 2:14, 20) Kodi ife tiphunzilapo ciyani? Yehova sangalekelele khalidwe lililonse la ciwelewele cabe cifukwa tam’tumikila kwa zaka zambili, ndipo pali pano tikusangalala na mautumiki owonjezela. (1 Sam. 15:22; 1 Pet. 2:16) Iye amafuna kuti timamatile ku miyezo yake yapamwamba, olo kuti anthu ambili m’dzikoli sacita zimenezo.—Aef. 6:11-13.

11. Kodi pofika pano tingati taphunzila ciyani? (Onani bokosi lakuti  “Zimene Tiphunzilapo.”)

11 Pofika pano, kodi mwacidule tingati taphunzila ciyani? Taona kuti tifunika kuonetsetsa kuti kulambila kwathu n’kovomelezeka kwa Yehova. Ngati timacita zina zake zimene zikupangitsa kulambila kwathu kukhala kosavomelezeka, tiyenela kucitapo kanthu mwamsanga kuti tikonze zinthu. (Chiv. 2:5, 16; 3:3, 16) Yesu anachulanso cina cake m’mauthenga ake opita ku mipingoyo. Kodi cinali ciyani?

KHALANI OKONZEKA KUPILILA CIZUNZO

Pambuyo pakuti Satana wapitikitsidwa kumwamba, kodi wakhala akuŵaukila motani anthu a Mulungu? (Onani ndime 12-16)

12. Kodi tiphunzilapo ciyani pa zimene Yesu anauza Akhristu a ku Simuna na ku Filadefiya? (Chivumbulutso 2:10)

12 Tsopano, tiyeni tikambilane mauthenga a Yesu opita ku mpingo wa Simuna na Filadefiya. Iye anauza Akhristu akumeneko kuti sayenela kuopa cizunzo cifukwa Yehova adzawadalitsa kaamba ka kukhulupilika kwawo. (Ŵelengani Chivumbulutso 2:10; 3:10) Kodi tiphunzilapo ciyani? Tiyenela kudziŵa kuti tidzazunzidwa, ndipo tizikhala okonzeka kupilila. (Mat. 24:9, 13; 2 Akor. 12:10) N’cifukwa ciyani kukumbutsidwa zimenezi n’kofunika?

13-14. Kodi zocitika zochulidwa pa Chivumbulutso caputala 12, zawakhudza bwanji anthu a Mulungu?

13 Buku la Chivumbulutso limatiuza kuti anthu a Mulungu adzazunzidwa “m’tsiku la Ambuye,” kutanthauza m’masiku athu ano. Chivumbulutso caputala 12 imaonetsa kuti kumwamba kunabuka nkhondo Ufumu wa Mulungu utangobadwa. Mikayeli amene ni Yesu Khristu waulemelelo, pamodzi na angelo anamenya nkhondo na Satana komanso ziŵanda zake. (Chiv. 12:7, 8) Zotulukapo, adani a Mulungu amenewo anagonjetsedwa na kuponyedwa padziko lapansi, zimene zinapangitsa kuti padziko lapansi pakhale mavuto aakulu. (Chiv. 12:9, 12) Koma kodi izi zinawakhudza bwanji anthu a Mulungu?

14 Buku la Chivumbulutso limatiuza zimene Satana anacita. Popeza tsopano alibe malo kumwamba, iye wakwiyila otsalila odzozedwa amene amaimilako Ufumu wa Mulungu padziko lapansi, komanso amene “ali ndi nchito yocitila umboni za Yesu.” (Chiv. 12:17; 2 Akor. 5:20; Aef. 6:19, 20) Kodi ulosi umenewu ukukwanilitsika bwanji?

15. Kodi “mboni ziŵili” zochulidwa pa Chivumbulutso caputala 11 ndani? Nanga n’ciyani cinawacitikila?

15 Satana anapangitsa kuti adani a Mulungu aukile abale odzozedwa amene anali kutsogolela pa nchito yolalikila za Ufumu. Abale amene anali kutsogolela pakati pawo ndiwo anali kuimila “mboni ziŵili” zophiphilitsa zochulidwa m’buku la Chivumbulutso zimene zinaphedwa. * (Chiv. 11:3, 7-11) Mu 1918, abale 8 otsogolela amenewo anasemeledwa mlandu wabodza, ndipo anagamulidwa kuti adzakhala m’ndende kwa nthawi yaitali. M’kaonedwe ka umunthu, zinaoneka monga kuti nchito ya odzozedwa amenewa ‘yaphedwa.’

16. Ni cinthu cocititsa cidwi citi cimene cinacitika mu 1919? Koma kodi Satana wapitiliza kucita ciyani kungocokela nthawiyo?

