Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ni Mphatso Yanji Imene Tingam’patse Yehova?

Ni Mphatso Yanji Imene Tingam’patse Yehova?

PA NTHAWI ina Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Mfundo imeneyi imagwilanso nchito pa ubwenzi wathu na Yehova. N’cifukwa ciani takamba conco? Yehova amatipatsa mphatso zambili zimene zimatipangitsa kukhala acimwemwe. Koma tingakhale na cimwemwe coculuka ngati na ise timam’patsako mphatso Yehova. Kodi ni mphatso yanji imene tingam’patse? Miyambo 3:9 imati: “Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.” ‘Zinthu zathu zamtengo wapatali’ ziphatikizapo, nthawi yathu, maluso, mphamvu, na cuma cathu. Ngati tiseŵenzetsa zinthu zimenezi popititsa patsogolo kulambila koona, ndiye kuti tikum’patsa mphatso Yehova. Ndipo kucita zimenezi, kumatibweletsela cimwemwe coculuka.

Kodi n’ciani cingatithandize kuti tisamanyalanyaze kupeleka cuma cathu monga mphatso kwa Yehova? Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti “aziika kenakake pambali” monga copeleka. (1 Akor. 16:2) Kodi mungacite ciani ngati mufuna kudziŵa njila zocitila copeleka zimene zilipo ku dela lanu? Onani pansipa.

M’maiko ena, n’zosatheka kutumiza zopeleka kupitila pa Intaneti. Koma kuti mudziŵe njila zina zotumizila zopeleka, onani pa peji ya pa jw.org yotumizila zopeleka. M’maiko ena, pa peji imeneyi pali nkhani imene ili na mayankho pa mafunso amene anthu amakhala nawo pa nkhani ya zopeleka.