Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 45

Mmene Yehova Amatithandizila Kugwila Nchito Yolalikila

Mmene Yehova Amatithandizila Kugwila Nchito Yolalikila

“Adzadziŵabe kuti pakati pawo panali mneneli.”—EZEK. 2:5.

NYIMBO 67 “Lalikila Mau”

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi tingayembekezele ciyani? Nanga sitikayikila za ciyani?

 PAMENE tikugwila nchito yathu yolalikila, tingayembekezele kutsutsidwa na anthu ena. N’zoonekelatu kuti kutsutsidwa kumeneku kungadzawonjeleke kutsogoloku. (Dan. 11:44; 2 Tim. 3:12; Chiv. 16:21) Komabe, sitikayikila kuti Yehova adzatipatsa thandizo lofunikila. Cifukwa ciyani? Yehova wakhala akuthandiza atumiki ake kucita mautumiki awo kaya akhale ovuta motani. Mwacitsanzo, tiyeni tikambilane zocitika pa umoyo wa mneneli Ezekieli, amene analalikila Ayuda amene anali mu ukapolo ku Babulo.

2. Kodi Yehova anawafotokoza bwanji anthu amene Ezekieli anali kuwalalikila? Nanga tikambilane ciyani m’nkhani ino? (Ezekieli 2:3-6)

2 Kodi anthu amene Ezekieli anali kuwalalikila anali otani? Yehova anawafotokoza kuti anali ‘amwano,’ ‘amakani,’ komanso ‘opanduka.’ Anali oipa ngati minga, komanso oopsa ngati zinkhanila. Ndiye cifukwa cake Yehova anauza Ezekieli mobweleza-bweleza kuti: “Usaope”! (Ŵelengani Ezekieli 2:3-6.) Ezekieli anakwanitsa kugwila nchito yolalikila imene anapatsidwa cifukwa (1) anatumidwa na Yehova, (2) anapatsidwa mphamvu na mzimu wa Mulungu, komanso (3) analimbikitsidwa na mawu a Mulungu. Kodi zinthu zitatu zimenezi zinam’thandiza bwanji Ezekieli? Nanga zingatithandize bwanji ifenso masiku ano?

YEHOVA ANATUMA EZEKIELI

3. Ni mawu ati amene ayenela kuti anam’limbikitsa Ezekieli? Nanga Yehova anam’tsimikizila motani kuti adzam’thandiza?

3 Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndikukutumiza.” (Ezek. 2:3, 4) Mawu amenewa ayenela kuti anam’limbikitsa Ezekieli. Cifukwa ciyani? Mosakayikila, iye anakumbukila kuti Yehova anagwilitsa nchito mawu ofananawo posankha Mose na Yesaya kuti akhale aneneli ake. (Eks. 3:10; Yes. 6:8) Ndipo Ezekieli anali kudziŵa mmene Yehova anathandizila aneneli aŵiliwo kucita mautumiki awo ovuta. Conco, pamene Yehova anauza Ezekieli kaŵili konse kuti: “ Ndikukutumiza,” mneneliyu anali na cifukwa cabwino cokhulupilila kuti Yehova adzam’thandiza. Kuwonjezela apo, m’buku la Ezekieli timapezamo mawu angapo akuti: “Yehova analankhula nane.” (Ezek. 3:16) Cina, mawu akuti “Yehova anapitiliza kulankhula nane,” amapezeka maulendo ambili m’buku la Ezekieli. (Ezek. 6:1) Ndithudi, Ezekieli anali wotsimikiza kuti anatumidwa na Yehova. Komanso, popeza iye anali mwana wa wansembe, n’kutheka kuti atate ake anam’simbila mmene Yehova anatsimikizila aneneli ake ena kuti adzawathandiza. Kwa Isaki, Yakobo, na Yeremiya, Yehova analankhula mawu akuti: “Ine ndili ndi iwe.”—Gen. 26:24; 28:15; Yer. 1:8.

