Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumayesetsa Kuona Zinthu Mmene Yehova Amazionela?

Kodi Mumayesetsa Kuona Zinthu Mmene Yehova Amazionela?

“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.”—AROMA 12:2.

NYIMBO: 56, 123

1, 2. Kodi timaphunzila kucita ciani pamene tikula mwauzimu? Fotokozani citsanzo.

YELEKEZELANI kuti mukuona mwana wamng’ono akulandila mphatso. Ndiyeno, makolo ake akumuuza kuti, “Uzicita zikomo.” Mwanayo adzacitadi zikomo, koma cifukwa cakuti makolo ake ndiwo amuuza. Koma pamene akula, iye amayamba kumvetsetsa cifukwa cake makolo ake amafuna kuti aziyamikila anthu akamucitila zabwino. Komanso, amayamba kuyamikila mocokela pansi pa mtima. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti akuzindikila kuti kuyamikila n’kofunika.

2 Mofananamo, pamene tinaphunzila coonadi, tinazindikila kufunika komvela malamulo a Yehova. Koma pamene tikukula mwauzimu, timaphunzila zambili zokhudza Yehova, monga zimene iye amakonda, zimene amazonda, komanso mmene amaonela zinthu pa nkhani zosiyana-siyana. Ndipo ngati tiphunzila kuona zinthu mmene iye amazionela, komanso kulola maganizo ake kutitsogolela pa zocita na zosankha zathu, timaonetsa kuti tayamba kuyendela maganizo a Yehova.

3. N’cifukwa ciani nthawi zina cingakhale covuta kuona zinthu mmene Yehova amazionela?

3 Kuphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela n’kokondweletsa, koma nthawi zina kumakhala kovuta. Zili conco cifukwa kupanda ungwilo kungatilepheletse kukhala na kaonedwe ka Yehova pa zinthu zina. Mwacitsanzo, nthawi zina cingakhale covuta kuona zinthu mmene Yehova amazionela pa nkhani ya kukonda cuma, nchito yolalikila, khalidwe la ciwelewele, kuseŵenzetsa magazi molakwika, na nkhani zina. Kodi tingacite ciani kuti tipitilize kuona zinthu mmene Mulungu amazionela? Nanga kucita izi kungakhudze bwanji zocita zathu pali pano komanso za kutsogolo?

KUPHUNZILA KUONA ZINTHU MMENE MULUNGU AMAZIONELA

4. Kuti ‘tisinthe maganizo athu’ monga mmene Paulo anatilangizila, n’ciani cimene tifunika kucita?

4 Ŵelengani Aroma 12:2. Pa lembali, mtumwi Paulo anakamba zimene tifunika kucita kuti tiphunzile kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Nkhani yapita inafotokoza zimene tingacite kuti tipewe ‘kutengela nzelu za nthawi ino.’ Inakamba kuti sitifunika kulola nzelu na maganizo a dziko kuloŵa mu mtima mwathu. Koma Paulo anakambanso kuti tifunika ‘kusintha maganizo athu.’ Kuti ticite izi, tifunika kumaŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha. Kucita zimenezi kumatithandiza kuti tidziŵe bwino mmene iye amaonela zinthu, komanso kuti tisinthe maganizo athu kukhala ogwilizana ndi ake.

5. Kodi kuŵelenga wamba na kuŵelenga kofuna kuphunzila kumasiyana bwanji?

5 Kuŵelenga kofuna kuphunzila zinthu n’kosiyana ndi kuŵelenga wamba, kapena kungoconga mayankho m’nkhani inayake yophunzila. Pamene tiŵelenga, tifunika kuganizila zimene nkhaniyo itiphunzitsa ponena za Yehova, njila zake, ndiponso mmene amaonela zinthu. Timafunikanso kumvetsetsa cifukwa cake Mulungu amatilamula kucita zinthu zina na kutiletsa kucita zina. Cinanso, tifunika kudzifunsa kuti, ‘Malinga n’zimene naŵelenga, n’ciani cimene nifunika kusintha pa zocita zanga komanso pa kaganizidwe kanga?’ Sikuti pa phunzilo lililonse laumwini, tiyenela kusinkha-sinkha zonse zimenezi. Koma kuti tipindule na phunzilolo, tiyenela kumapatula nthawi yokwanila yosinkha-sinkha pa zimene taŵelenga. Mwina tingapatule hafu ya nthawi imene timathela pocita phunzilo laumwini kuti tisinkhe-sinkhe.—Sal. 119:97; 1 Tim. 4:15.

