Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

Kodi Moredekai analikodi?

MYUDA wina dzina lake Moredekai anathandiza kwambili pa zocitika zochulidwa m’buku la m’Baibo la Esitere. Iye anali kapolo waciyuda amene anali kuseŵenzela m’nyumba yacifumu ku Perisiya. Uku kunali kuciyambi kwa zaka za m’ma 400 B.C.E., “m’masiku a [Mfumu] Ahasiwero.” (Masiku ano, mfumuyi imadziŵika na dzina lakuti Sasita Woyamba.) Moredekai anavumbula na kulepheletsa ciwembu cakuti mfumu iphedwe. Pofuna kuyamikila, mfumu inakonza zakuti Moredekai apatsidwe ulemu na anthu onse. Patapita nthawi, Hamani mdani wa Moredekai komanso wa Ayuda onse atafa, mfumu Ahasiwero anaika Moredekai kukhala nduna yaikulu. Pokhala nduna yaikulu, iye anakhazikitsa lamulo limene linapulumutsa mtundu wonse wa Ayuda mu Ufumu wa Perisiya kuti usaphedwe.—Esitere 1:1; 2:5, 21-23; 8:1, 2; 9:16.

Akatswili ena a mbili yakale a m’zaka za m’ma 1900 anakamba kuti buku la Esitere ni nthano cabe, komanso kuti kunalibe munthu wa dzina lakuti Moredekai. Koma mu 1941, ofukula za m’matongwe anapeza umboni woonetsa kuti zimene Baibo imakamba zokhudza Moredekai ni zenizeni. Kodi anapeza zotani?

Ocita kafuku-fuku anapeza phale lokhala na dzina la ciperisiya lakuti Marduka (m’Cizungu Moredekai). Cioneka kuti iye anali woyang’anila cuma ku Susani. Arthur Ungnad katswili wa mbili yakale, analemba kuti “aka kanali koyamba dzina lakuti Moredekai” kuchulidwa m’zolemba zimene si mbali ya Baibo.

Kucokela pamene Ungnad analemba lipoti lake, akatswili ena a Baibo amasulila mapale masauzande okhala na mawu aciperisiya. Amodzi mwa mapale amenewo ni miyala ya mumzinda wa Persepolis, imene anaipeza pa matongwe a malo osungilako cuma pafupi na mpanda wa mzindawo. Miyala imeneyo inakhalako mu ulamulilo wa Sasita Woyamba. Mawu olembedwa pa miyalayo ali m’cinenelo ca Aelami, ndipo pakupezeka maina ambili ochulidwa m’buku la Esitere. a

Dzina lakuti Mordecai (Marduka) lolembedwa pa phale la ku Perisiya

Mapale ambili a ku Persepolis amachula munthu wochedwa Marduka, amene anali mlembi pa nyumba yacifumu ku Susani panthawi ya ulamulilo wa Sasita Woyamba. Phale lina linafotokoza kuti Marduka anali womasulila. Izi n’zogwilizana kwambili na zimene Baibo imakamba zokhudza Moredekai. Iye anali nduna imene inali kutumikila m’bwalo la Mfumu Ahasiwero (Sasita Woyamba), ndipo anali kukamba zinenelo ziŵili. Nthawi zonse Moredekai anali kukhala pa cipata ca nyumba yacifumu ku Susani. (Esitere 2:19, 21; 3:3) Cipata cimeneci cinali cacikulu kwambili moti nduna za panyumba ya mfumu zinali kugwilila nchito pomwepo.

Pali kufanana kwakukulu pakati pa Marduka wochulidwa pa mapalewo, komanso Moredekai wochulidwa m’Baibo. Iwo anakhalako panthawi zofanana komanso pamalo amodzi, ndipo onse anali nduna za mfumu pa malo amodzi. Umboni wonsewu uonetsa kuti Marduka, komanso Moredekai wochulidwa m’buku la Esitere anali munthu mmodzi.

a Mu 1992, Pulofesa Edwin M. Yamauchi analemba nkhani imene munali maina 10 opezeka m’buku la Esitere kucokela ku zolemba za ku Persepolis.