4. Ni mfundo yotani imene iyenela kuti inam’limbikitsa Ezekieli?

4 Kodi Aisiraeli anacita ciyani atamva uthenga wa Ezekieli? Yehova anati: “A nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvela, cifukwa iwo safuna kundimvela.” (Ezek. 3:7) Pokana Ezekieli, anthuwo anali kukana Yehova. Mawu amenewo anam’tsimikizila Ezekieli kuti kukana kwa anthuwo sikunatanthauze kuti iye walephela nchito yake monga mneneli. Yehova anatsimikizilanso Ezekieli kuti mawu ake akadzakwanilitsidwa, anthu “adzadziŵa kuti pakati pawo panali mneneli.” (Ezek. 2:5; 33:33) Mosakayika konse, mawu olimbikitsa amenewa anapatsa Ezekieli mphamvu zofunikila kuti acite utumiki wake.

IFENSO TINATUMIDWA NA YEHOVA

Mofanana na Ezekieli, tingakumane na anthu opanda cidwi komanso otsutsa. Koma tidziŵa kuti Yehova ali nafe (Onani ndime 5-6)

5. Malinga na Yesaya 44:8, n’ciyani cimatithandiza kukhala olimba mtima?

5 Nafenso timalimba mtima podziŵa kuti Yehova ndiye anatituma kuti tizilalikila. Iye anatilemekeza poticha kuti “Mboni zake.” (Yes. 43:10) Uwu ni mwayi waukulu kwambili! Monga mmene Yehova anauzila Ezekieli kuti: “Usaope,” nafenso Yehova akutiuza kuti: “Musacite mantha.” N’cifukwa ciyani sitiyenela kuwaopa anthu amene amatitsutsa? Mofanana na Ezekieli, Yehova ndiye anatituma ndipo amatithandiza.—Ŵelengani Yesaya 44:8.

6. (a) Tidziŵa bwanji kuti Yehova adzatithandiza pa nchito yathu? (b) Nanga n’ciyani cimatilimbikitsa na kutithandiza kupeza mphamvu?

6 Yehova analonjeza kuti adzatithandiza. Mwacitsanzo, iye asanakambe kuti: “Inu ndinu Mboni zanga,” anati: “Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe. Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza. Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.” (Yes. 43:2) Tikamacita utumiki wathu, nthawi zina timakumana na mavuto okhala ngati madzi osefukila, komanso mayeso okhala ngati moto. Ngakhale n’conco, na thandizo la Yehova sitileka kulalikila. (Yes. 41:13) Monga zinalili m’nthawi ya Ezekieli, anthu ambili masiku ano amakana uthenga wathu. Koma timadziŵa kuti kukana kwawo sikutanthauza kuti talephela nchito yathu monga atumiki a Mulungu. Timalimbikitsidwa na kupeza mphamvu podziŵa kuti Yehova amakondwela tikapitiliza kulengeza uthenga wake mokhulupilika. Mtumwi Paulo anati: “Aliyense payekha adzalandila mphoto yake mogwilizana ndi nchito yake.” (1 Akor. 3:8; 4:1, 2) Mlongo wina amene watumikila monga mpainiya kwa nthawi yaitali anati: “Nimakhala wacimwemwe podziŵa kuti Yehova amadalitsa khama lathu.”

MZIMU WA MULUNGU UNAM’PATSA MPHAMVU EZEKIELI

Ezekieli akuona masomphenya a galeta la Yehova. Ndipo masomphenyawo akum’patsa cidalilo cakuti Yehova adzam’thandiza kucita utumiki wake (Onani ndime 7)

7. Kodi Ezekieli anali kupindula bwanji akaganizila masomphenya amene anaona? (Onani cithunzi pacikuto.)

7 Ezekieli anaona kuti mzimu wa Mulungu ni wamphamvu kwambili. M’masomphenya, iye anaona mzimu woyela ukugwila nchito pa zolengedwa zauzimu zamphamvu, komanso pa mawilo aakulu a galeta lakumwamba. (Ezek. 1:20, 21) Kodi Ezekieli anatani ataona zimenezi? Iye anati: “Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwelama mpaka nkhope yanga pansi.” Cifukwa cocita mantha, Ezekieli anagwada pansi. (Ezek. 1:28) Nthawi zonse Ezekieli akaganizila masomphenya ocititsa cidwi amenewa, anali kulimbitsa cidalilo cake cakuti mzimu wa Mulungu udzam’thandiza kucita utumiki wake.