6. N’ciani cimacitika ngati timasinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu?

6 Ngati nthawi zonse timasinkha-sinkha Mawu a Mulungu, kaonedwe kathu ka zinthu kamayamba kusintha mocititsa cidwi. Timafika ‘pozindikila,’ kapena kuti kukhutila kuti kaonedwe ka zinthu ka Yehova ndiko kabwino koposa. Conco, timayamba kuona zinthu monga mmene iye amazionela. Ndipo maganizo athu amasintha. Motelo, pang’ono-m’pang’ono, timayamba kuyendela maganizo a Yehova.

MAGANIZO ATHU AMAKHUDZA ZOCITA ZATHU

7, 8. (a) Kodi Yehova amaziona bwanji zinthu zakuthupi? (Onani mapikica kuciyambi.) (b) Ngati timaona zinthu mmene Yehova amazionela, kodi nthawi zonse tidzayamba kuika zinthu ziti patsogolo?

7 Tisaiŵale kuti zimene munthu amaganiza zimakhudza zocita zake. (Maliko 7:21-23; Yak. 2:17) Kuti timvetsetse zimenezi, tiyeni tikambilaneko zitsanzo zocepa cabe. Citsanzo coyamba ni ca mmene Yehova amaonela zinthu zakuthupi. Mabuku a Uthenga Wabwino amaonetsa bwino maganizo a Yehova pa nkhaniyi. Mulungu anasankha Mariya na Yosefe kuti adzalele Mwana wake, olo kuti iwo sanali olemela. (Lev. 12:8; Luka 2:24) Yesu atabadwa, Mariya ‘anamugoneka modyelamo ziweto, cifukwa anasoŵa malo m’nyumba ya alendo.’ (Luka 2:7) Yehova akanafuna, sembe anapeza njila yakuti Mwana wake akabadwile m’nyumba yabwino. Koma iye anaona kuti cofunika kwambili n’cakuti Yesu akaleledwe na makolo okonda zinthu zauzimu.

8 Nkhani imeneyi yokamba za kubadwa kwa Yesu, ingatithandize kumvetsetsa mmene Yehova amaonela zinthu zakuthupi. Makolo ena amayesetsa kuthandiza ana awo kuti adzakhale na zinthu zambili zakuthupi, ngakhale kuti kucita zimenezo kungawononge ubwenzi wa anawo na Yehova. Koma monga taonela, Yehova amaona kuti zinthu zauzimu ndizo zofunika kwambili. Kodi mumayendela maganizo a Yehova pa nkhaniyi? Nanga zocita zanu zimaonetsa kuti muli na maganizo otani?—Ŵelengani Aheberi 13:5.

9, 10. Tingaonetse bwanji kuti timaona nkhani yokhumudwitsa ena mmene Yehova amaionela?

9 Citsanzo cina n’ca mmene Mulungu amaonela nkhani yokhumudwitsa ena. Yesu anati: “Aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupililati, zingakhale bwino kwambili kuti amumangilile cimwala camphelo m’khosi mwake, ngati cimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.” (Maliko 9:42) Mawu amenewa aonetsa kuti kukhumudwitsa ena ni nkhani yaikulu kwambili. Popeza kuti Yesu anatengela ndendende makhalidwe a Atate wake, ndiye kuti Yehova nayenso amaipidwa kwambili ngati munthu amacita mwadala zinthu zimene zingakhumudwitse mmodzi wa otsatila a Yesu.—Yoh. 14:9.

10 Kodi timaona nkhaniyi mmene Yehova na Yesu amaionela? Kodi mumayendela maganizo a Yehova pa nkhaniyi? Nanga kodi zocita zanu zimaonetsadi kuti mumayendela maganizo ake? Mwacitsanzo, tinene kuti mwakopeka na sitayelo inayake ya kavalidwe na kudzikongoletsa, imene ingakhumudwitse ena mu mpingo kapena kudzutsa cilakolako coipa mu mtima mwawo. Kodi mudzapewa masitayelo otelo cifukwa coganizila Akhristu ena?—1 Tim. 2:9, 10.

