Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 22

Nzelu Zothandiza pa Umoyo Wathu

Nzelu Zothandiza pa Umoyo Wathu

“Yehova amapeleka nzelu.”—MIY. 2:6.

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’cifukwa ciani tonsefe tifunikila nzelu ya umulungu? (Miyambo 4:7)

 NGATI munapangapo cisankho cofunika kwambili, mosakayikila munapempha nzelu popanga cisankhoco. (Yak. 1:5) Mfumu Solomo analemba kuti: “Nzelu ndiyo cinthu cofunika kwambili.” (Ŵelengani Miyambo 4:7.) Apa Solomo sanali kutanthauza nzelu ina iliyonse ayi. Anali kukamba za nzelu yocokela kwa Yehova Mulungu. (Miy. 2:6) Koma kodi nzelu yaumulungu imeneyi ingatithandize kuthana na mavuto amene timakumana nawo? Inde ingatithandize, monga tionele m’nkhani ino.

2. Ni njila ina iti imene ingatithandize kukhala na nzelu zenizeni?

2 Njila imodzi imene ingatithandize kukhala na nzelu zenizeni, ni kuphunzila na kuseŵenzetsa zimene amuna aŵili amene anali anzelu kwambili anaphunzitsa. Coyamba, tikambilane za Solomo. Baibo imati Mulungu ‘anapatsa Solomo nzelu zopanda malile ndi luso lomvetsa zinthu losaneneka.’ (1 Mafumu 4:29) Kenaka, tikambilane za Yesu amene anali wanzelu kwambili kuposa wina aliyense. (Mat. 12:42) Ponena za iye, ulosi unati: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzelu [komanso] womvetsa zinthu.”—Yes. 11:2.

3. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 Pogwilitsa nchito nzelu zopatsidwa na Mulungu, Solomo komanso Yesu anapeleka malangizo othandiza pa nkhani zofunika kwambili. M’nkhani ino, tikambilane mbali zitatu pa nkhani zofunika zimenezo, zimene ni kuona ndalama moyenela, nchito, komanso mmene timadzionela.

KUONA NDALAMA MOYENELA

4. Kodi Solomo na Yesu anali kusiyana bwanji pa nkhani ya zacuma?

4 Solomo anali wolemela kwambili, ndipo sanali kusoŵa kanthu. (1 Maf. 10:7, 14, 15) Mosiyana na Solomo, Yesu anali na zinthu zocepa zakuthupi, ndipo analibe nyumba yake-yake. (Mat. 8:20) Komabe, amuna aŵiliwa anali kuona zinthu zakuthupi moyenela, cifukwa Gwelo la nzelu zawo anali mmodzi, Yehova Mulungu.

5. Kodi Solomo anali kuziona bwanji ndalama?

5 Solomo anati ndalama “zimatetezela.” (Mlal. 7:12) Ndalama zimatithandiza kupeza zofunikila pa umoyo, komanso zina zimene timafuna. Komabe, olo kuti anali wolemela kwambili, iye anazindikila kuti pali cinthu cina cofunika ngako kuposa ndalama. Mwacitsanzo, analemba kuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi cuma coculuka.” (Miy. 22:1) Solomo anaonanso kuti anthu okonda ndalama sakhutila kwenikweni na zinthu zimene ali nazo. (Mlal. 5:10, 12) Ndipo iye anacenjeza kuti sitiyenela kuika cidalilo cathu conse pa ndalama, cifukwa kaya tikhale nazo zoculuka motani, izo zimatha mwamsanga.—Miy. 23:4, 5.

Kodi kaonedwe kathu ka zinthu za kuthupi kamatilepheletsa kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu? (Onani ndime 6-7) *

6. Kodi Yesu anali kuziona bwanji zinthu zakuthupi? (Mateyu 6:31-33)

6 Yesu nayenso anali kuona zinthu zakuthupi moyenela. Anali kusangalala na cakudya komanso zakumwa. (Luka 19:2, 6, 7) Pa cocitika cina, iye anapanga vinyo wokoma kwambili. Ici cinali cozizwitsa cake coyamba. (Yoh. 2:10, 11) Ndipo patsiku limene anafa, anavala covala ca mtengo wapatali. (Yoh. 19:23, 24) Koma iye anapewa kuika maganizo ake pa zinthu zakuthupi. Anauza otsatila ake kuti: “Kapolo sangatumikile ambuye aŵili . . . Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Yesu anaphunzitsa kuti ngati tifuna-funa Ufumu coyamba, Yehova adzaonetsetsa kuti watipatsa zonse zimene tifunikila.—Ŵelengani Mateyu 6:31-33.

