Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 22

Yendanibe pa “Msewu wa Ciyelo”

Yendanibe pa “Msewu wa Ciyelo”

“Kumeneko kudzakhala msewu waukulu . . . Msewu wa Ciyelo.”—YES. 35:8.

NYIMBO 31 Uziyenda na Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. Ni cisankho cofunika citi cimene Ayuda okhala ku Babulo anafunika kupanga? (Ezara 1:2-4)

 MFUMU inalengeza kuti Ayuda amene anali akapolo ku Babulo kwa zaka 70, ni omasuka kubwelela kawo ku Isiraeli. (Ŵelengani Ezara 1:2-4.) Ni Yehova yekha akanatheketsa zimenezi. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa Ababulo sanali kumasula akapolo awo. (Yes. 14:4, 17) Koma Babulo anali atagonjetsedwa, ndipo wolamulila watsopano anauza Ayuda kuti angabwelele kwawo. Conco Myuda aliyense, maka-maka mitu ya mabanja, inayenela kusankha kaya kukhalabe ku Babulo kapena kucoka. Kupanga cisankho cimeneci sikunali kopepuka. Cifukwa?

2 Kwa okalamba, zinali zovuta kupanga ulendo umenewo. Cina, Ayuda ambili anabadwila ku Babulo, ndipo ndilo dziko lokhalo limene anali kudziŵa. Kwa iwo, Isiraeli inali dziko la makolo awo. Ndipo zioneka kuti Ayuda ena anali kukhala umoyo wa wofu-wofu ku Babulo. Conco, cinali covuta kusiya nyumba zawo zabwino na malonda awo, kuti akakhale m’dziko lacilendo limenelo.

3. Ni dalitso lotani lomwe Ayuda okhulupilika obwelela ku Isiraeli anali kuyembekezela?

3 Ayuda okhulupilika anadziŵa kuti akabwelela ku Isiraeli, adzapeza madalitso oculuka kuposa zimene angasiye ku Babulo. Dalitso lalikulu kwambili linali lokhudza kulambila kwawo. Ngakhale kuti ku Babulo kunali akacisi a milungu yonyenga opitilila 50, kunalibe kacisi wa Yehova. Kunalibenso guwa la nsembe limene Aisiraeli akanapelekelapo nsembe malinga na Cilamulo ca Mose. Komanso kunalibe ansembe olinganizidwa owathandiza kupeleka nsembezo. Kuwonjezela apo, anthu a Yehova anali kukhala pakati pa anthu ambili amene sanali kulemekeza Yehova kapena miyeso yake. Conco, Ayuda masauzande amene anali kuopa Yehova, anali kuyembekezela mwacidwi kubwelela ku dziko lawo kuti akabwezeletse kulambila koyela.

4. Kodi Yehova analonjeza kuti adzawapatsa thandizo lotani Ayuda obwelela kwawo?

4 Ulendo wocoka ku Babulo kupita ku Isiraeli unali kutenga miyezi inayi. Ulendowo unali na zovuta zake, koma Yehova analonjeza kuti adzacotsa zovutazo zimene zikanawalepheletsa kubwelela kwawo. Yesaya analemba kuti: “Konzani njila ya Yehova anthu inu! Wongolani msewu wa Mulungu wathu wodutsa m’cipululu. . . . Malo okumbikakumbika asalazidwe ndipo malo azitunda-zitunda akhale cigwa.” (Yes. 40:3, 4) Yelekezani kuti mukuona msewu waukulu wodutsa m’cipululu, komanso wosalazidwa bwino. Anthu apaulendo anali kudzasangalala kwambili kuyenda mu msewu umenewo. Zinali zosavuta kwa iwo kuyenda mu msewu waukulu wowongoka, kuposa kudutsa m’zikweza kapena m’zigwa. Ndipo akanafika mwamsanga.

5. Kodi msewu waukulu wophiphilitsa wocoka ku Babulo kupita ku Isiraeli unapatsidwa dzina lotani?

5 Masiku ano, misewu ikulu-ikulu imadziŵika na maina kapena manambala. Nawonso msewu waukulu wophiphilitsa umene Yesaya anachula uli na dzina. Timaŵelenga kuti: “Kumeneko kudzakhala msewu waukulu ndipo udzachedwa Msewu wa Ciyelo. Munthu wodetsedwa sadzayendamo.” (Yes. 35:8) Kodi lonjezo limeneli linawapindulila bwanji Aisiraeli kalelo? Nanga ife limatipindulila bwanji?

