Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

“Yehova Sananiiŵale”

“Yehova Sananiiŵale”

NIMAKHALA m’mudzi wa Orealla, wa anthu pafupi-fupi 2,000 m’dziko la Guyana, ku South America. Mudziwu uli kutali, ndipo mafikidwe a kumeneko ni pa ndeke yaing’ono kapena boti cabe.

N’nabadwa mu 1983. Nili mwana, thanzi langa linali bwino-bwino. Koma n’tafika zaka 10, thupi langa lonse linayamba kuphwanya. Pambuyo pazaka ziŵili, tsiku lina n’tauka m’mawa, n’nangoona kuti nikulephela kuyenda. N’nayesela pano-pano kuti niyende koma ayi ndithu, kukangilatu. Cicokeleni tsikulo, sin’nayendeponso mpaka pano. Matenda anga anapangitsanso kuti nileke kukula. Ngakhale lomba, nimaonekabe wamng’ono monga mwana.

Patapita miyezi ingapo cidwalileni, Mboni za Yehova ziŵili zinanifikila. Ndipo panthawiyo sin’nali kucoka panyumba. Nthawi zonse alendo akabwela n’nali kubisala, koma tsikulo n’nalola azimayiwo kukamba nane. Pamene anali kufotokoza za paradaiso, n’nakumbukila zimene n’namvela nili na zaka 5. Panthawiyo, mmishonale wina dzina lake Jethro, amene anali kukhala ku Suriname, anali kubwela m’mudzi mwathu kamodzi pa mwezi kudzaphunzila Baibo na atate. M’bale Jethro anali kucita nane mokoma mtima. N’nali kum’konda kwambili. Komanso ambuye anga aakazi ndi aamuna anali kunitengako ku misonkhano ya Mboni za Yehova, imene inali kucitikila m’mudzi mwathu. Mlongo Florence mmodzi wa azimayi amene ananifikila atanifunsa ngati ningakonde kudziŵa zambili, n’namuuza kuti nifuna.

Mlongo Florence anabwelanso na amuna ake a Justus, ndipo onse aŵili anayamba kuphunzila nane Baibo. Ataona kuti sinidziŵa kuŵelenga, anayamba kuniphunzitsa kuŵelenga. Patapita nthawi, n’nadziŵa kuŵelenga. Tsiku lina mlongo Florence na m’bale Justus ananiuza kuti anasinthidwa kuti akatumikile ku Suriname. Cacisoni n’cakuti m’mudzi mwathu munalibe aliyense amene akanapitiliza kuphunzila nane Baibo. Koma cokondweletsa n’cakuti Yehova sananiiŵale.

Posapita nthawi, mpainiya wina dzina lake Floyd anabwela m’mudzi mwathu, ndipo ananipeza pamene anali kulalikila nyumba na nyumba. Atakambilana nane zophunzila Baibo, n’namwetulila. Iye ananifunsa kuti: “Wakondwela ciani?” N’namuuza kuti n’natsiliza kale kuphunzila bulosha yakuti, Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndipo n’nayamba kuphunzila buku lakuti, Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * N’nafotokoza cifukwa cake phunzilo silinapitilize. Conco m’bale Floyd anapitiliza kuphunzila nane buku la Chidziŵitso, koma pambuyo pake nayenso anatumizidwa kukatumikila kwina. N’nasoŵanso woniphunzitsa Baibo.

Komabe mu 2004, m’bale Granville na m’bale Joshua apainiya apadela aŵili, anatumizidwa kudzatumikila m’mudzi mwathu. Iwonso ananipeza polalikila nyumba na nyumba. Atanifunsa ngati n’nali kufuna kuphunzila Baibo, n’namwetulila. N’nawapempha kuti tiyambenso kuphunzila buku la Chidziŵitso. N’nafuna kuona ngati zimene ena ananiphunzitsa kumbuyoko zidzafanana na zimene iwo adzaniphunzitsa. M’bale Granville ananiuza kuti misonkhano inali kucitika m’mudzi mwathu. Ngakhale kuti sin’nali kucoka panyumba kwa zaka pafupi-fupi 10, n’nafuna kupitako. Conco m’bale Granville ananinyamula na kuniika pa njinga ya olemala, n’kunikankha kupita ku Nyumba ya Ufumu.

