Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 48

Tsilizitsani Zimene Munayamba Kucita

Tsilizitsani Zimene Munayamba Kucita

“Munangoziyambitsa cabe, . . . tsopano, malizitsani.” ​—2 AKOR. 8:10, 11.

NYIMBO 35 ‘Tsimikizilani Zinthu Zofunika Kwambili’

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Yehova anatipatsa ufulu wotani?

YEHOVA anatipatsa ufulu wosankha zocita mu umoyo. Amatiphunzitsa mopangila zosankha zabwino, ndipo tikapanga zosankha zom’kondweletsa, amatithandiza kuzikwanilitsa. (Sal. 119:173) Conco, tikamaseŵenzetsa malangizo anzelu a m’Baibo, m’pamene timapanga zosankha zabwino.—Aheb. 5:14.

2. Kodi tingavutike kucita ciani pambuyo popanga cosankha?

2 Ngakhale pamene tapanga zosankha zabwino, nthawi zina zingativute kucita zimene tasankhazo. Ganizilani zitsanzo izi: M’bale wacicepele wadziikila colinga coŵelenga Baibo yonse. Poyamba, iye akucita bwino kwambili, koma pambuyo pa mawiki angapo akuleka kuŵelenga Baibo. Mlongo afuna kuyamba upainiya wa nthawi zonse, koma akuzengeleza kuyamba. Komanso, bungwe la akulu linagwilizana zakuti ayambe kucita maulendo aubusa kaŵili-kaŵili kwa abale na alongo mu mpingo, koma papita miyezi tsopano ndipo sakucitapo kanthu. Zocitika zimenezi n’zosiyana, koma zikufanana mbali ina. Onse sanakwanilitse zolinga zawo. M’nthawi ya Atumwi, Akhristu a ku Korinto anakumanapo na vuto ngati limeneli. Tiyeni tikambilane zambili kuti tione zimene tingaphunzilepo.

3. Kodi Akhristu a ku Korinto anapanga cosankha cabwanji? Nanga n’ciani cinacitika?

3 Ca m’ma 55 C.E., Akhristu a mu mpingo wa ku Korinto anapanga cosankha cofunika kwambili. Iwo anamvela zakuti abale awo ku Yerusalemu na ku Yudeya anali kukumana na mavuto, komanso anali pa umphawi. Anamvelanso kuti mipingo ina inali kusonkhanitsa ndalama zokathandizila abalewo. Cifukwa ca kukoma mtima na kuwoloŵa manja kwawo, Akhristu a ku Korinto anaganiza zopelekako thandizo, ndipo anapempha mtumwi Paulo kuti awauze zimene angacite. Paulo anatumizila mpingowo malangizo, ndipo anatuma Tito kuti akathandize kusonkhanitsa zopelekazo. (1 Akor. 16:1; 2 Akor. 8:6) Koma patapita miyezi yocepa, Paulo anamvela kuti Akhristu a ku Korinto sanatsatile malangizo amene anawatumizila. Izi zikanapangitsa kuti alephele kusonkhanitsa zopeleka zawo pa nthawi yake kuti zitumizidwe ku Yerusalemu pamodzi na zopeleka zocokela ku mipingo ina.—2 Akor. 9:4, 5.

4. Malinga na zimene 2 Akorinto 8:7, 10, 11 imakamba, kodi Paulo analimbikitsa Akorinto kucita ciani?

4 Akorinto anali atapanga cosankha cabwino. Ndipo Paulo anawayamikila cifukwa ca cikhulupililo cawo cacikulu na mtima wawo wofunitsitsa kuthandiza ena mowolowa manja. Koma anawalimbikitsanso kuti atsilizitse zimene anayamba kucita. (Ŵelengani 2 Akorinto 8:7, 10, 11.) Zimene zinacitikila Akhristu amenewa zionetsa kuti ngakhale Akhristu okhulupilika, nthawi zina angavutike kucita zinthu zabwino zimene asankha.

