Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 47

Musalole Ciliconse Kukulekanitsani na Yehova

Musalole Ciliconse Kukulekanitsani na Yehova

“Cikhulupililo canga cili mwa inu Yehova.” —SAL. 31:14.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi tidziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kutiyandikila?

 YEHOVA akutipempha kuti timuyandikile. (Yak. 4:8) Iye amafuna kuti akhale Mulungu wathu, Tate wathu, komanso Bwenzi lathu. Amayankha mapemphelo athu, na kutithandiza panthawi zovuta. Ndipo amagwilitsa nchito gulu lake kuti atiphunzitse na kutiteteza. Koma kodi tingacite ciyani kuti timuyandikile Yehova?

2. Kodi tingamuyandikile bwanji Yehova?

2 Yehova tingamuyandikile mwa kupemphela kwa iye, komanso kuŵelenga Mawu ake na kuwasinkhasinkha. Tikatelo, tidzam’konda kwambili na kumuyamikila. Cina, tidzalimbikitsidwa kumumvela na kum’patsa citamando comuyenelela. (Chiv. 4:11) Tikam’dziŵa bwino Yehova, tidzakulitsa cidalilo cathu pa iye na gulu lake limene wapeleka kuti lizitithandiza.

3. Kodi Mdyerekezi amayesa bwanji kutilekanitsa na Yehova? Nanga n’ciyani cidzatithandiza kuti tisamusiye Mulungu wathu na gulu lake? (Salimo 31:13, 14)

3 Komabe, Mdyerekezi amayesa kutilekanitsa na Yehova, maka-maka tikakumana na mavuto. Kodi amacita bwanji zimenezi? Mwapang’ono-pang’ono iye amacepetsa cidalilo cathu pa Yehova na gulu lake. Koma n’zotheka kukaniza macenjela ake. Cikhulupililo cathu mwa Yehova cikakhala colimba, komanso ngati cidalilo cathu mwa iye n’cosagwedela, sitidzamusiya Mulungu wathu na gulu lake.—Ŵelengani Salimo 31:13, 14.

4. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, tikambilane mayeso atatu amene timakumana nawo ocokela kwa anthu osalambila Mulungu. Mayeso amenewo angacepetse cidalilo cathu pa Yehova na gulu lake. Kodi mayesewo angatilekanitse bwanji na Yehova? Nanga tingacite ciyani kuti tikanize mayeso a Satana amenewo?

TIKAKUMANA NA MAVUTO

5. Kodi mavuto angacepetse bwanji cidalilo cathu pa Yehova na gulu lake?

5 Nthawi zina, timakumana na mavuto monga kutsutsidwa m’banja kapena nchito kutha. Kodi mavuto otelo angacepetse bwanji cidalilo cathu pa gulu la Yehova, komanso kutikanganula kwa iye? Mavutowo akatiumilila, tingathedwe nzelu ndiponso tingapsinjike maganizo. Satana amapezelapo mwayi, na kutipangitsa kuti tiyambe kukaikila ngati Yehova amatikonda. Iye amafuna kutipangitsa kuti tiziganiza kuti Yehova kapena gulu lake ndiye amacititsa mavuto amene timakumana nawo. Zofanana na zimenezi zinacitika kwa Aisiraeli ku Iguputo. Poyamba, iwo anakhulupilila kuti Yehova anasankha Mose na Aroni kuti awatsogolele kucoka mu ukapolo. (Eks. 4:29-31) Koma pambuyo posautsidwa kwambili na Farao, iwo anaimba mlandu Mose na Aroni cifukwa covutika. Anati: “Mwatinunkhitsa pamaso pa Farao ndi atumiki ake, moti mwawapatsa lupanga m’manja mwawo kuti atiphe.” (Eks. 5:19-21) N’zomvetsa cisoni kuti iwo anaimba mlandu atumiki a Mulungu okhulupilika amenewa. Ngati inunso mwakhala mukupilila mavuto kwa nthawi yaitali, kodi mungacite ciyani kuti mulimbitse cidalilo canu pa Yehova na gulu lake?

