Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 44

Limbitsani Ubwenzi Pakati Panu Mapeto Asanafike

Limbitsani Ubwenzi Pakati Panu Mapeto Asanafike

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”​—MIY. 17:17.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

Tidzafunikila mabwenzi abwino pa nthawi ya “cisautso cacikulu” (Onani ndime 2) *

1-2. Malinga na 1 Petulo 4:7, 8, n’ciani cidzatithandiza kupilila mavuto?

PAMENE tikuyandikila mapeto a “masiku otsiliza,” tingakumane na mavuto aakulu. (2 Tim. 3:1) Mwacitsanzo, m’dziko lina kumadzulo kwa Africa munabuka cipolowe coopsa pambuyo pa kampeni ya masankho. Kwa miyezi yoposa 6, abale na alongo athu sanali kuyenda momasuka cifukwa anthu anali kumenyana kwambili m’dela lawo. Kodi n’ciani cinawathandiza kupilila mavuto amenewa? Ena anathaŵila kwa abale amene anali kukhala ku dela lina limene kunaliko bata. M’bale wina anati: “Pa nthawi yovutayi, n’nakondwela cifukwa n’nali na mabwenzi pafupi. Ndipo tinali kulimbikitsana.”

2 “Cisautso cacikulu” cikadzayamba, mabwenzi abwino amene amatikonda adzakhala ofunika kwambili. (Chiv. 7:14) Conco, kulimbitsa ubwenzi na Akhristu anzathu pali pano n’kofunika ngako. (Ŵelengani 1 Petulo 4:7, 8.) Tingaphunzile zambili kwa Yeremiya. Mabwenzi ake anamuthandiza kuti apulumuke pa nthawi imene Yerusalemu anali pafupi kuwonongedwa. * Kodi tingatengele bwanji citsanzo cake?

ZIMENE TINGAPHUNZILE PA CITSANZO CA YEREMIYA

3. (a) N’ciani cikanapangitsa kuti Yeremiya ayambe kudzipatula? (b) Kodi Yeremiya anamufotokozela ciani mlembi wake Baruki? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

3 Kwa zaka zosacepela 40, Yeremiya anali kukhala pakati pa anthu osakhulupilika. Ena mwa anthu amenewo anali maneba ake, mwinanso kuphatikizapo acibululu ake ena a m’tauni ya kwawo ku “Anatoti.” (Yer. 11:21; 12:6) Olo zinali conco, Yeremiya sanadzipatule. Iye anali kufotokozela mlembi wake wokhulupilika Baruki mmene anali kumvelela. Ndipo naife timadziŵa mmene anali kumvelela cifukwa zimene anafotokozazo zinalembedwa m’Baibo. (Yer. 8:21; 9:1; 20:14-18; 45:1) Mwacionekele, pamene Baruki anali kulemba za umoyo wa Yeremiya na zina zimene timaŵelenga m’buku la Yeremiya, ubwenzi wa aŵiliwa unalimba, ndiponso anayamba kulemekezana kwambili.—Yer. 20:1, 2; 26:7-11.

4. Kodi Yehova anauza Yeremiya kuti acite nchito yanji? Nanga kugwila nchitoyi kunalimbitsa bwanji ubwenzi wa Yeremiya na Baruki?

4 Kwa zaka zambili, Yeremiya molimba mtima anacenjeza Aisiraeli kuti Yerusalemu adzawonongedwa. (Yer. 25:3) Yerusalemu atangotsala pang’ono kuwonongedwa, Yehova anauza Yeremiya kulemba macenjezo ake mu mpukutu kuti alimbikitse Aisiraeli kulapa. (Yer. 36:1-4) Yeremiya na Baruki anagwilila pamodzi nchito yolembayi, ndipo mwina inatenga miyezi. Zimene anali kukambilana pogwila nchitoyi ziyenela kuti zinalimbitsa kwambili cikhulupililo cawo.

