NKHANI YOPHUNZILA 21
Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Athu
“Timakhala ndi cikhulupililo kuti tilandila zinthu zimene tamupemphazo.”—1 YOH. 5:15.
NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde
ZIMENE TIKAMBILANE a
1-2. Tingakayikile ciyani za mapemphelo athu?
KODI munayamba mwakayikilapo ngati Yehova amayankha mapemphelo anu? Ngati n’conco, sindinu nokha. Abale na alongo athu ambili anamvapo conco, maka-maka pamene anakumana na mavuto aakulu. Nafenso tikamavutika, cingakhale covuta kuona mmene Yehova akuyankhila mapemphelo athu.
2 Tiyeni tikambilane cifukwa cake ndife otsimikiza kuti Yehova amayankha mapemphelo a alambili ake. (1 Yoh. 5:15) Tikambilanenso mafunso aya: N’cifukwa ciyani nthawi zina tingamaone kuti Yehova sakuyankha mapemphelo athu? Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphelo athu?
YEHOVA ANGAYANKHE M’NJILA IMENE SITIKUYEMBEKEZELA
3. N’cifukwa ciyani Yehova amafuna kuti tizipemphela kwa iye?
3 Malemba amatitsimikizila kuti Yehova amatikonda kwambili, komanso kuti ndife amtengo wapatali kwa iye. (Hag. 2:7; 1 Yoh. 4:10) Ndiye cifukwa cake amatilimbikitsa kupempha thandizo lake. (1 Pet. 5:6, 7) Iye amafuna kutithandiza kuti tikhalebe naye pa ubale, komanso kuti tithane nawo mavuto athu.
4. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amayankha mapemphelo a alambili ake? (Onaninso cithunzi.)
4 Tikamaŵelenga m’Baibo, nthawi zambili timapeza kuti Yehova anali kuyankha mapemphelo a alambili ake. Ganizilani za Mfumu Davide. Mu umoyo wake wonse, iye anayang’anizana na adani ambili oopsa. Koma nthawi zonse anali kupempha thandizo kwa Yehova m’pemphelo. Pa nthawi ina, iye anacondelela Mulungu kuti: “Inu Yehova, imvani pemphelo langa. Chelani khutu pamene ndikucondelela. Ndiyankheni mogwilizana ndi kukhulupilika kwanu ndi cilungamo canu.” (Sal. 143:1) Yehova anayankha mapemphelo a Davide opempha cipulumutso. (1 Sam. 19:10, 18-20; 2 Sam. 5:17-25) Mwacidalilo Davide anati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.” Nafenso tingakhale na cidalilo cimeneco.—Sal. 145:18.
5. Kodi Yehova nthawi zonse anali kuyankha mapemphelo a alambili ake akale mmene iwo anali kuyembekezela? Fotokozani citsanzo. (Onaninso cithunzi.)
5 Nthawi zina, Yehova angayankhe mapemphelo athu m’njila imene sitikuyembekezela. Umu ni mmene zinalili kwa mtumwi Paulo. Anapempha Mulungu kuti am’cotsele “munga m’thupi.” Katatu konse, Paulo anaipemphelela vuto lakelo. Kodi Yehova anayankha mapemphelowo? Inde, koma osati mmene Paulo anali kuyembekezela. M’malo mocotsa vutolo, Yehova anam’patsa mphamvu zofunikila kuti apitilize kum’tumikila mokhulupilika.—2 Akor. 12:7-10.
6. N’cifukwa ciyani nthawi zina tingaone monga Yehova sakuyankha mapemphelo athu?
6 Ifenso nthawi zina mapemphelo athu angayankhidwe m’njila imene sitinaiyembekezele. Koma sitikayikila kuti Yehova amadziŵa bwino mmene angatithandizile. Iye “angathe kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Pa cifukwa cimeneci, angayankhe mapemphelo athu panthawi kapena m’njila imene sitinali kuyembekezela.
