Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumayendela Maganizo a Ndani?

Kodi Mumayendela Maganizo a Ndani?

“Musamatengele nzelu za nthawi ino.”—AROMA 12:2.

NYIMBO: 88, 45

1, 2. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji pamene Petulo anamuuza kuti adzikomele mtima? (Onani pikica pamwambapa.) (b) N’cifukwa ciani Yesu anamuyankha mwanjila imeneyo?

OPHUNZILA a Yesu anadabwa na zimene iye anawauza. Iwo anali kuyembekezela kuti Yesu adzabwezeletsa ufumu kwa Isiraeli, koma iye anawauza kuti watsala pang’ono kuzunzidwa na kuphedwa. Atamva izi, Petulo anauza Yesu kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikucitikileni ngakhale pang’ono.” Koma Yesu anam’dzudzula. Amvekele: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”—Mat. 16:21-23; Mac. 1:6.

2 Pamene anakamba mawu aya, Yesu anaonetsa kuti maganizo a Mulungu ni osiyana na maganizo a dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Zimene Petulo anakamba zinaonetsa kuti anali na mzimu wa dziko, wokana kucita zoyenela pofuna kupewa mavuto. Koma Yesu anadziŵa kuti maganizo a Atate wake ni osiyana na maganizo amenewa. Panthawiyi, n’kuti watsala pang’ono kukumana na mavuto komanso kuphedwa, ndipo anadziŵa kuti Mulungu afuna kuti akhale wokonzeka kupilila mavuto amenewo. Zimene Yesu anayankha Petulo zinaonetsa kuti sanafune kutengela maganizo a dziko, koma anafuna kuyendela maganizo a Yehova.

3. N’cifukwa ciani zingakhale zovuta kukana maganizo a dziko na kutengela maganizo a Yehova?

3 Nanga bwanji ise? Kodi timayendela maganizo a Mulungu kapena a dziko? N’zacidziŵikile kuti pofika pano, tinasintha makhalidwe athu kuti akhale ogwilizana na malamulo a Mulungu. Koma bwanji za maganizo athu? Kodi timayesetsa kuwawongola kuti agwilizane na maganizo a Yehova? Kucita izi kumafuna kulimbika. Koma kutengela maganizo a dziko n’kosavuta. Zili conco cifukwa mzimu wa dziko uli paliponse. (Aef. 2:2) Komanso, tingathe kukopeka mosavuta na maganizo a dziko cifukwa amalimbikitsa khalidwe la kudzikonda. Conco, n’zosavuta munthu kutengela maganizo a dziko. Koma kutengela maganizo a Yehova, kumafuna kulimbika.

4. (a) N’ciani cimene cingacitike ngati titengela maganizo a dziko? (b) Kodi nkhani ino idzatithandiza bwanji?

4 Kutengela maganizo a dziko kungacititse kuti tikhale odzikonda komanso osafuna kuuzidwa zocita. (Maliko 7:21, 22) Conco, m’pofunika kuti tiziyesetsa kukhala na “maganizo a Mulungu,” osati “maganizo a anthu.” Ndipo nkhani ino idzatithandiza kucita zimenezi. Idzafotokoza mmene kuyendela maganizo a Yehova kumatipindulitsila komanso cifukwa cake sikutilanda ufulu. Idzafotokozanso mmene tingapewele kutengela maganizo a dziko. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene tingadziŵile maganizo a Yehova pa nkhani zosiyana-siyana, komanso zimene tingacite kuti tiziyendela maganizo ake.