8-9. (a) N’ciyani cinacitika kwa Ezekieli Yehova atamuuza kuti ‘aimilile’? (b) Kodi Yehova anam’limbikitsanso motani Ezekieli ponena za gawo lake louma?

8 Yehova anauza Ezekieli kuti: “Iwe mwana wa munthu, imilila kuti ndikulankhule.” Mawu amenewa na mzimu wa Mulungu zinapatsa mphamvu Ezekieli kuti aimilile. Iye analemba kuti: “Mzimu unaloŵa mwa ine ndipo unandiimilitsa.” (Ezek. 2:1, 2) Izi zitacitika komanso pa utumiki wake wonse, Ezekieli anali kutsogoleledwa na “dzanja” la Mulungu, kutanthauza mzimu woyela. (Ezek. 3:22; 8:1; 33:22; 37:1; 40:1) Mzimu wa Mulungu unalimbikitsa Ezekieli pa nchito imene anapatsidwa yolalikila anthu “amakani ndi osamva.” (Ezek. 3:7) Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndacititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo, ndiponso cipumi cako kuti cikhale colimba mofanana ndi zipumi zawo. Ndacititsa cipumi cako kukhala ngati mwala wa dayamondi, colimba kuposa mwala wa nsangalabwi. Usawaope, ndipo usacite mantha ndi nkhope zawo.” (Ezek. 3:8, 9) Zinali monga Yehova akuuza Ezekieli kuti: ‘Usalole kuti ankhutukumve amenewa akulefule. Nikulimbitsa.’

9 Pambuyo pa izi, mzimu wa Mulungu unatengela Ezekieli ku gawo lake lolalikila. Ezekieli analemba kuti: “Dzanja la Yehova linandigwila mwamphamvu.” Zinamutengela mlungu wathunthu kuti mneneli ameneyu amvetsetse uthenga wa Mulungu kotelo kuti akaulengeze mwacidalilo. (Ezek. 3:14, 15) Kenako, Yehova anamulamula kuti apite ku cigwa kumene “mzimu unaloŵa mwa [iye].” (Ezek. 3:23, 24) Apa tsopano Ezekieli anali wokonzeka kuyamba utumiki wake.

MZIMU WA MULUNGU UMATIPATSA MPHAMVU MASIKU ANO

Monga zinalili kwa Ezekieli, n’ciyani cimatithandiza kugwila nchito yolalikila? (Onani ndime 10)

10. Ni thandizo lotani limene timafunikila kuti tipitilize kugwila nchito yolalikila? Nanga n’cifukwa ciyani?

10 Ni thandizo lotani limene timafunikila kuti tigwile nchito yolalikila? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tiganizile zimene zinacitika kwa Ezekieli. Asanayambe nchito yake yolalikila, mzimu wa Mulungu unam’patsa mphamvu zofunikila. Masiku anonso, timakwanitsa kugwila nchito yolalikila kokha na thandizo la mzimu wa Mulungu monga zinalili kwa Ezekieli. N’cifukwa ciyani tikutelo? Cifukwa Satana akucita nafe nkhondo kuti aimitse nchito yathu yolalikila. (Chiv. 12:17) M’kaonedwe kaumunthu, zimaoneka monga Satana amatiposa mphamvu. Koma pamene tigwila nchito yathu yolalikila timamugonjetsa! (Chiv. 12:9-11) Kodi zimacitika motani? Tikamagwila nchito yolalikila, timaonetsa kuti siticita mantha na ziwopsezo za Satana. Nthawi iliyonse tikalalikila, timamugonjetsa Satana. Ndiye kodi ni mfundo iti yosatsutsika imene imaonekela tikamalalikilabe ngakhale kuti anthu amatitsutsa? Ni mfundo yakuti mzimu woyela ndiwo umatipatsa mphamvu, komanso kuti Yehova akutiyanja.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:14.