7. Kodi m’bale wina anapindula bwanji cifukwa coona ndalama moyenela?

7 Abale na alongo athu ambili apindula cifukwa coseŵenzetsa malangizo anzelu a Mulungu pa nkhani ya ndalama. Ganizilani citsanzo ca m’bale wina amene ni mbeta, dzina lake Daniel. Iye anati: “Nili wacinyamata, n’nadziikila colinga cakuti zinthu zakuuzimu zikakhale patsogolo mu umoyo wanga.” Cifukwa cokhala na umoyo wosalila zambili, Daniel wakhala akuseŵenzetsa nthawi yake na maluso ake pa nchito zambili za m’gulu lathu. Anawonjezela kuti: “Kukamba zoona, sin’nadziimbepo mlandu pa cisankho cimene n’napanga. N’zoona kuti n’kanakhala na ndalama zambili nikanasumika maganizo anga pa zinthu zakuthupi. Koma kodi ndalamazo zikanafanana na mabwenzi abwino amene napeza? Kodi zikananibweletsela cimwemwe cimene nili naco cifukwa coika za Ufumu patsogolo? Ndalama sizingalingane na madalitso amene Yehova wanipatsa.” Zoonadi, timapindula tikamasumika maganizo athu pa zinthu za kuuzimu, osati pa ndalama.

KUONA NCHITO YAKUTHUPI MOYENELA

8. Tidziŵa bwanji kuti Solomo anali kuona nchito moyenela? (Mlaliki 5:18, 19)

8 Solomo anati cimwemwe cimene timakhala naco pogwila nchito molimbika ni “mphatso yocokela kwa Mulungu.” (Ŵelengani Mlaliki 5:18, 19.) Iye analemba kuti: “Kugwila nchito iliyonse kumapindulitsa.” (Miy. 14:23) Solomo anadziŵa kuti mfundo imeneyi ni yoona. Iye anali kugwila nchito molimbika. Anamanga manyumba, kulima minda ya mpesa, minda yokongola, na madamu amadzi. Anadzimangilanso mizinda. (1 Maf. 9:19; Mlal. 2:4-6) Uku kunali kugwila nchito molimbika, ndipo mosakayikila izi zinamubweletsela cimwemwe. Koma Solomo sanadalile cabe zinthu zimenezo kuti akhale na cimwemwe ceniceni. Iye anacitanso zinthu zambili zakuuzimu. Mwacitsanzo, anatsogolela pa nchito yomanga kacisi waulemelelo wolambililamo Yehova, nchito imene inatenga zaka 7. (1 Maf. 6:38; 9:1) Pambuyo pogwila nchito yakuthupi komanso ya kuuzimu, Solomo anazindikila kuti kucita zakuuzimu ndiko kofunika kwambili kupambana zinthu zakuthupi. Iye anati: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake.”—Mlal. 12:13.

9. Kodi Yesu anaika motani nchito yakuthupi pamalo ake?

9 Yesu nayenso anali kugwila nchito molimbika. Iye ali wacicepele, anali kugwila nchito ya ukalipentala. (Maliko 6:3) Mosakayikila, makolo ake anayamikila kwambili cifukwa cowathandiza kusamalila zofunikila za banja lawo lalikulu. Yesu pokhala kalipentala komanso munthu wangwilo, n’kutheka kuti anthu ambili anali kupita kwa iye kuti akawapangile zinthu. Mwacionekele, iye anali kukondwela na nchito yake. Koma ngakhale kuti anali kugwila nchito yakuthupi molimbika, iye anali kupatula nthawi yocita zinthu zakuuzimu. (Yoh. 7: 15) Patapita nthawi, pokhala mtumiki wanthawi zonse, analangiza omvela ake kuti: “Musamagwile nchito kuti mungopeza cakudya cimene cimawonongeka, koma kuti mupeze cakudya cokhalitsa, copeleka moyo wosatha.” (Yoh. 6: 27) Ndipo pa ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anati: “Unjikani cuma canu kumwamba.”—Mat. 6:20.