11, 12. Kodi kuona zoipa mmene Mulungu amazionela na kukhala odziletsa kungatithandize bwanji kupewa makhalidwe oipa?

11 Citsanzo cotsiliza n’cakuti Yehova amadana ndi kupanda cilungamo. (Yes. 61:8) Yehova amadziŵa kuti cifukwa ca kupanda ungwilo, tili na cikhotelelo cocita zoipa. Olo n’telo, iye amafuna kuti tizidana na kupanda cilungamo monga mmene iye amacitila. (Ŵelengani Salimo 97:10.) Kusinkha-sinkha pa cifukwa cimene Yehova amazondela zoipa kudzatithandiza kuyamba kuona zinthu mmene iye amazionela, komanso kudzatilimbikitsa kupewa kucita zoipa.

12 Kuona zinthu zopanda cilungamo monga mmene Yehova amazionela, kudzatithandizanso kudziŵa kuti zinthu zina n’zoipa, olo kuti sizichulidwa mwacindunji m’Mawu a Mulungu. Mwacitsanzo, kuvina kodukulilana pa mendo koutsa cilako-lako (kochedwa lap dancing) ni khalidwe loipa limene layamba kufala kwambili m’dzikoli. Ena amapeleka zifukwa zodzikhululukila, n’kumakamba kuti kavinidwe kameneka si koipa mofanana ndi kucita ciwelewele ceni-ceni. * Koma kodi umu ni mmenedi Mulungu amaonela kavinidweko? Tisaiŵale kuti Yehova amazonda coipa ca mtundu uliwonse. Conco, tifunika kupewelatu zinthu zoipa mwa kukulitsa khalidwe la kudziletsa, na kuzonda zinthu zimene Yehova amazonda.—Aroma 12:9.

KUGANIZILA MMENE TIDZAPANGILA ZOSANKHA ZAKUTSOGOLO

13. Kodi kuganizila mmene Yehova amaonela zinthu kungakatithandize bwanji kutsogolo popanga zosankha?

13 Pamene tikuphunzila, tiyenela kumaganizila mmene Yehova amaonela zinthu, cifukwa kucita zimenezi kungakatithandize pa zosankha zakutsogolo. Mwacitsanzo, ngati pacitika zinthu zofuna kuti tipange cosankha mwamsanga, sicidzakhala covuta kusankha mwanzelu. (Miy. 22:3) Tsopano, tiyeni tikambilane zitsanzo zingapo za m’Baibo.

14. Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yosefe anakanila kugona ndi mkazi wa Potifara?

14 Pamene mkazi wa Potifara ananyengelela Yosefe kuti agone naye, iye anakana nthawi yomweyo. Izi zionetsa kuti Yosefe anali ataganizila pasadakhale za mmene Yehova amaonela nkhani ya kukhala wokhulupilika m’cikwati. (Ŵelengani Genesis 39:8, 9.) Kuwonjezela apo, pamene Yosefe anayankha mkazi wa Potifara kuti: “Ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?,” anaonetsa kuti anali kuyendela maganizo a Mulungu. Nanga bwanji imwe? Kodi mungacite ciani ngati munthu wina ku nchito wayamba kucita zinthu zoonetsa kuti amakufunani? Kapena bwanji ngati pa foni yanu mwalandila meseji kapena pikica youtsa cilako-lako ca kugonana? * Sitingagonje ku mayeselo amenewa ngati tinaganizila pasadakhale za mmene Yehova amaonela makhalidwe amenewa, komanso ngati tinasankhilatu zimene tingacite.

15. Mofanana ndi anyamata atatu aciheberi, kodi tingacite ciani kuti tidzakhale okhulupilika kwa Yehova tikadzakumana na ciyeso?

