Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 23

Musalole “Lawi la Ya” Kuzima

Musalole “Lawi la Ya” Kuzima

“Kuyaka [kwa cikondi] kuli ngati kuyaka kwa moto. Cikondico ndi lawi la Ya.”—NYIMBO 8:6.

NYIMBO 131 “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi Baibo imacifotokoza motani cikondi ceniceni?

 “KUYAKA [kwa cikondi] kuli ngati kuyaka kwa moto. Cikondico ndi lawi la Ya. Madzi ambili sangathe kuzimitsa cikondi, ndipo mitsinje singacikokolole.” b (Nyimbo 8:6, 7) Iyi ni njila yabwino kwambili yofotokozela cikondi ceniceni! Mawu amenewa amatsimikizila okwatilana kuti n’zotheka ndithu kukhala na cikondi cosatha.

2. Kodi okwatilana angacite ciyani kuti cikondi cawo cisazime?

2 Kuti okwatilana akhale na cikondi cosatha, pali zimene ayenela kucita. Mwacitsanzo, kuti moto usazime timasonkheza nkhuni. Tikaleka kusonkheza, pothela pake moto umazima. Mofananamo, mwamuna na mkazi wake ayenela kusonkheza cikondi cawo kuti cisazime. Nthawi zina, okwatilana angaone kuti cikondi cawo cayamba kuzima, maka-maka akakumana na mavuto azacuma, matenda, kapena akakhala na udindo wolela ana. Ngati muli pabanja, kodi mungatani kuti musalole “lawi la Ya” kuzima? M’nkhani ino, tikambilane njila zitatu zokuthandizani kuti cikondi canu cisazime, komanso kuti mukhale na banja lacimwemwe. c

MUSALEKE KULIMBITSA UBALE WANU NA YEHOVA

Monga Yosefe na Mariya, mwamuna na mkazi wake ayenela kukhala pa ubale wolimba na Yehova (Onani ndime 3

3. Kodi ubale wolimba na Yehova ungawathandize bwanji okwatilana kulimbitsa cikondi cawo? (Mlaliki 4:12) (Onaninso cithunzi.)

3 Kuti “lawi la Ya” lisazime, mwamuna na mkazi wake ayenela kulimbitsa ubale wawo na Yehova. Kodi ubalewo ungawathandize bwanji? Okwatilana akamaona ubale wawo na Atate wawo wakumwamba kukhala wofunika, amaseŵenzetsa ulangizi wake. Akatelo, amapewa komanso kuthana na mavuto amene angapangitse cikondi cawo kuzima. (Ŵelengani Mlaliki 4:12.) Anthu auzimu amayesetsa kutengela makhalidwe a Yehova, monga kukoma mtima, kuleza mtima, komanso kukhululuka. (Aef. 4:32–5:1) Okwatilana akamaonetsana makhalidwe amenewa, cikondi cawo cimakula. Mlongo Lena, amene wakhala mu ukwati zaka zoposa 25 anati: “Ngati mnzako wa mu ukwati ni wauzimu, n’cosavuta kum’konda na kum’lemekeza.”

4. N’cifukwa ninji Yehova anasankha Yosefe na Mariya kuti akhale makolo a Mesiya?

4 Ganizilani citsanzo ici ca m’Baibo. Pakati pa mbadwa zonse za Davide, Yehova anasankha Yosefe na Mariya kuti akhale makolo a Mesiya. Cifukwa ninji? Cifukwa onse aŵili anali pa ubale wolimba na Yehova, ndipo anadziŵa kuti cifukwa com’konda, banja lawo lidzakhala lolimba mwauzimu. Inu amene muli pabanja, kodi mungaphunzile ciyani kwa Yosefe na Mariya?

