Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NkHANI YOPHUNZILA 23

Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova

Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—MAT. 22:37.

NYIMBO 134 Ana ni Mphatso Zimene Mulungu Amaikiza kwa Makolo

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Fotokozani mmene mfundo za m’Baibo zimakhalila zothandiza zinthu zikasintha pa umoyo wathu.

 PA TSIKU lawo la cikwati, mkwati na mkwatibwi amamvetsela mwachelu nkhani yozikika pa Baibo yokamba za ukwati. Mfundo za m’nkhaniyo si zacilendo kwa iwo. Koma kucokela tsikulo, mfundozo zimakhala zofunika kwambili kwa iwo. Cifukwa ciyani? Cifukwa lomba adzayamba kuziseŵenzetsa monga banja.

2 N’cimodzimodzinso Akhristu okwatilana akayamba kukhala na ŵana. Kwa zaka, iwo akhala akumvetsela nkhani zokamba za kulela ana. Koma tsopano, mfundo za m’nkhanizo zidzakhala zofunika kwambili kwa iwo. Adzayamba kuzigwilitsa nchito polela ana awo. Uwu ni udindo waukulu! Zinthu zikasintha mu umoyo wathu, m’pamenenso mfundo zina za m’Baibo zimakhala zothandiza kwa ife. Ndiye cifukwa cake, alambili a Yehova amaŵelenga Malemba nthawi zonse. Izi n’zimenenso mafumu aciisiraeli anauzidwa kuti azisinkhasinkha malemba “masiku onse” a moyo wawo.—Deut. 17:19.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Inu makolo, muli na udindo waukulu wophunzitsa ana anu za Yehova. Koma muyenela kucita zambili kuposa pa kuwaphunzitsa za Mulungu wathu. Muyenela kuthandiza ana anu kuti azim’konda kwambili Mulungu. Kodi mungacite ciyani kuti muthandize ana anu kukhala na cikondi cozama pa Yehova? M’nkhani ino, tikambilane mfundo zinayi za m’Baibo zimene zingathandize inu makolo pophunzitsa ana anu. (2 Tim. 3:16) Tionenso mmene makolo ena acikhristu apindulila cifukwa coseŵenzetsa uphungu wa m’Baibo.

MFUNDO ZINAYI ZOTHANDIZA MAKOLO

Kodi ana anu amapindula motani ngati mufuna-funa citsogozo ca Yehova, komanso kukhala citsanzo cabwino? (Onani ndime 4, 8)

4. Ni mfundo iti imene ingathandize makolo kuphunzitsa ana awo kukhala na cikondi cozama pa Yehova? (Yakobo 1:5)

4 Mfundo yoyamba: Pemphani citsogozo ca Yehova. M’pempheni Yehova kuti akupatseni nzelu zokuthandizani kuphunzitsa ana anu kum’konda. (Ŵelengani Yakobo 1:5.) Iye ndiye woyenelela kwambili kupeleka malangizo. Cifukwa ciyani? Zifukwa zilipo zambili, koma onani ziŵilizi: Coyamba, iye pokhala kholo wa makolo onse, ali na cidziŵitso cacikulu. (Sal. 36:9) Caciŵili, malangizo anzelu amene iye amapeleka amakhala opindulitsa nthawi zonse.—Yes. 48:17.

5. (a) Kodi gulu la Yehova lapeleka zinthu zotani kwa makolo? (b) Monga tinaonela mu vidiyo, mwaphunzila ciyani za mmene M’bale na Mlongo Amorim analelela ana awo?

5 Kupitila m’Mawu ake komanso gulu lake, Yehova wapeleka cakudya cauzimu coculuka cimene cingakuthandizeni kuphunzitsa ana anu kukonda Yehova. (Mat. 24:45) Mwacitsanzo, mungapeze malangizo othandiza m’nkhani zimene zinatuluka mu Galamukani! zaka zambili kumbuyoku zakuti, “Mfundo Zothandiza Mabanja.” Nkhanizi zipezekanso pa webusaiti yathu ku Chichewa. Cina, mavidiyo ambili amene ali pa jw.org pambali yofunsa mafunso, komanso mafilimu aakulu, angathandize makolo kuseŵenzetsa malangizo a Yehova polela ana awo. *Miy. 2:4-6.