5. Ni mafunso ati amene tikambilane?

5 Mofanana na Akhristu a ku Korinto, nthawi zina zingativute kukwanilitsa zimene tasankha kucita. Cifukwa ciani? Popeza ndife opanda ungwilo, mwina tingayambe kuzengeleza. Kapena zinthu zosayembekezeleka zingatilepheletse kukwanilitsa zimene tinasankha kucita. (Mlal. 9:11; Aroma 7:18) Kodi tingapange bwanji zosankha zabwino? Nanga tingasinthe bwanji cosankha cimene tinapanga kale pakakhala pofunikila? Komanso, tingacite ciani kuti titsilizitse zimene tinayamba kale kucita?

MMENE TINGAPANGILE ZOSANKHA ZABWINO

6. N’cifukwa ciani nthawi zina tingafunike kusintha cosankha cathu?

6 Pali zosankha zina zikulu-zikulu zimene sitingazisinthe. Mwacitsanzo, sitingasinthe cosankha cathu cotumikila Yehova. Ndiponso ndife otsimikiza mtima kukhalabe okhulupilika kwa mnzathu wa m’cikwati. (Mat. 16:24; 19:6) Koma zosankha zina, nthawi zina tingafunikile kuzisintha. Cifukwa ciani? Cifukwa zocitika mu umoyo zimasintha. Nanga n’ciani cingatithandize kupanga zosankha zabwino?

7. Kodi tiyenela kupempha ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

7 Pemphani nzelu. Mouzilidwa na Yehova, Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka mowolowa manja kwa onse.” (Yak. 1:5) Kukamba zoona, tonsefe ‘timasowa nzelu’ nthawi zina. Conco, tiyenela kudalila Yehova pamene tipanga zosankha komanso pamene tipendanso bwino zosankha zimene tinapanga. Tikacita zimenezi, Yehova adzatithandiza kupanga zosankha zabwino.

8. Kodi tiyenela kucita ciani tisanapange cosankha?

8 Fufuzani mokwanila. Citani khama kufufuza malangizo m’Mawu a Mulungu na m’zofalitsa za gulu la Yehova. Cinanso, mungafunsile nzelu kwa munthu amene mumam’dalila. (Miy. 20:18) Kucita izi n’kofunika kwambili tisanapange zosankha monga kusintha nchito, kukuka, kapena kusankha maphunzilo owonjezela amene angatithandize kuti tizipeza ndalama zogulila zofunikila pamene titumikila Yehova.

9. Kodi tidzapindula bwanji tikakhala oona mtima?

9 Pendani zolinga zanu. Yehova amakhudzidwa na zolinga zathu pocita zinthu. (Miy. 16:2) Iye amafuna kuti tizicita zinthu zonse moona mtima. Conco, popanga zosankha, tiyenela kuonetsetsa kuti tilidi na zolinga zoyenela. Tiyenelanso kupewa kuonetsa monga tili na zolinga zabwino pamaso pa ena pamene ayi. Ngati zolinga zathu si zoyenela, cimakhala covuta kupitiliza kucita zimene tinasankha tikakumana na zopinga. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti m’bale wacicepele wasankha kuyamba upainiya wa nthawi zonse. Koma m’kupita kwa nthawi, iye sakukwanitsa maola ofunikila, ndiponso sakupeza cimwemwe mu utumiki wake. Mwina anali kuona kuti colinga cake cacikulu poyamba upainiya cinali kukondweletsa Yehova. Komabe, kodi n’kutheka kuti colinga cake cacikulu cinali kukondweletsa makolo ake kapena munthu wina wake?

10. N’ciani cofunika kuti munthu asinthe khalidwe lake?

10 Ganizilani za wophunzila Baibo amene wasankha kuleka kupepa fwaka. Iye akulimbikila moti akutenga wiki imodzi kapena aŵili osapepa, koma pa nthawi ina akugonja n’kupepanso. M’kupita kwa nthawi, akulekelatu kupepa. Cifukwa cokonda Yehova na kufuna kum’kondweletsa, iye wakwanitsa kuleka cizoloŵezi coipaco.—Akol. 1:10; 3:23.