6. Kodi tiphunzilapo ciyani kwa mneneli Habakuku pa nkhani yopilila mavuto? (Habakuku 3:17-19)

6 M’khuthulileni za mumtima mwanu Yehova m’pemphelo, ndipo yang’anani kwa iye kuti akuthandizeni. Habakuku anakumana na mavuto ambili. Pa nthawi ina, iye anakayikila ngati Yehova amasamala za iye. Conco, anauza Yehova m’pemphelo mmene anali kumvela. Iye anati: “Inu Yehova, kodi ndidzalilila thandizo koma inu osandimva kufikila liti? . . . N’cifukwa ciyani mukupitiliza kuyang’ana khalidwe loipa?” (Hab. 1:2, 3) Yehova anayankha pemphelo locokela pansi pamtima la mtumiki wake wokhulupilika ameneyu. (Hab. 2:2, 3) Habakuku ataganizila nchito zopulumutsa za Yehova, anakhalanso wacimwemwe. Iye anakhala wotsimikiza kuti Yehova amasamaladi za iye, komanso kuti adzam’thandiza kupilila mavuto. (Ŵelengani Habakuku 3:17-19.) Kodi tiphunzilapo ciyani pamenepa? Tikakumana na mavuto, tizipemphela kwa Yehova na kumuuza mmene tikumvela. Kenako, tiziyang’ana kwa iye kuti atithandize. Tikatelo, tidzakhala na cidalilo conse kuti Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila kuti tipilile. Ndipo tikaona mmene watithandizila, cikhulupilila cathu mwa iye cidzalimbilako.

7. Kodi acibale a mlongo Shirley anayesa kum’pangitsa kukayikila ciyani? Nanga n’ciyani cinam’thandiza kuti asataye cikhulupililo cake mwa Yehova?

7 Musaleke kucita zauzimu. Onani mmene kucita zimenezi kunathandizila mlongo wina dzina lake Shirley, wa ku Papua New Guinea, pamene anakumana na mavuto. b Banja lake linali losauka, ndipo nthawi zina anali kuvutika kuti apeza cakudya. Wacibale wake wina anayesa kucepetsa cidalilo cake mwa Yehova. Iye anamuuza kuti: “Umakamba kuti mzimu woyela wa Mulungu umakuthandizani, ndiye thandizolo lili kuti? Ndinu osaukabe. Umangotaya nthawi na nchito yako yolalikila.” Mlongo Shirley anati: “N’nadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amasamaladi za ife kapena ayi?’ Nthawi yomweyo n’napemphela kwa Yehova na kuumuza zonse za mumtima mwanga. Sin’naleke kuŵelenga Baibo na zofalitsa zathu, kulalikila, komanso kupezeka ku misonkhano.” Posakhalitsa, anazindikila kuti Yehova anali kusamaliladi banja lake. Iwo sanasoŵepo cakudya, ndipo anali acimwemwe. Mlongo Shirley anati: “N’naona kuti Yehova anali kuyankha mapemphelo anga.” (1 Tim. 6:6-8) Inde, ngati mupitiliza kucita zauzimu, inunso simudzalola mavuto kapena zikayiko kukukanganulani kwa Yehova.

ABALE OTSOGOLELA AKACITILIDWA MOPANDA CILUNGAMO

8. N’ciyani cingacitikile abale otsogolela m’gulu la Yehova?

8 Kupitila m’manyuzipepala, pa wailesi, pa TV, komanso pa Intaneti, adani athu amafalitsa mabodza onena za abale otsogolela m’gulu la Yehova. (Sal. 31:13) Abale ena amangidwa na kuweluzidwa kuti ni ophwanya malamulo. Zaconco zinawacitikila Akhristu a m’zaka za zana loyamba pamene mtumwi Paulo anamuimba mlandu wabodza na kum’manga. Kodi iwo anacita ciyani?

9. Kodi Akhristu ena anacita ciyani pamene Paulo anali m’ndende?

9 Akhristu ena m’zaka za zana loyamba, analeka kum’cilikiza Paulo pamene anali m’ndende ku Roma. (2 Tim. 1:8, 15) Cifukwa ciyani? Kodi anali kucita manyazi na Paulo cifukwa anthu anali kumuona ngati wocita zoipa? (2 Tim. 2:8, 9) Kapena anali kuopa kuti nawonso angazunzidwe? Kaya cifukwa cawo cinali cotani, ganizilani mmene Paulo anamvela. Iye anali atapilila mavuto ambili, ngakhale kuika moyo wake pa ciwopsezo cifukwa ca iwo. (Mac. 20:18-21; 2 Akor. 1:8) Conde, tisakhale monga Akhristu amene anasiya Paulo panthawi imene anali kufunikila thandizo. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani abale otsogolela akamazunzidwa?

10. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani abale otsogolela akamazunzidwa? Nanga n’cifukwa ciyani?

10 Tizikumbukila cifukwa cake timazunzidwa, komanso amene amakupangitsa. Lemba la 2 Timoteyo 3:12 limati: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” Conco, sitiyenela kudabwa kuti Satana amaukila kwambili abale otsogolela. Iye amacita zimenezi pofuna kuwononga cikhulupililo cawo, komanso kuti atiwopseze.—1 Pet. 5:8.

