Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 24

N’zotheka Kuzikwanilitsa Zolinga Zanu Zauzimu

N’zotheka Kuzikwanilitsa Zolinga Zanu Zauzimu

“Tisaleke kucita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”—AGAL. 6:9.

NYIMBO 84 Kudzipeleka na Mtima Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi ambili a ife cakhala cotivuta kucita ciyani?

 KODI munadziikilapo colinga cauzimu, koma cinakuvutani kucikwanilitsa? b Ngati n’telo, sindinu nokha. Mwacitsanzo, m’bale Philip anadziikila colinga cakuti awongolele mapempelo ake komanso kupemphela pafupi-pafupi. Koma cinali kumuvuta kupeza nthawi yopemphela. Mlongo Erika anadziikila colinga cofika mofulumila pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki. Ngakhale n’conco, iye anali kufikabe mocedwa. M’bale Tomáš anayesa kangapo konse kuti akwanilitse colinga cake coŵelenga Baibo yonse. Iye anati: “Kuŵelenga Baibo sikunali konisangalatsa kwenikweni. N’nayesapo katatu konse, koma nthawi zonse n’nali kulekezela pa buku la Levitiko.”

2. N’cifukwa ciyani sitiyenela kulefuka ngati palipano sitinakwanilitse colinga cathu cauzimu?

2 Ngati palipano simunakwanilitse colinga canu, dziŵani kuti sindinu wolephela. Ngakhale kukwanilitsa colinga cacing’ono kumafuna nthawi na kulimbika. Kuyesetsa kuti mukwanilitse colinga canu, kumaonetsa kuti mumaona ubale wanu na Yehova kukhala wofunika kwambili, komanso kuti mumafuna kum’patsa zabwino kopambana. Yehova amayamikila kuyesetsa kwanu. Komabe, iye sayembekezela kuti mucite zimene simungathe. (Sal. 103:14; Mika 6:8) Conco, dziikileni colinga cimene mungacikwanilitse, malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wanu. Mukadziikila colinga, kodi mungacite ciyani kuti mucikwanilitse? Tiyeni tikambilane malingalilo otsatilawa.

KUKHALA NA CIKHUMBO N’KOFUNIKA KWAMBILI

Pemphelani kuti mukhale na cikhumbo ceniceni (Onani ndime 3-4)

3. N’cifukwa ninji kukhala na cikhumbo n’kofunika?

3 Cikhumbo n’cofunika kwambili kuti mukwanilitse zolinga zauzimu. Munthu akakhala na cikhumbo, amacita zotheka kuti akwanilitse colinga cake. Cikhumbo cimeneco cili monga mphepo imene imakankha boti kuti ikafike kumene ikupita. Ngati mphepo ikupitiliza kuwomba, woyendetsayo adzafika kumene akupita. Ndipo ngati mphepoyo ni yamphamvu, iye angafike mwamsanga. Mofananamo, tikakhala na cikhumbo, tidzatha kukwanilitsa zolinga zathu. M’bale David wa ku El Salvador anati: “Ukakhala na cikhumbo, umalimbikila. Sulola ciliconse kukulepheletsa kukwanilitsa colinga cako.” Ndiye mungatani kuti mukhale na cikhumbo camphamvu?

4. Kodi tingapemphelele ciyani? (Afilipi 2:13) (Onaninso cithunzi.)

4 Pemphelani kuti mukhale na cikhumbo cacikulu. Yehova angagwilitse nchito mzimu wake kuti akulimbikitseni kukwanilitsa colinga canu. (Ŵelengani Afilipi 2:13.) Nthawi zina timadziikila colinga, maka-maka cifukwa n’zimene tiyenela kucita, ndipo zimenezi zili bwino. Koma tingakhale tilibe cikhumbo ceniceni cofuna kukwanilitsa colingaco. Umu ni mmene zinalili kwa mlongo Norina wa ku Uganda. Iye anadziikila colinga cokhala na phunzilo la Baibo, koma analibe cikhumbo cifukwa coona kuti alibe luso lophunzitsa. N’ciyani cinam’thandiza? Mwiniwakeyo anati: “N’nayamba kupempha Yehova tsiku lililonse kuti anithandize kukulitsa cikhumbo cokhala na phunzilo la Baibo. Panthawi imodzimodziyo, n’nali kuyesetsa kunola luso langa la kuphunzitsa. Patapita miyezi ingapo, n’nazindikila kuti cikhumbo canga cayamba kukula. M’caka cimeneco, n’nakhala na maphunzilo a Baibo aŵili.”