M’kupita kwa nthawi, m’bale Granville ananilimbikitsa kulembetsa mu Sukulu ya Ulaliki. Iye anati: “Ndiwe wolemala koma umatha kukamba. Tsiku lina udzakamba nkhani ya anthu onse. Zidzacitika ndithu.” N’nalimbikitsidwa kwambili na mawu ake.

N’nayamba kulalikila na m’bale Granville. Komabe, misewu yafumbi yambili inali yoipa, mwakuti zinali zovuta kuyenda pa njinga ya olemala. Conco n’napempha m’bale Granville kuti angonikhazika mu wilibala, n’kumanikankha. N’zimene zinathandiza. Ndipo mu April 2005, n’nabatizika. Posapita nthawi, n’nayamba kusamalila mabuku a mpingo komanso kutumikila ku saundi mu Nyumba ya Ufumu.

Mwa tsoka lanji, mu 2007 atate anamwalila pa ngozi ya boti. Banja lathu linakhudzidwa kwambili. M’bale Granville anapemphela nafe limodzi, komanso kutiŵelengela malemba otonthoza a m’Baibo. Patapita zaka ziŵili, tsoka linanso linatigwela—m’bale Granville nayenso anafa pangozi ya boti.

Mpingo wathu waung’ono wacisoniwo, unatsala ulibe mkulu. Unangotsala na mtumiki wothandiza mmodzi. Imfa ya m’bale Granville inaniŵaŵa, n’nali kum’konda ngako. Iye anali kunithandiza kuuzimu na kuthupi. Pamsonkhano wotsatila pambuyo pa imfa yake, n’nali na mbali yoŵelenga Nsanja ya Mlonda. N’nakwanitsa kuŵelenga ndime ziŵili zoyamba, kenako n’nayamba kusisima misozi ili mbwe-mbwe-mbwe. N’nangocokapo pa pulatifomu.

N’nayamba kumvelako bwino pamene abale a ku mpingo wina anayamba kubwela kudzathandiza mpingo wathu ku Orealla. Kuwonjezela apo, ofesi yanthambi inatumiza mpainiya wapadela dzina lake Kojo. N’nakondwela pamene amayi na mng’ono wanga anayamba kuphunzila Baibo mpaka kubatizika. Ndiyeno mu March 2015, n’naikidwa kukhala mtumiki wothandiza. Patapita nthawi, n’napeleka nkhani yoyamba ya anthu onse. Tsikulo, nili wacimwemwe komanso nikukhetsa misozi ya cisangalalo, n’nakumbukila zimene m’bale Granville ananiuza zaka zingapo kumbuyoko. Iye anati: “Tsiku lina udzakamba nkhani ya anthu onse. Zidzacitika ndithu.”

Kupitila pa mapulogilamu apa JW Broadcasting®, nadziŵa za Mboni zina zimene nazonso ni zolemala monga ine. Ngakhale kuti ni olemala amacita zambili mu utumiki komanso ni acimwemwe. Nanenso ningacite zambili. Cikhumbo canga copatsa Yehova mphamvu zonse zimene nili nazo, cinanilimbikitsa kukhala mpainiya wa nthawi zonse. Ndipo mu September 2019, kunacitika zimene sin’nayembekezele. M’mweziwo, n’naikidwa kukhala mkulu mu mpingo wathu wa ofalitsa pafupi-fupi 40.

Niyamikila abale na alongo amene anaphunzila nane Baibo na kunithandiza kuyamba kutumikila Yehova. Koposa zonse ndine woyamikila kwambili kuti Yehova sananiiŵale.

^ ndime 8 Lofalitsidwa na Mboni za Yehova, koma tsopano analeka kuipulinta.