KUYENDELA MAGANIZO A YEHOVA N’KWABWINO KOMANSO N’KOTHANDIZA

5. N’cifukwa ciani anthu ena amakamba kuti safuna kutengela maganizo a munthu wina aliyense?

5 Anthu ena amakamba kuti safuna kutengela maganizo a munthu wina aliyense. Iwo angakambe kuti, “Na ine nili na nzelu.” Pokamba mawu amenewa, mwina iwo amatanthauza kuti amafuna kusankha okha zocita, ndiponso kuti ali na ufulu wocita zimenezo. Iwo safuna kuti ena azingowauza zocita, kapena kuwaumiliza kutengela zocita za anthu ena. *

6. (a) Ni ufulu wanji umene Yehova anatipatsa? (b) Kodi ufulu umenewu ulibe malile?

6 Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti tikayamba kuyendela maganizo a Yehova, timakhalabe na ufulu wosankha. Monga mmene 2 Akorinto 3:17 imakambila, “pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” Timakhala na ufulu wosankha kuti tidzakhala munthu wotani. Timakhalanso na ufulu wosankha zocita malinga n’zokonda zathu. Umu ni mmene Yehova anatilengela. Komabe, ufulu umenewu uli na malile. (Ŵelengani 1 Petulo 2:16.) Pa nkhani ya cabwino na coipa, Yehova amafuna kuti tiziyendela maganizo ake olembedwa m’Baibo. Kodi kucita zimenezi kuli na phindu kapena kumatilanda ufulu?

7, 8. N’cifukwa ciani tingakambe kuti kuyendela maganizo a Yehova sikutilanda ufulu? Fotokozani citsanzo.

7 Ganizilani citsanzo ici: Makolo amayesetsa kuphunzitsa ana awo mfundo za makhalidwe abwino. Angawaphunzitse kukhala oona mtima, olimbikila nchito, komanso oganizila ena. Kuphunzitsa ana zimenezi sikuti n’kuwaphela ufulu. Koma n’kuwakonzekeletsa kuti akakhale na umoyo wabwino m’tsogolo. Anawo akakula, n’kukakhala kwaokha, amakhala na ufulu wodzisankhila okha zocita. Ndipo ngati asankha kutsatila mfundo za makhalidwe abwino zimene makolo awo anawaphunzitsa, amapanga zosankha mwanzelu. Akatelo, amapewa kudzibweletsela mavuto.

8 Molingana na kholo labwino, Yehova amafuna kuti ise ana ake tikhale na umoyo wacimwemwe kwambili. (Yes. 48:17, 18) Mwa ici, iye watiphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino. Yehova amafuna kuti tiziona zinthu mmene iye amazionela, komanso kuti tizitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino. Kucita izi sikutilanda ufulu, koma kumatithandiza kukulitsa luso la kuganiza. (Sal. 92:5; Miy. 2:1-5; Yes. 55:9) Ngati titsatila mfundo za Yehova, timakhalabe na mwayi wocita zinthu malinga n’zokonda zathu. Ndipo timatha kupanga zosankha zimene zingatibweletsele cimwemwe. (Sal. 1:2, 3) Zoonadi, kutengela maganizo a Yehova n’kwabwino komanso n’kothandiza.

MAGANIZO A YEHOVA NI APAMWAMBA KWAMBILI

9, 10. N’ciani cionetsa kuti maganizo a Yehova ni apamwamba kuposa a dziko?

9 Cifukwa cina cimene ise atumiki a Yehova timafunila kutengela maganizo ake, n’cakuti maganizo akewo ni apamwamba ngako kuposa a dzikoli. Anthu m’dzikoli amapeleka malangizo pa nkhani zokhudza makhalidwe, umoyo wa banja, kupeza cimwemwe pa nchito, komanso pa mbali zina za umoyo wa munthu. Koma ambili mwa malangizowo sagwilizana na maganizo a Yehova. Mwacitsanzo, malangizo a m’dzikoli amalimbikitsa anthu kukhala na mtima wodzikonda, komanso kuona kuti khalidwe la ciwelewele lilibe vuto. Nthawi zina, anthu apabanja amalangiziwa kuti ngati ali na mavuto m’banja, ngakhale aang’ono, afunika kungopatukana kapena kusudzulana, kuti akhalenso na cimwemwe. Koma malangizo aconco ni osagwilizana na Malemba ngakhale pang’ono. Ena amaganiza kuti malangizo aconco ni othandiza kulingana ndi nthawi imene tikukhalamo. Koma kodi zimenezi n’zoona?

