Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 48

Yang’anani Kutsogolo

Yang’anani Kutsogolo

Maso ako aziyang’ana patsogolo. Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.”—MIY. 4:25.

NYIMBO 77 Kuwala m’Dziko la Mdima

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Tingatsatile bwanji malangizo a pa Miyambo 4:25? Fotokozani zitsanzo.

GANIZILANI zitsanzo izi: Mlongo wokalamba akuganizila za masiku osangalatsa a kale lake. Ngakhale kuti akukumana na mavuto palipano, akucitabe zonse zimene angathe potumikila Yehova. (1 Akor. 15:58) Tsiku lililonse amayelekeza kuti ali m’dziko latsopano, pamodzi na anthu amene amawakonda. Mlongo wina, akukumbukila kuti Mkhristu mnzake anamukhumudwitsa kumbuyoku, koma waganiza zongoiiŵala nkhaniyo. (Akol. 3:13) M’bale wina wakumbukila zolakwa zimene anacitapo kumbuyoku, koma akusumika maganizo ake pa kukhalabe wokhulupilika tsopano.—Sal. 51:10.

2 Kodi Akhristu atatuwa akufanana pa ciani? Onse akukumbukila zimene zinacitika mu umoyo wawo wakumbuyo, koma sakhalila kungoganizila zimenezo. M’malomwake, ‘akuyang’ana kutsogolo.’—Ŵelengani Miyambo 4:25.

3. N’cifukwa ciani tiyenela ‘kuyang’ana kutsogolo’?

3 N’cifukwa ciani ‘kuyang’ana kutsogolo n’kofunika’? Munthu sangathe kuyenda bwino-bwino mu msewu ngati akungoyang’ana-yang’ana kumbuyo. Mofananamo, sitingapite patsogolo mu utumiki wathu kwa Yehova ngati nthawi zonse timangoganizila zakumbuyo.—Luka 9:62.

4. Tikambilane ciani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tikambilane misampha itatu imene ingatipangitse kumakhalabe mu umoyo wakale. * Imeneyi ni: (1) kulakalaka umoyo wakale, (2) kusunga mkwiyo, komanso (3) kudziimba mlandu mopitilila malile. Pa msampha uliwonse, tidzaona mmene mfundo za m’Baibo zingatithandizile kupewa kusumika maganizo athu pa “zinthu zakumbuyo,” na kuyesetsa kuika maganizo athu pa “zakutsogolo.”—Afil. 3:13.

MSAMPHA WOYEWA UMOYO WAKALE

N’ciani cingatilepheletse kuyang’ana kutsogolo? (Onani ndime 5, 9, 13) *

5. Kodi Mlaliki 7:10 iticenjeza za msampha uti?

5 Ŵelengani Mlaliki 7:10. Onani kuti vesili silikamba kuti n’kulakwa kufunsa kuti: “N’cifukwa ciani kale zinthu zinali bwino?” Kukumbukila zabwino zakumbuyo ni mphatso yocokela kwa Yehova. Koma vesili likamba kuti: “Usanene kuti: ‘N’cifukwa ciani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?’” M’mawu ena, msampha uli pa kuyelekezela umoyo wathu wakale na umoyo wathu tsopano, n’kumaganiza kuti zonse sizili bwino tsopano.

Kodi Aisiraeli analakwitsa ciani atatuluka mu Iguputo? (Onani ndime 6)

6. N’cifukwa ciani si canzelu kumangoganiza zakuti umoyo wathu unali bwino kale kuposa masiku ano? Fotokozani citsanzo.

6 N’cifukwa ciani si kwanzelu kumangoniza zakuti umoyo wathu unali bwino kale kuposa masiku ano? Kulakalaka umoyo wakale kungatipangitse kumangokumbukila cabe zinthu zabwino zakale, na kutiiŵalitsa mavuto amene tinakumana nawo. Mwacitsanzo, ganizilani za Aisiraeli akale. Atatuluka mu Iguputo, iwo mwamsanga anaiŵala kuti umoyo wawo unali wa mavuto m’dzikolo. M’malomwake, anangosumika maganizo awo pa zakudya zabwino zimene anali kukonda ku Iguputo. Iwo anati: “Tikukumbukila nsomba zaulele zimene tinali kudya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!” (Numeri 11:5) Kodi n’zoona kuti zakudyazo zinali “zaulele”? Ayi. Aisiraeli anali kupeleka malipilo oŵaŵa. Panthawiyo, iwo anali kukhala umoyo wopondelezedwa mwankhanza monga akapolo ku Iguputo. (Eks. 1:13, 14; 3:6-9) Ngakhale n’telo, anaiŵalilatu za mavuto onsewo, n’kuyamba kulakalaka umoyo wakale. Anasankha kusumika maganizo pa zinthu zabwino zakale, m’malo moika maganizo awo pa zabwino zimene Yehova anali atangowacitila. Khalidwe limenelo linaputa mkwiyo wa Yehova.—Num. 11:10.