Pamene Paulo anali m’ndende, molimba mtima Onesiforo anabwela kudzam’limbikitsa. Masiku ano, abale na alongo amalimbikitsa Akhristu anzawo amene ali m’ndende monga tikuonela pa cithunzi apa (Onani ndime 11-12)

11. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Onesiforo? (2 Timoteyo 1:16-18)

11 Pitilizani kuthandiza abale anu, na kuwamamatila mokhulupilika. (Ŵelengani 2 Timoteyo 1:16-18.) Onesiforo, Mkhristu wa m’zaka za zana loyamba anacita zinthu mosiyana na Akhristu ena pamene Paulo anali m’ndende. Iye “sanacite manyazi ndi maunyolo [a Paulo].” M’malo mwake, Onesiforo anafuna-funa Paulo mwakhama, ndipo atam’peza anapeleka thandizo lofunikila kwa iye. Pocita zimenezo, iye anaika moyo wake pa ciwopsezo. Kodi tiphunzilapo ciyani? Tisalole kuti kuopa anthu kutilepheletse kuthandiza abale athu amene akuzunzidwa. Koma tiziwakhalila kumbuyo na kuwathandiza. (Miy. 17:17) Iwo afunikila cikondi cathu na thandizo lathu.

12. Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca abale na alongo ku Russia?

12 Ganizilani mmene abale na alongo athu ku Russia akuthandizila abale awo amene ali m’ndende. Ena mwa abale athu akapita kukaonekela pamaso pa khoti, abale na alongo ambili amapita kukhotiko kukawalimbikitsa. Kodi tiphunzilapo ciyani? Abale otsogolela akanenezedwa, akamangidwa, kapena akamazunzidwa, tisamacite mantha. Koma tiziwapemphelela, kuthandiza a m’banja mwawo, komanso kuyesa kupeza njila zina za mmene tingawathandizile.—Mac. 12:5; 2 Akor. 1:10, 11.

PAMENE ENA AKUTITONZA

13. Kodi anthu otonza angacepetse bwanji cidalilo cathu pa Yehova na gulu lake?

13 Acibale osakhulupilila, anzathu a kunchito, kapena kusukulu, angatitonze cifukwa ca nchito yathu yolalikila, kapena cifukwa cotsatila malamulo a Yehova. (1 Pet. 4:4) Mwina iwo angakambe kuti: “Iwe nilibe nawe vuto, koma cipembedzo cako cimakhwimitsa kwambili zinthu, ndipo n’cacikale-kale.” Ena angafune kutipeza zifukwa poona kuti sitiyanjana na ocotsedwa. Iwo angatiuze kuti: “Zimene mukucitazi si cikondi ayi.” Mawu ngati amenewa angabyale mbewu zacikayiko mu mtima mwathu. Tingayambe kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndiye kuti Yehova amayembekezela zoculuka kwa ine? Kodi gulu lake limaumitsa kwambili zinthu?’ Ngati izi n’zimene zikukucitikilani, kodi mungacite ciyani kuti mukhalebe wokhulupilika kwa Yehova na gulu lake?

Yobu sanakhulupilile mabodza amene anzake abodza anali kukamba pomunena. M’malo mwake, iye anali wofunitsitsa kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova (Onani ndime 14)

14. Kodi tiyenela kucita ciyani anthu akamatinyoza cifukwa cotsatila malamulo a Yehova? (Salimo 119:50-52)

14 Musaleke kutsatila malamulo a Yehova. Yobu anali kutsatilabe malamulo a Yehova ngakhale kuti anthu ena anali kumunyoza cifukwa cocita zimenezo. Mmodzi wa anzake a Yobu abodza anayesa kum’pangitsa kuganiza kuti Mulungu analibe nazo nchito zakuti iye anali kutsatila malamulo a Mulungu kapena ayi. (Yobu 4:17, 18; 22:3) Koma Yobu sanawakhulupilile mabodzawo. Iye anadziŵa kuti malamulo a Yehova a cabwino na coipa ni opindulitsa, ndipo anali wotsimikiza mtima kuwatsatila. Sanalole kuti anthu ena am’pangitse kukhala na mtima wogaŵanika. (Yobu 27:5, 6) Kodi ife tiphunzilapo ciyani? Tisalole kuti anthu onyoza atipangitse kuyamba kukayikila malamulo a Yehova. Ganizilani zimene zakucitikilani pa umoyo. Mobweleza-bweleza mwaona mmene malamulo a Yehova a cabwino na coipa akupindulilani, si conco kodi? Nthawi zonse khalani ofunitsitsa kuyendela pamodzi na gulu limene limatsatila malamulowo. Mukatelo, anthu onyoza ngakhale atayesa bwanji, sadzakwanitsa kutilekanitsa na Yehova.—Ŵelengani Salimo 119:50-52.