7. N’cifukwa ciyani nthawi zina tingafunike kusintha zopempha zathu? Fotokozani citsanzo.
7 Tikafika pocidziŵa bwino cifunilo ca Yehova, tingafunike kusintha zimene timapempha kwa iye. Ganizilani citsanzo ca m’bale Martin Poetzinger. Atangokwatila, anamangidwa na kuponyedwa m’ndende yacibalo mu ulamulilo wa Nazi. Poyamba, anali kupempha Yehova kuti amasulidwe na colinga coti akasamalile mkazi wake, na kuyambilanso kulalikila. Komabe, patapita milungu iŵili, iye sanaone cizindikilo coonetsa kuti Yehova akumutsegulila njila yakuti atuluke m’ndendemo. Conco, anayamba kupemphela kuti: “Yehova, conde n’thandizeni kuzindikila zimene mufuna kuti nicite.” Ndiyeno anayamba kuganizila mavuto amene abale ena m’ndendemo anali kukumana nawo. Ambili a iwo anali kudela nkhawa kwambili akazi awo komanso ana awo. Kenako, m’bale Poetzinger anapemphela kuti: “Zikomo Yehova ponipatsa utumiki watsopano. N’thandizeni kuti nizilimbikitsa abale anga.” Ndipo iye anacita zimenezi kwa zaka 9 zimene anakhala m’ndendeyo!
8. Ni mfundo yofunika iti imene tiyenela kuikumbukila tikamapemphela?
8 Tizikumbukila kuti Yehova ali na colinga cimene adzacikwanilitsa panthawi yake yoikika. Colingaco cimaphatikizapo kucotselatu mavuto onse amene amapangitsa anthu kuvutika masiku ano—monga matsoka azacilengedwe, matenda, komanso imfa. Yehova adzakwanilitsa colinga cake pogwilitsa nchito Ufumu wake. (Dan. 2:44; Chiv. 21:3, 4) Koma pakalipano, Yehova walola Satana kuti alamulile dzikoli. b (Yoh. 12:31; Chiv. 12:9) Ngati Yehova angathetse mavuto palipano, zingaoneke monga Satana akulamulila bwino. Pamene tikuyembekezela kuti Yehova adzakwanilitse ena mwa malonjezo ake, tisaganize kuti anatisiya popanda thandizo. Tiyeni tikambilane zina mwa njila zimene Yehova amatithandizila.
MMENE YEHOVA AMAYANKHILA MAPEMPHELO MASIKU ANO
9. Kodi Yehova angatithandize bwanji tikafuna kupanga zisankho? Fotokozani citsanzo.
9 Amatipatsa nzelu. Yehova analonjeza kuti adzatipatsa nzelu zofunikila kuti tipange zisankho zabwino. Timafunikila nzelu zaumulungu, maka-maka popanga zisankho zimene zidzatikhudza kwa moyo wathu wonse, monga kukhalabe mbeta kapena kuloŵa m’banja. (Yak. 1:5) Ganizilani za mlongo Maria amene ni mbeta. c Anali kutumikila mwacimwemwe monga mpainiya wa nthawi zonse pamene anapeza m’bale. Iye anati: “Titafika podziŵana bwino, tinayamba kukondana kwambili. N’nadziŵa kuti apa niyenela kupanga cisankho. Conco, n’naipemphelela kwambili nkhani imeneyi. N’nafunikila citsogozo ca Yehova, koma n’nadziŵa kuti iye sanganipangile cisankho.” Mlongoyo amaona kuti Yehova anayankha mapemphelo ake opempha nzelu. Motani? Pofufuza m’zofalitsa zathu, anapeza nkhani zimene zinam’thandiza pa nkhaniyo. Cina, anatsatila ulangizi wa amayi ake okhulupilika. Ulangizi umenewo unam’thandiza kudziŵa zocita. Ndipo pothela pake, anapanga cisankho canzelu.
10. Malinga na Afilipi 4:13, kodi Yehova amacita ciyani kuti athandize alambili ake? Fotokozani citsanzo. (Onaninso cithunzi.)