7. N’ciani cinathandiza mlongo wina kupewa msampha woyewa umoyo wakale?

7 Kodi tingapewe bwanji msampha woyewa umoyo wakale? Ganizilani citsanzo ca mlongo wina amene anayamba kutumikila pa Beteli ku Brooklyn mu 1945. Patapita zaka, iye anakwatiwa kwa m’bale amene nayenso anali kutumikila pa Betelipo, ndipo anatumikila limodzi kwa zaka zambili. Koma mu 1976, mwamuna wake anayamba kudwala. Mlongoyo anati mwamuna wake atadziŵa kuti analibe masiku ambili okhala na moyo, anam’patsa malangizo omuthandiza kupilila monga mkazi wamasiye. Mwamuna wakeyo anamuuza kuti: “Takhala limodzi monga banja lacimwemwe. Mabanja ambili sapeza cimwemwe monga cathuci.” Koma analimbikitsanso mkazi wake kuti: “Ngakhale kuti uzikumbukilabe zabwino zakumbuyo, osakhala mu umoyo wakale. M’kupita kwanthawi, cisoni cako cidzayamba kucepa. Osakhala wokhumudwa na kumadzimvela cisoni. Uzikondwela kuti tinatumikila limodzi mwacimwemwe na kulandila madalitso ambili. Kukumbukila zinthu zabwino zakumbuyo ni mphatso imene tinapatsidwa na Mulungu.” Kodi simungavomeleze kuti malangizo amenewa analidi abwino?

8. Kodi mlongo wathu anapindula bwanji cifukwa copewa kukhalabe mu umoyo wakale?

8 Mlongo wathu ameneyu anaseŵenzetsa malangizo amenewa. Anatumikila Yehova mokhulupilika kufikila imfa yake ali na zaka 92. Asanamwalile anati: “Nakhala mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka zoposa 63 lomba, ndipo nikayang’ana kumbuyo, umoyo wanga wakhala wokhutilitsa kwambili.” Cifukwa ciani? Iye anafotokoza kuti: “Kweni-kweni, cimene cimapangitsa umoyo kukhala wokhutilitsa ni ubale wathu wacikhristu, na ciyembekezo cokakhala m’paradaiso padziko lapansi pamodzi na abale na alongo athu, n’kumatumikila Mlengi wathu Wamkulu, Mulungu yekhayo woona, Yehova, mpaka kalekale.” * Ndithudi! Ici n’citsanzo cabwino zedi ca munthu amene anayang’ana kutsogolo.

MSAMPHA WA KUSUNGA MKWIYO

9. Mogwilizana na Levitiko 19:18, ni panthawi iti pamene zingakhale zovuta kwambili kucotsa mkwiyo?

9 Ŵelengani Levitiko 19:18. Nthawi zambili cimakhala covuta kucotselatu mkwiyo ngati anatikhumudwitsa ni Mkhristu mnzathu, mnzathu amene timagwilizana naye, kapena m’bululu wathu. Mwacitsanzo, mlongo wina ananamizilidwa na Mkhristu mnzake kuti anam’bela ndalama. Patapita nthawi, mlongo amene ananamizila mnzake molakwika uja anapepesa. Koma mlongo wonamizilidwayo anapitilizabe kuganizila zimene zinacitikazo. Ngati zaconco zinakucitikilamponi, kodi munamvela bwanji? Ngakhale ngati sizinaticitikile mwa njila imeneyi, ambili a ife tinakhumudwapo, ndipo tinaona monga sizikatheka kum’khululukila munthu anatilakwilayo.

10. Kodi n’ciani cingatithandize tikakhumudwa?

10 Kodi cingatithandize n’ciani tikakhumudwa? Tisaiŵale kuti Yehova amaona zonse. Iye amadziŵa zonse zimene timapitamo, kuphatikizapo zopanda cilungamo zonse zimene zimaticitikila. (Aheb. 4:13) Amamvela kuipa tikamavutika. (Yes. 63:9) Ndipo analonjeza kuti adzacotsapo mavuto onse obwela cifukwa ca zinthu zopanda cilungamo zimene zinaticitikila.—Chiv. 21:3, 4.