5. Kodi amuna angaphunzile ciyani kwa Yosefe?

5 Mofunitsitsa Yosefe anatsatila citsogozo ca Yehova. Mwa ici, anakhala mwamuna wabwino. Katatu konse, Mulungu anam’patsa malangizo okhudza banja lake. Pa nthawi zonsezo, anatsatila malangizowo ngakhale pamene zinali zovuta kutelo. (Mat. 1:20, 24; 2:13-15, 19-21) Cifukwa cotsatila malangizo a Mulungu, Yosefe anateteza Mariya, kum’thandiza, komanso kum’samalila. Izi zinapangitsa Mariya kuti azim’konda Yosefe na kum’lemekeza. Inu amuna, mungatengele citsanzo ca Yosefe mwa kutsatila ulangizi wa m’Baibo posamalila banja lanu. d Mukatelo, ngakhale pamene n’zovuta, mumaonetsa kuti mumam’konda mkazi wanu, ndipo mumalimbitsa ukwati wanu. Mlongo wina ku Vanuatu, amene wakhala m’banja zaka zoposa 20 anati: “Mwamuna wanga akamafufuza na kutsatila malangizo a m’Baibo, nimam’lemekeza kwambili. Nimamva kukhala wotetezeka, ndipo sinimakayikila zisankho zake.”

6. Kodi akazi angaphunzile ciyani kwa Mariya?

6 Mariya anali pa ubale wolimba na Yehova, ndipo uzimu wake sunadalile Yofese. Iye anali kuwadziŵa bwino Malemba, ndipo anali kupatula nthawi yowasinkhasinkha. (Luka 2:19, 51) Mosakayikila, uzimu wake unam’pangitsa kukhala mkazi wabwino. Masiku ano, akazi ambili a pabanja amayesetsa kutengela citsanzo cake. Mwacitsanzo, mlongo Emiko anati: “Pamene n’nali mbeta, n’nali kucita zauzimu panekha. N’taloŵa m’banja, cikhulupililo canga cinayamba kudalila pa mwamuna wanga cifukwa ndiye anali kupemphela, komanso kucititsa kulambila kwa pabanja. Koma n’nazindikila kuti niyenela kulimbitsa ubale wanga na Yehova panekha. Conco, n’nayamba kupatula nthawi yopemphela, yoŵelenga Malemba, na kusinkhasinkha za iye.” (Agal. 6:5) Inu akazi, mukamalimbitsa ubale wanu na Yehova, mwamuna wanu azikutamandani na kukukondani kwambili.—Miy. 31:30.

7. Kodi okwatilana angaphunzile ciyani kwa Yosefe na Mariya za kulambila capamodzi?

7 Yosefe na Mariya analinso kucitila pamodzi zauzimu kuti alimbitse ubale wawo na Yehova. Iwo anadziŵa kuti kulambila Yehova capamodzi monga banja n’kofunika kwambili. (Luka 2:22-24, 41; 4:16) Mwina zinali zovuta kucita zimenezi, maka-maka banja litakula. Koma anakwanitsa. Ici n’citsanzo cabwino ngako kwa okwatilana masiku ano. Ngati muli na ŵana, monga Yosefe na Mariya, cingakhale covuta kupezeka kumisonkhano kapena kucita kulambila kwa pabanja. Mwina cingakhalenso covuta kwambili kupeza nthawi yoŵelenga kapena kupemphela monga okwatilana. Koma kumbukilani kuti mukamalambila Yehova capamodzi, mumamuyandikila kwambili komanso mumagwilizana. Conco, ikani kulambila Mulungu patsogolo.

8. Kodi okwatilana amene m’banja mwawo muli kusamvana angacite ciyani kuti azipindula kwambili na kulambila kwa pabanja?

8 Bwanji ngati m’banja mwanu muli kusamvana? Cingakhale covuta kuti mucite kulambila kwa pabanja. Ngati zilidi conco, muzisankha nkhani zazifupi komanso zosangalatsa kwa nonse aŵili. Izi zidzakuthandizani kulimbitsa cikondi pakati panu, na kukulitsa cifuno cocita zinthu zauzimu capamodzi.

