Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 48

Khalanibe Oganiza Bwino Kukhulupilika Kwanu Kukayesedwa

Khalanibe Oganiza Bwino Kukhulupilika Kwanu Kukayesedwa

“Ukhalebe woganiza bwino pa zinthu zonse.”—2 TIM. 4:5.

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi kukhalabe oganiza bwino kutanthauza ciyani? (2 Timoteyo 4:5)

 TIKAKUMANA na zokhumudwitsa, kukhulupilika kwathu kwa Yehova na gulu lake kungayesedwe. Kodi mavuto aconco tingawagonjetse motani? Tiyenela kukhala oganiza bwino, kukhala maso, komanso olimba m’cikhulupililo. (Ŵelengani 2 Timoteyo 4:5.) Timakhala oganiza bwino ngati tikhalabe odekha, komanso ngati timayesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Tikatelo, sitidzacita zinthu potengela mmene tikumvela mumtima.

2. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 M’nkhani yapita, tinakambilana mayeso atatu ocokela kwa anthu osalambila Mulungu. M’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zocokela kwa abale na alongo mu mpingo zimene zingayese kukhulupilika kwathu kwa Yehova. Zinthuzo ni (1) Mkhristu mnzathu akatikhumudwitsa, (2) tikapatsidwa uphungu kapena cilango, komanso (3) tikamavutika kugwilizana na masinthidwe a gulu. Kodi tingacite ciyani kuti tikhalebe oganiza bwino na kumamatilabe Yehova na gulu lake zotele zikaticitikila?

MKHRISTU MNZATHU AKATIKHUMUDWITSA

3. Kodi mungamve bwanji ngati Mkhristu mnzanu wakukhumudwitsani?

3 Kodi Mkhristu mnzanu kapena m’bale waudindo mu mpingo anakukhumudwitsamponi? N’kutheka kuti m’baleyo sanali na colinga cokukhumudwitsani. (Aroma 3:23; Yak. 3:2) Ngakhale n’telo, zocita zake simunakondwele nazo. Mwina munalephela ngakhale kugona cifukwa coganizila zimene anakucitani. N’kutheka kuti munadzifunsa kuti, ‘Ngati m’bale angacite zinthu mwa njila iyi, kodi n’zoonadi kuti ili ni gulu la Mulungu?’ Izi n’zimene Satana amafuna kuti tizicita. (2 Akor. 2:11) Maganizo olakwika amenewo angapangitse kuti tidzilekanitse na Yehova komanso gulu lake. Ndiye tikaona kuti m’bale kapena mlongo watikhumudwitsa, tingacite ciyani kuti tikhalebe oganiza bwino, na kupewa kuganiza molakwika?

4. Kodi Yosefe anaonetsa bwanji kuti anali woganiza bwino pamene anali kucitidwa zacipongwe? Nanga tiphunzilapo ciyani pa citsanzo cake? (Genesis 50:19-21)

4 Musamakhumudwe. Pamene Yosefe anali wacicepele, abale ake anam’cita zankhanza. Anali kudana naye, moti ena mwa iwo anafuna mpaka kumupha. (Gen. 37:4, 18-22) Pamapeto pake, iwo anam’gulitsa ku ukapolo. Zotulukapo zake zinali zakuti, Yosefe anakumana na mayeso aakulu amene anamutengela zaka 13 kuti athe. Cifukwa ca mavutowo, Yosefe akanakayikila ngati Yehova anali kum’kondadi. Ndipo iye akanaganiza kuti Yehova wamusiya pa nthawi imene anali kufunikila thandizo lake. Koma Yosefe sanakhumudwe. Anakhalabe woganiza bwino mwa kukhala wodekha. Mpata utapezeka woti awabwezele abale ake, iye sanatelo. M’malo mwake, anawaonetsa cikondi, ndipo anawakhululukila. (Gen. 45:4, 5) Yosefe anacita zimenezo cifukwa anali kuona zinthu moyenela. Iye sanaike maganizo ake pa mavuto amene anali kukumana nawo. Koma anapitiliza kuganizila colinga ca Yehova. (Ŵelengani Genesis 50:19-21.) Kodi tiphunzilapo ciyani? Ngati wina wakukhumudwitsani, musamukwiyile Yehova kapena kuona monga wakusiyani. M’malo mwake, ganizilani mmene iye akukuthandizilani kupilila mayesowo. Kuwonjezela apo, ena akakukhumudwitsani, yesani kuphimba zophophonya zawo mwa kuwaonetsa cikondi.—1 Pet. 4:8.