5. Kodi Baruki anaonetsa bwanji kuti anali bwenzi labwino la Yeremiya?

5 Atatsiliza kulemba mpukutuwo, Yeremiya anadalila bwenzi lake Baruki kuti akauze Ayuda uthenga wa mu mpukutuwo. (Yer. 36:5, 6) Baruki anacitadi zimenezo molimba mtima olo kuti zikanaika moyo wake pa ciwopsezo. Yeremiya ayenela kuti anakondwela kwambili pamene Baruki anapita ku bwalo la kacisi kukaŵelenga mpukutuwo kwa anthu. (Yer. 36:8-10) Akalonga aciyuda anamvela zimene Baruki anacita, ndipo anam’pempha kuti awaŵelengele mokweza mpukutuwo. (Yer. 36:14, 15) Akalongawo anaganiza zokauza Mfumu Yehoyakimu mawu a Yeremiya. Pom’ganizila Baruki, iwo anamuuza kuti: “Pita, iweyo ndi Yeremiya mukabisale ndipo munthu aliyense asadziwe kumene mwapita.” (Yer. 36:16-19) Ndithudi! Amenewa anali malangizo abwino kwambili.

6. Kodi Yeremiya na Baruki anacita ciani pamene anali kutsutsidwa?

6 Mfumu Yehoyakimu anakwiya kwambili na mawu amene Yeremiya analemba cakuti anatentha mpukutuwo, na kulamula kuti Yeremiya na Baruki agwidwe. Olo zinali telo, Yeremiya sanayope. Anatenganso mpukutu wina na kupatsa Baruki. Kenako anayamba kukamba uthenga wocokela kwa Yehova, ndipo Baruki analembanso “mawu onse amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha.”—Yer. 36:26-28, 32.

7. N’ciani mwacionekele cimene cinacitika pamene Yeremiya na Baruki anali kuseŵenzela pamodzi?

7 Anthu amene apilila mayeselo pamodzi, nthawi zambili amapanga ubwenzi wolimba. Conco, n’zoonekelatu kuti pamene Baruki na Yeremiya anali kugwilila pamodzi nchito yolembanso mpukutu umene Mfumu yoipa Yehoyakimu inatentha, anadziŵana bwino kwambili cakuti anakhala mabwenzi apamtima. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca amuna aŵili okhulupilika amenewa?

KUKAMBILANA MOONA MTIMA

8. N’ciani cingatilepheletse kupanga ubwenzi wolimba na ena? Nanga n’cifukwa ciani sitiyenela kucita mphwayi?

8 Tingalephele kukamba zinthu moona mtima kwa ena, mwina cifukwa cakuti winawake anatikhumudwitsapo pa nthawi ina. (Miy. 18:19, 24) Mwinanso tingaone kuti timakhala wolema kwambili kapena tilibe nthawi yokwanila yopanga ubwenzi wolimba na ena. Koma sitifunika kucita mphwayi na zimenezi. Kuti abale athu akaticilikize tikakakumana na mayeselo, tifunika kuyamba pali pano kuwadalila na mtima wathu wonse. Kudalilana n’kofunika kwambili kuti anthu akhale mabwenzi eni-eni.—1 Pet. 1:22.

9. (a) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kuwakhulupilila mabwenzi ake? (b) Kodi kukambilana moona mtima na momasuka kungalimbitse bwanji ubwenzi wanu na ena? Fotokozani citsanzo.