10 Yesu anati: “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mat. 11:19) Dzikoli lapita patsogolo kwambili pa zasayansi. Koma lakangiwa kuthetsa mavuto aakulu amene alanda anthu cimwemwe—mavuto monga nkhondo, kusankhana mitundu, na upandu. Nanga bwanji za kulekelela khalidwe la ciwelewele? Anthu ambili amavomeleza kuti kulekelela khalidweli kwawonjezela mavuto monga kusila kwa vikwati, matenda, na mavuto ena. Koma Akhristu oona pa dziko lonse, amene amayendela maganizo a Mulungu, amakhala na mabanja abwino, umoyo wathanzi, na mtendele pakati pawo. (Yes. 2:4; Mac. 10:34, 35; 1 Akor. 6:9-11) Kodi uwu si umboni wakuti maganizo a Yehova ni apamwamba kuposa maganizo a dziko?

11. Kodi Mose anali kutsogoleledwa na maganizo a ndani? Nanga zotulukapo zake zinali zotani?

11 Atumiki a Mulungu akale, nawonso anali kudziŵa kuti maganizo a Yehova ni apamwamba kwambili. Mwacitsanzo, ngakhale kuti Mose anali ‘ataphunzila nzelu zonse za Aiguputo,’ anapempha Mulungu kuti amuthandize kukhala na “mtima wanzelu.” (Mac. 7:22; Sal. 90:12) Iye anamupemphanso kuti: “Ndidziwitseni njila zanu.” (Eks. 33:13) Popeza Mose analola Yehova kum’tsogolela, iye anam’seŵenzetsa mwapadela pokwanilitsa colinga cake. Ndipo Malemba amachula Mose monga munthu wa cikhulupililo cacikulu.—Aheb. 11:24-27.

12. Kodi Paulo anali kuyendela mfundo zotani mu umoyo wake?

12 Mtumwi Paulo anali munthu wanzelu komanso wophunzila kwambili, ndipo anali kudziŵa zitundu zosacepela ziŵili. (Mac. 5:34; 21:37, 39; 22:2, 3) Ngakhale zinali conco, iye anakana kuyendela nzelu za dziko mu umoyo wake. M’malomwake, anali kutsatila mfundo za m’Malemba. (Ŵelengani Machitidwe 17:2; 1 Akorinto 2:6, 7, 13) Zotulukapo zake zinali zakuti zinthu zinamuyendela bwino mu utumiki wake, ndipo anakhala na ciyembekezo cokalandila mphoto yamuyaya.—2 Tim. 4:8.

13. N’ndani ali na udindo wowongolela maganizo athu kuti akhale ogwilizana na maganizo a Yehova?

13 Malinga n’zimene takambilana, n’zoonekelatu kuti maganizo a Mulungu ni apamwamba kuposa a dzikoli. Ndipo ngati tiyendela maganizo ake, zinthu zidzatiyendela bwino, komanso tidzakhala na cimwemwe coculuka. Ngakhale n’conco, Yehova satikakamiza kuyendela maganizo ake. Nayenso “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” komanso akulu salamulila maganizo a wina aliyense wa ise. (Mat. 24:45; 2 Akor. 1:24) Koma Mkhristu aliyense payekha ali na udindo woyesetsa kuwongolela maganizo ake, kuti akhale ogwilizana na maganizo a Mulungu. Kodi tingacite bwanji zimenezi?

PEWANI KUTENGELA NZELU ZA NTHAWI INO

14, 15. (a) Kodi tifunika kumasinkha-sinkha ciani kuti titengele maganizo a Yehova? (b) Malinga n’zimene Aroma 12:2 imakamba, n’cifukwa ciani tifunika kupewa kuganizila zinthu zoipa? Fotokozani citsanzo.

