Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Gula Coonadi Ndipo Usacigulitse”

“Gula Coonadi Ndipo Usacigulitse”

“Gula coonadi ndipo usacigulitse. Gula nzelu, malangizo ndi kumvetsa zinthu.”—MIY. 23:23.

NYIMBO: 94, 96

1, 2. (a) N’cinthu camtengo wapatali citi cimene tili naco? (b) Ni ziphunzitso ziti za coonadi zimene timaziyamikila kwambili? Nanga n’cifukwa ciani? (Onani mapikica pamwambapa.)

KODI cinthu camtengo wapatali kwambili cimene muli naco n’ciani? Kodi mungacisinthanitse na cinthu cina cotsika mtengo? Kwa atumiki a Yehova odzipatulila, yankho pa mafunso aŵili onsewa ni yosavuta. Cinthu camtengo wapatali kwambili kwa ise ni ubwenzi wathu na Yehova, ndipo sitingausinthanitse na cina ciliconse. Timaonanso coonadi ca m’Baibo kukhala cinthu camtengo wapatali, cifukwa n’cimene catheketsa kuti tikhale pa ubwenzi wabwino na Atate wathu wakumwamba.—Akol. 1:9, 10.

2 Kukamba zoona, Mlangizi wathu Wamkulu watiphunzitsa zambili kupitila m’Mawu ake, Baibo! Iye watiphunzitsa coonadi ponena za dzina lake komanso makhalidwe ake abwino. Watiphunzitsanso za mphatso yamtengo wapatali ya dipo, imene anaipeleka mwacikondi kupitila mwa Mwana wake, Yesu. Kuwonjezela apo, Yehova watiphunzitsa za Ufumu wa Mesiya. Ndipo wapatsa Akhristu odzozedwa ciyembekezo cokalamulila kumwamba, komanso wapatsa a “nkhosa zina” ciyembekezo codzakhala m’Paradaiso pano pa dziko lapansi. (Yoh. 10:16) Iye amatiphunzitsa kukhala na makhalidwe abwino. Timayamikila kwambili ziphunzitso za coonadi zimenezi cifukwa zimatithandiza kuyandikila Mlengi wathu. Zimatithandizanso kukhala na umoyo wacimwemwe.

3. Kodi kugula coonadi sikutanthauza ciani?

3 Yehova ni Mulungu wooloŵa manja. Iye sawamana zabwino anthu amene amasakila coonadi. Yehova anacita kupeleka moyo wa Mwana wake wokondedwa monga mphatso yaulele. Conco, sayembekezela kuti timupatse ndalama kuti atiphunzitse coonadi. Mwacitsanzo, mwamuna wina, dzina lake Simoni, anafuna kupatsa mtumwi Petulo ndalama kuti alandile mphamvu yopatsa anthu mzimu woyela. Koma Petulo anam’dzulula. Anati: “Siliva wakoyo awonongeke nawe limodzi, cifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulele ya Mulungu ungaipeze ndi ndalama.” (Mac. 8:18-20) Nanga kodi Baibo imatanthauzanji pamene imati: “Gula coonadi”?

KODI ‘KUGULA’ COONADI KUMATANTHAUZA CIANI?

4. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani ponena za coonadi?

4 Ŵelengani Miyambo 23:23. Kuti tipeze coonadi m’Mawu a Mulungu, pamafunika khama. Tifunika kukhala okonzeka kudzimana ciliconse kuti tipeze coonadi. Monga mmene wolemba buku la Miyambo anakambila, ‘tikagula’ kapena kuti kupeza “coonadi,” tifunika kusamala kuti ‘tisacigulitse’ kapena kucitaya. Tsopano, tiyeni tikambilane zimene ‘kugula’ coonadi kumatanthauza, komanso zimene tingafunike kutailapo kuti ticigule. Kukambilana zimenezi, kudzathandiza kuti tizikonda kwambili coonadi, komanso kuti tipeweletu ‘kucigulitsa.’ Monga mmene tidzaonela, tikagula coonadi, tidzapeza madalitso ambili.

5, 6. (a) Kodi tingagule bwanji coonadi popanda kulipila ndalama? Fotokozani fanizo. (b) Kodi coonadi cimatipindulitsa bwanji?