Tingacite ciyani kuti tiziona moyenela nchito ya kuthupi komanso zinthu za kuuzimu? (Onani ndime 10-11) *

10. Ni vuto lotani limene ena angakumane nalo kunchito?

10 Nzelu yaumulungu imatithandiza kuona nchito yakuthupi moyenela. Ife Akhristu, timaphunzila kuti tiyenela kugwila “nchito molimbikila . . . , [komanso] nchito yabwino.” (Aef. 4:28) Nthawi zambili abwana athu amaona khama lathu pa nchito komanso kuona mtima kwathu, ndipo angatiuze kuti amayamikila kwambili mmene timagwilila nchito. Tili na zolinga zabwino, tingayambe kuseŵenza maola ambili, pofuna kupangitsa abwana athu kukhala na kapenyedwe kabwino ponena za Mboni za Yehova. Koma posakhalitsa, tingazindikile kuti tayamba kunyalanyaza maudindo a m’banja, komanso zinthu zauzimu. Tiyenela kusintha kuti tikhale na nthawi yoculuka yocita za kuuzimu.

11. Kodi m’bale wina anaphunzila ciyani pa nkhani yoona nchito moyenela?

11 M’bale wacinyamata dzina lake William, anadzionela yekha ubwino woika nchito yakuthupi pamalo ake. Ponena za m’bale wina amene anali kuseŵenzela, William anati: “[M’baleyu] ni citsanzo cabwino ngako pa nkhani yoona nchito moyenela. Iye amagwila nchito molimbika, ndipo makasitomala ake amam’konda cifukwa cogwila bwino nchito yake. Koma nthawi yoweluka ikakwana, amasiya nchito yake, n’kupita kunyumba kukaona banja komanso kukacita zakuuzimu. Ndipo iye ni mmodzi mwa anthu acimwemwe amene nimadziwa.” *

KUDZIONA MOYENELA

12. Kodi Solomo anaonetsa bwanji kuti anali kudziona moyenela? Nanga anasiya bwanji kudziona moyenela?

12 Pamene Solomo anali mlambili wa Yehova wokhulupilika, iye anali kudziona moyenela. Ali wacinyamata, modzicepetsa anazindikila zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anapempha citsogozo ca Yehova. (1 Maf. 3:7-9) Cina, kuciyambi kwa ulamulilo wake, Solomo anali kudziŵa za kuwopsa kokhala wonyada. Iye analemba kuti: “Kunyada kumafikitsa munthu ku ciwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umacititsa munthu kupunthwa.” (Miy. 16:18) N’zomvetsa cisoni kuti pambuyo pake Solomo analephela kutsatila uphungu wa iye mwini. Pa nthawi ina mu ulamulilo wake, iye anayamba kunyalanyaza malamulo a Mulungu. Mwacitsanzo, limodzi mwa malamulowo linali lakuti mfumu yaciheberi siyenela ‘kudziculukitsila akazi kuti mtima wake ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Koma Solomo ananyalanyaza lamulo limeneli, ndipo anadzitengela akazi 700 komanso ena apambali 300. Ambili mwa akaziwo anali acikunja. (1 Maf. 11:1-3) Mwina iye anaganiza kuti kucita zimenezo kunalibe vuto. Mulimonsemo, m’kupita kwa nthawi, Solomo anakumana na mavuto obwela cifukwa cosiya Yehova.—1 Maf. 11:9-13.

13. Kodi tingaphunzile ciyani pa kudzicepetsa kwa Yesu?

13 Yesu anapitiliza kudziona moyenela na kukhala wodzicepetsa. Asanabwele padziko lapansi, iye anadzipangila mbili yabwino potumikila Yehova. Kudzela mwa Yesu, “zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” (Akol. 1:16) Pa ubatizo wake, mwacionekele iye anakumbukila zinthu zambili zimene anakwanitsa kucita ali limodzi na Atate wake. (Mat. 3:16; Yoh. 17:5) Koma zimenezo sizinapangitse Yesu kukhala wonyada. Komanso, iye sanacite zinthu moonetsa kuti amaposa ena. Anauza ophunzila ake kuti iye anabwela padziko lapansi “[osati] kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila ndi kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.” (Mat. 20:28) Iye modzicepetsa anakambanso kuti sanacite ciliconse congoganiza payekha. (Yoh. 5:19) Kunali kudzicepetsa cotani nanga kumene Yesu anaonetsa! Iye n’citsanzo cabwino koposa cimene tingatengele.