MUZIPATULA NTHAWI YOCEZA

9. N’cifukwa ciyani mwamuna na mkazi wake ayenela kupeza nthawi yoceza?

9 Inu okwatilana, mungakulitsenso cikondi canu mwa kupatula nthawi yocezako pamodzi. Izi zidzakuthandizani kudziŵa mmene mnzanu amaonela zinthu, komanso mmene amamvela. (Gen. 2:24) Onani zimene Lilia na Ruslan anazindikila atangokwatilana zaka zoposa 15 zapitazo. Mlongoyo ananena kuti: “Tinaona kuti sitinali kukhala na nthawi yocezako mmene tinali kuganizila, cifukwa tinali kutangwanika na nchito, kusamalila pakhomo, komanso kulela ana. Tinazindikila kuti tikapanda kupatula nthawi yoceza aŵiliŵili, tingatalikilane.”

10. Kodi okwatilana angaseŵenzetse bwanji mfundo ya pa Aefeso 5:15, 16?

10 Kodi inu okwatilana mungacite ciyani kuti muziceza pamodzi? Muzipatula nthawi yokhalako aŵiliŵili. (Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.) M’bale Ozondu wa ku Nigeria anati: “Pa pulogilamu yanga ya zocita, nimaikaponso nthawi yoceza na mkazi wanga, ndipo nimaonetsetsa kuti tacitadi zimenezo.” (Afil. 1:10) Onani mmene mlongo Anastasia, mkazi wa woyang’anila wadela ku Moldova amagwilitsila nchito bwino nthawi yake. Iye anati: “Nimagwililatu nchito zanga pamene mwamuna wanga akusamalila maudindo ake. Izi zimatithandiza kupeza nthawi yocezako pamodzi pambuyo pake.” Bwanji ngati zocita zimakuculukilani moti n’kusoŵa nthawi yocezako pamodzi?

Ni nchito ziti zimene mungacitile pamodzi monga banja? (Onani ndime 11-12)

11. Ni zinthu zotani zimene Akula na Purisikila anali kucitila pamodzi?

11 Okwatilana angaphunzile zambili kwa Akula na Purisikila. Banja limenelo linali kukondedwa na Akhristu oyambilila. (Aroma 16:3, 4) Baibo siikamba zambili zokhudza banja lawo. Imangoonetsa kuti iwo anali kucitila zinthu pamodzi, monga kugwila nchito, kulalikila, na kuthandiza anthu ena. (Mac. 18:2, 3, 24-26) Ndipo nthawi zonse, Baibo imachula Akula na Purisikila ali limodzi.

12. Kodi mwamuna na mkazi wake angacite ciyani kuti azipeza nthawi yoculuka yoceza? (Onaninso cithunzi.)

12 Kodi okwatilana angatengele bwanji citsanzo ca Akula na Purisikila? Ganizilani nchito zambili zimene inu muli nazo, na zimene mnzanu wa mu ukwati ali nazo. Kodi mungagwilile pamodzi zina mwa nchitozo, m’malo mocita payekha-payekha? Mwacitsanzo, Akula na Purisikila anali kulalikila pamodzi. Kodi inunso mumacita zimenezi kaŵili-kaŵili? Akula na Purisikila analinso kuseŵenzela pamodzi. Mwina inu na mnzanu wa mu ukwati simugwila nchito yofanana. Koma kodi mungagwilileko pamodzi nchito zapakhomo? (Mlal. 4:9) Mukamagwilila pamodzi nchitozo, mumakhala ogwilizana, ndipo mumakhala na mpata woceza. Robert na mkazi wake Linda akhala mu ukwati zaka zopitilila 50. Iye anakamba kuti: “Kunena zoona, sitikhala na nthawi yoculuka yocitila pamodzi zosangalatsa. Koma nikamatsuka mbale ndiyeno mkazi wanga akuzipukuta, kapena nikamaseula pakhomo ndiyeno mkazi wanga wabwela kudzanithandiza, nimasangalala kwambili. Tikamacitila zinthu pamodzi timayandikilana, ndipo cikondi cathu cimapitiliza kukula.”