11. Timapindula bwanji tikacotsa mkwiyo?

11 Tiyenelanso kukumbukila kuti tikacotsa mkwiyo, timadzipindulitsa ife eni. N’zimene mlongo wonamizilidwa uja anazindikila. Patapita nthawi, anakwanitsa kukhululuka. Anazindikila kuti tikamakhululukila ena, Yehova nayenso amatikhululukila. (Mat. 6:14) Mlongoyo anadziŵa kuti zimene Mkhristu mnzake anam’citila zinali zoipa ndithu, koma anasankha kucotsa mkwiyo. Zotulukapo zake n’zakuti mlongo wathuyu anakhala wacimwemwe, ndipo anaika maganizo ake pa kutumikila Yehova.

MSAMPHA WODZIIMBA MLANDU MOPITILILA MALILE

12. Kodi tiphunzilapo ciani pa 1 Yohane 3:19, 20?

12 Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20. Tonsefe timadziimba mlandu nthawi zina. Mwacitsanzo, ena amadziimba mlandu pa zoipa zimene anacita asanaphunzile coonadi. Enanso amadziimba mlandu pa zoipa zimene anacita pambuyo pa ubatizo. (Aroma 3:23) Timafuna kucita zoyenela, koma “tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yak. 3:2; Aroma 7:21-23) Koma ngakhale kuti kudziimba mlandu si cinthu cokondweletsa, kungakhaleko na ubwino wake. Cifukwa ciani? Kungatilimbikitse kuwongolela njila zathu, na kusafuna kudzabwelezanso zolakwazo.—Aheb. 12:12, 13.

13. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa msampha wodziiimba mlandu mopitilila malile?

13 Komabe, zingatheke kudziimba mlandu mopitilila malile—kutanthauza kumadziimbabe mlandu ngakhale pambuyo pakuti talapa ndipo Yehova waonetsa kuti watikhululukila. Kudziimba mlandu koteloko n’kovulaza. (Sal. 31:10; 38:3, 4) Motani? Ganizilani za mlongo wina amene anapitiliza kudziimba mlandu pa macimo ake akumbuyo. Iye anati: “N’nali kuona kuti kudzipeleka kwambili potumikila Yehova kunalibe phindu, cifukwa mwina ananiweluza kale.” Ambili a ife mwina tinamvelapo monga anamvelela mlongoyu. Tifunika kudziteteza ku msampha wodziimba mlandu mopitilila malile. Tangoganizani mmene Satana angakondwele ngati tingayambe kuganiza kuti ndine wolephela ndipo Yehova ananifulatila kale, pamene iye Yehova anatikhululukila.—Yelekezelani na 2 Akorinto 2:5-7, 11.

14. Tingatsimikize bwanji kuti Yehova anatikhululukiladi?

14 Koma mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi ningatsimikize bwanji kuti Yehova sananifulatile?’ Kudzifunsa kwanu funso limeneli, kuonetsa kuti mtima wanu ukukuuzani kuti Yehova angakukhululukileni. Zaka zambili kumbuyoku, magazini ina ya Nsanja ya Mlonda inakamba kuti: “Ti[nga]gwe n’kulephela mobweleza-bweleza pa cizoloŵezi cina coipa cimene cinazika kwambili mizu mu umoyo wathu wakale . . . Koma musataye mtima. Musaganize kuti munacita chimo losakhululukidwa. Umu ni mmene Satana amafuna kuti muzionela. Ndipo ngati mudzimvela cisoni pa khalidwe lanu, umenewo ni umboni wakuti simunafike pokhala munthu woipa amene Yehova sangakhululukile. Musaleme kutembenukila kwa Mulungu modzicepetsa komanso mocokela pansi pamtima, kuti akukhululukileni, akuyeletseni komanso akuthandizeni. Pitani kwa iye monga mmene mwana amapitila kwa atate ake pamene ali m’mavuto, mosasamala kanthu kuti mudzapita maulendo angati kwa iye pa cofooka canu cimeneco. Ndipo Yehova mwa cisomo cake, adzakuthandizani.”

15-16. Kodi ena amvela bwanji atadziŵa kuti Yehova akali kuŵakonda?

15 Atumiki a Yehova ambili alimbikitsidwa atadziŵa kuti Yehova sanaleke kuŵakonda. Mwacitsanzo, zaka zingapo zapitazo, m’bale wina analimbikitsidwa na nkhani imene anaŵelenga m’nkhani zakuti “Baibo Imasintha Anthu.” M’nkhaniyo, mlongo wina anakamba kuti cifukwa ca zimene zinacitika mu umoyo wake kumbuyoko, zinali zovuta kukhulupilila kuti Mulungu angam’konde. Anavutika na maganizo amenewo kwa zaka ngakhale pambuyo pa ubatizo. Koma pambuyo posinkha-sinkha za nsembe ya dipo, anayamba kuona zinthu moyenela. *

