Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukoma Mtima—Khalidwe Limene Limaonekela M’mawu na M’zocita

Kukoma Mtima—Khalidwe Limene Limaonekela M’mawu na M’zocita

ZIMAKHALA zotsitsimula komanso zolimbikitsa kwambili ngati munthu waticitila zinazake zoonetsa kukoma mtima. Timakondwela pozindikila kuti munthuyo amatikonda. Popeza kuti tonse timafuna kucitilidwa zinthu mokoma mtima, kodi tingakulitse bwanji khalidwe labwino limeneli?

Munthu wokoma mtima amadela nkhawa za umoyo wa ena. Timaonetsa kuti ndise okoma mtima mwa kucita zinthu zothandiza ena na kukamba mawu olimbikitsa. Kukoma mtima kweni-kweni si kungodzionetsela cabe kuti tili na khalidwe labwino. Koma ni khalidwe limene munthu amaonetsa cifukwa cokonda ena na kuwamvelela cifundo. Kuwonjezela apo, kukoma mtima ni mbali ya cipatso cimene mzimu woyela wa Mulungu umabala. Ndipo ise Akhristu timalimbikitsidwa kukulitsa khalidwe limeneli. (Agal. 5:22, 23) Conco, tiyeni lomba tikambilane mmene Yehova na Yesu amaonetsela khalidwe limeneli, komanso mmene ise tingatsatilile citsanzo cawo.

YEHOVA AMAONETSA KUKOMA MTIMA KWA ONSE

Yehova amaganizila aliyense ndipo ni wokoma mtima kwa onse, ngakhale “kwa osayamika ndi kwa oipa.” (Luka 6:35) Mwacitsanzo, Yehova “amawalitsila dzuŵa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsila mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:45) Motelo, ngakhale anthu amene sakhulupilila Yehova monga Mlengi wawo, amapindula ndi zinthu zocilikiza moyo zimene iye amatipatsa mokoma mtima. Ndipo amakhalako na cimwemwe mu umoyo wawo.

Yehova anaonetsa kukoma mtima kwapadela pa zimene anacitila Adamu na Hava. Atangocimwa, Adamu na Hava “anadzisokela masamba a mkuyu n’kupanga zovala zomangila m’ciuno.” Komabe, Yehova anadziŵa kuti pokakhala kunja kwa Edeni, Adamu na Hava adzafunika zovala zoyenelela zimene zikanawateteza ku “minga ndi zitsamba zobaya,” cifukwa nthaka inali yotembeleledwa. Cotelo, Yehova mokoma mtima, anapangila Adamu ndi mkazi wake “zovala zazitali zacikopa.”—Gen. 3:7, 17, 18, 21.

Ngakhale kuti Yehova ni wokoma mtima kwa “anthu oipa ndi abwino,” iye amakonda kuonetsa kukoma mtima kwa atumiki ake okhulupilika. Mwacitsanzo, m’masiku a mneneli Zekariya, mngelo wina anadandaula poona kuti nchito yomanganso kacisi ku Yerusalemu yaima. Yehova anamvela dandaulo lake ndipo “anamuyankha ndi mawu abwino ndiponso olimbikitsa.” (Zek. 1:12, 13) Yehova anacitanso cimodzi-modzi na mneneli Eliya. Panthawi ina, mneneliyo anavutika kwambili maganizo moti anapempha kwa Yehova kuti afe. Yehova anakhudzika mtima na mavuto amene Eliya anakumana nawo, ndipo anatumiza mngelo kuti akam’limbikitse. Komanso anam’limbikitsa mwa kumuuza kuti sanali yekha. Atalandila thandizo komanso mawu acilimbikitso amenewo, Eliya anapeza mphamvu zopitilizila kucita utumiki wake. (1 Maf. 19:1-18) Pakati pa atumiki a Mulungu, n’ndani anaonetsa bwino kwambili khalidwe la Yehova la kukoma mtima?

YESU ANALI MUNTHU WOKOMA MTIMA KWAMBILI

Pa utumiki wake wa pa dziko lapansi, Yesu anali wokoma mtima kwambili komanso woganizila ena. Sanali wankhanza kapena wopondeleza. Mokoma mtima, iye anati: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. . . pakuti goli langa ndi lofewa.” (Mat. 11:28-30) Cifukwa ca kukoma mtima kwake, anthu anali kumukonkha kulikonse kumene wayenda. ‘Powamvela cifundo,’ Yesu anawapatsa cakudya, kuwacilitsa, na kuwaphunzitsa “zinthu zambili” zokhudza Atate wake.—Maliko 6:34; Mat. 14:14; 15:32-38.