14 Aroma 12:2 imatilangiza kuti: “Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.” Mawu ouzilidwa amenewa aonetsa kuti kaya tinali na maganizo otani kale, tikaphunzila coonadi, n’zotheka kuwongolela maganizo athu kuti akhale ogwilizana kwambili ndi a Mulungu. N’zoona kuti cibadwa cathu copanda ungwilo, komanso zokumana nazo mu umoyo zimapangitsa kuti tikhale na maganizo opotoka pa mbali zina. Komabe, maganizo a munthu amatha kusintha. Ndipo kuti maganizo athu asinthe, mbali yaikulu zimadalila pa zimene timalola kuti ziloŵe mu mtima mwathu, komanso zimene timakonda kuziganizila. Ngati timayesetsa kuganizila mmene Yehova amaonela zinthu, timafika pozindikila kuti maganizo ake ndiwo oyenela. Tikatelo, cimakhala cosavuta kusintha maganizo athu kuti agwilizane ndi maganizo ake.

15 Komabe, malinga n’zimene Aroma 12:2 yakamba, kuti tisinthe maganizo athu kukhala ogwilizana ndi a Yehova, tifunika kuleka ‘kutengela nzelu za nthawi ino.’ Tiyenela kuleka kuloŵetsa mu mtima mwathu maganizo oipa amene ni osagwilizana na maganizo a Mulungu. Kuti timvetsetse kufunika kocita zimenezi, tiyelekezele na cakudya. Tikambe kuti munthu winawake amayesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi n’colinga cakuti akhale na thanzi labwino. Koma kodi izi zingakhale na phindu iliyonse ngati pa nthawi imodzi-modziyo munthuyo amadya zakudya zina zoipa? Iyai. Na ise n’cimodzi-modzi. Sitingathe kuwongola maganizo athu ngati timasinkha-sinkha zinthu zabwino, koma pa nthawi imodzi-modzi n’kumawaipitsa mwa kuganizila zinthu zoipa.

16. Kodi tiyenela kupewa ciani?

16 Kodi n’zotheka kupewelatu maganizo a dziko? Iyai. N’zosatheka cifuwa tikukhala m’dziko lomweli. (1 Akor. 5:9, 10) Mwacitsanzo, tikayenda mu ulaliki, timakambilana na anthu amene ali na zikhulupililo zabodza. Ngakhale kuti n’zosatheka kupewelatu maganizo a dziko, sitiyenela kuwalekelela akabwela mu mtima mwathu kapena kuwalola kuzika mizu. Mofanana ndi Yesu, mwamsanga tiyenela kukana maganizo alionse ogwilizana na zolinga za Satana. Kuwonjezela apo, pali zinthu zina zimene tingacite kuti tipewe kutengela nzelu za dziko.—Ŵelengani Miyambo 4:23.

17. N’zinthu zina ziti zimene tingacite kuti tipewe kutengela maganizo a dziko?

17 Mwacitsanzo, tiyenela kusamala posankha mabwenzi. Baibo imaticenjeza kuti ngati tigwilizana na anthu amene salambila Yehova, tingayambe kutengela maganizo awo. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:12, 32, 33) Tiyenelanso kusankha mosamala zosangalatsa. Tifunika kupewa zosangalatsa zimene zimalimbikitsa ciphunzitso ca cisanduliko, zaciwawa, kapena zaciwelewele. Tikatelo, tidzapewa kuipitsa maganizo athu ndi mfundo ‘zotsutsana ndi kudziŵa Mulungu.’—2 Akor. 10:5.

Kodi mumathandiza ana anu kupewa zosangalatsa zoipa? (Onani mapalagilafu 18, 19)

18, 19. (a) N’cifukwa ciani tifunika kusamala na maganizo a dziko amene amafalitsidwa m’njila zovutilapo kuzizindikila? (b) Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati? Nanga n’cifukwa ciani?