14. Kodi tiphunzila ciyani kwa Yesu pa nkhani yodziona moyenela?

14 Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti azidziona moyenela. Pa nthawi ina, iye anawatsimikizila kuti: “Tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliŵelenga.” (Mat. 10:30) Mfundo imeneyi ni yolimbikitsa kwa ife, maka-maka tikamadziona mosayenela. Izi zionetsa kuti Atate wathu wakumwamba amasamala kwambili za ife, ndipo ndife a mtengo wapatali kwa iye. Sitiyenela kukaikila mwayi umene Yehova watipatsa wokhala alambili ake, komanso wokalandila moyo wosatha, n’kumadziona kuti sindife oyenelela madalitso amenewa.

Kodi kudziona mosayenela kungatimanitse madalitso otani? (Onani ndime 15) *

15. (a) Kodi Nsanja ya Mlonda ina inati tiyenela kukhala na kapenyedwe koyenela kotani ka ife eni? (b) Malinga na zithunzi zili pa tsamba 24, tikamadziona mosayenela, timaphonya madalitso otani?

15 Zaka ngati 15 zapitazo, Nsanja ya Mlonda inakamba kuti tiyenela kudziona moyenela. Inati: “Sitiyenela kuganiza kuti ndife ofunika kwambili mpaka kuyamba kunyada, komanso tisacite kudzitsitsa monyanyila n’kufika pomadziona ngati ndife opanda nchito. Colinga cathu ciyenela kukhala comadziona moyenela, moganizila zinthu zimene timakwanitsa kucita na zimene sitingathe kucita. Mlongo wina ananena mfundo imeneyi motele: ‘Nimadziŵa kuti sindine munthu woipitsitsa kuposa wina aliyense; koma panthawi imodzimodziyo nimadziŵanso kuti sindine munthu wabwino kwambili kuposa wina aliyense. Nili na makhalidwe abwino komanso nili na makhalidwe ena oipa, ndipo umu ni mmene aliyense alili.’” * Kodi mwaona cifukwa cake kuli kofunika kudziona moyenela?

16. N’cifukwa ciyani Yehova amatipatsa malangizo anzelu?

16 Kupitilila m’Mawu ake, Yehova amatipatsa malangizo anzelu. Iye amatikonda, ndipo amafuna kuti tizisangalala. (Yes. 48:17, 18) Conco, cinthu canzelu cimene tingacite kuti tikhale na cimwemwe coculuka, ni kuika patsogolo cifunilo ca Yehova mu umoyo wathu. Tikatelo, tidzapewa mavuto amene anthu okonda ndalama, nchito ya kuthupi, kapena odziona mosayenela amakumana nawo. Lekani kuti tonsefe tiyesetse kukhala anzelu na kukondweletsa mtima wa Yehova.—Miy. 23:15.

NYIMBO 94 Tiyamikila Mau a Mulungu

^ Solomo komanso Yesu anali anthu anzelu kwambili. Gwelo la nzelu zimenezo anali Yehova Mulungu. M’nkhani ino, tiona zimene tingaphunzile ku uphungu wouzilidwa wa Solomo komanso Yesu, pa nkhani ya mmene tiyenela kuonela ndalama, nchito ya kuthupi, komanso mmene timadzionela. Cina, tione mmene abale na alongo apindulila poseŵenzetsa mwanzelu uphungu wozikika pa Baibo pa mbali zimenezi.

^ Onani nkhani yakuti, “Mungacite Ciani Kuti Muzisangalala Ngati Mumagwila Nchito Yolimba?” mu Nsanja ya Mlonda ya February 1, 2015.

^ Onani nkhani yakuti “Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Wosangalala” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2005.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: John na Tom ni abale acinyamata amene ali mu mpingo umodzi. John amathela nthawi yoculuka kusamalila motoka yake. Koma Tom amaseŵenzetsa motoka yake pothandiza ena kuyenda mu ulaliki na kupita ku misonkhano yampingo.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: John amaseŵenza ovataimu. Iye safuna kukhumudwitsa abwana ake. Conco, nthawi iliyonse abwana ake akamuuza kuti agwile ovataimu John amavomela. Koma madzulo amodzi-modziwo, Tom, amene ni mtumiki wothandiza, wapita ku ulendo waubusa na mkulu wina. Kumbuyoku, Tom anauza abwana ake kuti madzulo alionse amapatula nthawi yocita zinthu zokhudza kulambila Yehova.

^ MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: John amangocita zofuna zake. Koma Tom, amene amaika za kuuzimu patsogolo pa zofuna zake, wapeza mabwenzi ambili pamene akuthandiza kukonza Bwalo la Misonkhano.