11. N’cifukwa ciani tifunika kudziikila zolinga zacindunji?

11 Dziikileni zolinga zacindunji. Ngati mwadziikila zolinga zacindunji, sizikhala zovuta kuzikwanilitsa. Mwacitsanzo, mwina mungadziikile colinga cakuti muziŵelenga Baibo tsiku lililonse. Koma ngati simunakonze ndandanda, mwina simungakwanilitse colinga canuco. * Ndiponso, tinene kuti akulu mu mpingo akonza zakuti azicita maulendo aubusa kaŵili-kaŵili kwa abale na alongo, koma nthawi ikungopita popanda kucitapo kanthu. Kodi n’ciani cingawathandize? Angafunike kudzifunsa mafunso monga awa: “Ni abale na alongo ati maka-maka amene afunika ulendo waubusa? Nanga ni masiku ati amene tingapiteko?”

12. Kodi nthawi zina tingafunike kucita ciani? Cifukwa ciani?

12 Musadziikile zolinga zimene simungakwanitse. Palibe munthu amene ali na mphamvu, cuma, kapena nthawi yocita ciliconse cimene afuna. Conco, khalani oganiza bwino, ndipo musadziikile zolinga zimene simungakwanitse. Pakakhala pofunikila, mungafunike kusintha cosankha canu ngati muona kuti simungakwanitse kucita zimene munasankhazo. (Mlal. 3:6) Lomba tikambe kuti mwapendanso bwino cosankha canu na kusintha zinthu zina, ndipo muona kuti tsopano mungacite zimene munasankhazo. Onani masitepu asanu amene mungatsatile kuti mutsilizitse zimene munayamba kucita.

MASITEPU AMENE MUNGATSATILE KUTI MUKWANITSE KUCITA ZIMENE MUNASANKHA

13. Kodi mungapeze bwanji mphamvu zokuthandizani kukwanilitsa zimene munasankha?

13 Pemphani mphamvu zokuthandizani kucita zimene munasankha. Mulungu angakupatseni mphamvu kuti mukwanitse kucita zimene munasankha. (Afil. 2:13) Conco, pemphani Yehova kuti akupatseni mzimu woyela, umene udzakupatsani mphamvu zimene mufunikila. Pitilizani kupemphela olo muona kuti pemphelo lanu silikuyankhidwa mwamsanga. Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani [mzimu woyela].”—Luka 11:9, 13.

14. Kodi mfundo ya pa Miyambo 21:5, ingakuthandizeni bwanji kukwanilitsa zimene munasankha kucita?

14 Pangani pulani. (Ŵelengani Miyambo 21:5.) Kuti mutsilize nchito iliyonse imene mwayamba, mufunika kukhala na pulani. Ndipo muyenela kucita zinthu motsatila pulaniyo. Mofananamo, mukapanga cosankha, muyenela kulemba zinthu zofunika kucita kuti mukwanilitse colinga canu. Ngati colingaco n’cacikulu, mungayambe mwa kudziikila zolinga zing’ono-zing’ono na kuzikwanilitsa. Mukatelo, mudzaona bwino mmene mukupitila patsogolo pokwanilitsa colinga canu cacikuluco. Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti pa “tsiku lililonse loyamba la mlungu,” aziika kenakake pambali m’malo moyembekezela kuti iye akabwela m’pamene adzasonkhanitsa zopelekazo. (1 Akor. 16:2) Kudziikila zolinga zing’ono-zing’ono zokuthandizani kukwanilitsa colinga cacikulu, kudzakulimbikitsaninso kukwanilitsa colingaco.