9 Yesu anaonetsa kuti anali kuwakhulupilila mabwenzi ake mwa kukamba nawo moona mtima popanda kubisa ciliconse. (Yoh. 15:15) Tingatengele citsanzo cake mwa kuuzako mabwenzi athu zinthu zimene zimatikondweletsa, nkhawa zathu, ndiponso zinthu zimene zimatikhumudwitsa. Muzimvetsela mwachelu ena akamakamba namwe. Mukatelo, mudzazindikila kuti mumafanana pa zambili, kaya ni pa zolinga zanu, mmene mumaonela zinthu, ngakhale mmene mumamvelela. Ganizilani citsanzo ca mlongo wina wa zaka za m’ma 20, dzina lake Cindy. Iye anapalana ubwenzi na mpainiya wina wa zaka za m’ma 60, dzina lake Marie-Louise. Cindy na Marie-Louise amayendela limodzi mu ulaliki pa Cinayi paliponse m’maŵa. Ndipo amakambilana momasuka nkhani zosiyana-siyana. Cindy anati: “Nimakondwela kukambilana na mabwenzi anga zinthu zofunika kwambili, cifukwa kucita zimenezi kumanithandiza kuti niwadziŵe bwino na kuwamvetsetsa.” Kukambilana mwaubwenzi, momasuka, na moona mtima kumalimbitsa ubwenzi. Conco, mofanana na Cindy, ngati mumayesetsa kukambilana na ena mwaubwenzi ndiponso momasuka, ubwenzi wanu na iwo udzalimba kwambili.—Miy. 27:9.

MUZISEŴENZELA PAMODZI

Mabwenzi abwino amaseŵenzela pamodzi mu ulaliki(Onani ndime 10)

10. Mogwilizana na Miyambo 27:17, n’ciani cimacitika ngati tiseŵenzela pamodzi na okhulupilila anzathu?

10 Monga mmene zinalili pakati pa Yeremiya na Baruki, ngati tiseŵenzela pamodzi na okhulupilila anzathu na kuona makhalidwe awo abwino, timaphunzilapo kanthu kwa iwo na kuyamba kuwakonda kwambili. (Ŵelengani Miyambo 27:17.) Mwacitsanzo, kodi mumamvela bwanji ngati muli mu ulaliki, ndipo mwaona mnzanu akukamba molimba mtima poteteza coonadi, kapena akukamba mwacidalilo zimene amakhulupilila ponena za Yehova na zolinga zake? Mwacionekele, mumayamba kumukonda kwambili.

11-12. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene kuseŵenzela pamodzi mu ulaliki kungatithandizile kulimbitsa ubwenzi.

11 Onani zitsanzo ziŵili izi zoonetsa mmene kuseŵenzela pamodzi mu ulaliki kumalimbitsila ubwenzi. Coyamba, mlongo wina wa zaka 23, dzina lake Adeline, anapempha mnzake Candice, kuti azipitila limodzi kukalalikila m’gawo losalalikidwa kaŵili-kaŵili. Adeline anati: “Tinali kufuna kucita zinthu zimene zikanatilimbikitsa kulalikila mokangalika, komanso kuwonjezela cimwemwe cathu pa nchitoyi. Tonsefe tinafunika kulimbikitsidwa kuti tipitilize kucita zonse zimene tikanatha potumikila Yehova.” Kodi alongowa anapindula bwanji cifukwa coseŵenzela pamodzi? Adeline anati: “Tsiku lililonse tikakomboka mu ulaliki, tinali kukambilana mmene tinali kumvelela. Tinali kukambilananso zimene zinatikondweletsa polalikila kwa anthu, ndiponso zimene tinaona zoonetsa kuti Yehova anali kutitsogolela. Tonse tinali kusangalala pokambilana zimenezi, ndipo tinafika podziŵana bwino kwambili.”

12 Citsanzo caciŵili ni ca alongo aŵili amene ni mbeta, ndipo amakhala ku France. Maina awo ni Laïla na Marianne. Pa nthawi ina, iwo anapita kukalalikila kwa mawiki asanu ku Bangui, mzinda waukulu wa ku Central African Republic, umene uli ndi anthu ambili. Laïla anati: “Ine na Marianne, sitinali kumvetsetsana pa zinthu zina. Koma cifukwa cokambilana momasuka na kuonetsana cikondi ceni-ceni, ubwenzi wathu unalimba kwambili. N’naona luso la Marianne lotha kujaila mosavuta umoyo watsopano, cikondi cake pa anthu a kumeneko, na cangu cake pa nchito yolalikila. Izi zinanithandiza kuti niyambe kumulemekeza kwambili.” Simufunika kucita kukukila ku dziko lina kuti mupeze madalitso ngati amenewa. Nthawi iliyonse imene mulalikila m’gawo lanu pamodzi na m’bale kapena mlongo, mumakhala na mwayi womudziŵa bwino na kulimbitsa ubwenzi wanu na iye.