13. Kodi mwamuna na mkazi wake ayenela kucita ciyani kuti azigwilizana kwambili?

13 Koma kumbukilani kuti kupatula nthawi yokhalako aŵiliŵili, pakokha sikokwanila kuti mukhale ogwilizana. Mlongo wina ku Brazil amene ali pabanja ananena kuti: “Popeza masiku ano pali zotangwanitsa zambili, n’capafupi kuganiza kuti mumakhala na nthawi yokwanila yoceza, cifukwa mukhala nyumba imodzi. Koma naphunzila kuti kuceza capamodzi ni sitepe loyamba. Sitepe laciŵili ni kumuonetsa cidwi mnzako wa mu ukwati poceza.” Onani mmene Bruno na mkazi wake Tays amacitila zimenezi. Iye anakamba kuti: “Tikamaceza tili aŵili, timaika pambali mafoni athu kuti asatisokoneze.”

14. Kodi okwatilana angacite ciyani ngati kuceza aŵiliŵili sikuwasangalatsa?

14 Koma bwanji ngati inu na mnzanu wa mu ukwati kuceza aŵiliŵili sikumakusangalatsani? Mwina n’cifukwa cakuti mumakonda zinthu zosiyana, kapena mumakhumudwitsana. Kodi mungacitenji? Ganizilani citsanzo ca moto cimene tachula kumayambililo. Timayatsa moto na tunkhuni tung’ono-tung’ono, ndipo sukhala waukulu nthawi yomweyo. Kuti ukule, pang’ono-pang’ono timayamba kuusonkheza na nkhuni zikulu-zikulu. Mofananamo, mungayambe mwa kucezako kwa mphindi zocepa tsiku lililonse. Yesani kucita zinthu zimene nonse aŵili mungasangalale nazo, osati zimene zingabweletse mkangano. (Yak. 3:18) Mwakutelo, cikondi canu cingayambenso kuyaka.

MUZIPATSANA ULEMU

15. N’cifukwa ciyani ulemu ni wofunika m’banja kuti cikondi cisazime?

15 Ulemu ni wofunika kwambili mu ukwati. Uli ngati mpweya umene umathandiza kuti moto uyake. Popanda mpweya umenewu, moto umazima. Mofananamo, ngati okwatilana sapatsana ulemu, cikondi cawo cingazime. Koma mwamuna na mkazi akamayesetsa kulemekezana, amateteza cikondi cawo kuti cisazime. Komabe, kumbukilani kuti cofunika kwambili ni mnzanu wa mu ukwati kumva kuti mumam’lemekeza, osati inuyo kungoganiza kuti mumam’lemekeza. Penny na mwamuna wake Aret akhala m’banja zaka zoposa 25. Mlongoyo anafotokoza kuti: “Cifukwa copatsana ulemu, timakondana kwambili. Timakhala omasuka kupelekapo malingalilo, cifukwa aliyense amaona malingalilo a mnzake kukhala ofunika.” N’ciyani cimene mungacite kuti mnzanu wa mu ukwati adzimva kuti mumam’lemekeza? Ganizilani citsanzo ca Abulahamu na Sara.

Mwamuna wacikhristu ayenela kulemekeza mmene mkazi wake akumvela mwa kumvetsela akamalankhula (Onani ndime 16)

16. Kodi amuna okwatila angaphunzile ciyani kwa Abulahamu? (1 Petulo 3:7) (Onaninso cithunzi.)

16 Abulahamu anali kum’lemekeza Sara. Anali kumvetsela malingalilo ake, na kuganizila mmene anali kumvela. Panthawi ina, Sara anapsinjika maganizo moti anauza Abulahamu mmene anali kumvela, ndipo anamuimba mlandu. Kodi Abulahamu anamuyankha mwaukali? Ayi. Iye anali kudziŵa kuti Sara anali mkazi wogonjela. Abulahamu anamvetsela, ndipo anayesa kupeza njila yothetsela vutolo. (Gen. 16:5, 6) Kodi tiphunzilapo ciyani? Amunanu, muli na udindo wopanga zisankho za banja lanu. (1 Akor. 11:3) Koma popanga zisankho, muyenela kumvako maganizo a mkazi wanu coyamba, maka-maka ngati cisankhoco cikum’khudza nayenso. (1 Akor. 13:4, 5) Nthawi zina, mkazi wanu angapsinjike maganizo, ndipo angafune kukuuzani mmene akumvela. Kodi mumam’lemekeza mwa kumvetsela mwachelu akamalankhula? (Ŵelengani 1 Petulo 3:7.) Angela na mwamuna wake Dmitry akhala mu ukwati zaka pafupifupi 30. Iye anafotokoza zimene mwamuna wake amacita pomupatsa ulemu. Anati: “Mwamuna wanga amakhala wokonzeka nthawi zonse kunimvetsela nikapsinjika maganizo, kapena nikamalankhula naye. Amanilezela mtima ngakhale pamene nili wokhumudwa.”