5. N’ciyani cinathandiza m’bale Miqueas kukhalabe woganiza bwino pamene anaona kuti ena amucitila zinthu mopanda cilungamo?

5 Ganizilani citsanzo camakono ici ca m’bale wa ku South America dzina lake Miqueas. b Iye anakamba kuti akumbukila nthawi pamene anaona kuti abale apaudindo amuweluza molakwika. Anati: “Pa nthawiyo n’napsinjika maganizo kwambili kuposa kale lonse. N’nali na nkhawa. Usiku, tulo sin’nali kutuona, ndipo n’nali kukhalila kulila cifukwa cosoŵa mtengo wogwila.” Ngakhale n’telo, m’bale Miqueas anakhalabe woganiza bwino, ndipo anayesetsa kuwongolela maganizo ake. Anali kupemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili kuti am’patse mzimu woyela na mphamvu zom’thandiza kupilila. Anafufuzanso mfundo zina m’zofalitsa zathu zimene zinam’thandiza. Kodi tiphunzilapo ciyani? Ngati mwaona kuti m’bale kapena mlongo wakukhumudwitsani, khalanibe wodekha ndipo yesetsani kuwongolela maganizo alionse olakwika amene mungakhale nawo. Sitingadziŵe zimene zinapangitsa munthuyo kulankhula kapena kucita zinthu mwa njila imeneyo. Conco, muuzeni Yehova m’pemphelo na kum’pempha kuti akuthandizeni kuona zinthu mmene munthuyo amazionela. Kucita zimenezo kungakuthandizeni kuona kuti m’baleyo kapena mlongoyo sanali na colinga cokukhumudwitsani, ndipo mudzam’khululukila. (Miy. 19:11) Yehova amaona zimene mukupitamo, ndipo adzakupatsani mphamvu zofunikila kuti mupilile.—2 Mbiri 16:9; Mlal. 5:8.

TIKAPATSIDWA UPHUNGU KAPENA CILANGO

6. N’cifukwa ciyani n’kofunika kwambili kuona kuti cilango ni njila imene Yehova amaonetsela kuti amatikonda? (Aheberi 12:5, 6, 11)

6 Cilango pocilandila cingakhale coŵaŵa. Koma tikaika maganizo pa kuŵaŵa kwa cilangoco, tingayambe kucipeputsa, na kuona kuti sicinapelekedwe m’njila ya cilungamo kapena kuti si coyenela kwa ife. Zotulukapo n’zakuti tingalephele kuona mfundo yofunika yakuti cilangoco ni njila imene Yehova amaonetsela kuti amatikonda. (Ŵelengani Aheberi 12:5, 6, 11.) Ngati timangoganizila kuŵaŵa kwa cilango, timapatsa mpata Satana wakuti atisocoletse. Iye amafuna kuti tikane cilango, komanso kuti tidzilekanitse na Yehova ndiponso na mpingo. Tikalandila uphungu kapena cilango, kodi tingacite ciyani kuti tikhalebe oganiza bwino?

Modzicepetsa Petulo analandila uphungu, ndipo Yehova anam’konda kwambili (Onani ndime 7)

7. (a) Malinga na cithunzi, kodi Yehova anam’gwilitsa nchito motani Petulo atalandila uphungu? (b) Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Petulo?

7 Landilani cilango na kupanga masinthidwe ofunikila. Kangapo konse, Yesu anapatsa uphungu Petulo pamaso pa atumwi anzake. (Maliko 8:33; Luka 22:31-34) N’kutheka kuti Petulo anacita manyazi. Komabe, iye anakhalabe wokhulupilika kwa Yesu. Analandila uphungu na kuphunzila pa zolakwa zake. Yehova anadalitsa Petulo cifukwa cokhalabe wokhulupilika, ndipo anam’patsa maudindo aakulu mu mpingo. (Yoh. 21:15-17; Mac. 10:24-33; 1 Pet. 1:1) Tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Petulo? M’malo moika maganizo pa kucititsidwa manyazi kumene kungakhalepo, ife eni komanso anthu ena timapindula tikalandila uphungu kapena cilango, na kupanga masinthidwe ofunikila. Tikatelo, tidzakhala ofunika kwambili kwa Yehova komanso kwa abale athu.