KHALANI OKHULULUKA, NDIPO MUZIYANG’ANA ZABWINO MWA ENA

13. N’ciani cimacitika nthawi zina tikamaseŵenza na anzathu?

13 Nthawi zina pamene tiseŵenza na Akhristu anzathu, timaona makhalidwe awo abwino komanso zophophonya zawo. N’ciani cingatithandize kuti tiziwakondabe olo kuti pali zinthu zina zimene sacita bwino? Ganizilaninso citsanzo cija ca Yeremiya. Kodi n’ciani cinamuthandiza kuti aziona zabwino mwa ena na kunyalanyaza zophophonya zawo?

14. Kodi Yeremiya anaphunzila ciani za Yehova? Nanga zimenezi zinam’limbikitsa kucita ciani?

14 Yeremiya ndiye analemba buku la m’Baibo lochedwa Yeremiya. Ndipo ayenela kuti ndiyenso analemba 1 Mafumu na 2 Mafumu. N’zoonekelatu kuti kulemba mabuku amenewa kunam’thandiza kuona cifundo cacikulu cimene Yehova amaonetsa kwa anthu opanda ungwilo. Mwacitsanzo, iye anadziŵa kuti pamene Mfumu Ahabu analapa macimo ake, Yehova anamuonetsa cifundo moti sanalole kuti aone banja lake lonse likuwonongedwa pa nthawi imene iye anali na moyo. (1 Maf. 21:27-29) Cinanso, Yeremiya anadziŵa kuti Manase anacita macimo ambili amene anakhumudwitsa Yehova kuposa Ahabu. Olo zinali telo, Yehova anamukhululukila Manase cifukwa analapa. (2 Maf. 21:16,17; 2 Mbiri 33:10-13) Zitsanzo zimenezi ziyenela kuti zinam’limbikitsa Yeremiya kutengela khalidwe la Mulungu la kuleza mtima na cifundo pocita zinthu na mabwenzi ake.—Sal. 103:8,  9.

15. Kodi Yeremiya anatengela bwanji citsanzo ca Yehova ca kuleza mtima pamene Baruki analola zinthu zina kusokoneza utumiki wake?

15 Ganizilani mmene Yeremiya anacitila zinthu na Baruki, pamene Barukiyo analola zinthu zina kusokoneza utumiki wake kwa kanthawi. Yeremiya sanangomusiya mnzakeyo poganiza kuti sangasinthe. M’malomwake, anam’thandiza mwa kumufotokozela uthenga wa Mulungu woonetsa kukoma mtima, koma wosapita m’mbali. (Yer. 45:1-5) Kodi tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cimeneci?

Mabwenzi abwino amakhululukilana na mtima wonse (Onani ndime 16)

16. Monga mmene Miyambo 17:9 imakambila, tiyenela kucita ciani kuti tilimbitse ubwenzi na ena?

16 Kukamba zoona sitingayembekezele kuti abale na alongo athu azicita zinthu mwangwilo. Conco, tikapanga ubwenzi na abale kapena alongo athu, tifunika kucita zonse zotheka kuti ubwenziwo ukhalebe wolimba. Mwacitsanzo, ngati mnzathu walakwitsa zina zake, tifunika kum’patsa uphungu wa m’Malemba mosapita m’mbali, koma mokoma mtima. (Sal. 141:5) Akatikhumudwitsa, tiyenela kum’khululukila. Ndipo tikam’khululukila, tiyenela kupewa kukumbutsanso za colakwaco kapena kuyamba kuuzako ena. (Ŵelengani Miyambo 17:9.) M’masiku ano ovuta, n’kofunika kwambili kuti tiziyang’ana pa zabwino zimene abale na alongo amacita osati pa zofooka zawo. Kucita zimenezi kudzalimbitsa ubwenzi wathu na iwo. Ndipo mabwenzi aconco adzakhala ofunika kwambili pa cisautso cacikulu.