11. Kodi mzimu wa Mulungu umatithandiza bwanji? Nanga tingacite ciyani kuti tipitilize kuulandila?

11 Kodi kudziŵa kuti Yehova mophiphilitsa analimbitsa nkhope komanso cipumi ca Ezekieli kutiphunzitsanso ciyani? Tiphunzilapo kuti mzimu wa Mulungu ungatithandize kuthana na vuto lililonse limene tingakumane nalo mu ulaliki. (2 Akor. 4:7-9) Nanga tiyenela kucita ciyani kuti tipitilize kulandila mzimu wa Mulungu? Tiyenela kuupempha mobweleza-bweleza tili na cidalilo cakuti Yehova adzamva mapemphelo athu. Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti: “Pemphanibe, . . . pitilizani kufunafuna, . . . gogodanibe.” Tikatelo, Yehova “adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:9, 13; Mac. 1:14; 2:4.

MAWU A MULUNGU ANAM’LIMBIKITSA EZEKIELI

12. Malinga n’kunena kwa Ezekieli 2:9–3:3, kodi mpukutu wochulidwa pa lembali unacokela kuti? Nanga kodi mu mpukutuwo munali ciyani?

12 Ezekieli analimbikitsidwa na mzimu wa Mulungu komanso mawu a Mulungu. M’masomphenya, iye anaona dzanja litagwila mpukutu. (Ŵelengani Ezekieli 2:9–3:3.) Kodi mpukutuwo unacokela kuti? Nanga munali ciyani? Kodi unam’limbikitsa motani Ezekieli? Tiyeni tione. Mpukutuwo unacokela ku mpando wacifumu wa Mulungu. N’kutheka kuti Yehova anagwilitsa nchito mmodzi wa angelo anayi amene Ezekieli anaona poyamba kuti am’patse mpukutuwo. (Ezek. 1:8; 10:7, 20) Mu mpukutuwo munali mawu a Mulungu—inde uthenga waciweluzo umene Ezekieli anafunika kukaulengeza kwa Aisiraeli opanduka amene anacoka ku ukapolo. (Ezek. 2:7) Uthengawo unali wolembedwa kumbali zonse ziŵili, kumaso na kumbuyo kwa mpukutuwo.

13. Kodi Yehova anauza Ezekieli kuti aucite ciyani mpukutu? Nanga n’cifukwa ciyani mpukutuwo unali wotsekemela?

13 Yehova anauza mneneli wake kuti adye mpukutuwo ‘kuti mimba yake ikhute.’ Ezekieli anamvela, ndipo anadya mpukutu wonsewo. Kodi mbali imeneyi ya masomphenya itanthauza ciyani? Ezekieli anafunika kuumvetsetsa uthenga umene anali kudzaulengeza. Iye anafunika kuukhulupilila uthengawo kuti um’sonkhezele kukaulengeza kwa Aisiraeli. Ezekieli ataudya mpukutuwo, anaona kuti “unali wotsekemela ngati uci.” (Ezek. 3:3) Cifukwa ciyani? Kwa Ezekieli, kuimilako Yehova unali mwayi wotsekemela, kapena wokondweletsa. (Sal. 19:8-11) Iye anamuyamikila kwambili Yehova pomusankha kuti akhale mneneli wake.

14. N’ciyani cinam’thandiza Ezekieli kuti akhale wokonzeka kugwila nchito yake?

14 Patapita nthawi, Yehova anauza Ezekieli kuti: “Usunge mumtima mwako mawu anga onse amene ndikukuuza.” (Ezek. 3:10) Na mawu amenewa, Yehova anauza Ezekieli kuti azikumbukila mumtima wake mawu olembedwa mu mpukutuwo na kuwasinkhasinkha. Kucita zimenezo kunam’limbikitsa kwambili Ezekieli. Cina, mu mpukutuwo munali uthenga wamphamvu umene anafunika kukaulengeza kwa anthu. (Ezek. 3:11) Uthenga wa Mulungu utakhazikika mu mtima mwake komanso pa milomo yake, Ezekieli anali wokonzeka kugwila nchito yolalikila mpaka kumapeto kwake.—Yelekezelani na Salimo 19:14.