10 Amatipatsa mphamvu kuti tipilile. Monga zinalili kwa mtumwi Paulo, nafenso Yehova angatipatse mphamvu kuti tipilile mayeso. (Ŵelengani Afilipi 4:13.) Onani mmene Yehova anathandizila m’bale wina dzina lake Benjamin kupilila zinthu zovuta pa umoyo wake. Ali mnyamata, iye na a m’banja lake anakhala nthawi yoculuka mu msasa wa anthu othaŵa kwawo mu Africa. Iye anati: “N’nali kupemphela kwa Yehova kuti anipatse mphamvu zonithandiza kucita zinthu zom’kondweletsa. Anayankha mapemphelo anga mwa kunipatsa mtendele wa mumtima, kunilimbitsa mtima kuti nipitilize kulalikila, komanso kunipatsa zofalitsa kuti nikhalebe wolimba kuuzimu.” Anapitiliza kuti: “Kuŵelenga nkhani za abale na alongo, na kuona mmene Yehova anawathandizila kupilila, kunanithandiza kuti nikhalebe wokhulupilika.”
11-12. Kodi Yehova amaseŵenzetsa bwanji banja lathu lauzimu poyankha mapemphelo athu? (Onaninso cithunzi.)
11 Amagwilitsa nchito banja lathu lauzimu. Usiku woti maŵa apeleka moyo wake monga nsembe, Yesu anapemphela mocokela pansi pamtima. Iye anacondelela Yehova kuti amupewetse ku citonzo cimene anthu angamuneneze naco cakuti ni wonyoza Mulungu. M’malo mocita zimenezo, Yehova anathandiza Yesu mwa kutumiza mmodzi wa abale ake a kumwamba, kapena kuti mngelo kudzam’limbikitsa. (Luka 22:42, 43) Nafenso Yehova angatithandize poseŵenzetsa m’bale kapena mlongo kuti atilimbikitse mwa kutitumila foni kapena kudzaticezela. Tonsefe tiyenela kumafuna-funa mipata yokamba “mawu abwino” kwa okhulupilila anzathu.—Miy. 12:25.
12 Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Miriam. Patapita milungu ingapo mwamuna wake atamwalila, iye anali kukhala yekha-yekha pa nyumba, ndipo anali na cisoni komanso wopsinjika maganizo. Anali kukhalila kulila, ndipo anali kufunika munthu wokamba naye. Iye anati: “N’nalibe mphamvu zotumila foni aliyense. Conco n’nali kungopemphela kwa Yehova. Nili mkati molila na kupemphela, n’nangomva foni yalila. Anatuma ni mkulu, amenenso anali mnzanga.” Mlongo Miriam analandila citonthozo kwa mkuluyo na mkazi wake. Iye sakayikila kuti Yehova ndiye analimbikitsa m’baleyo kuti am’tumile foni.
13. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yehova amayankhila mapemphelo athu, poseŵenzetsa anthu osamulambila.
13 Angaseŵenzetse anthu amene samulambila. (Miy. 21:1) Nthawi zina, Yehova amayankha mapemphelo a anthu ake mwa kusonkhezela anthu osakhulupilila kuti awathandize. Mwacitsanzo, iye anasonkhezela Mfumu Aritasasita kuti alole Nehemiya kubwelela ku Yerusalemu kukathandiza pa nchito yomanganso mzinda. (Neh 2:3-6) Masiku anonso, Yehova angapangitse anthu amene samulambila kuti atithandize tikafunikila thandizo.
14. N’ciyani cakulimbikitsani pa cocitika ca mlongo Soo Hing? (Onaninso cithunzi.)
14 Mlongo wina dzina lake Soo Hing, anaona kuti Yehova anam’thandiza kupitila mwa dokotala wake. Mwana wake wamwamuna ali na matenda angapo okhudza maganizo. Pamene mwanayo anapezeka pa ngozi yaikulu, mlongoyo na mwamuna wake analeka nchito kuti azimusamalila. Izi zinabweletsa mavuto a zacuma. Mlongo Soo Hing anati anaona monga wafika poti sangathenso kupilila. Iye anakhuthulila Yehova nkhawa zake, kum’pempha thandizo. Dokotala uja anathandiza mlongoyo na banja lake. Iye anawathandiza kulandila cithandizo ca boma, na kupeza nyumba yochipako. Pambuyo pake, mlongo Soo Hing anati: “Tinaona dzanja la Yehova panthawiyo. Zoonadi, iye ni ‘Wakumva pemphelo.’”—Sal. 65:2.