ONETSANI CIKONDI COKHULUPILIKA

17. Kodi Yeremiya anaonetsa bwanji kuti anali bwenzi leni-leni pa nthawi ya mavuto?

17 Mneneli Yeremiya anaonetsa kuti anali bwenzi leni-leni pa nthawi ya mavuto. Mwacitsanzo, pa nthawi ina, Ebedi-meleki, amene anali nduna m’nyumba ya mfumu, anapulumutsa Yeremiya kuti asafe m’cisime ca matope cimene anaponyedwamo. Pambuyo pake, Ebedi-meleki anayamba kuda nkhawa kuti akalonga a Yuda adzamupha. Yeremiya atamva zimenezo, sanangokhala cete poganiza kuti mnzakeyo adzakwanitsa yekha kupilila. Olo kuti pa nthawiyo Yeremiya anali m’ndende, anacita zonse zotheka kuti alimbikitse Ebedi-meleki. Anam’fotokozela lonjezo la Yehova lolimbikitsa.—Yer. 38:7-13; 39:15-18.

Mabwenzi abwino amathandiza abale na alongo awo amene akukumana na mavuto (Onani ndime 18)

18. Malinga na Miyambo 17:17, kodi tiyenela kucita ciani ngati bwenzi lathu lakumana na vuto?

18 Masiku ano, abale na alongo athu amakumana na mavuto osiyana-siyana. Mwacitsanzo, ambili amavutika cifukwa ca ngozi zacilengedwe kapena masoka ena obwela cifukwa ca zocita za anthu. Zotelo zikacitika, ena a ife tingawalandile abale athu amenewa kuti azikhala nafe m’nyumba zathu. Enanso angathe kuthandiza mwa kupeleka ndalama. Koma ife tonse tingapemphe Yehova kuti athandize abale na alongo athu amenewa. Tikadziŵa kuti m’bale kapena mlongo wathu ali na nkhawa, tingasoŵe cocita kapena cokamba kuti tim’limbikitse. Koma pali zambili zimene tonsefe tingacite. Mwacitsanzo, tingapatule nthawi yokaceza naye. Tingamvetsele mokoma mtima pamene akutifotokozela nkhawa zake. Ndiponso tingamufotokozeleko lemba lolimbikitsa limene timakonda. (Yes. 50:4) Cofunika kwambili ni kukhala pafupi na bwenzi lanu pamene lakumana na vuto.—Ŵelengani Miyambo 17:17.

19. Kodi kulimbitsa ubwenzi wathu pali pano kudzatithandiza bwanji kutsogolo?

19 Ino ndiyo nthawi yofunika kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu na abale na alongo athu. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa adani athu adzayesa kutigawanitsa mwa kufalitsa mabodza. Adzayesa kutipangitsa kuyamba kukayikilana na kuleka kuthandizana. Koma adzalephela. Sadzakwanitsa kuthetsa cikondi cimene tili naco pa abale athu. Palibe ciliconse cimene cidzathetsa ubwenzi umene tili nawo pakati pathu. Ndipo ubwenzi wathu na abale athu udzakhalapobe mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu, komanso mpaka muyaya.

NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova

^ ndime 5 Pamene mapeto akuyandikila, tonse tifunika kulimbitsa ubwenzi wathu na abale na alongo athu. M’nkhani ino, tikambilana zimene tingaphunzilepo pa zimene zinacitikila Yeremiya. Tikambilananso mmene kulimbitsa ubwenzi wathu pali pano kudzatithandizila pa nthawi ya mavuto.

^ ndime 2 Zocitika za m’buku la Yeremiya sizinalembedwe motsatila ndondomeko ya nthawi imene zinacitika.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Cithunzi coonetsa zimene zingadzacitike pa “cisautso cacikulu.” Abale na alongo ali pa malo otetezeka m’cipinda ca m’mwamba m’nyumba ya m’bale. Monga mabwenzi, iwo akulimbikitsana pa nthawi yovuta imeneyi.