6. Kodi tate wina na mkazi wake amaciona bwanji citsogozo ca gulu la Yehova?

6 Makolo ambili amayamikila thandizo limene Yehova amapeleka kupitila m’gulu lake. Tate wina dzina lake Joe anavomeleza kuti: “Kulela ana atatu m’coonadi si kopepuka. Ine na mkazi wanga, timapempha thandizo kwa Yehova nthawi zonse. Ndipo nthawi zambili zacitikapo kuti nkhani kapena vidiyo imene yatuluka, imakhala ya panthawi yake kwa ife, cifukwa imatithandiza kugonjetsa vuto limene takumana nalo. Nthawi zonse timadalila citsogozo ca Yehova mu umoyo wathu.” M’bale Joe na mkazi wake amaona kuti nkhani na mavidiyo amenewa zimathandiza ana awo kuyandikila Yehova.

7. N’cifukwa ciyani makolo ayenela kukhala citsanzo cabwino? (Aroma 2:21)

7 Mfundo yaciŵili: Khalani citsanzo cabwino. Ana amaona zonse zimene makolo awo amacita, ndipo nthawi zambili amatengela citsanzo cawo. N’zoona kuti palibe kholo langwilo. (Aroma 3:23) Ngakhale n’telo, makolo anzelu amayesetsa kukhala citsanzo cabwino kwa ana awo. (Ŵelengani Aroma 2:21.) Pokamba za ana, tate wina anati: “Iwo ali ngati thonje limene limayamwa zilizonse. Adzatiuza akaona kuti zocita zathu sizigwilizana na zimene timawaphunzitsa.” Conco, ngati tifuna kuti ana athu azikonda Yehova, cikondi ca ife makolo pa iye ciyenela kukhala colimba ndipo zizionekela.

8-9. Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene m’bale Andrew na mlongo Emma anakamba?

8 Pali njila zambili zimene makolo angaphunzitsile ana awo kukonda Yehova. Onani zimene m’bale wina wa zaka 17 dzina lake Andrew anakamba. Iye anati: “Nthawi zonse makolo anga anali kuniuza kufunika kwa pemphelo. Usiku uliwonse atate anali kupemphela pamodzi na ine, olo kuti n’nali n’tapemphela kale panekha. Makolo anga nthawi zonse anali kuniuza kuti: ‘Ungakambe na Yehova nthawi iliyonse imene wafuna.’ Zimene ananiphunzitsa pa nkhani ya pemphelo, zinanifika pamtima kwambili. Tsopano nimamasuka kupemphela kwa Yehova, ndipo nimamuona kuti ni Tate wacikondi.” Inu makolo, muzikumbukila kuti cikondi canu cacikulu pa Yehova cingapangitse kuti ana anu nawonso ayambe kum’konda.

9 Onaninso citsanzo ca mlongo wina dzina lake Emma. Pamene atate ake anasiya banja lawo, iwo anasiila amayi ake nkhongole zambili. Iye anati: “Nthawi zambili zinali kuwavuta amayi kupeza ndalama. Koma iwo nthawi zonse anali kukamba za mmene Yehova amasamalila atumiki ake. Ndipo mmene anali kucitila zinthu pa umoyo wawo, zinanionetsa kuti anali kukhulupililadi zimenezo. Amayi anali kucita zimene anali kuphunzitsa.” Kodi tiphunzilapo ciyani? Makolo angaphunzitse ana awo mwacitsanzo cawo ngakhale panthawi zovuta.—Agal. 6:9.

10. Kodi makolo ambili aciisiraeli anali na mipata iti yokambilana na ana awo? (Deuteronomo 6:6, 7)

10 Mfundo yacitatu: Muzikambilana na ana anu nthawi zonse. M’nthawi zakale, Yehova analamula Aisiraeli kuti aziphunzitsa ana awo za iye nthawi zonse. (Ŵelengani Deuteronomo 6:6, 7.) Makolowo anali na mipata yambili patsiku yokambilana na ana awo za Yehova, na kuwaphunzitsa kuti azimukonda kwambili. Mwacitsanzo, mwana wamwamuna waciisiraeli anali kuthela nthawi yoculuka kuthandiza atate ake kubyala mbewu kapena kukolola. Ndipo mwana wamkazi anali kuthela nthawi yoculuka kuthandiza amayi ake kusoka zovala na nchito zina za pakhomo. Makolo poseŵenzela pamodzi na ana awo, anali kukambilana zinthu zambili zofunika. Mwacitsanzo, anali kukambilana ubwino wa Yehova, komanso mmene anali kuthandizila banja lawo.