MAWU A MULUNGU AMATILIMBIKITSA MASIKU ANO

15. Kuti tizitha kupilila, kodi tiyenela ‘kusunga ciyani mumtima mwathu’?

15 Kuti tizitha kupilila mu ulaliki, nafenso tiyenela kupitiliza kulimbikitsidwa na mawu a Mulungu. Tiyenela ‘kusunga mu mtima mwathu’ zonse zimene Yehova amatiuza. Masiku ano, Yehova amakamba nafe kupitila m’Mawu ake Baibo. Kodi tingacite ciyani kuti mawu a Mulungu apitilize kutsogolela maganizo athu, komanso zocita zathu?

16. Kodi tiyenela kucita nawo ciyani Mawu a Mulungu? Nanga tingacite ciyani kuti mawuwo tiwamvetsetse?

16 Tikadya cakudya cakuthupi, cakudyaco cimagaika, ndipo matupi athu amakhala athanzi. Mofananamo, tikamaŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkhasinkha, cikhulupililo cathu cimalimba. Izi n’zimene tikuphunzilapo ponena za mpukutu. Ponena za mawu a Mulungu, Yehova amafuna kuti “mimba [yathu] ikhute” na mawuwo. Kutanthauza kuti tiyenela kuwamvetsetsa bwino Mawu ake. Tingacite zimenezo mwa kupemphela, kuŵelenga, na kusinkhasinkha. Coyamba, timapemphela kuti tikonzekeletse mtima wathu kulandila mawu a Mulungu. Kenako, timayamba kuŵelenga Baibo. Cotsatila, timaima kuti tisinkhesinkhe zimene taŵelengazo. Kodi padzakhala zotulukapo zotani? Tikamasinkhasinkha kwambili, mtima wathu wophiphilitsa udzawamvetsa bwino kwambili Mawu a Mulungu.

17. N’cifukwa ciyani kusinkhasinkha zimene taŵelenga m’Baibo n’kofunika?

17 N’cifukwa ciyani kuŵelenga Baibo na kusinkhasinkha n’kofunika? Cifukwa kucita zimenezo kumatipatsa mphamvu zofunikila kuti tilalikile uthenga wa Ufumu pali pano, komanso kumatikonzekeletsa kudzalengeza uthenga wa ciweluzo woŵaŵa m’tsogolomu. Cina, tikamasinkhasinkha makhalidwe a Yehova osililika, ubale wathu na iye umalimba kwambili. Zotulukapo n’zakuti timakhala na mtendele wa mumtima komanso okhutila, zimene n’zokondweletsa kwambili.—Sal. 119:103.

CIMENE CIMATILIMBIKITSA KUPILILA

18. Kodi anthu a m’gawo lathu adzazindikila ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani?

18 Mosiyana na Ezekieli, ife sindife aneneli. Ngakhale n’telo, ndife ofunitsitsa kupitiliza kulengeza uthenga wouzilidwa wa Yehova wopezeka m’Mawu ake, mpaka pamene iye mwini adzanene kuti nchito yolalikila yatha. Nthawi ya ciweluzo ikadzafika, anthu m’gawo lathu sadzakhala na cifukwa codandaulila kuti sanacenjezedwe, kapena kuti Mulungu anawanyalanyaza. (Ezek. 3:19; 18:23) M’malo mwake, iwo adzazindikila kuti uthenga umene tinali kulalikila unali wocokela kwa Mulungu.

19. N’ciyani cimatipatsa mphamvu kuti ticite utumiki wathu?

19 N’ciyani cidzatipatsa mphamvu kuti ticite utumiki wathu? Ni zinthu zitatu zija zimene zinalimbikitsa Ezekieli. Sitileka kulalikila cifukwa timadziŵa kuti tatumidwa na Yehova, mzimu wa Mulungu umatipatsa mphamvu, komanso timalimbikitsidwa na Mawu a Mulungu. Na thandizo la Yehova, timalimbikitsidwa kupitiliza kugwila nchito yolalikila na kupilila “mpaka pa mapeto.”—Mat. 24:13.

NYIMBO 65 Pita Patsogolo

a M’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zimene zinathandiza mneneli Ezekieli kugwila nchito yolalikila imene anapatsidwa. Pokambilana mmene Yehova anathandizila mneneli wake ameneyu, tidzalimbitsa cidalilo cathu cakuti Yehova adzatithandiza nafenso kugwila nchito yathu yolalikila.