“MSEWU WA CIYELO”—KALELO KOMANSO MASIKU ANO

6. N’cifukwa ciyani msewu umenewo unachedwa woyela?

6 Mpake kuti msewu waukulu umenewo unali kuchedwa “Msewu wa Ciyelo.” Cifukwa ciyani? Cifukwa Myuda aliyense waciwelewele, wolambila mafano, kapena amene anali kucita macimo ena aakulu sakanaloledwa kukhala m’dziko la Isiraeli. Ayuda obwelela kwawo anali kudzakhala “anthu oyela” kwa Mulungu wawo. (Deut. 7:6) Komabe, izi sizinatanthauze kuti aja amene anacoka ku Babulo sanafunike kupanga masinthidwe kuti Yehova awayanje.

7. Ni masinthidwe otani amene Ayuda ena anafunika kupanga? Fotokozani citsanzo.

7 Monga takambila kale, Ayuda ambili anabadwila ku Babulo, ndipo n’kutheka kuti ena anatengela maganizo na cikhalidwe ca Ababulo. Patapita zaka zambili Ayuda oyamba atabwelela ku Isiraeli, Ezara anazindikila kuti ena a iwo anapanga mgwilizano wa ukwati na akazi acikunja. (Eks. 34:15, 16; Ezara 9:1, 2) Pambuyo pake, Bwanamkubwa Nehemiya anadabwa ataona kuti ana obadwila ku Isiraeli sanali kudziŵa cinenelo ca Ayuda. (Deut. 6:6, 7; Neh. 13:23, 24) Popeza mbali yaikulu ya Mawu a Mulungu inali m’Ciheberi, kodi anawo akanaphunzila bwanji kukonda Yehova na kum’lambila? (Ezara 10:3, 44) Conco, Ayudawo anafunika kupanga masinthidwe aakulu. Koma cikanakhala copepuka kwa iwo kucita zimenezo ku Isiraeli komwe kulambila koona kunali kubwelezeletsedwa mwapang’ono-pang’ono.—Neh. 8:8, 9.

Kuyambila 1919, amuna, akazi, komanso ana, acoka mu Babulo Wamkulu, ndipo ayamba kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo.” (Onani ndime 8)

8. N’cifukwa ciyani zimene zinacitikila Ayuda kalelo zikutikhudza masiku ano? (Onani cithunzi pacikuto.)

8 Koma ena angafunse kuti, ‘Zimenezi n’zocitsa cidwi. Koma kodi zimene zinacitikila Ayuda kalelo zitikhudza masiku ano?’ Inde, cifukwa nafenso tingati tikuyenda pa “Msewu wa Ciyelo.” Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tiyenela kuyendabe pa “Msewu wa Ciyelo,” umene ukutitsogolela ku paradaiso wauzimu, komanso ku madalitso a Ufumu a m’tsogolo. b (Yoh. 10:16) Kuyambila 1919, amuna, akazi, komanso ana akhala akucoka mu Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conyenga, ndipo ayamba kuyenda pa msewu wophiphilitsa umenewo. N’kutheka kuti ndinu mmodzi wa iwo. Nchito yokonza msewu umenewo inayamba zaka zambili-mbili kumbuyoko. Koma anthu anayamba kuyendamo zaka ngati 100 zapitazo.

KUKONZA MSEWU

9. Malinga na Yesaya 57:14, kodi “Msewu wa Ciyelo” unakonzedwa mlingalilo lotani?

9 Yehova anaonetsetsa kuti wacotsa zopinga zonse zimene Ayuda akanakumana nazo pa ulendo wawo wocoka ku Babulo. (Ŵelengani Yesaya 57:14.) Nanga bwanji za “Msewu wa Ciyelo” wamakono? Kwa zaka mahandiledi ambili cisanafike caka ca 1919, Yehova anaseŵenzetsa amuna omuopa kukonza msewu wothandiza anthu kutuluka m’Babulo Wamkulu. (Yelekezelani na Yesaya 40:3.) Iwo anayamba kukonza msewu wauzimu, kuti athandize anthu a maganizo abwino kucoka mu Babulo Wamkulu, na kuloŵa m’paradaiso wauzimu. Kodi nchito “yokonza msewu” imeneyo inaloŵetsamo ciyani? Onani zina mwa nchito zimene anagwila pokonza msewuwo.