11. Kodi makolo angaseŵenzetsa mpata uti kukambilana na ana awo?

11 Masiku ano zinthu zinasintha. M’maiko ambili, makolo na ana sakhala na nthawi yocitila zinthu pamodzi kwa tsiku lonse. Makolo amakhala kuti ali ku nchito, ndipo nawonso ana amakhala kusukulu. Zikakhala conco, makolo ayenela kuyesetsa kupeza mipata yokambilana na ana awo. (Aef. 5:15, 16; Afil. 1:10) Ina mwa mipata imeneyo ni pa kulambila kwa pabanja. M’bale wina wacinyamata dzina lake Alexander anati: “Nthawi zonse atate amayesetsa kuti tizikhala na kulambila kwa pabanja, ndipo salola ciliconse kusokoneza nthawi imeneyo. Tikatsiliza kulambila kwa pabanja, timangoceza basi.”

12. Kodi mutu wa banja ayenela kumbukila ciyani panthawi ya kulambila kwa pabanja?

12 Ngati ndinu mutu wa banja, kodi mungacite ciyani kuti kulambila kwanu kwa pabanja kuzikhala kosangalatsa kwa ana anu? Mwina mungakonze zoyamba kuphunzila na ana anu buku lathu latsopano lakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Buku limeneli lidzakuthandizani kuti muzikambilana momasuka. Mumafuna kuti ana anu azikhala omasuka kufotokoza mmene amvelela, komanso zimene ziwadetsa nkhawa. Conco, pewani kuwadzudzula kapena kuwapatsa uphungu panthawi ya kulambila kwa pabanja. Cina, pewani kukwiya mwana wanu akakamba zinthu zosagwilizana na mfundo za m’Baibo. M’malo mwake, muziyamikila kuti akufotokoza maganizo ake moona mtima, ndipo muzimulimbikitsa kuti azicita zimenezo momasuka. Mudzakwanitsa kuthandiza bwino ana anu kokha mukadziŵa bwino mmene iwo amvelela.

Kodi makolo angaseŵenzetse motani cilengedwe pophunzitsa ana awo makhalidwe a Yehova? (Onani ndime 13)

13. Ni mpata winanso uti umene makolo ali nawo kuti athandize ana awo kuyandikila Yehova?

13 Inu makolo, muziyesetsa kupeza mipata tsiku lililonse kuti muthandize ana anu kuyandikila Yehova. Musacite kuyembekezela tsiku limene mumaphunzila nawo Baibo kuti muwaphunzitse za Mulungu wathu wacikondi. Onani zimene mayi wina dzina lake Lisa anakamba. Iye anati: “Timathandiza ana athu kuona kugwilizana pakati pa Yehova na cilengedwe. Mwacitsanzo, galu wathu akacita zoseketsa ana athu, timatengelapo mwayi wowafotokozela kuti Mlengi wathu ni wacimwemwe, ndipo anatilenga m’njila yakuti tizikondwela na moyo.”

Inu makolo, kodi mumawadziŵa mabwenzi a ana anu? (Onani ndime 14) *

14. N’cifukwa ciyani makolo ayenela kuthandiza ana awo kusankha mabwenzi mwanzelu? (Miyambo 13:20)

14 Mfundo yacinayi: Thandizani ana anu kusankha mabwenzi mwanzelu. Mawu a Mulungu amakamba momveka bwino kuti mabwenzi athu angatisonkhezela kucita zabwino kapena zoipa. (Ŵelengani Miyambo 13:20.) Makolo, kodi mumawadziŵa mabwenzi a ana anu? Kodi munaŵaonapo na kucezako nawo? Kodi mungacite ciyani kuti muthandize ana anu kupalana ubwenzi na aja amene akonda Yehova? (1 Akor. 15:33) Mungawathandize kupanga zisankho zanzelu mwa kuitanila ena amene amacita bwino kuuzimu kuti mukhale nawo pa zocitika za banja.—Sal. 119:63.