Cimene cionetsa kuti Yesu anali wokoma mtima kwambili n’cakuti anali womvetsetsa komanso wozindikila pocita zinthu ndi ena. Ngakhale pamene anali wolema, Yesu anali kuwalandila bwino anthu amene anabwela kwa iye kudzapempha thandizo. (Luka 9:10, 11) Mwacitsanzo, mayi wina amene anali wodetsedwa malinga na Cilamulo ca Mose, anagwila malaya a Yesu akunja ali na cikhulupililo cakuti acila matenda ake otaya magazi. Mayiyo anacita mantha kwambili, koma Yesu sanamudzudzule. (Lev. 15:25-28) Iye anali atavutika na matenda akewo kwa zaka 12, ndipo Yesu anamumvelela cifundo na kumuuza kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, matenda ako aakuluwo atheletu.” (Maliko 5:25-34) Uku kunali kukoma mtima kwakukulu cotani nanga!

KUKOMA MTIMA KUMAFUNA KUCITAPO KANTHU

M’zitsanzo zimene takambilana, taona kuti kukoma mtima kweni-kweni kumaonekela mwa zocita zathu. M’fanizo la Msamariya wacifundo, Yesu anaonetsa kuti kukoma mtima kumafuna kucitapo kanthu. Olo kuti pa nthawiyo Asamariya na Ayuda anali kuzondana, Msamariya wa m’fanizoli anacitila cifundo Myuda wina amene anamenyewa na kulandiwa zinthu na acifwamba. Acifwambawo anamusiya pa msewu atatsala pang’ono kufa. Cifukwa ca kukoma mtima, Msamariyayo anacitapo kanthu. Anamanga zilonda zake na kum’peleka ku nyumba ya alendo. Ndiyeno, anapeleka ndalama kwa mwininyumba ya alendoyo, na kum’lonjeza kuti ngati adzawononga ndalama zina pomusamalila, adzamubwezela.—Luka 10:29-37.

Nthawi zambili, kukoma mtima kumaonekela m’zocita. Koma kumaonekelanso m’mawu abwino na olimbikitsa. Baibo imati: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” (Miy. 12:25) Makhalidwe a kukoma mtima na ubwino amatisonkhezela kukamba mawu olimbikitsa kwa ena, ndipo tikatelo timawathandiza kukhala acimwemwe. * Kukamba mawu abwino kwa ena, kumaonetsa kuti timawakonda. Tikawalimbikitsa na mawu abwino, amakhala na mphamvu zopilila mavuto amene amakumana nawo mu umoyo wawo.—Miy. 16:24.

MMENE TINGAKULITSILE KHALIDWE LA KUKOMA MTIMA

Popeza kuti tinalengedwa ‘m’cifanizilo ca Mulungu,’ tonse tingathe kukulitsa khalidwe la kukoma mtima. (Gen. 1:27) Mwacitsanzo, Yuliyo mkulu wa asilikali a Roma amene anali kuyang’anila mtumwi Paulo paulendo wopita ku Roma, ‘anam’komela mtima kwambili ndipo anamulola kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalile’ mu mzinda wa Sidoni. (Mac. 27:3) Panthawi inanso, anthu a pa cisumbu ca Melita anaonetsa Paulo na anthu ena “kukoma mtima kwapadela,” pamene ngalawa inasweka paulendo wawo wapamadzi. Anthuwo anacita kusonkha moto kuti Paulo na anzakewo awothe. (Mac. 28:1, 2) Zinthu zimene anthu amenewa anacita pa nthawiyi zinali zabwino. Koma kuti tikondweletse Yehova, tifunika kukhala okoma mtima nthawi zonse osati cabe mwa apa na apo iyai.

Mulungu amafuna kuti nthawi zonse tizicita zinthu mokoma mtima mu umoyo wathu. Ndiye cifukwa cake iye amatiuza kuti ‘tivale’ kukoma mtima. (Akol. 3:12) Komabe, pena zimativuta kuonetsa khalidwe labwino limeneli. Cifukwa ciani? Nthawi zina cingapangitse ni manyazi, kudzikaikila, kutsutsidwa, kapena kamtima kodzikonda kamene tingakhale nako. Ngakhale n’conco, tingathe kukulitsa khalidwe la kukoma mtima mwa kudalila mzimu woyela na kutengela mmene Yehova amaonetsela khalidweli.—1 Akor. 2:12.