8-9. Kodi poyamba m’bale Bernardo anamvela bwanji atapatsidwa cilango? Nanga n’ciyani cinam’thandiza kuwongolela kaganizidwe kake?

8 Onani zimene zinacitikila m’bale wina ku Mozambique, dzina lake Bernardo. Iye anatsitsidwa pa ukulu. Kodi poyamba m’bale Bernardo anamva bwanji? Iye anati: “N’nakhumudwa cifukwa sin’nasangalale na cilangoco cimene n’napatsidwa.” Anada nkhawa na mmene ena akanamuonela mu mpingo. Iye anakamba kuti: “Zinan’tengela miyezi yambili kuti niyambe kuona cilango moyenela, na kuyambanso kukhulupilila Yehova na gulu lake.” N’ciyani cinathandiza m’bale Bernardo kuyamba kuona zinthu moyenela?

9 M’baleyu anasintha kaganizidwe kake. Iye anati: “Pamene n’nali mkulu, n’nali kugwilitsa nchito Aheberi 12:7 pothandiza ena kuona cilango ca Yehova moyenela. Conco, n’nadzifunsa kuti: ‘Ndani afunika kugwilitsa nchito lembali?’ Ni atumiki onse a Yehova, kuphatikizapo ine amene.” Kenako, m’bale Bernardo anacitanso zina kuti ayambenso kukhulupilila Yehova na gulu lake. Anayamba kuŵelenga Baibo nthawi zonse, na kusinkhasinkha mozama zimene anali kuŵelengazo. Olo kuti anali kudelabe nkhawa mmene abale na alongo anali kumuonela, iye anali kulalikila nawo komanso kutengako mbali pa misonkhano ya mpingo. M’kupita kwa nthawi, anaikidwanso kukhala mkulu. Ngati inunso munalandila cilango monga m’bale Bernardo, pewani kuika maganizo anu pa kucititsidwa manyazi. M’malo mwake, landilani cilangoco, na kupanga masinthidwe ofunikila. c (Miy. 8:33; 22:4) Mukatelo, mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakufupani cifukwa comamatilabe mokhulupilika kwa iye na gulu lake.

TIKAMAVUTIKA KUGWILIZANA NAWO MASINTHIDWE A GULU

10. Ni kusintha kotani kumene kukanaika kukhulupilika kwa Aisiraeli ena pa mayeso?

10 Nawonso masinthidwe a gulu angayese kukhulupilika kwathu. Tikapanda kusamala, angatilekanitse na Yehova. Mwacitsanzo, onani mmene kusintha kwa zinthu m’Cilamulo ca Mose kunakhudzila Aisiraeli ena. Cilamuloco cisanapelekedwe, mitu ya mabanja ndiyo inali kugwila nchito za ansembe. Anali kumanga maguwa ansembe, na kupeleka nsembe kwa Yehova moimilako mabanja awo. (Gen. 8:20, 21; 12:7; 26:25; 35:1, 6, 7; Yobu 1:5) Koma Cilamuloco citapelekedwa, mitu ya mabanja inaleka kucita mautumiki amenewo. Yehova anadzoza ansembe kucokela m’banja la Aroni kuti ndiwo azipeleka nsembe. Kusintha kumeneku kutayamba kugwila nchito, mutu wa banja amene sanali mbadwa ya Aroni akagwila nchito ya ansembe, anali kuphedwa. d (Lev. 17:3-6, 8, 9) Kodi n’kutheka kuti kusintha kumeneku kungakhale cimodzi mwa zifukwa zimene zinapangitsa Kora, Datani, Abiramu, komanso atsogoleli ena 250 kutsutsa ulamulilo wa Mose na Aroni? (Num. 16:1-3) Sitingakambe motsimikiza. Koma cimene tidziŵa n’cakuti Kora na amuna ena amene anali naye analephela kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Kodi mungacite ciyani ngati masinthidwe a gulu ayesa kukhulupilika kwanu?