15. Kodi muyenela kucita ciani mukapanga pulani?

15 Mukalemba zimene mufuna kucita, cimakhala cosavuta kuzikwanilitsa. (1 Akor. 14:40) Mwacitsanzo, bungwe la akulu limalangizidwa kusankha mkulu amene adzalemba cosankha ciliconse cimene bungwelo lapanga. Mkuluyo amalembanso amene adzacita nchitoyo, na tsiku limene adzafunika kutsiliza nchitoyo. Akulu amene amatsatila malangizo amenewa, nthawi zambili amakwanilitsa zimene asankha kucita. (1 Akor. 9:26) Na imwe mungatsatile malangizo amenewa pa zocita zanu za tsiku na tsiku. Mwacitsanzo, mungalembe zinthu zimene mufunika kucita pa tsiku, ndipo zimene mudzayambila kucita mungazilembe koyambilila. Izi zidzakuthandizani kukwanilitsa zimene mwasankha kucita. Zidzakuthandizaninso kucita zambili m’nthawi yocepa.

16. Cofunika n’ciani kuti tikwanilitse colinga cathu? Nanga Aroma 12:11 imacilikiza bwanji mfundoyi?

16 Limbikilani. Zimafuna khama kuti mutsatile pulani yanu na kutsiliza zimene munayamba kucita. (Ŵelengani Aroma 12:11.) Paulo anauza Timoteyo kuti “pitiliza kukhala wodzipeleka.” Anamuuzanso kuti alimbikile kuti akhale mphunzitsi wabwino. Kulimbikila n’kofunika kuti tikwanilitse zolinga zilizonse zauzimu zimene tingakhale nazo.—1 Tim. 4:13, 16.

17. Kodi mfundo ya pa Aefeso 5:15, 16, ingakuthandizeni bwanji kukwanilitsa zosankha zanu?

17 Seŵenzetsani nthawi yanu mwanzelu. (Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.) Sankhani nthawi imene mufuna kudzacita zimene mwasankha, ndipo musaisinthe. Musazengeleze poyembekezela kuti zonse zikhaliletu bwino, cifukwa mwina nthawi yotelo sidzapezeka. (Mlal. 11:4) Samalani kuti zinthu zosafunika kweni-kweni zisakuwonongeleni mphamvu na nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. (Afil. 1:10) Ngati n’zotheka, sankhani nthawi imene ena sangakusokonezeni pa zimene mucita. Auzeni kuti ndimwe wotangwanika. Cina, mungazime foni yanu na kuŵelenga nthawi ina mameseji a pa kompyuta kapena a pa malo ocezela pa intaneti. *

18-19. N’ciani cingakuthandizeni kukwanilitsa cosankha canu olo kuti mukukumana na zovuta zina?

18 Sumikani maganizo pa zotulukapo zabwino. Zotulukapo zabwino za cosankha canu, tingaziyelekezele na malo amene mukupita mukakhala pa ulendo. Ngati mufunadi kufika kumene mupita, mudzapitiliza ulendo wanu olo mukumane na zovuta zina. Mwacitsanzo, ngati msewu ni wotseka, mungapitile njila ina. Mofananamo, ngati muganizila kwambili pa zotulukapo zabwino za cosankha canu, simudzabwelela m’mbuyo pokwanilitsa colinga canu mukakumana na zovuta zina, kapena ngati mwaona kuti pafunika nthawi yaitali kuti muzikwanilitse.—Agal. 6:9.

19 Kupanga zosankha zabwino na kuzikwanilitsa, nthawi zina kumavuta. Koma mothandizidwa na Yehova, mungapeze nzelu na mphamvu zokuthandizani kukwanilitsa zimene munasankha kucita.

NYIMBO 65 Pita Patsogolo!

^ ndime 5 Kodi mumadziimba mlandu cifukwa ca zosankha zina zimene munapanga? Kapena mwina nthawi zina zimakuvutani kupanga zosankha na kucita zimene mwasankha? Nkhani ino, idzakuthandizani kugonjetsa zopinga zimenezi na kutsiliza zimene munayamba kucita.

^ ndime 11Ndandanda Yowerengera Baibulo” imene ili pa jw.org® ku Chichewa ingakuthandizeni kupanga pulogilamu yabwino yoŵelenga Baibo.

^ ndime 17 Kuti mudziŵe zina zimene zingakuthandizeni kuseŵenzetsa bwino nthawi yanu, onani nkhani yakuti “Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala ndi Nthawi Yokwanira,” mu Galamukani! ya April 2010.