NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA November 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya December 30, 2019–February 2, 2020.

Limbitsani Ubwenzi Pakati Panu Mapeto Asanafike

Tingaphunzile zambili kwa Yeremiya. Mabwenzi ake anamuthandiza kuti apulumuke pa nthawi imene Yerusalemu anali pafupi kuwonongedwa.

Mmene Mzimu Woyela Umatithandizila

Mzimu woyela wa Mulungu umatithandiza kupilila mavuto. Koma kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela pali zinthu zinayi zimene tifunika kucita.

Kodi Mumasamalila Cishango Canu Cacikulu Cacikhulupililo?

Cikhulupililo cathu cili ngati cishango cimene cimatiteteza pa nkhondo yauzimu. Kodi tifunika kucita ciani kuti cishango cathu cacikhulupililo cikhalebe colimba?

Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko

M’buku la Levitiko muli malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli akale. Popeza ndife Akhristu, sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Ngakhale n’telo, tingapindule na malamulo a m’bukuli.

Tsilizitsani Zimene Munayamba Kucita

Ngakhale pamene tapanga zosankha zabwino, nthawi zina zingativute kucita zimene tasankhazo. Onani njila zimene zingakuthandizeni kuti mutsilizitse zimene munayamba kucita.

Kodi Mudziŵa?

Kodi mtumiki woyang’anila nyumba anali kugwila nchito yanji m’nthawi yakale?