18 Cinanso, tifunika kuzindikila na kukana mfundo za dziko zimene zimafalitsidwa m’njila zovutilapo kuzizindikila. Mwacitsanzo, tingamvetsele nyuzi pa wailesi kapena pa TV, yoonetsa kuti mfundo zinazake zandale n’zabwino. Kapena tingamvetsele nkhani imene colinga cake n’kulimbikitsa anthu kuona kuti zolinga za anthu komanso zocita zawo n’zothandiza komanso n’zabwino. Palinso mabuku na mafilimu ena amene amalimbikitsa anthu kuona kuti kuika zofuna zawo kapena za banja lawo patsogolo pa zonse n’kwabwino. Koma kucita izi n’kosagwilizana na mfundo za m’Baibo. Malemba amaonetsa kuti munthu amafunika kukonda Yehova kuposa zonse kuti akhale na umoyo wabwino komanso banja lacimwemwe. (Mat. 22:36-39) Kuwonjezela apo, pali tunkhani twa ŵana toŵelenga na tumafilimu twa akadoli tumene tumaoneka monga twabwino-bwino, koma tungabyale mbewu za khalidwe loipa m’mitima ya anawo.

19 Koma izi sizitanthauza kuti kucita zosangalatsa zoyenela n’kulakwa. Ngakhale n’conco, ni bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimakwanitsa kuzindikila mfundo za dziko ngakhale pamene zikufalitsidwa m’njila yovutilapo kuizindikila? Kodi nimapewa kumvetsela mapulogilamu kapena kuŵelenga mabuku na zinthu zina zosayenela? Kodi nimayesetsa kuthandizanso ana anga kupewa zimenezi? Ngati ana anga amva kapena kuona zinthu zolakwika, kodi nimayesetsa kuwongolela maganizo awo mwa kuwaphunzitsa mmene Yehova amaonela zinthu?’ Ngati timakwanitsa kusiyanitsa maganizo a dziko ndi a Mulungu, ndiye kuti tingathe kupewa ‘kutengela nzelu za nthawi ino.’

KODI MUMAYENDELA MAGANIZO A NDANI?

20. Kodi zimadalila pa ciani kuti munthu aziyendela maganizo a Mulungu kapena a dziko?

20 Kumbukilani kuti tingasankhe kumvetsela kwa Yehova kapena kumvetsela nzelu za dziko la Satanali. Kodi imwe mumayendela maganizo a ndani? A Yehova kapena a dzikoli? Yankho yagona pakuti timamvetsela kwa ndani. Ngati timamvetsela nzelu za dziko, timayamba kuyendela maganizo a dziko. Izi zingapangitse kuti tiziona zinthu mwakuthupi komanso kuti tikhale na makhalidwe oipa. Ndiye cifukwa cake tifunika kusamala na zimene timakonda kuganizila.

21. Ni mbali yofunika iti imene tidzakambilana m’nkhani yotsatila?

21 Monga taphunzilila, kuti titengele maganizo a Yehova, pali zambili zimene timafunika kucita kuposa kungopewa zinthu zimene zingaipitse maganizo athu. Tifunikanso kuphunzila mmene Mulungu amaonela zinthu n’colinga cakuti tiziona zinthu mmene iye amazionela. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene tingacitile zimenezi.

^ par. 5 Kukamba zoona, ngakhale anthu amene amakanitsitsa kutengela nzelu za ena, sangapeweletu kusonkhezeledwa na maganizo a anthu ena. Kaya ni poganizila nkhani yaikulu monga ya ciyambi ca moyo, kapena pa nkhani yaing’ono monga ya kusankha covala cakuti avale, munthu aliyense amasonkhezeledwako ndithu na maganizo a ena. Komabe, tili na ufulu wosankha kuti tidzatengela maganizo a ndani.