15. Kodi makolo angacite ciyani kuti athandize ana awo kupanga mabwenzi abwino?

15 Ganizilani citsanzo ca tate wina dzina lake Tony. Anafotokoza zimene iye na mkazi wake anacita pothandiza ana awo kupanga mabwenzi abwino. Iye anati: “Kwa zaka, ine na mkazi wanga takhala tikuitanila abale na alongo a misinkhu yosiyana-siyana na zikhalidwe zosiyana-siyana. Timadyela cakudya pamodzi komanso kucita nawo kulambila kwa pabanja. Imeneyi ndiyo njila yabwino kwambili yodziŵana na amene amakonda Yehova na kum’tumikila mwacimwemwe. Takhalako na mwayi wolandila oyang’anila madela, amishonale, komanso abale na alongo ena m’nyumba mwathu. Zocitika mu utumiki wawo, cangu cawo, komanso mzimu wawo wodzimana zathandiza ana athu kuyandikila kwambili Yehova.” Makolo, yesetsani kuthandiza ana anu kupanga mabwenzi abwino.

MUSATAYE MTIMA!

16. Kodi makolo angacite ciyani ngati mwana wawo wasankha kuleka kutumikila Yehova?

16 Nanga bwanji ngati inu monga kholo mwacita zonse zotheka, koma mwana wanu wina n’kukuuzani kuti safuna kutumikila Yehova? Pewani kuganiza kuti inu monga kholo mwalephela udindo wanu. Yehova anapatsa aliyense wa ife, kuphatikizapo mwana wanu, ufulu wosankha kaya kum’tumikila kapena ayi. Mwana wanu akasankha kusiya Yehova, musataye mtima cifukwa tsiku lina adzabwelela kwa iye. Muzikumbukila fanizo la mwana woloŵelela. (Luka 15:11-19, 22-24) Mwanayo analoŵelela m’makhalidwe oipa, koma pamapeto pake iye anabwelela. Ena angakambe kuti: “Lija linali fanizo cabe, kodi zingacitikedi mu umoyo wa munthu?” Inde zingacitikedi! Ndipo izi n’zimene zinacitikila wacinyamata wina dzina lake Elie.

17. Kodi citsanzo ca Elie n’cothandiza bwanji kwa inu?

17 Ponena za makolo ake, Elie anati: “Makolo anga anayesetsa kunithandiza kum’konda kwambili Yehova komanso Mawu ake, Baibo. Koma n’tafika zaka 15, n’napanduka.” Elie anayamba kukhala moyo wapaŵili, ndipo makolo ake akayesa kum’thandiza kuuzimu anali kukana. Atacoka panyumba, anayamba makhalidwe oipa. Ngakhale n’conco, nthawi zina iye anali kuuzako mnzake nkhani za m’Baibo. Elie anati: “Nikamakamba kwambili za Yehova kwa mnzanga, m’pamenenso n’nali kuganizila kwambili za Yehova. Pang’ono-m’pang’ono, mbewu za coonadi zimene makolo anga anabyala zinayamba kukula.” M’kupita kwa nthawi, Elie anabwelela m’coonadi. * Tangoganizilani cimwemwe cimene makolo ake anali naco, poona kuti iwo anam’thandiza ali wacicepele kukonda Yehova.—2 Tim. 3:14, 15.

18. Kodi mumamva bwanji mukaona makolo amene amayesetsa kuthandiza ana awo kukonda Yehova?

18 Inu makolo, mwapatsidwa udindo wabwino kwambili wothandiza ana anu kukhala alambili a Yehova. (Sal. 78:4-6) Iyi si nchito yopepuka. Conco, timakuyamikila mocokela pansi pa mtima cifukwa coyesetsa kuthandiza ana anu. Mukapitiliza kucita zimene mungathe pothandiza ana anu kukonda Yehova, komanso kuwalela m’malangizo ake na kuwaphunzitsa kaganizidwe kake, mungakhale otsimikiza kuti Atate wathu wacikondi wakumwamba adzakondwela nanu.—Aef. 6:4.

NYIMBO 135 Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”

^ Makolo acikhristu amakonda kwambili ana awo. Iwo amagwila nchito mwakhama kuti asamalila ana awo kuthupi. Koma koposa zonse, makolo amenewa amayesetsa kuthandiza ana awo kukonda kwambili Yehova. M’nkhani ino, tikambilane mfundo zinayi za m’Baibo zimene zingathandize makolo pophunzitsa ana awo.

^ Onani nkhani yakuti, “Baibulo Limasintha Anthu,” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2012.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pofuna kudziŵa bwino mabwenzi a mwana wake, tate akuseŵela mpila wamanja na mwana wake komanso bwenzi la mwana wake.