16 Ulosi wa pa Chivumbulutso caputala 11 umakambanso kuti “mboni ziŵili” zinaukitsidwa patapita nthawi yocepa. Ulosiwu unakwanilitsika m’njila yocititsa cidwi kwambili m’caka cotsatila kucokela pamene abalewo anaikidwa m’ndende. Mu March 1919, abale odzodzedwa amenewa anatulutsidwa m’ndende, ndipo posapita nthawi mlandu wawo unatha. Nthawi yomweyo, abalewo anayambanso kugwila nchito ya Ufumu. Koma Satana sanaleke kuukila anthu a Mulungu. Kungocokela nthawiyo, Satana wakhala akubweletsa “mtsinje” wa mazunzo kwa anthu a Mulungu. (Chiv. 12:15) Kunena zoona, “apa m’pamene [aliyense wa ife] akufunika kupilila ndiponso kukhala ndi cikhulupililo.”—Chiv. 13:10

MUZITENGAKO MBALI MOKWANILA M’NCHITO IMENE YEHOVA WATIPATSA

17. Kodi anthu a Mulungu alandila thandizo lotani, olo kuti Satana amafunitsitsa kuwazunza?

17 Chivumbulutso caputala 12 cimaonetsa kuti anthu a Mulungu adzalandila thandizo kucokela ku magwelo osayembekezeleka. Zidzakhala ngati “dziko lapansi” lameza “mtsinje” wa cizunzo. (Chiv. 12:16) Ndipo izi n’zimene zakhala zikucitika. Nthawi zina, mbali zodalilika za dziko la Satanali, monga zamalamulo, zathandiza anthu a Mulungu. Nthawi zambili, atumiki a Yehova amapambana milandu m’makhoti, zimene zimapangitsa kuti akhale na ufulu wa kulambila. Kodi ufulu umenewo amauseŵenzetsa bwanji? Iwo amaseŵenzetsa mpata uliwonse kugwila nchito imene Yehova waapatsa. (1 Akor. 16:9) Kodi nchitoyo ni iti?

Ni mauthenga aŵili ati amene akulengezedwa na anthu a Mulungu? (Onani ndime 18-19)

18. Kodi nchito yathu yaikulu ni iti m’masiku ano otsiliza?

18 Yesu analosela kuti anthu ake adzalengeza “Uthenga wabwino wa ufumu [wa Mulungu].” (Mat. 24:14) Pogwila nchito imeneyi iwo amalandila thandizo la mngelo, kapena gulu la angelo, amene amafotokozedwa kuti ali na “uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.”—Chiv. 14:6.

19. Ni uthenga wina uti umene anthu okonda Yehova ayenela kuulengeza?

19 Uthenga wabwino wa Ufumu si uthenga wokhawo umene anthu a Mulungu afunika kulengeza. Iwo afunikanso kucilikiza nchito ya angelo ochulidwa pa Chivumbulutso caputala 8 mpaka 10. Ndiye cifukwa cake, Mboni za Yehova zakhala zikulengeza uthenga waciweluzo umene uli ngati “matalala ndi moto.” Uthengawo umaonetsa ciweluzo ca Mulungu pa mbali zosiyana-siyana za dziko loipali la Satana. (Chiv. 8:7, 13) Anthu ayenela kudziŵa kuti mapeto ali pafupi, n’colinga cakuti apange masinthidwe mwamsanga kuti akapulumuke mkwiyo wa Yehova. (Zef. 2:2, 3) Koma uthenga waciweluzowo ambili saudziŵa. Timafunika kukhala olimba mtima kuti tiulengeze. Pa cisautso cacikulu, uthenga waciweluzo wothela udzakhala woŵaŵa kwambili.—Chiv. 16:21.

MVELANI MAWU A ULOSI

20. Tidzakambilana ciyani m’nkhani ziŵili zokonkhapo?

20 Kukamba zoona tiyenela kumvela “mawu a ulosi,” cifukwa nafenso timakhudzidwa na kukwanilitsika kwa zimene timaŵelenga m’buku la Chivumbulutso. (Chiv. 1:3) Koma kodi tingacite ciyani kuti tipilile cizunzo mokhulupilika, na kupitiliza kulalikila molimba mtima? Tidzalimbikitsidwa na mbali ziŵilizi: Yoyamba, zimene buku la Chivumbulutso limakamba ponena za adani a Mulungu. Yaciŵili, madalitso amene tidzalandila kutsogolo tikakhalabe okhulupilika. M’nkhani ziŵili zokonkhapo, tidzakambilana mbali zimenezi.

NYIMBO 32 Ima ku Mbali ya Yehova

^ Tikukhala m’nthawi yapadela! Maulosi a m’buku la Chivumbulutso akukwanilitsika masiku ano. Kodi maulosi amenewo amatikhudza motani? Nkhani ino komanso ziŵili zotsatilapo, zidzafotokoza mfundo za m’buku la Chivumbulutso. Cina, zidzationetsa kuti kutsatila zonse zolembedwa m’buku la Chivumbulutso kungatithandize kuti kulambila kwathu kukhalebe kovomelezeka kwa Yehova Mulungu.

^ Onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga”, mu Nsanja ya Mlonda ya November 15, 2014, tsa. 30.