5. Kodi tiyenela kusinkhasinkha ciyani kuti tikulitse cikhumbo cathu?

5 Muzisinkhasinkha zimene Yehova wakucitilani. (Sal. 143:5) Mtumwi Paulo anali kusinkhasinkha za cisomo ca Yehova pa iye, ndipo izi zinam’limbikitsa kum’tumikila molimbika. (1 Akor. 15:9, 10; 1 Tim. 1:12-14) Mofananamo, mukamasinkhasinkha zimene Yehova wakucitilani, mudzalimbikitsidwa kuti mukwanilitse colinga canu. (Sal. 116:12) Onani cimene cinathandiza mlongo wa ku Honduras kuti akwanilitse colinga cake cokhala mpainiya wanthawi zonse. Iye anati: “N’nali kuganizila za cikondi ca Yehova pa ine. Iye ananikokela m’gulu lake, ndipo amanisamalila na kuniteteza. Kusinkhasinkha zimenezi kunakulitsa cikondi canga pa iye, komanso cikhumbo canga cokhala mpainiya.”

6. N’ciyani cina cingatithandize kukulitsa cikhumbo cathu?

6 Ganizilani za mapindu a kukwanilitsa colinga canu. Onani cinathandiza mlongo Erika, amene tam’chula m’ndime yoyamba, kuti akwanilitse colinga cake. Iye anati: “N’nazindikila kuti n’nali kuphonya zambili nikafika mocedwa pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki. Koma nikafulumila, n’nali kukhala na mpata wopatsa moni abale na alongo, na kuceza nawo. Cina, n’nali kupindula na malangizo onithandiza kupeza cimwemwe mu ulaliki, komanso kunola maluso anga.” Mlongo Erika anaika maganizo ake pa mapindu a kufika mofulumila, ndipo anakwanilitsa colinga cake. Nanga inu mungaike maganizo anu pa mapindu ati? Ngati colinga canu cikhudza kuŵelengela Baibo kapena kupemphela, ganizilani mmene ubwenzi wanu na Yehova udzalimbila. (Sal. 145:18, 19) Ngati muli na colinga cokulitsa khalidwe linalake lacikhristu, ganizilani mmene lidzakuthandizilani kulimbitsa ubwenzi wanu na anthu ena. (Akol. 3:14) Cina, mungacite kulemba ndithu zifukwa zimene mufunila kukwanilitsa colingaco. Ndiyeno muzibwelelapo pa zifukwazo nthawi na nthawi. Tomáš, amene tam’chula uja, anati: “Nikakhala na zifukwa zambili, zimanisonkhezela kuti nikwanilitse colinga canga.”

7. N’ciyani cinathandiza m’bale Julio na mkazi wake kukwanilitsa colinga cawo?

7 Muziceza nawo anthu amene angakulimbikitseni. (Miy. 13:20) Onani cinathandiza m’bale Julio na mkazi wake kukwanilitsa colinga cawo cowonjezela utumiki. Iye anati: “Tinasankha mabwenzi amene anatithandiza kukwanilitsa colinga cathu, ndipo tinali kuwauzako colingaco. Ambili a iwo anakwanilitsa zolinga zofanana na colinga cathu, ndipo anali kutipatsa malingalilo othandiza. Cina, anali kutifunsa zimene tacitapo pa colingaco, ndipo anali kutilimbikitsa.”