17. Kodi akazi okwatiwa angaphunzile ciyani kwa Sara? (1 Petulo 3:5, 6)

17 Sara anali kum’lemekeza Abulahamu mwa kugwilizana naye pa zisankho zake. (Gen. 12:5) Panthawi ina, Abulahamu analandila alendo mosayembekezela, ndipo anafuna kuwaceleza. Iye anapempha Sara kuti aleke zimene anali kucita kuti aphikile alendo mkate wambili. (Gen. 18:6) Mwamsanga Sara anacita zimene Abulahamu anam’pempha. Inu akazi okwatiwa, tengelani citsanzo ca Sara mwa kucilikiza zisankho za amuna anu. Mukatelo, mudzalimbitsa ukwati wanu. (Ŵelengani 1 Petulo 3:5, 6.) Dmitry amene tam’chula m’ndime yapita anafotokoza zimene mkazi wake amacita pom’lemekeza. Iye anati: “Nimayamikila kuti mkazi wanga amacilikiza zisankho zanga, olo kuti sizinam’komele. Ngati cisankhoco sicinayende bwino kwenikweni, iye samaniimba mlandu.” Ndithudi, n’cosavuta kukonda munthu amene amakulemekeza.

18. Kodi okwatilana amapindula bwanji akamateteza cikondi cawo kuti cisazime?

18 Masiku ano, Satana amafuna kuzimitsa cikondi pakati pa Akhristu okwatilana. Iye adziŵa kuti ngati cikondi pakati pawo cikuzima, angayambe kutalikilana na Yehova. Komabe, cikondi ceniceni sicizima. Conco, lolani kuti cikondi mu ukwati wanu cikhale ngati cija cochulidwa m’Nyimbo ya Solomo. Yesetsani kuika Yehova patsogolo mu ukwati wanu, kupatula nthawi yoceza muli aŵiliŵili, komanso kuganizila zofunikila za mnzanu wa mu ukwati na mmene akumvela. Mukatelo, ukwati wanu udzalemekeza Yehova amene ni Gwelo la cikondi ceniceni. Ndipo mofanana na moto umene ukusonkhezedwa, cikondi canu cidzapitiliza kuyaka mpaka kalekale.

NYIMBO 132 Lomba Ndise Thupi Limodzi

a Ukwati ni mphatso imene Yehova anapatsa anthu. Mphatso imeneyi imapeleka mwayi kwa okwatilana kusangalala na cikondi capadela pakati pawo. Koma nthawi zina, cikondico cingazime. Ngati muli pabanja, nkhani ino idzakuthandizani kuti cikondi canu cisazime, komanso kuti mukhale na banja lacimwemwe.

b Cikondi ceniceni cimene sicitha, cimachedwa “lawi la Ya.” Zili conco cifukwa Yehova ndiye Gwelo la cikondico.

c Olo kuti mnzanu wa mu ukwati si Mboni, mfundo za m’nkhani ino zingakuthandizeni kulimbitsa cikondi canu.—1 Akor. 7:12-14; 1 Pet. 3:1, 2.

d Mwacitsanzo, ganizilani ulangizi wothandiza wopezeka mu mpambo wa nkhani zakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja.” Nkhanizi zipezeka pa jw.org ku Chichewa, komanso pa JW Library®.