15 Tsopano, ganizilani citsanzo ca anyamata atatu aciheberi, Sadirake, Mesake ndi Abedinego. Iwo anakanitsitsa kulambila fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiimika, komanso anayankha mosazengeleza atafunsiwa mafunso. Izi zionetsa kuti anyamatawa anali ataganizilapo pasadakhale za kukhala okhulupilika kwa Yehova. (Eks. 20:4, 5; Dan. 3:4-6, 12, 16-18) Nanga bwanji imwe? Tiyelekezele kuti abwana anu akupemphani kuti mupeleke ndalama zocilikizila cikondwelelo cokhudzana ndi cipembedzo conyenga. Kodi mungacite ciani? M’malo moyembekezela mpaka zaconco zikakucitikileni, mungacite bwino kusinkha-sinkha pasadakhale mmene Yehova amaonela nkhani zimenezi. Ndipo ngati zotelo zakucitikilani, sicidzakhala covuta kucita zinthu moyenelela kapena kuyankha mwanzelu mofanana ndi anyamata atatu aja aciheberi.

Kodi munafufuza mfundo zokhudza kusankha cithandizo ca mankhwala, kusaina khadi ya DPA, komanso kufotokozela madokota zosankha zanu? (Onani palagilafu 16)

16. Kodi kudziŵa bwino mmene Yehova amaonela zinthu kungatithandize bwanji tikadwala mosayembekezeleka?

16 Kuganizila pasadakhale za kufunika kokhala wokhulupilika, kungakhalenso kothandiza ngati tadwala matenda aakulu mwadzidzidzi. N’zoona kuti timapewa kuikiwa magazi athunthu, kapena ciliconse mwa zigawo zake zinayi zikulu-zikulu. Komabe, njila zina za kucipatala zothandizila odwala poseŵenzetsa magazi, zimafuna kuti tidzipangile tekha cosankha mogwilizana na mfundo za m’Baibo, zimene zimaonetsa maganizo a Yehova. (Mac. 15:28, 29) Kodi nthawi yabwino yopanga cosankha pa nkhaniyi ni iti? Kodi ni pa nthawi imene tili m’cipatala, mwina tikumvela ululu, ndipo tikufunikila kupanga cosankha mwamsanga-msanga? Mwacionekele, yankho ni yakuti iyai. Ino ndiyo nthawi yabwino yofufuza mfundo zokhudza nkhaniyi, kusaina khadi ya DPA yoonetsa zosankha zathu pa cithandizo camankhwala, komanso kufotokozela madokota zosankha zathu. *

17-19. N’cifukwa ciani kuphunzililatu pali pano mmene Yehova amaonela zinthu n’kofunika? Fotokozani cimodzi mwa zocitika zimene tiyenela kuzikonzekelelatu.

17 Potsiliza, ganizilani citsanzo ca Yesu. Pamene Petulo anam’patsa malangizo olakwika akuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye,” iye anayankha mosazengeleza. Mwacidziŵikile, Yesu anali ataganizilapo kale mwakuya za colinga cimene Mulungu anali naco pa iye, komanso zimene Malemba anakambilatu ponena za umoyo na imfa yake pano padziko lapansi. Kuganizila zimenezi kunamulimbikitsa kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova, na kupeleka moyo wake monga dipo la anthu onse.—Ŵelengani Mateyu 16:21-23.

18 Masiku anonso, Mulungu amafuna kuti anthu ake akhale naye pa ubwenzi wolimba, na kuti azigwila nchito yake modzipeleka. (Mat. 6:33; 28:19, 20; Yak. 4:8) Koma monga mmene zinalili kwa Yesu, anthu ena ooneka monga akutifunila zabwino angayese kutilepheletsa kuika cifunilo ca Mulungu patsogolo. Mwacitsanzo, bwanji ngati abwana anu alonjeza kuti adzakukwezani pa nchito na kuwonjezela malipilo anu, koma muona kuti izi zingasokoneze pulogilamu yanu yocita zinthu zauzimu? Kapena bwanji ngati ndimwe mwana wa sukulu, ndipo mwapatsiwa mwayi wokacita maphunzilo owonjezela ku sukulu inayake ya kutali na kwanu? Kodi iyi ndiyo nthawi yopemphela na kufufuza malangizo othandiza pa nkhanizi, kufunsa anthu a m’banja mwanu kapena akulu, kenako n’kupanga cosankha? Zingakhale bwino kuphunzililatu pali pano mmene Yehova amaonela nkhani zimenezi na kuyamba kuziona monga mmene iye amazionela. Mukatelo, ndiye kuti ngati mutapatsiwa mwayi wa nchito kapena wa maphunzilo ngati umenewo, simudzavutika kupanga cosankha. Mumakhala kuti mwadziikila kale zolinga zauzimu, mwakonzekeletsa mtima wanu, ndipo cangotsala n’kucita zinthu mogwilizana ndi cosankha canu.