NGATI CIKHUMBO CENICENI TILIBE

Yesetsani kukwanilitsa colinga canu (Onani ndime 8)

8. N’ciyani cingacitike tikacita kuyembekezela kuti mpaka tikakhale na cikhumbo camphamvu? (Onaninso cithunzi.)

8 Kunena zoona, tonsefe timadziŵa kuti masiku sakoma onse. Kodi izi zitanthauza kuti sitingakwanilitse colinga cathu? Ayi. Mwacitsanzo, mphepo imatha kukankhila boti kumene ikupita. Komabe, nthawi zina mphepoyo siikhala yamphamvu, pena siikhalako n’komwe. Kodi izi zitanthauza kuti woyendetsa botiyo sangapitilize ulendo wake? Osati kwenikweni. Maboti ena amakhala na injini, ena amakhala na nkhafi zopalasila. Woyendetsa boti angagwilitse nchito zimenezi kuti apitilize ulendo wake. Cikhumbo cathu cokwanilitsa colinga cili monga mphepoyo. Nthawi zina cimakhala camphamvu, pena sicikhala camphamvu, penanso sicingakhalepo n’komwe. Conco, tikacita kuyembekezela kuti mpaka tikakhale na cikhumbo camphamvu, sitidzakwanilitsa colinga cathu. Koma monga mmene woyendetsa boti amapezela njila zina zopitiliza ulendo wake, nafenso tingakwanilitse colinga cathu ngakhale pamene tilibe cikhumbo kwenikweni. Ngakhale kuti kucita izi sikopepuka, pamakhala zotulukapo zabwino. Tisanakambilane zimene tiyenela kucita, coyamba tiyeni tiyankhe funso limene lingabuke.

9. Kodi n’kopanda pake kulimbikila kukwanilitsa colinga cathu pamene tilibe cikhumbo kwenikweni? Fotokozani.

9 Yehova amafuna kuti tizim’tumikila mokondwela komanso mofunitsitsa. (Sal. 100:2; 2 Akor. 9:7) Koma kodi tiyenela kuyesetsa kukwanilitsa colinga cathu ngakhale pamene tilibe cikhumbo? Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anati: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolela ngati kapolo.” (1 Akor. 9:25-27) Paulo anadzikakamiza kucita zoyenela ngakhale pamene analibe cikhumbo cocita zimenezo. Kodi Yehova anakondwela nawo utumiki wa Paulo? Inde! Ndipo Yehova anam’dalitsa kaamba ka kuyesetsa kwake.—2 Tim. 4:7, 8.

10. Ni mapindu otani amene tidzapeza tikamayesetsa kukwanilitsa zolinga zathu ngakhale pamene tilibe cikhumbo?

10 Mofananamo, Yehova amakondwela akationa tikuyesetsa kukwanilitsa zolinga zathu ngakhale pamene tilibe cikhumbo cocita zimenezo. Amakondwela cifukwa amadziŵa kuti timacita zimenezo cifukwa com’konda, ngakhale pamene tilibe cikhumbo cocita utumikiwo. Monga Paulo, nafenso Yehova adzatidalitsa pa kuyesetsa kwathu. (Sal. 126:5) Ndipo tikadziŵa kuti Yehova akutidalitsa, cikhumbo cathu cimakula. Mlongo Lucyna wa ku Poland anati: “Nthawi zina, sinimafuna kupita mu ulaliki maka-maka ngati ndine wotopa. Komabe, nikapita nimakhala na cimwemwe cacikulu.” Tiyeni lomba tikambilane zimene tiyenela kucita ngati tilibe cikhumbo.