5 Ngakhale cinthu camahala timafunika kutailapo cinacake kuti ticipeze. Liwu la Ciheberi lomasulidwa kuti “kugula” pa Miyambo 23:23, lingatanthauzenso “kupeza.” Liwu lakuti “kugula” litanthauza kusinthanitsa cinthu cinacake na cina camtengo wapatali. Ndipo liwu lakuti “kupeza” lionetsa kufunika kocita khama. Kuti timvetsetse tanthauzo la kugula coonadi, tiyelekezele motele. Tikambe kuti winawake wakuuzani kuti ku maketi kuli “mabanana amahala.” Kodi nthocizo zingabwele zokha mozizwitsa ku nyumba kwathu? Iyai. Tidzafunika kucitapo kanthu. N’zoona kuti n’zamahala, koma tidzafunika kutailapo nthawi na mphamvu zathu mwa kupita ku maketi kukazitenga. N’cimodzimodzi na coonadi. Sitimacigula na ndalama. Komabe, timafunika kucita khama kuti ticipeze.

6 Ŵelengani Yesaya 55:1-3. Mawu a Yehova amene Yesaya analemba pa mavesi amenewa, atithandiza kumvetsa bwino zimene kugula coonadi kumatanthauza. Pa lembali, Yehova anayelekezela mawu ake na madzi, mkaka, na vinyo. Mofanana ndi madzi akumwa ozizila bwino, coonadi ca m’Mawu a Mulungu cimatitsitsimula. Komanso, monga mmene mkaka umalimbitsila matupi athu na kuthandiza ana kukula, mawu a Yehova amatilimbikitsa na kutithandiza kukula mwauzimu. Kuwonjezela apo, mawu a Yehova ali monga vinyo. Motani? Baibo imakamba kuti vinyo amabweletsa cisangalalo. (Sal. 104:15) Conco, pamene Yehova anauza anthu ake kuti ‘agule vinyo,’ anaonetsa kuti tikamatsatila mfundo za m’Mawu ake mu umoyo wathu, timakhala acimwemwe. (Sal. 19:8) Ndithudi, amenewa ni mawu ofanizila ocititsa cidwi, oonetsa mapindu amene timapeza ngati tiphunzila na kuseŵenzetsa coonadi ca m’Baibo. Conco, tingakambe kuti, timagula coonadi mwa kucita khama kuphunzila Mawu a Mulungu na kuseŵenzetsa zimene timaphunzila. Lomba tiyeni tikambilane zinthu zisanu zimene tingatailepo kuti tigule coonadi.

KODI MUNATAILAPO CIANI KUTI MUGULE COONADI?

7, 8. (a) N’cifukwa ciani tifunika kupatula nthawi kuti tigule coonadi? (b) Kodi mtsikana wina anadzimana ciani kuti aphunzile coonadi? Nanga panakhala zotulukapo zanji?

7 Nthawi. Ici ni cinthu cimene munthu aliyense amatailapo kuti apeze coonadi. Zimafuna nthawi kuti munthu amvetsele uthenga wa Ufumu na kuti aziŵelenga Baibo na mabuku ophunzilila Baibo. Zimafunanso nthawi kuti tizicita phunzilo laumwini, kukonzekela misonkhano komanso kukapezekapo. Conco, timafunika ‘kugula nthawi,’ kapena kuti kuiwombola ku zinthu zosafunika kweni-kweni. (Ŵelengani Aefeso 5:15, 16, na mawu a munsi.) Kodi zimatenga nthawi itali bwanji kuti munthu aphunzile mfundo zoyambilila za coonadi ca m’Baibo? Zimadalila mmene zinthu zilili mu umoyo wa munthuyo. Komabe, kuphunzila nzelu za Yehova, njila zake, na nchito zake, kulibe malile. (Aroma 11:33) Nsanja ya Mlonda yoyambilila inayelekezela mfundo imodzi ya coonadi na “duŵa laling’ono.” Ndiyeno, inakamba kuti: “Musakhutile ndi duŵa limodzi cabe la coonadi. Ngati kupeza duŵa limodzi, kapena kuti mfundo imodzi ya coonadi kunali kokwanila, Mulungu sakanapeleka mfundo zambili za coonadi. Pitilizani kusakila ena ambili, musaleke.” Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nili na cidziŵitso coculuka bwanji ca coonadi?’ Olo tikakhale na moyo wamuyaya, sitidzakwanitsa kuphunzila zonse zokhudza Yehova. Masiku ano, cofunika kwambili ni kuseŵenzetsa nthawi yathu mwanzelu kuti tiphunzile mfundo zambili za coonadi mmene tingathele. Ganizilani citsanzo ca munthu wina amene anali na njala ya coonadi.