Utumiki wa Akohati utasintha, iwo anakhala oimba, alonda a pazipata, komanso oyang’anila nyumba zosungilamo katundu. Ndipo anacita mautumikiwo modzipeleka (Onani ndime 11)

11. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Alevi Acikohati?

11 Labadilani masinthidwe alionse a gulu. Pa ulendo wawo wa m’cipululu, Akohati anali kucita utumiki wapadela kwambili. Nthawi zonse Aisiraeli akamasamuka kupita kwina, ena mwa Akohatiwo anali kunyamula likasa la pangano patsogolo pa anthu. (Num. 3:29, 31; 10:33; Yos. 3:2-4) Umenewo unali mwayi waukulu kwambili. Koma zinthu zinasintha pamene Aisiraeli anakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa. Likasalo silinafunikenso kumanyamulidwa kaŵili-kaŵili. Conco podzafika m’nthawi ya mfumu Solomo, Akohati ena anaikidwa kukhala oimba, alonda a pazipata, komanso oyang’anila nyumba zosungilamo katundu. (1 Mbiri 6:31-33; 26:1, 24) Palibe paliponse m’Baibo pamene paonetsa kuti Akohati anadandaula kapena kufuna malo apamwamba cifukwa cakuti kumbuyoku anali kucita utumiki wapadela. Kodi tiphunzilapo ciyani? Tizilabadila na mtima wonse masinthidwe alionse amene gulu la Yehova lapanga, kuphatikizapo amene akhudza utumiki wathu. Tizisangalala na utumiki uliwonse umene tapatsidwa. Kumbukilani kuti utumiki wanu sindiwo umapangitsa kuti mukhale wofunika kwambili kwa Yehova. Iye amaona kuti kumvela ndiko kofunika kwambili kuposa utumiki uliwonse.—1 Sam. 15:22.

12. Kodi mlongo Zaina anamva bwanji utumiki wake wa pa Beteli utatha?

12 Ganizilani citsanzo ca mlongo Zaina wa ku Middle East, amene anam’sintha utumiki umene anali kuukonda. Iye anauzidwa kukatumikila m’munda pambuyo potumikila pa Beteli zaka zoposa 23. Iye anati: “Sin’nayembekezele kuti utumiki wanga ungasinthe. N’nadziona ngati wopanda pake, ndipo n’nali kungodzifunsa kuti, ‘Kodi n’nalakwanji?’” Zacisoni n’zakuti, abale na alongo ena mumpingo anawonjezela cisoni cake mwa kumuuza kuti: “Ukanakhala kuti unali kucita bwino, sukanacoka pa Beteli.” Mlongo Zaina anakhala wopwetekedwa mtima kwa nthawi yaitali, ndipo anali kulila usiku uliwonse. Koma iye anati: “Sin’nalole kuti niyambe kukayikila cikondi ca Yehova kapena gulu lake.” N’ciyani cinathandiza mlongo Zaina kukhalabe woganiza bwino?

13. Kodi mlongo Zaina anacita ciyani kuti kuthetsa maganizo ake olakwika?

13 Mlongo Zaina anakwanitsa kuthetsa maganizo ake olakwika. Motani? Iye anali kuŵelenga nkhani m’zofalitsa zathu zofotokoza mavuto amene anali kukumana nawo. Nkhani yakuti “Mungathe Kupitirizabe Polefulidwa!” ya mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2001, inam’thandiza kwambili. Nkhaniyo inafotokoza mmene wolemba Baibo Maliko anagonjetsela maganizo ofanana na ake pamene utumiki wake unasintha. Mlongo Zaina anati: “Citsanzo ca Maliko cinanithandiza kwambili kugonjetsa zolefula.” Cina, mlongoyu anali kukhala pafupi na mabwenzi ake. Sanali kudzipatula kapena kumangodzimvela cisoni. Iye anazindikila kuti mzimu wa Yehova umagwila nchito kupitila m’gulu lake, komanso kuti amene amatsogolela amam’konda kwambili. Anazindikilanso kuti gulu la Mulungu limacita zonse zotheka kuti nchito ya Yehova icitike.

