NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA November 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya December 31, 2018-February 3, 2019.

“Gula Coonadi Ndipo Usacigulitse”

Kodi kugula coonadi kumatanthauza ciani? Tikagula coonadi, tingacite ciani kuti tisacigulitse?

“Ndidzayenda M’coonadi Canu”

Tingacite ciani kuti tigwilitsitse coonadi cimene Yehova anatiphunzitsa?

Dalilani Yehova Kuti Mukhalebe na Moyo!

Buku la Habakuku lingatithandize kukhalabe na mtendele wa mu mtima ngakhale pamene tikumana na mavuto.

Kodi Mumayendela Maganizo a Ndani?

Tingatengele bwanji maganizo a Yehova na kupewa kutengela maganizo a anthu?

Kodi Mumayesetsa Kuona Zinthu Mmene Yehova Amazionela?

Tingacite ciani kuti tipewe kutengela maganizo a dzikoli?

Kukoma Mtima—Khalidwe Limene Limaonekela M’mawu na M’zocita

Kukoma mtima n’limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyela wa Mulungu umabala. Tingakulitse bwanji khalidwe labwino limeneli?

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Opeleka Zabwino amene Yesu anachula madzulo akuti maŵa adzaphedwa anali ndani? Nanga n’cifukwa ciani anali kuchulidwa na mawu aulemu amenewa?

Ni Mphatso Yanji Imene Tingam’patse Yehova?

Kodi “zinthu za mtengo wapatali” zochulidwa pa Miyambo Proverbs 3:9 n’ciani, nanga tingaziseŵenzetse bwanji popititsa patsogolo kulambila koona?