8 Mayi wina wa ku Japan, dzina lake Mamiko, * anapita kukacita maphunzilo ena ake ku America, mumzinda wa New York. Panthawiyo, anali m’kagulu kenakake kacipembedzo kamene kanayamba mu 1959 ku Japan. Tsiku lina, mlongo wina amene ni mpainiya anakumana na Mamiko mu ulaliki wa ku nyumba na nyumba. Pamene Mamiko anayamba kuphunzila coonadi, anakondwela kwambili, cakuti anapempha mlongoyo kuti aziphunzila naye Baibo kaŵili pa wiki. Atangoyamba kuphunzila, Mamiko anayamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo olo kuti anali na zocita zambili ku sukulu, komanso anali kuseŵenza. Cinanso, iye analeka kucita zosangalatsa zina n’colinga cakuti azipeza nthawi yophunzila coonadi. Kucita izi kunam’thandiza kuti apite patsogolo mofulumila mwauzimu. Caka cikalibe kusila, iye anabatizika. Patapita miyezi 6, mu 2006, Mamiko anayamba upainiya, ndipo akutumikilabe monga mpainiya.

9, 10. (a) Kodi kugula coonadi kumakhudza bwanji mmene timaonela zinthu zakuthupi? (b) Ni mwayi wotani umene mtsikana wina analola kuti um’pite pofuna kugula coonadi? Nanga amamvela bwanji na cosankha cimene anapanga?

9 Cuma cakuthupi. Kuti tigule coonadi, nthawi zina tingafunike kusiya nchito yapamwamba. Mwacitsanzo, Petulo na Andireya anali asodzi a nsomba. Koma pamene Yesu anawaitana kuti akhale “asodzi a anthu,” iwo “anasiya maukonde awo.” (Mat. 4:18-20) Sikuti anthu onse amene amaphunzila coonadi masiku ano, angafunike kusiya nchito yawo. Zili conco cifukwa ambili mwa iwo ali na udindo wa m’Malemba wosamalila mabanja awo. (1 Tim. 5:8) Koma nthawi zambili, anthu akaphunzila coonadi, amafunika kusintha kaonedwe kawo ka zinthu zakuthupi. Komanso, amafunika kusintha zinthu zimene amaika patsogolo mu umoyo wawo. Yesu anati: “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi, . . . Koma unjikani cuma canu kumwamba.” (Mat. 6:19, 20) Ganizilani citsanzo cotsatilaci.

10 Maria anali kukonda maseŵela a gofu kucokela ali wacicepele, asanayambe sukulu. Pamene anali ku sukulu ya sekondale, anapitiliza kuwonjezela luso pa maseŵelewa. Ndipo m’kupita kwa nthawi, anapatsiwa mwayi wokacita maphunzilo apamwamba ku yunivesiti. Maseŵela a gofu anali monga cakudya cake. Ndipo colinga cake cinali cokapeza nchito ya ndalama zambili monga katswili wa maseŵelawa. Koma atatsiliza maphunzilowo, Maria anayamba kuphunzila Baibo, ndipo anacikonda coonadi. Iye anakondwela na mmene coonadi cinamuthandizila kusintha umoyo wake. Maria anati: “Pamene n’nayesetsa kusintha umoyo wanga kuti ugwilizane na miyezo ya m’Baibo, m’pamene n’nakhala wacimwemwe kwambili.” Maria anazindikila kuti n’zosatheka kwa iye kufuna-funa cuma cauzimu ndi cakuthupi pa nthawi imodzi. (Mat. 6:24) Iye anagula coonadi mwa kusiya colinga cake cokhala katswili wa maseŵela a gofu, cimene cikanamupangitsa kukhala wolemela ndi wochuka. Maria tsopano akutumikila monga mpainiya, ndipo anakamba kuti ali na “umoyo wacimwemwe kwambili komanso waphindu.”