Kwa zaka mahandiledi ambili, Mulungu anaseŵenzetsa amuna omuopa kukonza msewu wothandiza anthu kutuluka mu Babulo Wamkulu (Onani ndime 10-11))

10-11. Kodi nchito yopulinta Mabaibo na kuwamasulila inathandiza bwanji kuti anthu akhale na cidziŵitso ca m’Baibo? (Onaninso cithunzi.)

10 Kupulinta. Anthu anali kukopela Baibo pamanja mpaka ca m’ma 1450. Nchitoyo inali kutenga nthawi yaitali, ndipo makope a Baibo anali ocepa komanso odula. Koma pamene anapanga makina opulintila, cinakhala cosavuta kupanga makope ambili a Baibo na kuwafalitsa.

11 Kumasulila. Kwa zaka mahandiledi ambili, Baibo inali kupezeka m‘Cilatini, cinenelo cimene ni anthu ophunzila okha anali kucimvetsa. Komabe, pamene makina opulintila anafala, anthu oopa Mulunga anayamba kugwila nchito molimbika kuti amasulile Baiboyo m’zinenelo zambili. Tsopano anthu anayamba kuyelekezela zimene atsogoleli acipembezo anali kuwaphunzitsa na zimene Baibo imaphunzitsa.

Mulungu anaseŵenzetsa amuna omuopa kukonza msewu wothandiza anthu kutuluka mu Babulo Wamkulu (Onani ndime 12-14) c

12-13. Fotokozani citsanzo ca mmene anthu oona mtima okonda kuphunzila Baibo anayambila kuvumbula ziphunzitso za zipembedzo zonyenga ca m’ma 1835.

12 Zida zophunzilila Baibo. Ophunzila Baibo anaphunzila zinthu zambili zoona m’Mawu a Mulungu. Ndipo anayamba kuuzako ena zimene anali kuphunzila. Mwacitsanzo, ca m’ma 1835, kagulu ka amuna okhulupilika kanayamba kufalitsa tumathilakiti tumene tunavumbula ziphunzitso zonama za machalichi. Izi zinakwiyitsa atsogoleli acipembedzo.

13 Ca m’ma 1835, munthu wina woopa Mulungu, dzina lake Henry Grew anafalitsa kathilakiti kokamba za mkhalidwe wa akufa. Mmenemo anapeleka maumboni a m’Malemba oonetsa kuti moyo wosafa ni mphatso yocokela kwa Mulungu, osati mkhalidwe wobadwa nawo, monga mmene machalichi ambili anali kuphunzitsila. Mu 1837, m’busa wina dzina lake George Storrs anapeza kope la kathilakiti kameneko pomwe anali paulendo wa pasitima. Atakaŵelenga, anatsimikiza kuti wapeza coonadi. Iye anaganiza zouzako ena zimene anaŵelengazo. Mu 1842, iye anakamba nkhani zotsatizana pa mutu wakuti, “Kufufuza—Kodi Anthu Oipa Ali na Moyo Wosafa?” Ndipo zimene George Storrs analemba zinakhudza mtima mnyamata wina dzina lake Charles Taze Russell.

14. Kodi M’bale Russel na ophunzila Baibo anzake anapindula bwanji na nchito yokonza msewu wauzimu imene inacitika kumbuyoko? (Onaninso cithunzi.)

14 Kodi M’bale Russell na ophunzila Baibo anzake anapindula bwanji na nchito yokonza msewu wauzimu imene inacitika kumbuyoko? Pophunzila malemba, iwo anali kufufuza m’madikishonale ofotokoza za Baibo, komanso m’Mabaibo osiyana-siyana, zimene zinakonzedwa iwo asanayambe nchito yawo. Iwo anapindulanso na zimene Henry Grew, George Storrs, komanso anthu ena anafufuza zokhudza Baibo. M’bale Russell na anzake anathandizila pa nchito yokonza msewu wauzimu, mwa kufalitsa mabuku na mathilakiti ambili-mbili a nkhani za m’Baibo.