TIFUNIKILA CIKHULUPILILO KUTI TIZINDIKILE YANKHO KU MAPEMPHELO ATHU NA KULIVOMELEZA
15. N’ciyani cinathandiza mlongo wina kuzindikila kuti mapemphelo ake anali kuyankhidwa?
15 Nthawi zambili, mapemphelo athu sayankhidwa mogometsa ayi. Koma mayankho amene timalandila amakhala okwanila potithandiza kukhalabe okhulupilika kwa Atate wathu wakumwamba. Conco, muzikhala chelu kuona mmene Yehova akuyankhila mapemphelo anu. Mlongo wina dzina lake Yoko, anali kuona monga Yehova sayankha mapemphelo ake. Koma pambuyo pake anayamba kulemba zimene wapempha Yehova. Patapita nthawi, iye anayang’ana m’buku lake ndipo anazindikila kuti Yehova anali atayankha mapemphelo ake ambili, kuphatikizapo aja amene mlongoyo anawaiŵala. Conco, nthawi na nthawi tiziima na kuganizila mmene Yehova akuyankhila mapemphelo athu.—Sal. 66:19, 20.
16. Tingaonetse bwanji cikhulupililo pa nkhani ya mapemphelo? (Aheberi 11:6)
16 Timaonetsa cikhulupililo mwa kupemphela kwa Yehova, komanso kuvomeleza yankho yake mulimonse mmene angayankhile. (Ŵelengani Aheberi 11:6.) Ganizilani citsanzo ca m’bale Mike na mkazi wake Chrissy. Iwo anali na colinga cokatumikila pa Beteli. Mike anati: “Ine na mkazi wanga tinafunsila utumikiwu kwa zaka zambili, ndipo tinapemphela kwa Yehova maulendo ambili za colingaci, koma sitinaitanidwe panthawi yonseyo.” M’bale Mike na mkazi wake anakhalabe na cidalilo cakuti Yehova ndiye adziŵa bwino mmene angawaseŵenzetsele mu utumiki wake. Iwo anapitiliza kucita zimene angathe, mwa kutumikila monga apainiya anthawi zonse kumalo osoŵa, komanso kuthandizila pa nchito zomanga za gulu. Pano tikamba, ali m’nchito yadela. M’bale Mike anati: “Si nthawi zonse pamene Yehova anayankha mapemphelo athu mmene tinali kuyembekezela. Koma anawayankha ndithu mapemphelowo, ndipo anatelo m’njila yabwino kuposa mmene tinali kuganizila.”
17-18. Malinga na Salimo 86:6, 7, kodi tingakhale na cidalilo cotani?
17 Ŵelengani Salimo 86:6, 7. Wamasalimo Davide anali wotsimikiza kuti Yehova anamva komanso kuyankha mapemphelo ake. Inunso mungakhale na cidalilo cimeneco. Zitsanzo zimene takambilana m’nkhani ino, zatitsimikizila kuti Yehova adzatipatsa nzelu komanso mphamvu zofunikila kuti tipilile. Iye angaseŵenzetse banja lathu lauzimu, kapena aja amene sam’lambila kuti atithandize.
18 Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene Yehova angayankhe mapemphelo athu mmene tifunila, tidziŵa kuti amayankhabe. Iye amatipatsa zimene tikufunikila komanso panthawi yake. Conco musaleke kupemphela, muli na cidalilo cakuti Yehova adzakusamalilani palipano, komanso kuti ‘adzakhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse’ m’dziko latsopano.—Sal. 145:16.
NYIMBO 46 Tikuyamikani Yehova
a Yehova amatitsimikizila kuti amayankha mapemphelo athu ogwilizana na cifunilo cake. Tikakumana na mavuto, timakhala otsimikiza kuti iye adzatithandiza kuti tikhalebe okhulupilika kwa iye. Tiyeni tikambilane mmene Yehova amayankhila mapemphelo athu.
b Kuti mudziŵe cifukwa cake Yehova walola Satana kulamulila dziko, onani nkhani yakuti, “Muziika Maganizo Anu pa Nkhani Yaikulu,” yofalitsidwa mu Nsanja ya Mlonda ya June 2017.
c Maina ena asinthidwa.
d MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Mayi na mwana wake wamkazi akufika m’dziko lina ngati anthu othaŵa kwawo. Okhulupilila anzawo akuwalandila na manja aŵili, komanso kuwathandiza.