11. Kodi mgwilizano wathu na anzathu komanso acibululu ungakhudziwe bwanji ngati tagula coonadi?

11 Mabwenzi komanso acibululu. Tikayamba kutsatila mfundo za coonadi cimene taphunzila, mgwilizano wathu na anzathu komanso acibululu ungasokonezeke. Cifukwa ciani? Kumbukilani kuti Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti: “Ayeletseni ndi coonadi. Mawu anu ndiwo coonadi.” (Yoh. 17:17) Mawu akuti “ayeletseni” angatanthauzenso kuti “apatuleni.” Pamene taphunzila coonadi, timakhala ngati tapatulidwa m’dzikoli, cifukwa sitiyendelanso nzelu za anthu a m’dzikoli. Timaoneka osiyana ndi anthu ena cifukwa ca mfundo zimene timayendela. Timatsatila mfundo za m’Baibo. Sikuti timafuna kusokoneza mgwilizano. Koma nthawi zina, anzathu komanso acibululu angayambe kutisala kapena kutitsutsa cifukwa cakuti taphunzila coonadi. Izi n’zosadabwitsa, cifukwa Yesu anati: “Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:36) Koma iye analonjeza kuti tikagula coonadi, tidzapeza madalitso oculuka kuposa zilizonse zimene tingadzimane.—Ŵelengani Maliko 10:28-30.

12. Kodi mwamuna wina waciyuda anatailapo ciani kuti aphunzile coonadi?

12 Myuda wina wa zamalonda, dzina lake Aaron, kuyambila ali wacicepele anaphunzitsidwa kuti dzina la Mulungu siliyenela kuchulidwa. Komabe, Aaron anali na njala ya coonadi. Iye anakondwela kwambili wa Mboni wina atam’fotokozela kuti ngati taphatikiza mavawelo ku zilembo zinayi za Ciheberi za dzina la Mulungu, dzinalo lingachulidwe kuti “Yehova.” Ali na cimwemwe, iye anapita kwa atsogoleli a cipembedzo cawo kuti akawauzeko zimene anamvazo. Zimene iwo anacita si zimene Aaron anali kuyembekezela. Atsogoleliwo anakhumudwa kwambili na zimene iye anaphunzila ponena za dzina la Mulungu, moti anam’thila mata komanso anayamba kumusala. Acibululu ake nawonso analeka kugwilizana naye. Koma izi sizinamubweze m’mbuyo. Aaron sanaleke kuphunzila coonadi. Ndipo anatumikila Yehova monga Mboni yolimba mtima kwa moyo wake wonse. Mofanana ndi Aaron, kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, tifunika kupilila olo pamene anzathu kapena acibululu ayamba kutisala kapena kutitsutsa.

13, 14. Kodi tifunika kusintha bwanji maganizo na khalidwe lathu kuti tigule coonadi? Fotokozani citsanzo.

13 Maganizo komanso makhalidwe oipa. Kuti tilabadile coonadi na kuyamba kutsatila miyezo ya m’Baibo ya makhalidwe abwino, tifunika kukhala okonzeka kusintha maganizo na kuleka makhalidwe oipa. Onani zimene Petulo anakamba pa nkhaniyi. Iye anati: “Monga ana omvela, lekani kukhala motsatila zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziŵa. Koma . . . khalani oyela m’makhalidwe anu onse.” (1 Pet. 1:14, 15) Mzinda wa Korinto unali wodzala na makhalidwe oipa. Conco, kuti anthu a mu mzindawo agule coonadi, anafunika kupanga masinthidwe aakulu mu umoyo wawo. (1 Akor. 6:9-11) Mofananamo, anthu ambili masiku ano asiya makhalidwe oipa n’colinga cakuti agule coonadi. Petulo anakumbutsanso Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Nthawi imene yapitayi inali yokwanila kwa inu kucita cifunilo ca anthu a m’dzikoli pamene munali kucita zinthu zosonyeza khalidwe lotayilila, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitilila muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Pet. 4:3.