11. Kodi Yehova angatithandize bwanji kukulitsa khalidwe la kudziletsa?

11 Pemphelani kuti mukhale wodziletsa. Kudziletsa ni khalidwe limene limathandiza munthu kupewa kucita zoipa, kapena kudzigwila. Komabe, kudziletsa n’kofunikanso kuti ticite cinthu cabwino, maka-maka ngati cinthuco n’covuta kapena ngati tilibe cikhumbo cofuna kucita cinthuco. Kumbukilani kuti kudziletsa ni cipatso ca mzimu. Conco, pemphani mzimu woyela kwa Yehova kuti ukuthandizeni kukulitsa khalidwe lofunika limeneli. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Davide amene tam’chula kale, anafotokoza mmene pemphelo linam’thandizila. Anali kufuna kumacita phunzilo la munthu mwini lokhazikika. Iye anati: “N’nali kupempha Yehova kuti anithandize kukhala wodziletsa. Mwa thandizo lake, n’natha kukhala na pulogilamu ya phunzilo la munthu mwini yokhazikika.”

12. Kodi Mlaliki 11:4 ingatithandize bwanji kukwanilitsa zolinga zathu zauzimu?

12 Musayembekezele kuti mpaka zinthu zikakhale bwino. M’dziko lino, n’zosatheka kukhala na umoyo wopanda mavuto. Tikayembekezela kuti mpaka zinthu zikhale bwino, sitingakwanilitse colinga cathu. (Ŵelengani Mlaliki 11:4.) M’bale Dayniel anati: “Kulibe angakhale na umoyo wopanda mavuto. Mukangoyambapo, zinthu zimayamba kufewa.” M’bale Paul wa ku Uganda, anachula cifukwa cina cimene sitiyenela kuzengelezela. Iye anati: “Tikalimbikila kuti tikwanilitse zolinga zathu, olo pamene zili zovuta kutelo, Yehova adzadalitsa khama lathu.—Malaki 3:10.

13. Kodi timapindula bwanji tikadziikila zolinga zing’ono-zing’ono?

13 Dziikileni zolinga zing’ono-zing’ono. Ngati colinga cathu cikuoneka kuti n’covuta kucikwanilitsa, cingatithyole m’nkhongono. Ngati ni mmene zilili kwa inu, bwanji colinga canuco osacigaŵa m’zolinga zing’ono-zing’ono? Mwacitsanzo, ngati colinga canu ni kukulitsa khalidwe lina lake, bwanji osayamba kuonetsa khalidwelo m’njila zing’ono-zing’ono? Ngati colinga canu ni kuŵelenga Baibo yonse, bwanji osayamba mwa kuŵelengako mavesi ocepa? M’bale Tomáš amene tam’chula m’ndime yoyamba, cinali kumuvuta kukwanilitsa colinga cake coŵelenga Baibo yonse m’caka cimodzi. Iye anati: “N’nazindikila kuti n’nali kuŵelenga macaputala ambili, komanso mothamanga. Conco, n’naganiza zoyambilanso. Koma pa nthawiyi, n’nali kuŵelenga mavesi ocepa tsiku lililonse na kuwasinkhasinkha. Zotulukapo n’zakuti kuŵelenga Baibo kunayamba kunisangalatsa.” Pa cifukwa cimeneci, m’bale Tomáš anayamba kuthela nthawi yoculuka pa kuŵelenga Baibo. Pamapeto pake, anamaliza Baibo yonse. c

MUSALEFUKE MUKALEPHELAKO NTHAWI ZINA

14. Ni zinthu ziti zingatibweze kumbuyo pa zolinga zathu?

14 Ngakhale titakhala na cikhumbo kapena odziletsa, nthawi zina tingalepheleko ndithu. Mwacitsanzo, “zinthu zosayembekezeleka” zingatilande nthawi yokwanilitsa zolinga zathu. (Mlaliki 9:11) Tingakumane na vuto lalikulu limene lingatilefule na kutilanda mphamvu. (Miy. 24:10) Ndipo cifukwa ca kupanda ungwilo, tingalakwitse zinazake. Izi zingatilepheletse kukwanilitsa colinga cathu. (Aroma 7:23) Cina, tingafike potopa nazo. (Mat. 26:43) N’ciyani cingatithandize kugonjetsa zobweza kumbuyo zimenezi?