14. Ni masinthidwe ati a gulu amene m’bale Vlado anavutika kuwalabadila? Nanga n’ciyani cinam’thandiza?

14 M’bale Vlado wa ku Slovenia wa zaka 73, amene ni mkulu, cinamuvuta kulabadila pamene mpingo wawo anauphatikiza na mpingo wina, komanso poona kuti Nyumba ya Ufumu imene anali kugwilitsa nchito inatsekedwa. Iye anati: “Sin’namvetse cifukwa cimene Nyumba ya Ufumu yokongola conco anaitsekela. Cinaniŵaŵa cifukwa caposacedwa, tinali titaikonzanso. Ndine kalipentala, ndipo n’nagwila nawo nchito yoika zinthu zina zatsopano mu holoyo. Kuwonjezela apo, masinthidwe amenewo anaphatikizapo zinthu zambili zimene sizinali zopepuka kwa ife okalamba.” Nanga n’ciyani cinathandiza m’bale Vlado kulabadila citsogozo cimeneco? Mwini wake anati: “Kulabadila masinthidwe a gulu la Yehova nthawi zonse kumabweletsa madalitso. Masinthidwe amenewa akutikonzekeletsa masinthidwe aakulu a m’tsogolo.” Kodi cikukuvutani kulabadila masinthidwe okhudza kuphatikiza mipingo kapena kusintha kwa utumiki? Dziŵani kuti Yehova akumvetsa mmene mukumvela. Mukamatsatila masinthidwe otelo na kumumamatila Yehova mokhulupilika, komanso gulu limene akuligwilitsa nchito, mosakayika mudzadalitsidwa.—Sal. 18:25.

KHALANIBE OGANIZA BWINO M’ZINTHU ZONSE

15. Kodi tingatani kuti tikhalebe oganiza bwino tikakumana na zokhumudwitsa mumpingo?

15 Pamene tikuyandikila kwambili mapeto a dongosolo lino la zinthu, tingakumane na zokhumudwitsa kucokela kwa abale na alongo mu mpingo. Zokhumudwitsa zimenezo zingayese kukhulupilika kwathu kwa Yehova. Ndiye cifukwa cake tiyenela kukhalabe oganiza bwino. Mukaona kuti Mkhristu mnzanu wakulakwilani, inu musakhumudwe. Mukalandila uphungu, musacite manyazi. M’malo mwake, ulandileni na kupanga masinthidwe ofunikila. Ndipo ngati gulu la Yehova lapanga masinthidwe amene akukhudzani, alandileni na kuwatsatila na mtima wonse.

16. Kodi mungatani kuti muzidalilabe Yehova na gulu lake?

16 N’zotheka kudalilabe Yehova na gulu lake pamene kukhulupilika kwanu kukuyesedwa. Koma kuti mucite zimenezo muyenela kukhalabe oganiza bwino, kutanthauza kuti muyenela kukhala odekha, na kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Khalani na colinga cophunzila zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo amene anakwanitsa kulimbana na mavuto ofanana na anu, ndipo sinkhasinkhani zitsanzo zawo. Pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni. Ndipo musamadzipatule kwa abale na alongo mu mpingo. Mukatelo, Satana sadzatha kukulekanitsani na Yehova komanso gulu lake zivute zitani.—Yak. 4:7.

NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu

a Kukhulupilika kwathu kwa Yehova na gulu lake kungayesedwe, maka-maka pamene takumana na zokhumudwitsa mu mpingo. M’nkhani ino, tikambilane zovuta zitatu, komanso zimene tingacite kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova na gulu lake.

b Maina ena asinthidwa.

c Mungapezenso mfundo zina zothandiza m’nkhani yakuti, “Ngati Munatumikilapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikilenso?” Nkhaniyi mungaipeze mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2009.

d Cilamulo cinafuna kuti mutu wa banja akafuna kupha nyama kuti adye na banja lake, nyamayo anafunika kuitenga kupita nayo ku malo opatulika, kupatulapo ngati akukhala kutali na malo opatulikawo.—Deut. 12:21.