14 Kwa zaka zambili, Devynn na Jasmine anali zidakwa. Cifukwa ca ucidakwa, Devynn sanali kupeza nchito yodalilika, olo kuti anali kudziŵa bwino nchito yolemba za kayendetsedwe ka ndalama za kampani. Mkazi wake Jasmine anali wamkali komanso waciwawa. Tsiku lina pamene Jasmine anali kuyenda atakolewa, anakumana na amishonale aŵili a Mboni. Amishonalewo anapangana naye zophunzila Baibo. Koma atafika pa nyumba pawo wiki yotsatila, anapeza kuti Jasmine na mwamuna wake Devynn ni okolewa. Iwo sanayembekezele kuti amishonalewo angawaganizile mpaka kubwela ku nyumba kwawo. Ulendo wotsatila, anawapeza osakolewa. Kuyambila nthawi imeneyo, Jasmine na Devynn anayamba kuphunzila Baibo mwakhama na kuseŵenzetsa zimene anali kuphunzila. M’miyezi itatu cabe, iwo analeka kumwa moŵa, ndipo pambuyo pake anakalembetsa cikwati cawo ku boma. Anthu ambili m’mudzi mwawo anadziŵa za kusintha kwawo, ndipo anayamba kuphunzila Baibo.

15. N’ciani cimene cingakhale covuta kwambili kuleka pamene munthu wayamba kuphunzila coonadi? Nanga n’cifukwa ciani?

15 Miyambo na zikondwelelo zosagwilizana na Malemba. Cimodzi mwa zinthu zimene zimavuta kwambili kuti munthu aleke akayamba kuphunzila coonadi, ni miyambo yosagwilizana na Malemba. Anthu ena siciwavuta kumvetsetsa zifukwa zimene Malemba amaletsela kucita miyambo imeneyi. Koma kuti aileke, amadodoma cifukwa coopa acibululu, anzawo a ku nchito, na mabwenzi. Zimakhala zovuta kwambili, maka-maka ngati miyambo imeneyo iphatikizapo kulemekeza acibululu amene anamwalila. (Deut. 14:1) Koma kuganizila citsanzo ca anthu amene anaonetsa kulimba mtima, kungatilimbikitse kuleka miyambo yosagwilizana na Malemba. Tsopano, tiyeni tikambilane mmene anthu a m’nthawi ya atumwi okhala ku Efeso, anaonetsela kulimba mtima pankhaniyi.

16. Kodi anthu ena ku Efeso anacita ciani kuti agule coonadi?

16 Mzinda wa Efeso unali wodziŵika kwambili ndi zamatsenga. Kodi anthu ongotembenukila kumene ku Cikhristu, amene poyamba anali kucita zamatsenga, anacitanji kuti asiye miyambo yosagwilizana na Malemba ndi kugula coonadi? Baibo imati: “Ambili ndithu amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000. Conco mawu a Yehova anapitiliza kufalikila ndi kugonjetsa zopinga zambili.” (Mac. 19:19, 20) Akhristu okhulupilika amenewo anataya zambili kuti agule coonadi, ndipo anapeza madalitso osaneneka.

17. (a) N’zinthu zina ziti zimene timatailapo kuti tigule coonadi? (b) Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani yotsatila?

17 Kodi imwe munatailapo ciani kuti mugule coonadi? Tonse timatailapo nthawi kuti tiphunzile mfundo zatsopano za coonadi. Pali anthu ena amene anatailapo cuma cakuthupi kuti aphunzile coonadi, ndipo ena analolela kusalidwa na acibululu awo kapena anzawo. Ambili asintha maganizo awo na makhalidwe awo oipa, kapena aleka kucita miyambo yosagwilizana na mfundo za m’Baibo kuti agule coonadi. Zilibe kanthu kuti tinatailapo ciani, tidziŵa kuti coonadi ca m’Baibo cimene tinapeza n’camtengo wapatali kwambili kuposa cina ciliconse cimene tinatailapo. Cimatipatsa mwayi wapadela wokhala pa ubwenzi na Yehova. Tikaganizila madalitso amene tapeza cifukwa cophunzila coonadi, cingakhale comvetsa cisoni kwambili ngati wina angafune kucigulitsa. N’ciani cingacititse munthu kugulitsa coonadi? Nanga tingapewe bwanji kucita zimenezi? Tidzakambilana mafunso amenewa m’nkhani yokonkhapo.

^ par. 8 Maina ena m’nkhani ino asinthiwa.