15. N’cifukwa ciyani mlongo Brizit anali kunyozedwa?

15 Onani citsanzo ici ca mlongo Brizit wa ku India. Acibale ake anali kumunyoza cifukwa ca cikhulupililo cake. Atangobatizika mu 1997, mwamuna wake wosakhulupilila anacotsedwa nchito. Conco, mwamuna wakeyo anasankha kuti iye, mkazi wake Brizit, na anawo aakazi asamuke n’kukhala na makolo a mwamunayo, amene anali kukhala mumzinda wina. Kumeneko, mlongo Brizit anakumana na mavuto aakulu. Popeza mwamuna wake sanali panchito, mlongoyu anafunika kuseŵenza maola ambili kuti azisamalila banja lake. Kuwonjezela apo, mpingo wosonkhanako unali pa mtunda wa makilomita 350. Ndipo zacisoni n’zakuti acibale a mwamuna wake anali kumutsutsa cifukwa ca cikhulupililo cake. Zinthu zinafika poipa kwambili cakuti mlongo Brizit na banja lake anasamukanso. Koma mwatsoka lanji, mwamuna wake anamwalila. Ndipo patapita nthawi, mwana wake wamkazi anamwalilanso na khansa ali na zaka 12 cabe. Kuwonjezela pa mavutowa, acibale a mlongo Brizit anamuimba mlandu pa zimene zinacitikazo. Iwo anali kukamba kuti iye akanapanda kukhala wa Mboni za Yehova, sakanakumana na mavuto onsewo. Ngakhale n’telo, iye anadalilabe Yehova, na kukhalabe wokhulupilika ku gulu lake.

16. Kodi mlongo Brizit anadalitsidwa bwanji cifukwa cokhalabe wokhulupilika kwa Yehova na gulu lake?

16 Popeza kuti kumene mlongo Brizit anali kukhala kunalibe mpingo pafupi, woyang’anila dela anam’limbikitsa kuti azilalikila anthu a m’dela lake, na kucititsa misonkhano m’nyumba yake. Poyamba, iye anaona monga sadzakwanitsa. Koma anatsatila malangizo amene anapatsidwa. Anali kuuzako ena uthenga wabwino, kucititsa misonkhano m’nyumba yake, na kupatula nthawi yocita kulambila kwa pabanja na ana ake. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iye anakwanitsa kuyambitsa na kutsogoza maphunzilo ambili a Baibo, ndipo ena mwa iwo anabatizika. Mu 2005 anayamba upainiya wanthawi zonse. Cifukwa codalila Yehova, na kukhala wokhulupilika ku gulu lake, mlongoyu anadalitsidwa. Ana ake akutumikila Yehova mokhulupilika, ndipo lomba kudelalo kuli mipingo iŵili. Mlongo Brizit sakayikila kuti Yehova ndiye anam’patsa mphamvu kuti apilile mavutowo, komanso citonzo ca acibale ake.

KHALANIBE WOKHULUPILIKA KWA YEHOVA NA GULU LAKE

17. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani?

17 Satana amafuna kuti tiziona kuti Yehova amatisiya tikakumana na mavuto, komanso kuti kukhalabe m’gulu lake kungapangitse zinthu kuipilaipila pa umoyo wathu. Iye amafuna kuti tizicita mantha abale otsogolela akamanenezedwa, akamazunzidwa, kapena akaponyedwa m’ndende. Ndipo kupyolela mwa anthu onyoza, iye amafuna kuti tizikayikila malamulo a Yehova na gulu lake. Komabe, ife tidziŵa bwino ziwembu zake, ndipo sitipusitsidwa nazo. (2 Akor. 2:11) Conco, yesetsani kukaniza mabodza a Satana, ndipo khalanibe wokhulupilika kwa Yehova na gulu lake. Kumbukilani kuti Yehova sadzakusiyani ngakhale pang’ono. (Sal. 28:7) Motelo, musalole ciliconse kuti cikulekanitseni na Yehova!—Aroma 8:35-39.

18. Kodi tidzakambilana ciyani m’nkhani yotsatila?

18 M’nkhani ino, takambilana mayeso amene angabwele kucokela kwa anthu osalambila Mulungu. Koma cidalilo cathu mwa Yehova na gulu lake cingaikidwe pa mayeso cifukwa ca mavuto ocokela kwa abale na alongo. Kodi tingathane nawo bwanji mavuto amenewo? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

a Kuti tipilile mokhulupilika m’masiku ano otsiliza, tiyenela kupitiliza kukhulupilila Yehova na gulu lake. Mdyerekezi amagwilitsa nchito mayeso kuti atipangitse kuleka kukhulupilila Mulungu. M’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zimene Mdyerekezi amagwilitsa nchito potiyesa, komanso zimene tingacite kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova na gulu lake.

b Maina ena asinthidwa.