Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi Opeleka Zabwino amene Yesu anachula madzulo akuti maŵa adzaphedwa anali ndani? Nanga n’cifukwa ciani anali kuchulidwa na mawu aulemu amenewa?

Madzulo akuti maŵa adzaphedwa, Yesu analangiza ophunzila ake kuti sayenela kudzifunila udindo wapamwamba pakati pa olambila anzawo. Iye anawauza kuti, “Mafumu a mitundu ya anthu amacita ulamulilo pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amachedwa Opeleka zabwino. Inu musakhale otelo.”—Luka 22:25, 26.

Kodi Opeleka Zabwino amene Yesu anachula anali ndani? Mawu olembedwa pa ndalama zakobili, komanso ozokotedwa pa miyala, ndi zolemba zina zakale, aonetsa kuti cinali cizolowezi ca Agiriki na Aroma kupeleka ulemu kwa anthu ochuka kapena olamulila mwa kuwachula na mawu aulemu akuti Euergetes, kapena kuti Opeleka Zabwino. Anthu amenewa anali kuchulidwa na mawu aulemu amenewa cifukwa ca zabwino zinazake zimene anacita pothandiza anthu.

Mafumu angapo anali kuchulidwa na mawu aulemu amenewa akuti Opeleka Zabwino. Ena mwa iwo ni olamulila a Iguputo monga Tolemi III na Tolemi VIII, komanso olamulila a Roma, Juliasi Kaisara ndi Augusito. Nayenso Herode Wamkulu, mfumu ya Yudeya, anali kuchulidwa na mawu amenewa. Cioneka kuti Herode anayamba kuchulidwa na mawu aulemu amenewa cifukwa cakuti anagula tiligu na kupatsa anthu a m’dziko lake pa nthawi imene kunali njala, komanso anapatsa zovala anthu osauka.

Katswili wina wa Baibo wa ku German, dzina lake Adolf Deissmann, anakamba kuti anthu kale anali kuseŵenzetsa kwambili mawu akuti Opeleka Zabwino. Iye anati: “Ngati munthu wafufuza m’zolemba zakale zozokotedwa pa miyala, angathe kupeza [dzina laulemu limeneli] maulendo okwana 100, m’kanthawi kocepa cabe.”

Nanga Yesu anatanthauza ciani pamene anauza ophunzila ake kuti, “Inu musakhale otelo”? Kodi tingati Yesu anali kuwaletsa kuti asamadele nkhawa za ena kapena kuwathandiza? Iyai. Cioneka kuti Yesu anakamba mawuwa pofuna kucenjeza ophunzila ake kuti sayenela kukhala na zolinga zadyela pothandiza ena.

Anthu ambili acuma m’nthawi ya Yesu, pofuna kudzipangila dzina labwino, anali kupeleka ndalama zothandizila pomanga mapaki na makacisi, zocilikizila zionetselo na maseŵela osiyana-siyana, komanso zothandizila pa nchito zina. Koma anali kucita izi n’colinga cakuti achuke, anthu aziwatamanda, komanso kuti awavotele. Buku lina linakamba kuti: “Ngakhale kuti nthawi zina anthu amenewa anali kuthandiza ena na zolinga zabwino, kambili anali kucita izi na zolinga zadyela zandale.” Conco, Yesu anali kulangiza ophunzila ake kuti ayenela kupewa mtima wadyela ndi wodzifunila ulemelelo ndi udindo ngati umenewo.

Patapita zaka, mtumwi Paulo anagogomeza mfundo yofunika kwambili imeneyi, yakuti tiyenela kukhala na zolinga zabwino pamene tipatsa ena zinthu. Polembela Akhristu anzake ku Korinto, iye anati: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”—2 Akor. 9:7.