15. N’ciyani capadela cinacitika mu 1919?

15 Mu 1919, anthu a Mulungu anamasuka ku Babulo Wamkulu. M’caka cimeneco, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” anaikidwa kuti athandize anthu oona mtima kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo” wamakono. (Mat. 24: 45-47) Nchito yokonza msewu umenewo imene amuna okhulupilika anagwila kalelo, ikuthandiza anthu oyenda pa msewu waukuluwo kuti adziŵe zambili zokhudza colinga ca Yehova. (Miy. 4:18) Iwo amathanso kusintha umoyo wawo kuti ugwilizane na miyeso ya Yehova. Yehova sayembekezela anthu ake kupanga masinthidwe onse panthawi imodzi. M’malo mwake, iye wakhala akuyenga anthu ake pang’ono-pang’ono. (Onani bokosi lakuti, “ Yehova Akuyenga Anthu Ake Pang’ono-pang’ono.”) Tonsefe tidzakhala okondwa panthawi imene zocita zathu zonse zizikondweletsa Mulungu wathu!—Akol. 1:10.

“MSEWU WA CIYELO” UKALI WOTSEGUKA

16. Kucokela mu 1919, kodi pacitika zotani pokonzanso “Msewu wa Ciyelo”? (Yesaya 48:17; 60:17)

16 Msewu uliwonse umafunika kukonzedwa nthawi na nthawi. Kucokela mu 1919, nchito yokonza “Msewu wa Ciyelo” yakhala ikucitika, kuti anthu ambili acoke m’Babulo Wamkulu. Kapolo wokhulupilila ndi wanzelu atasankhidwa, anayamba kugwila nchito yake. Ndipo mu 1921, anafalitsa cida cothandiza anthu kuphunzila Baibo. Cidaco cinali buku lakuti Zeze wa Mulungu. Makope pafupifupi 6 miliyoni anafalitsidwa m’zinenelo 36, ndipo anthu ambili anaphunzila coonadi. Posacedwapa, tinalandila cida cabwino ngako cophunzitsila Baibo—buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! M’masiku otsiliza ano, Yehova akuseŵenzetsa gulu lake popeleka cakudya cauzimu ca mwana alilenji, kuti tonsefe tisaleke kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo.”—Ŵelengani Yesaya 48:17; 60:17.

17-18. Kodi “Msewu wa Ciyelo” umatifikitsa kuti?

17 Munthu akavomela kuphunzila Baibo, amakhala na mwayi woyenda pa “Msewu wa Ciyelo.” Ena amaleka kuyenda pa msewuwo. Koma ena amakhala ofunitsitsa kuyendabe pa msewuwo mpaka akafike kumalo kumene akupita. Kodi malowo n’ciyani?

18 Amene ali na ciyembekezo codzapita kumwamba, “Msewu wa Ciyelo” udzawafikitsa “m’paradaiso wa Mulungu” kumwamba. (Chiv. 2:7) Koma amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, msewu waukuluwo udzawafikitsa kumoyo wangwilo kumapeto kwa zaka 1,000. Ngati mukuyenda pa msewu waukulu umenewo, conde musachokove na kuyang’ana zakumbuyo. Musacokemo mu msewuwo mpaka mukafike m’dziko latsopano. Tikufunikilani “zabwino zonse paulendo wanu.”

NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova

a Yehova anacha msewu waukulu wophiphilitsa wocoka ku Babulo kupita ku Isiraeli kuti “Msewu wa Ciyelo.” M’nthawi zino zamakono, Yehova wakonzela anthu ake msewu. Ndipo kucokela mu 1919, anthu mamiliyoni acoka mu Babulo Wamkulu, na kuyamba kuyenda pa “Msewu wa Ciyelo.” Tonsefe tifunika kupitiliza kuyenda pa msewu umenewo, mpaka tikafike kumene tikupita.

c MAWU OFOTOKOZELA: M’bale Russell na anzake anagwilitsa nchito zida zophunzilila Baibo zimene zinakonzedwa kale-kale iwo asanayambe nchito yawo.