16 Kodi nkhani imeneyi inam’thandiza bwanji m’bale uja? Iye analemba kuti: “Nili wacinyamata, n’nayesetsa kuti nileke kutamba zamalisece, mpaka n’napambana. Koma posacedwapa n’nagwelanso mu msamphawo. N’napempha akulu mu mpingo kuti anithandize, ndipo nayesetsa ndithu kuligonjetsa vutoli. Akuluwo ananitsimikizila kuti Mulungu amanikonda ndipo ni wacifundo. Ngakhale n’telo, nthawi zina nimangodzimva wacabe-cabe, woti Yehova sanganikondenso. N’taŵelenga nkhani ya [mlongo ameneyu] n’nazindikila kuti ngati nimaganiza kuti Mulungu sanganikhululukile, mwanjila ina nikamba kuti nsembe ya Mwana wake si yokwanila kuphimba macimo anga. Nkhani imeneyi n’naisunga kuti nthawi zonse nikayamba kudziona wosafunika, niziiŵelenga na kuisinkha-sinkha.”

17. Kodi mtumwi Paulo anapewa bwanji msampha wodziimba mlandu mopitilila malile?

17 Zocitika monga izi zitikumbutsa za mtumwi Paulo. Asanakhale Mkhristu, anacita macimo aakulu ambili. Paulo anali kukumbukila zimene anacita kumbuyoko, koma sanali kungokhalila kuganizila zimenezo. (1 Tim. 1:12-15) Anali kuona dipo kukhala mphatso yake imene Mulungu anam’patsa. (Agal. 2:20) Mwa ici, Paulo anapewa msampha wodziimba mlandu mopitilila malile, na kuika maganizo ake pa kucita zonse zotheka potumikila Yehova.

YANG’ANANI KUTSOGOLO!

Tiyeni tiike maganizo athu pa zakutsogolo (Onani ndime 18-19) *

18. Taphunzila ciani m’nkhani ino?

18 Kodi taphunzilanji pa misampha itatu imene takambilana m’nkhani ino? (1) Kukumbukila zabwino zakumbuyo ni mphatso yocokela kwa Yehova. Koma kaya umoyo wathu unali wabwino motani kale, si kanthu pouyelekezela na umoyo wa m’dziko latsopano. (2) Ena angatikhumudwitse, koma tikasankha kuwakhululukila, tidzaika maganizo athu pa kutumikilabe Yehova. (3) Kudziimba mlandu mopitilila malile kungatilepheletse kutumikila Yehova mwacimwemwe. Conco mofanana na Paulo, tiyeni tikhulupilile kuti Yehova anatikhululukiladi.

19. Tidziŵa bwanji kuti m’dziko latsopano sitidzavutitsidwa na maganizo a zinthu zakale?

19 Tili na ciyembekezo cokhala na moyo wosatha. Ndipo m’dziko la Mulungu latsopano, sitidzavutitsidwa na maganizo a zinthu zakale. Pokamba za nthawiyo, Baibo imati: “Zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso.” (Yes. 65:17) Tangoganizani: Ena a ife takalamba tikutumikila Yehova, koma m’dziko latsopano, tidzakhalanso acinyamata. (Yobu 33:25) Conco, tiyeni tonsefe tikaniletu kusakhala mu umoyo wakale. M’malomwake, tiyang’ane kutsogolo ku dziko latsopano, na kucita zonse zotheka kuti tikaloŵe!

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

^ ndime 5 Kuganizila zakumbuyo mu umoyo wathu kulibe vuto. Koma sitifuna kuganizila zakumbuyo mopambanitsa cakuti n’kulephela kuona ubwino wa umoyo wathu palipano, kapena kutiphimba ku madalitso akutsogolo. Nkhani ino ifotokoza misampha itatu imene ingatipangitse kumakhalabe mu umoyo wakumbuyo. Tikambilane mfundo za m’Baibo na zitsanzo za masiku ano zimene zingatithandize kupewa misampha imeneyi.

^ ndime 4 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’nkhani ino, “kukhalabe mu umoyo wakale” kutanthauza kupitiliza kuganizila zinthu zakale mu umoyo wathu—kumakambapo nthawi zonse, kubwelelako m’maganizo, kapena kumangoganiza kuti umoyo wathu wakale unali wabwino kuposa wa lelo.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kulakalaka umoyo wakale, kusunga mkwiyo, komanso kudziimba mlandu mopitilila malile, kuli monga kukoka zinthu zolema pamene tikuyenda pa msewu wa kumoyo, ndipo zingatilepheletse kupita kutsogolo.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Koma tikataya zolemetsa zimenezi, timadzimva omasuka komanso acimwemwe, ndipo timapezanso mphamvu. Tikatelo, tidzatha kuyang’ana bwino kutsogolo