15. Mukalephelako nthawi zina, kodi ndiye kuti basi ndinu wolephela? Fotokozani. (Salimo 145:14)

15 Kumbukilani kuti dzedzele-dzedzele si kugwa. Baibo imati tingakumane na mavuto mobweleza-bweleza. Koma imakambanso kuti mwa thandizo la Yehova, tinganyamukenso. (Ŵelengani Salimo 145:14.) M’bale Philip amene tam’chula uja anati: “Siniganizila kwambili za kulephela kwanga. M’malo mwake, nimaika maganizo anga pa zimene nikucitapo kuti nikwanilitse colinga canga. Nayenso m’bale Davide anati: “Nimaona zonibweza kumbuyo kapena zopinga kukhala mwayi woonetsa kukula kwa cikondi canga pa Yehova.” Inde, mukamayesetsa kukwanilitsa zolinga zanu olo kuti mumalephelako nthawi zina, mumaonetsa Yehova kuti mukufuna kum’kondweletsa. Yehova amakondwela kwambili akakuonani mukuyesetsa kukwanilitsa colinga canu.

16. Kodi nthawi zina tikalephela kukwanilitsa colinga cathu, zingatanthauze ciyani?

16 Mukalephelako nthawi zina, tengam’poni phunzilo. Ganizilani cimene cinapangitsa kuti m’bwelele kumbuyo, na kudzifunsa kuti, ‘Kodi ningacite ciyani kuti n’sadzalephelenso?’ (Miy. 27:12) Nthawi zina, kubwelela m’mbuyo kumaonetsa kuti tinadziikila colinga cimene sitingathe kucikwanilitsa. Ngati ni mmene zilili kwa inu, unikaninso colinga canuco kuti muone ngati n’zothekabe kucikwanilitsa. d Mukalephela kukwanilitsa colinga cimene simukanacikwanitsa, Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephela.—2 Akor. 8:12.

17. N’cifukwa ciyani sitiyenela kuiŵala zolinga zimene tinakwanilitsapo kale?

17 Musamaiŵale zolinga zimene munakwanilitsapo kale. Baibo imati: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu.” (Aheb. 6:10) Conco inunso musamaiŵale. Muziganizila zimene mwakwanilitsapo kale, monga kupalana ubwenzi na Yehova, kuuzako ena za iye, kapena kubatizika. Ngati munakwanilitsa zolinga zanu zauzimu kumbuyoku, n’zotheka kukwanilitsanso zolinga zimene muli nazo palipano.—Afil. 3:16.

Sangalalani nawo ulendo (Onani ndime 18)

18. Kodi tiyenela kukumbukilanji pamene tikuyesetsa kukwanilitsa colinga cathu? (Onaninso cithunzi.)

18 Mwa thandizo la Yehova, n’zotheka kukwanilitsa zolinga zanu, mofanana na woyendetsa boti amene amafika kumene akupita. Koma kumbukilani kuti oyendetsa boti ambili amasangalala nawo ulendo wa pamadzi. Mofananamo, pamene muyesetsa kukwanilitsa zolinga zanu, muzisangalala poona mmene Yehova akukuthandizilani kukwanilitsa colinga canu. (2 Akor. 4:7) Mukapanda kutopa, mudzalandila madalitso osaneneka.—Agal. 6:9.

NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu

a Nthawi zonse timalimbikitsidwa kudziikila zolinga zauzimu. Nanga bwanji ngati tinadziikila kale colinga koma zikutivuta kucikwanilitsa? Nkhani ino, ili na malingalilo angapo otithandiza kukwanilitsa zolinga zathu.

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Colinga cauzimu, ni ciliconse cimene timayesetsa kucita kuti ticikwanilitse kotelo kuti ticite zambili potumikila Yehova na kum’kondweletsa. Mwacitsanzo, mungadziikile colinga cokulitsa khalidwe linalake lacikhristu, kapena kuwongolela mbali inayake yokhudza kulambila, monga kuŵelenga Baibo, kucita phunzilo la munthu mwini, kapena ulaliki.

d Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti, “Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe.” Nkhaniyi ipezeka mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya July 15, 2008.