19 Mwina mungaganizilenso zocitika zina zosayembekezeleka zimene zingayese kukhulupilika kwanu kwa Yehova. N’zoona kuti sitingathe kukonzekela zonse zimene zingaticitikile. Koma ngati pocita phunzilo laumwini timasinkha-sinkha mmene Yehova amaonela zinthu, cidzakhala cosavuta kukumbukila mfundo zimene timaphunzila, na kuziseŵenzetsa popanga zosankha pa cocitika ciliconse mu umoyo wathu. Conco, tiyeni tiziyesetsa kuphunzila mmene Yehova amaonela zinthu pa nkhani zosiyana-siyana na kuyamba kuyendela maganizo ake. Komanso, tiziganizila mmene kukhala na kaonedwe ka Mulungu pa nkhani zimenezo kungakhudzile zocita zathu, tsopano na kutsogolo.

KUONA ZINTHU MMENE YEHOVA AMAZIONELA KUMAKHUDZA TSOGOLO LATHU

20, 21. (a) Ni ufulu wanji umene tidzakondwela nawo m’dziko latsopano? (b) N’ciani cimene tiyenela kucita kuti tikhale na cimwemwe pali pano?

20 Tikuyembekezela mwacidwi dziko latsopano. Ambili a ise tikuyembekezela kukakhala na moyo wosatha m’paradaiso pano pa dziko lapansi. Mu Ufumu wa Mulungu, tidzamasuka ku mavuto amene timakumana nawo m’dzikoli. Koma ngakhale pa nthawiyo, tidzakhalabe na ufulu wodzisankhila zocita. Aliyense adzakhala na ufulu wopanga zosankha malinga na zokonda zake.

21 Komabe, ufuluwo udzakhala na malile. Pofuna kusankha pakati pa cabwino na coipa, ofatsa adzapitiliza kutsatila malamulo a Yehova na kuyendela maganizo ake. Kucita izi kudzakhala kokondweletsa, ndipo kudzapangitsa anthu kukapeza cimwemwe cosaneneka komanso mtendele woculuka. (Sal. 37:11) Koma ngakhale pali pano, tingathe kukhala na cimwemwe ngati tiyendela maganizo a Yehova.

^ par. 12 Pa kuvina kodukulilana pa mendo kumeneku kochedwa lap dancing, “nthawi zambili mkazi wovala twamkati cabe amakhala pa mendo pa mwamuna n’kumavina modukula.” Malinga na mmene zingacitikile, kuvina kwa lap dancing kungafanane ndi khalidwe la ciwelewele, ndipo kungafunikile komiti ya ciweluzo. Conco, Mkhristu aliyense amene watengako mbali pa mcitidwe umenewu afunika kukapempha thandizo kwa akulu.—Yak. 5:14, 15.

^ par. 14 Anthu ena amatumizilana mameseji, mapikica, kapena mavidiyo pa foni okhudza zakugonana. Malinga na mmene zinacitikila, anthu ocita zimenezi angafunike kuwapangila komiti ya ciweluzo. Nthawi zina, ngakhale acicepele amene amacita khalidwe limeneli, angaimbidwe mlandu na boma. Kuti mudziŵe zambili, pitani pa jw.org (ku Chichewa), na kuŵelenga nkhani yakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?” (Onani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACINYAMATA.) Kapena onani nkhani yakuti, “Kukambirana ndi Mwana Wanu Nkhani Yotumizirana Zinthu Zolaula,” mu Galamukani! ya November 2013, mape. 4-5.

^ par. 16 Mfundo zina za m’Baibo zothandiza pa nkhaniyi zinafotokozedwa m’mabuku athu. Mwacitsanzo, onani buku lakuti, ‘Khalanibe M’cikondi ca Mulungu,’ mape. 246-249.