MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU
Kupilila Zopanda Cilungamo
Ŵelengani Genesis 37:23-28; 39:17-23 kuti muphunzile ku citsanzo ca Yosefe ca kupilila zopanda cilungamo.
Mvetsani nkhani yonse. N’ciyani cinacititsa ena kucitila Yosefe zopanda cilungamo? (Gen. 37:3-11; 39:1, 6-10) Kodi Yosefe anapilila zinthu zopanda cilungamo kwa utali wotani? (Gen. 37:2; 41:46) Kodi Yehova anamucitila ciyani Yosefe pa nthawiyo? Nanga sanamucitile ciyani?—Gen. 39:2, 21; w23.01 17 ¶13.
Kumbani mozamilapo. Baibo sinachulepo kuti Yosefe anayesa kudziteteza ku zinenezo zabodza za mkazi wa Potifara. Kodi Malemba otsatilawa angatithandize bwanji kudziŵa cifukwa cimene Yosefe anakhalila cete, kapena cifukwa cake sitiyenela kuyembekezela kuuzidwa mfundo zonse? (Miy. 20:2; Yoh. 21:25; Mac. 21:37) Ni makhalidwe ati amene ayenela kuti anathandiza Yosefe kupilila zopanda cilungamo?—Mika 7:7; Luka 14:11; Yak. 1:2, 3.
Onani zimene muphunzilapo. Dzifunseni kuti:
-
‘Ni zopanda cilungamo zotani zimene ningakumane nazo pokhala wophunzila wa Yesu?’(Luka 21:12, 16, 17; Aheb. 10:33, 34)
-
‘Kodi ningakonzekele bwanji kupilila zopanda cilungamo?’ (Sal. 62:7, 8; 105:17-19; w19.07 2-7)