Kodi tingadziŵe bwanji mbali zofunika kuwongolela kuti tikulitse khalidwe la kukoma mtima? Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimamvetsela mwacifundo pamene ena akunifotokozela mavuto awo? Kodi nimakhala chelu kuti nidziŵe zimene ena akufunikila? Kodi nili na cizoloŵezi cocita zinthu mokomela mtima anthu ena, ngakhale amene si anzanga kapena a m’banja langa?’ Ndiyeno, tingadziikile zolinga, monga cofuna kudziŵa bwino anthu amene timakhala nawo, maka-maka Akhristu anzathu. Tikatelo, tidzatha kudziŵa mavuto amene akukumana nawo, komanso mmene tingawathandizile. Kenako, tiyenela kuyesetsa kuwathandiza mokoma mtima monga mmene ise tingafunile kuti iwo atithandizile. (Mat. 7:12) Komanso, tiyenela kupempha thandizo kwa Yehova, ndipo iye adzatithandiza kukulitsa khalidwe la kukoma mtima.—Luka 11:13.

KHALIDWE LA KUKOMA MTIMA LIMAKOPA ANTHU

Pochula zinthu zimene zinam’thandiza kukhala mtumiki wabwino wa Mulungu, mtumwi Paulo anachulapo khalidwe la ‘kukoma mtima’. (2 Akor. 6:3-6) Anthu anali kukopeka naye Paulo, cifukwa cakuti zimene anali kukamba na kucita zinaonetsa kuti anali kuwadela nkhawa anthuwo. (Mac. 28:30, 31) Mofananamo, ngati timacita zinthu mokoma mtima, anthu ena angakopeke mpaka kuphunzila coonadi. Ndiponso, ngati timakomela mtima aliyense, olo amene amatitsutsa, tingafewetse mitima yawo na kupangitsa kuti aleke kutitsutsa. (Aroma 12:20) M’kupita kwa nthawi, iwo angakopeke na uthenga wa m’Baibo umene timawalalikila.

Mosakaiyikila, anthu osaŵelengeka amene adzaukitsidwa m’Paradaiso, adzakondwela na kukoma mtima kweni-kweni kumene adzaonetsedwa, mwina kwa nthawi yoyamba. Izi zidzawalimbikitsa kuti nawonso azikacitila ena zinthu mokoma mtima. Munthu aliyense wokhalapo pa nthawiyo, amene sazikakomela mtima ena na kuwathandiza, sadzakhala m’Paradaiso kwamuyaya. Koma anthu amene Mulungu adzawapatsa moyo wosatha, adzapitiliza kucitilana zinthu mwacikondi ndi mokoma mtima. (Sal. 37:9-11) Ndithudi, anthu m’dzikolo adzakhala pa mtendele komanso motetezeka. Komabe, pamene tikuyembekezela nthawi yokondweletsa imeneyi, kodi tingapindule bwanji pali pano ngati timakomela ena mtima?

MAPINDU AMENE TIMAPEZA NGATI TIMAKOMELA ENA MTIMA

Baibo imati: “Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake.” (Miy. 11:17) Ngati munthu ni wokoma mtima, anthu amamukonda, ndipo amamucitilanso zinthu mokoma mtima. Yesu anati: “Muyezo umene mukuyezela ena, iwonso adzakuyezelani womwewo.” (Luka 6:38) Conco, munthu wokoma mtima amapeza mabwenzi abwino mosavuta, komanso ubwenzi wake ndi anthuwo umakhala wolimba.

Mtumwi Paulo analangiza Akhristu a mu mpingo wa ku Efeso kuti: “Khalani okomelana mtima, acifundo cacikulu, okhululukilana ndi mtima wonse.” (Aef. 4:32) Mpingo umalimba na kukhala wogwilizana ngati muli Akhristu acifundo amene amathandizana na kukomelana mtima. Akhristu otelo sacita kufika polankhula mawu aukali, kudzudzulana mwankhanza, kapena kunyodolana. Komanso, safalitsa misece. M’malo mwake, amayesetsa kuseŵenzetsa lilime lawo polimbikitsa ena. (Miy. 12:18) Zotulukapo zake, mpingo umatumikila Yehova mwacimwemwe.

Inde, kukoma mtima ni khalidwe limene limaonekela m’mawu na m’zocita. Tikakhala okoma mtima, ndiye kuti tikutengela Yehova Mulungu wathu wacikondi komanso woolowa manja. (Aef. 5:1) Kucita izi kumalimbitsa mipingo na kukopa anthu kuti ayambe kulambila koona. Conco, tiyeni nthawi zonse tizidziŵika monga anthu okoma mtima.

^ par. 13 Ino ni imodzi mwa nkhani 9 zofotokoza “cipatso ca mzimu.” Khalidwe la ubwino tidzalikambilana m’nkhani ina ya kutsogolo.